Kudziwa Mulungu Vesi Loloweza: “Wokhala nazo nzeru asamalire izi, ndipo azindikire zachifundo za Yehova” Masalmo 107:43.
Zowerenga Zoonjezera:
Steps to Christ, pp.85–91.
“Chidziwitso chonse chowona ndi kukula kwenikweni zonse zimachokera mu kudziwa Mulungu.”—Education, p. 14.
1. MULUNGU AMADZIWULULA YEKHA Loyamba, Ogasti 30
a. Kodi ndikudzera mu zinthu ziti za m’dziko lino m’mene Yehova akuitanira anthu kuti abwere kwa Iye? Masalmo 19:1–6; Miyambo 2:1–5.“Pali njira zambiri zomwe Mulungu akufuna kuti adzibvumbulutsire yekhz kwa ife ndi kutibweretsa mu chiyanjano ndi Iye. Chilengedwe chimalankhula ndi malingaliro athu mosalekeza. Mtima wotseguka udzakhutitsidwa ndi chikondi ndi ulemerero wa Mulungu monga zabvumbulutsidwa kudzera mu ntchito za manja ake. Khutu lomvetsera limatha kumva ndikumvetsetsa zolankhula za Mulungu kudzera mu zinthu zachilengedwe. Minda yobiriŵira, mitengo italiitali, mphukira ndi maluwa, mtambo wodutsa, mvula yokugwa, kasupe wotumphuka, ulemelero wakumwamba, zimalankhula ndi mitima yathu, ndi kutiitanira ife kuti timudziŵe Iye amene anazipanga zonsezo.”—Steps to Christ, p. 85.b. Kodi Yesu anagwiritsa ntchito chiyani kukhazikitsa choonadi m'malingaliro a omvera ake? Mateyu 13:3, 34.“Mpulumutsi wathu anamanga maphunziro ake a mtengo wapatali ndi zinthu za chilengedwe. Mitengo, mbalame, maluwa a m’zigwa, zitunda, nyanja, ndi miyamba yokongola, limodzinso ndi zochitika ndi malo ozungulira moyo wa tsiku ndi tsiku, zonsezo zinagwirizanitsidwa ndi mawu a chowonadi, kuti motero maphunziro Ake akakumbukiridwe kaŵirikaŵiri m’maganizo, ngakhale pakati pa zotangwanitsa za moyo wa munthu wotopetsa.“Mulungu akufuna kuti ana Ake ayamikire ntchito Zake ndi kusangalala ndi kukongola kophweka, kwachete kumene Iye wakometsera nako dziko lathu lapansi lino.”—Ibid
2. NTCHITO YA ZOLENGEDWA ZA MULUNGU Lachiwiri, Ogasiti 31
a. Ndi phunziro lanji limene lingaphunziridwe kuchokera mu chilengedwe—mwachitsanzo maluwa, mbalame, ndi nyenyezi? Aroma 1:20; Machitidwe 14:17.““M’kafukufuku wa sayansi . . . tiyenera kupeza chidziŵitso cha Mlengi. Sayansi yowona yonse imangotanthauza kumasulira kwa manja a Mulungu m’zinthu zakuthupi. Sayansi imabweretsa umboni watsopano chabe wa nzeru ndi mphamvu za Mulungu kuchokera mu kafukufuku wake. Moyenerera, buku la chilengedwe ndi mawu olembedwa zimatithandiza kudziŵa Mulungu mwa kutiphunzitsa kanthu kena ka malamulo anzeru ndi opindulitsa amene Iye amagwiritsira ntchito.”—Patriarchs and Prophets, p. 599.“Ngati titakhala anthu omvetsera, ntchito zolengedwa za Mulungu zidzatiphunzitsa maphunziro amtengo wapatali a kumvera ndi kukhulupirira. Kuchokera ku nyenyezi zimene zimayenda m’njira zawo zosawoneka mlengalenga nthawi ndi nthawi, kufikira ku kachidutswa kochepetsetsa, zinthu za m’chilengedwe zimamvera chifuniro cha Mlengi. Ndipo Mulungu amasamalira chirichonse ndipo amasunga chirichonse chimene Iye adachilenga.”—Steps to Christ, pp. 85, 86.b. Pamene tikuganizira kukongola ndi mtendere wa chilengedwe chosawonongeka, tiyenera kukumbukira chiyani chokhudza dziko latsopano lolonjezedwa? 1 Akorinto 2:9; Chibvumbulutso 21:1.“Lolani malingaliro anu ajambule nyumba ya opulumutsidwa, ndipo kumbukirani kuti idzakhala yokongola kuposa momwe mungaganizire. Mu mphatso zosiyanasiyana za Mulungu m’chilengedwe, timangowona kuwala kochepa kokha kwa ulemerero wake.”—Steps to Christ, pp. 86, 87.