Ntchito komanso Moyo Vesi Loloweza: ‘Koma onse amene anamulandira Iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupilira dzina lake;’(Yohane 1:12)
Zowerenga Zoonjezera:
Steps to Christ, pp. 7783
“Mzimu wa Khristu wachikondi wozipereka msembe ndi mzimu womwe umalamulira kumwamba ndi fungo lokoma mukufukiza kwake. Uwu ndi mzimu umene otsatira ake akhristu akuyenera kuonetsera, ntchito imene ayenera kuichita.”—Steps to Christ, p.77.
1. MOYO KOMANSO KUUNIKA Loyamba, Ogasti, 23
a. Ndichiyani chimene chinanyozeledwa ndi mtima wachibadwa— ndipo izi zinali ndi zotsatira zanji? Yohane1:4,5.“Mulungu ndi gwero la moyo ndi kuunika ndi chisangalaro kudziko lonse lapansi monga milezo ya kuunika yochokera ku dzuwa, monga akasupe amadzi otuluka kuchokera ku misinje yamoyo, madalitso amatuluka kuchokera kwa Iye kupita kuzolengedwa zake zonse. Ndipo kulikonse komwe moyo wa Mulungu ukhala m'mitima ya anthu, udzayenda kupita kwa ena mu chikondi ndi mdalitso.”— Steps to Christ, p. 77.b. Pamene chikondi cha Khristu chili mumtima, Ndichiyani chidzaonekere m’moyo? 2 Akolinto2:14,15; 5:14.“Pamene chikondi cha Khristu chikuonetseredwa mumtima, monga ngati zonunkhira zokoma sichingabisidwe. Chikoka chake chopatulika chidzakhala pa onse amene tikulumikizana nawo. Mzimu wa Khristu mumtima monga ngati msinje muchipululu, umayenda kutsitsimutsa onse ndi kukopa iwo amene ali okonzekera kuchionongeko, kukhala ndi khumbo lokumwa ku madzi a moyo.”—Ibid.“Lolani dziko lione kuti ife sitinamizidwe muchidwi cha ife eni, koma kuti tikukhumba ena kugawana nawo mdalitso wathu ndinso mwayi wathu. Aloleni iwo kuona kuti chipembezo chathu sichimatipanga ife kukhala opanda chifundo kapena ozikweza.Tilole onse amene amazitcha kuti a Khristu, atumikire monga Iye mwini amachitira kuubwino wa anthu.”—The Desire of Ages, p. 152.
2. OTENGA NAWO MBALI MU CHISOMO CHAKE Lachiwiri, Ogasti 24
a. Pamene tamulandira Yesu monga mpulumutsi wathu, ndi chosowa chanji chomwe chimaperekedwa? Yohane 1:12,13; 1 Akolinto 1:4,5; Aroma 5:1,2.“Iwo amene ali ogawana nawo chisomo cha khristu azakhala okonzeka kupereka nsembe iliyonse, kuti ena omwe Iye anawafera akagawane nawo mphatso za kumwamba. Iwo azachita zonse zomwe angakwanitse kulipanga dziko kukhala lokoma kukhalamo. Mzimu umenewu ndiweniweni wotuluka ku moyo wotembenuka moona. Munthu akangobwera kwa Khristu, nthawi yomweyo mtima wake umayamba kukhala ndi chilakolako chofuna kudziwitsa ena za Bwenzi lamtengo wapatali limene wapeza mwa Yesu; choonadi chopulumutsa ndi chopatulitsa sichingabisike m’mtima mwake. Pamene tabvekedwa ndi chilungamo cha Khristu ndi kuzazidwa ndi chimwemwe cha mzimu wake wokhala mwa Iye, sitingakwanitse kuusunga mtendere wathu. Pamene talawa ndikuona kuti Ambuye ndi wabwino tidzakhala ndi chinachake cholankhula. Monga Filipo pamene anapedza mpulumutsi, tidzaitanira ena mukupezeka kwake.”— Steps to Christ, p. 78b. Pamene tikukumana ndi mabvuto ndi zovuta, ndi uphungu wanji womwe tikupeza kwa mtumwi Paulo? Ahebri 4:16“Yesu amaziwa zosowa za ana ake, ndipo Iye amakonda kumvetsera kupemphero lawo. Tilore ana kuchoka kudziko lapansi ndi zilizonse zimene zingachotse malingaliro kuchoka kwa Mulungu, ndipo tiwalore iwo kuti amve kuti iwo ali okha pamodzi ndi Mulungu kuti maso ake amaona mkati mwa mtima, ndi kuwelenga zokhumba za moyo, ndikuti angathe kulankhula ndi Mulungu,”—Sons and Daughters of God, p. 121.c. Pamene takhala mwana wa Mulungu, ndi chiyani tingangongole kwa ena? Aroma1:14,15.