Back to top

Sabbath Bible Lessons

Kuyenda ndi Yesu

 <<    >> 
Zopereka Za Sabata Loyamba Lasabata, September 5, 2026 Sukulu ya Maphunziro a Utumiki wa Baibulo ku Philippines Pamene tikukumbutsidwa za ntchito yaikulu yopita ku dziko lonse lapansi ndikukapanga ophunzira, tikuyenera kuchitapo kanthu. Sukulu ya Maphunziro a Utumiki wa Baibulo ndi malo apadera osulira ndi kukonzetsera antchito ku munda wa Mphesa wa Ambuye. Kuyambira pomwe inayambitsidwa mu February 1984, sukuluyi yakhala nyali ya chikhulupiriro, kukonzetsera mitima ndi malingaliro a iwo amene ali ndi chikhumbo chokalalikira uthenga wabwino kwa mitundu yonse. Ophunzira ambiri amene amaliza pulogalamu ya zaka ziwiri ya maphunziro a utumiki yomwe malowa amapereka ena a iwo tsopano ndi atumiki ofalitsa uthenga wabwino kunja kwa dzikolo, ndipo ena ambiri ndi atsogoleri komanso azibusa omwe akufalitsa uthenga wa chipulumutso m'madera okhala anthu ambiri ku zilumba za ku Philippines. Pokhala mu Cabatang, Tiaong, ku chigawo cha Quezon mdziko la Philippines, Sukulu ya Maphunziro a Utumiki wa Baibuloyi yakhala ikugwira ntchito mosalekeza kupereka maziko olimba a Baibulo kwa omwe akufuna kukhala atumiki a uthenga wabwino ku Philippines komanso m’dera lonse la Pacific. Malowa apereka kuthekera kuti ophunzira adzitha kukhalako, kuphunzira Chingerezi, komanso kuphunzitsidwa kukhala atumiki a uthenga wabwino, ogulitsa mabuku, ogwira ntchito zaumoyo, ndi oyang’anira omwenso akufunikira kwambiri mdzikolo komanso kunja kwake. Malowanso agwiritsidwapo ntchito ngati kochitira maseminale, misonkhano ya achinyamata, komanso makonferensi. Pamene ntchito ya kukonzanso yakula ku Philippines, kukulitsa ndi kukonzanso malowa kwakhala kofunikira kwambiri tsopano kuti apitirize kuthandiza moyenera ntchito ya Mulungu kupita chitsogolo. Poyang’anira zosowa zimenezi, madongosolo akuchitikanso kuti msonkhano wa General Conference udzachitikirenso pamalo pomwepa. Ndi dalitso lalikulu bwanji kudzakhala ndi msonkhano wa okhulupirira kumeneko, komwenso masomphenya a mautumiki olalikira ndi kutsitsimuka mu uzimu zidzakhala patsogolo! Zopereka zanu za Sabata Loyamba lero zithandiza kwambiri pomangira kukulitsa komwe kwakhala kofunikira kwambiri pa malowa. Pamene tikupereka, tiyeni tikumbukire mawu a 2 Akorinto 9:7, “Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwachisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.” Zopereka zanu zithandize kukweza sukuluyi, kulimbikitsa cholinga chake, ndi kubweretsa antchito okonzeka kulalikira uthenga wabwino wosatha. Tiyeni tipereke mwa chikhulupiriro ndi chimwemwe, podziwa kuti zopereka zathu zibalila zipatso zosatha za ufumu wa Mulungu. Zikomo, ndipo Ambuye akudalitseni koposa pamene mukupereka! Abale ndi Alongo anu ku Philipine
 <<    >>