Kuyenda ndi Yesu << >> Zopereka Za Sabata Loyamba Lasabata, Ogasiti 1, 2026 Nthambi ya General Conference yowona za Maphunziro “Phunzitsani mwana poyamba njira yake; Ndipo angakhale akakalamba sadzachokamo” (Miyambo 22:6). Tikukhala m'nthawi zovuta. Pakati pa anthu moyo wa chikunja omwe ukuchulukirachulukirabe, udindo wophunzitsa ana athu ndi achinyamata athu kuwopa Ambuye wakhala wofunika kwambiri kuposa kale lonse. Monga makolo, aphunzitsi, ndi ziwalo za thupi la Khristu, tili ndi ntchito yopatulika yokonzetsera m'badwo womwe udzatha kuteteza chikhulupiriro molimba mtima, modzichepetsa, komanso motsimikiza mtima. “Sayansi ya maphunziro enieni ndi chowonadi, chomwe chikuyenera kuzikika kwambiri m'moyo chomwe sichingachotsedwe ndi chinyengo chomwe chili ponseponse.”—Testimonies for the Church, vol. 6, p. 131. Mu nkhani yi, Dipatimenti yowona za maphunziro ya la likulu la mpingo yakhala ikugwira ntchito molimbikila kuti ilimbikitse ndikukuza masukulu athu amaphunziro ofalitsa utgenga wa bwino padziko lonse lapansi. Malo athu ambiri a maphunziro alibe zomangamanga zokwanira, maphunziro amakono, ndi zida zogwirizana ndi zinthu zenizeni za uzimu za ophunzira athu. Kuphatikizapo, mayiko angapo apempha za kutsekulidwa kwa masukulu atsopano amaphunziro omwe samangolimbikitsa chidziwitso chamaphunziro okha komanso mfundo za uthenga wabwino wosatha. Chopereka chapaderachi chithandizira madera atatu ofunikira: 1. Kukonzanso masukulu ofalitsira uthenga wabwino omwe alipo; 2. Kukhazikitsa masukulu atsopano m'madera omwe akufunika mwayi wopeza maphunziro achikhristu a SDARM; 3. Kupititsa patsogolo ntchito yomasulira ndi kusintha kwazipangizo zophunzitsira zomwe zapangidwa ndi gulu lathu lophunzitsa kuti litumikire masukulu akudziko ndi masukulumofalitsa utyenga wa bwino mu zilankhulo zosiyanasiyana komanso m'madera osiyanasiyana. “Maphunziro owona ndi maphunziro ofalitsa uthenga wa bwino. Mwana aliyense wamwamuna ndi wamkazi wa Mulungu amayitanidwa kukhala ofalitsa uthenga wa bwino; tayitanidwa kutumikira Mulungu komanso anthu anzathu; ndipo kuti ife tikayenerezedwe kutumikira mu utumiki umenewu chukuyenera kukhala cholinga chofunikira cha maphunziro athu.”—The Ministry of Healing, p. 395. Chifukwa chake, tikukupemphani, abale ndi alongo okondedwa, kuti mupereke chopereka chanu ndi mtima wonse komanso malibgaliro ofalitsa uthenga wa bwino. Kuyika ndalama zathu mu maphunziro a ana athu ndi achinyamata ndiko kuyika ndalama mu tsogolo la mpingo, kufalitsa uthenga wabwino, komanso mu kholola lomaliza. Ambuye awonjezere zopereka zanu ndikulimbitsa utumiki wofunikawu—ndipo masukulu athu akhaledi nyali zowala mumdima, kukonzetsera gulu lokhulupirika llkukakomana ndi Mpulumutsi wathu yenwe akubweranso posachedwa. Nthambi ya General Conference Yowona za Maphunziro << >>