“Ndi mwanjira yanji imene Paulo anakhalira wangongole pakati pa onse Ayuda ndi amitundu? Kwa iye kunapelekedwa ntchito, monga imene imaperekedwa kwa ophunzira aliyense wa Khristu, pitani kudziko lonse, ndikuphuzitsa ku dziko lonse ndikuwabatiza iwo mudzina la atate ndi mwana ndi mzimu woyera ; ndikuwaphunzitsa iwo kuti asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu, ndipo onani Ine ndili pamodzi ndi inu nthawi zonse, kufikira kumapeto a dziko lonse lapansi; Mukumulandira Khristu, Paulo anabvomeleza utumiki umenewu. Iye anazindikira kuti pa iye panagonera mwayi wogwirira ntchito anthu amitundu yonse kwa ayuda ndi Amitundu, ophunzira ndi osaphunzira, kwa iwo okhala m’maudindo apamwamba ndi iwo otsikitsitsa pomwe anali moyo.’”—The SDA Bible Commentary (E.G. White Comments),Vol6,p.1067.
3. CHIPATSO CHA KUTEMBENUKA MTIMA Lachitatu, Ogasti 25
a. Ngati mzimu woyera uli mumtima mwathu, kodi ndi chiyani chidzakhale choyambilira m’machitachita athu? Yohane 1:41, 42.“Tiyenera kufuna kupeleka kwa ena chikoka cha Khristu ndi zenizeni zake zosaonekazo za dziko likudzalo. Padzakhala chidwi chokhumba kutsatira mu njira imene Yesu anayenda. Payenera kukhala khumbo loona kuti iwo otizungulira ife ‘awone mwana wankhosa wa Mulungu, amene achotsa chimo lake la dziko lapansi.’Yohane1:29.“Pakuyetsetsa kudalitsa ena mdalitso udzatsatiranso pa ife eni. Ichi ndi cholinga cha Mulungu mukutipatsa mbali yochita mudongosolo la chiombolo. Iye anapeleka kwa anthu mwayi mukutenga nawo mbali mukhalidwe la umulungu ndipo ku mbali yawo, kuti apeleke mdalitso kwa anthu anzawo. Uwu ndiwo ulemu waukulu koposa, ndicho chimwemwe chachikulu koposa, chimene Mulungu angathe kupereka kwa anthu. Iwo amene angatenge nawo mbali mukugwira ntchito ya chikondi amabweletsedwa chifupi ndi Mlengi wawo.“Mulungu akhoza kupereka mauthenga a choonadi, komanso ntchito yonse ya utumiki wa chikondi kwa angelo akumwamba. Iye akhoza kugwiritsa ntchito njira zina mukumalizitsa cholinga chake. Koma muchikondi chake chosaneneka Iye amasankha kutipanga ife ogwira nawo ntchito pamodzi ndi Iye mwini, mwa Khristu ndi angelo, kuti tikhoza kukagawana madalitso, chimwemwe, kukwedza uzimu, zimene zidzatsatira kutuluka muutumiki wopanda undekha.Tinabweletsedwa muchiyanjano pamodzi ndi Khristu kudzera mukugawana naye mazunzo ake. Machitidwe onse ozipereka nsembe kuubwino wa ena umalimbikitsa mzimu wopambanitsa m’mitima yopereka, kuisendezera chifupi kwambiri kwa mombolo wadziko lapansi, Iye amene anali wolemera chifukwa cha ife… anakhala wosauka, kotero kuti kudzera mu uphawi wake tikakhale olemera.’ 2 akolinto 8:9. Ndipo ndikuzera pamene tikwanilitsa cholinga cha Umulungu mukulengedwa kwathu kuti moyo ukhale mdalitso kwa ife.”—Steps to Christ, pp. 7880.b. Ndi chisanzo chanji cha Khristu chimene chingatitsogolere ife muubale wathu ndi abale athu ndi otizungulira athu? Agalatiya 6:9,10; Yohane 9:4.