Mawu Otsogolera Mndandanda wa maphunziro oti aphunziridwe m’kotala ino, “Kuyenda ndi Yesu,” ndi wachokera m'buku la Steps to Christ. Bukuli likhoza kuwerengedwa, mutu ndi mutu, ngati ndemanga pa maphunziro a Malemba.Ophunzira ena a Sabata Skulu adzakumbukira nthawi yomwe nkhaniyi idakambidwa mu kota yoyamba ya chaka cha 1980. Ndichikondwero chathu kuiperekanso phunziroli ndi kapangidwe katsopano ndi zipangizo zina zowonjezera, koma ndi zoonadi zozama zomwezo zomwe zidanenedwa kalekale.Kawirikawiri anthu amaganiza kuti Atate wawo wakumwamba ndi wouma mtima komanso otalikana nawo, woweruza wankhanza komanso wouma mtima. Iwo samawona kuzama kwa chikondi Chake pa iwo, komanso chisamaliro Chake chachikondi chomwe ali nacho mumtima Mwake pa ana ake onse.Chikondi cha Mulungu chiyenera kukhala chinthu choyamba chomwe chikuwonetsedwa. Kenako chiyenera kutsatirapo ndi mfundo yakuti wochimwayo ndi wopanda thandizo komanso wopanda chiyembekezo, ndipo ndiwosowa Mpulumutsi. Moyo wa Khristu, yemwe anabwera kudzapulumutsa ochimwa, umasonyeza kuti pali njira yotsimikizika yobwerera kwa Atate wakumwamba.Mitu yomwe yakambidwa m'maphunzirowa ikukhudzana ndi zochitika zazikulu m'moyo wachikhristu ndipo makamaka imagwirizana ndi wokhulupirira watsopano m'chikhulupiriro amene akufuna kukula mu chisomo. Okhulupirira onse ayenera kuwunikanso mituyi nthawi ndi nthawi—osati ku phindu laokha, komanso kuti adziwe nawonso njira yabwino kwambiri yothandizira ena kubwera kwa Khristu.Kupereka mfundo za choonadi mwadongosolo kungathandize munthu kumvetsa bwino ndi kuzilandira izo, ndipo kumathandiza munthu kulandiridwa kukhala membala wa mpingo. Koma ngati munthu wotereyu salumikizidwa ndi Khristu, alibe moyo weniweni—moyo wosatha. Zoonadi, “yekhayo amene akhulupirira Mwanayo ali ndi moyo wosatha” (Yohane 3:36).Aliyense wa Sabata Skulu ayenera kukhala ndi umboni wa Mzimu ndi mzimu wake kuti walandiridwadi m'banja la Mulungu. Aliyense ayenera kuzindikira kuti chitsanzo chake, kudalira kwawo kosalekeza pa Atate wakumwamba, nthawi zonse komanso pazinthu zonse, kuyenera kukhala kwenikweni komanso koonekera mmachitachita. Pakufunika zambiri kuposa chikondi chofooka cha anthu. Onse amafunikira chikondi cha Mulungu—chikondi chopanda dyera cha Mulungu—chobzalidwa mumtima ndi m'miyoyo yawo kuti akonde monga momwe Iye anakondera.Izi zikhale zodutsamo za moyo za membala aliyense wa m'Sabata Skulu.Nthambi ya Sabata Skulu ya General Conference