“Ngati mungapite ku ntchito monga khristu anapangira kuti ophunzira ake azikhala, ndikupindula miyoyo kwa Iye, mudzazimva kusowekera kwanu kwa zodutsamo zanu zokuya ndinso chiziwitso chachikulu mu zinthu za Umulungu, ndipo mudzamva njala ndi ludzu la chilungamo. Mudzachonderera Ambuye ,ndipo chikhulupiliro chanu chidzalimbikitsidwa , ndipo moyo wanu uzamwa modzama pa chisime chachipulumutso. Zotsutsa ndi Mayetsero osawelengeka adzakutsogolera iwe ku Buku lopatulika ndi pemphero. Inu mudzakula mwachisomo ndi chiziwitso cha Khristu, ndipo muzakudza zodutsamo zapamwamba.”—Ibid., p.80.
4. NTCHITO YOPANDA UNDEKHA Lachinayi, Ogasti 26
a. Tchulani choopsa chachikulu kwa ife monga mamembala ampingo lero. Malaki 3:8—8.“Munthawi yathu ino (Osunga sabata oyembekezera kubwela kwa Khristu) choopsa chawo chachikulu ndicho kuchuluka kwa katundu wawo. Ambiri akupitilira kuchulukitsa zotsamalira zawo ndi ntchito zawo; iwo ali ndi zochuluka. Zotsatira zake , Mulungu ndi zosowekela zake ku ntchito yake zili chifupi kuiwalidwa ndi iwo; iwo afa kuuzimu. Akusowekera kupereka nsembe kwa Mulungu mu zopereka. Nsembe sizikumachuluka, koma malomwale zikutsika ndi kuonongedwa…mochuluka pakati pa anthu athu. Izi mangoonetsera kuonongeka kwa iwo amene akuimilira mu ichi.”—Testimonies for the church, vol. 1, p. 492.b. Ndi thandizo lanji la akhristu lomwe lingathandize okhulupilira kukula muchisomo ndi mchiziwitso cha Ambuye wathu Yesu Khristu?1 Peter 4:8—10; Ahebri 13:2.“Mwayi womwe unaperekedwa kwa Abrahamu ndi Loti sunatimanenso ife. Mukuonetsa kulandila alendo kwa ana a Mulungu, ifenso tidzalandira angelo m'nyumba zathu. Ingakhale masiku athu ano, Angelo mumaonekedwe aumunthu amalowa m’nyumba za anthu ndikusamaliridwa ndi iwo. Ndipo Akhristu amene amakhala mu kuwala kwa nkhope ya Mulungu amatsagana nthawi zonse ndi angelo osawoneka, ndipo Angelo oyera mtima amenewa amasiya mdalitso m’nyumba zathu. ”—Ibid., vol.6,p.342.c. Ndi chosowa chanji chimene chingakwanilitsidwe ndi okhulupilira lero? 2 Akolinto 10:16.“Mamembala a mipingo yathu akhoza kukwanilitsa ntchito imene, tsopano lino, movuta iwo angoyiyamba. Palibe amene angapite kudela latsopano ndicholinga chongozisangalatsa mu dziko lapansi; koma pamene pali potsegula kupeza zosamalira zamoyo uno, tilole mabanja amene ali odzika midzu mchikhulupiliro alowe, banja limodzi kapena awiri apite kudera , kukagwira ntchito monga atumiki. Ayenera kukhala ndi chikondi pa miyoyo, ndi kunyamula udindo wogwira ntchito chifukwa cha iwo, ndipo ayenera kuphunzira njira zowabweretsera iwo m’choonadi. Iwo atha kugawa zowelenga zathu, kupanga mikumano mnyumba zawo, kukhala olumikizana ndi anzawo owazungulira, ndikuwaitanira iwo kufika ku mkumanowu . Umu ndi momwe iwo angaonetsere kuunika kwawo kuti kuwalire mu ntchito zabwino.”—Ibid., vol.8. p.245.“Kwa nthawi yaitali Mulungu wakhala akudikira mzimu wautumiki kulamulira mu mpingo wonse ndicholinga choti wina aliyense atha kumugwilira ntchito Iye molingana ndi kuthekera kwake. Pamene mamembala amumpingo wa Mulungu akuchita ntchito yawo yosankhidwira mumadera awo osowa, m'nyumba ndi mutalimutali, pokwanilitsa utumiki wa uthenga wabwino, posachedwapa dziko lonse la pansi lidzachenjezedwa ndipo Ambuye Yesu adzafika kudziko lino ndi mphanvu ndi ulemerero.”—The Acts of the Apostles, p. 111.
5. NTHUMWI ZOKHULUPIRIKA Lachisanu, Ogasti 27
a. Ndichiyani chimene tikuyembekezera kwa onse amene apatsidwa uthenga wabwino makamaka kwa ogwira ntchito ya Ambuye? 1.Akolinto 4:1,2; Chibvumbulutso 2:10.“Ndi mwayi wa alonda pamakoma a Zioni kukhala chifupi ndi Mulungu, ndikukhala obvomelezeka mukulandira mzimu wake, ndicholinga choti atha kukagwira ntchito kudzera mwa iwo kuwauza ochimwa za chionongeko chawo, ndikuwalodzera iwo ku malo otetezeka. Osankhidwa a Mulungu, osindikizidwa ndi mwadzi wozipereka, ayenera kulanditsa amuna ndi amayi ku chionogeko chikudza. Mokhulupilika iwo ayenera kuchenjeza anthu amzawo za zotsatira zenizeni zakuphwanya kwa lamulo, ndipo mokhulupirika iwo ayenera kuyang’anira chidwi cha Mpingo.”—Gospel Workers, p. 15.b. Ndi chitsanzo chanji chimene Daniel anaika pa achinyamata alero? Daniel 1:8, 15.“Ambuye akufuna ife tiphunzirenso phunziro kuchokera mu zodutsamo za Daniel. Pali ambiri amene angakhale amuna amphanvu monga ngati ahebri okhulupilikawa iwo akuyenera kudalira pa Mulungu ku chisomo kukhala ogonjetsa, ndi mu mphanvu ndi kuyesetsa kwawo mu ntchito zawo. Danieli anaonetsera khalidwe labwino la ungwiro, kwa onse kuyambira atsogoleri ndinso pa achinyamata. Iye anaima monga wochitira umboni Mulungu,ndipo anafuna kutenga ntchitoyi kuti asachitise manyazi kumwamba mukumva mawu ake kapena mukuyang’ana ntchito yake. Pamene Danieli amafunikira mukutenga gawo lozikondweretsa la pagome la a Mfumu, iye sanathamangire mu mudyo wake, ingakhale kuzionetsera chidwi choti atha kudya ndi kumwa monga angazikondwerestere. Opanda kuyankhulapo mawu oipa, iye anaitengela nkhaniyi kwa Mulungu. Iye ndi azanke anafuna mzeru kuchokera kwa Mulungu, ndipo pamene anabwela kuchokera kumapemphero okhulupilika mfundo zawo zinachitika. Ndi chidaliro chawo choona ndi chikhristu chawo cha ulemu, Danieli anapereka mlandu kwa olamulira amene anali owalamulira, kuwapempha kuti akuyenera awapatse chokudya chophweka. Achinyamatawa anaganiza kuti mfundo zawo zachipembezo zili pangozi, ndipo iwo anadalira pa Mulungu , amene amamukonda ndi kumtumikira.”—Testimonies to Ministers, p. 263.