“Mpingo wa Mulungu wapatsidwa mavumbulutso a cholinga chosatha cha Yehova. Anthu ake aloledwa kupenya mopitirira mayesero a tsopano lino kufikira ku zipambano za mtsogolo, pamene nkhondo ikadzatha, opulumutsidwa adzalowa ndikukhala m’dziko lolonjezedwa. Masomphenya awa a ulemerero wa mtsogolo, zojambulidwa ndi dzanja la Mulungu, ziyenera kukhala zokondedwa ku mpingo wake lero.”—Prophets and Kings, p. 722.“M’Baibulo cholowa cha opulumutsidwa chimatchedwa ‘dziko.’ Ahebri 11:14—16. Kumeneko Mbusa wakumwamba amatsogolera gulu Lake ku akasupe a madzi amoyo. Mtengo wa moyo upatsa zipatso zake mwezi ndi mwezi, ndi masamba a mtengowo ndi ochiritsira amitundu. Pali mitsinje yoyenda nthawi zonse, yonyezimira ngati krustalo, ndipo pambali pake mitengo yoweyula yomwe imayika mithunzi yake panjira zokonzedwera owomboledwa a Yehova. Kumeneko zigwa zotambalala zimasefukira kukhala mapiri okongola, ndipo mapiri a Mulungu amakulitsa nsonga zake zazitali. M’zigwa zamtendere zimenezo, pambali pa mitsinje yamoyo imeneyo, anthu a Mulungu, omwe kwa nthawi yayitari akhala alendo ndi ogonera, adzapeza pokhalapo.”—The Great Controversy, p.675.
3. UMBONI WA KUTSOGOLERA KWA MULUNGU Lachitatu, Septemba 1
a. Ndi maphunziro ati ofunikira kwambiri omwe tingaphunzire kuchokera kwa aneneri kuti atilimbikitse pa nthawi ya kufooka ndi mayesero? Yakobo 5:17; Aroma 8:28; 1 Yohane 5:14.“Muzokumana nazo zathu komanso malo otizungulira, m’zosintha zatsiku ndi tsiku zimene zikuchitika mozungulira ife, tingapeze maphunziro amtengo wapatali ngati mitima yathu ili yotseguka kuti tiizindikire. . . . [Makolo akale ndi aneneri] anthu ‘omvera zilakolako monga ife.’ Yakobo 5:17 . Timaona mmene anavutikira mu zofooketsa monga zathu, m’mene anagwera m’mayesero monga ife tachitira, ndipo komabe analimbikanso mtima ndi kugonjetsa mwa chisomo cha Mulungu; ndipo, poyang’anitsitsa, titonthozedwa m’kulondola kwathu chilungamo.” — Steps to Christ, pp. 87, 88.b. Ngati Mulungu amasamalira zinthu za chilengedwe, kodi sadzasamalira kwambiri ana ake? Masalmo 107:43; 145:15, 16.“Chilengedwe ndi mabvumbulutso zonse pamodzi zimachitira umboni za chikondi cha Mulungu. Atate wathu wakumwamba ndiye gwero la moyo, la nzeru, ndi la chimwemwe. Talingalirani za kusintha kwawo kodabwitsa ku zosoŵa ndi chimwemwe, osati cha munthu kokha, komanso cha zamoyo zonse. Dzuwa ndi mvula, zimene zimasangalatsa ndi kutsitsimutsa nthaka ya dziko, zitunda, nyanja, ndi zigwa, zonse zimatiuza za chikondi cha Mlengi.” — Ibid., p. 9.c. Kodi lonjezo la chisamaliro cha Mulungu liyenera kutitsogolera ku chiyani? Mateyu 6:30–34.“Tikamayesa kusamalira tokha zinthu zomwe tikuyenera kuchita, ndi kudalira nzeru zathu zokha kuti tipambane, timakhala tikutenga umene Mulungu sanatipatse, ndipo tikuyesera kuwunyamula popanda thandizo lake. Tikudzitengera udindo womwe uli wa Mulungu, potero tikudziyika tokha m’malo mwa Mulunguyo. Tikhoza kukhala ndi nkhawa ndi kuyembekezera ngozi ndi imfa, chifukwa zidzatigwera ndithu. Koma tikamakhulupiriradi kuti Mulungu amatikonda ndipo amafuna kutichitira zabwino tidzasiya kudera nkhawa za m’tsogolo. Tidzakhulupirira Mulungu monga mmene mwana amadalirira kholo lake lachikondi. Ndiye mavuto athu ndi zowawa zidzatha, chifukwa chifuniro chathu chidzamezedwa ndi chifuniro cha Mulungu.”— Thoughts from the Mount of Blessing, pp. 100, 101.
4. BVUMBULUTSO LA MULUNGU Lachinayi, Septemba 2
a. Ndikuti komwe Khristu anayika mabvumbulutso omveka bwino a dongosolo la Mulungu la chipulumutso cha anthu? Yohane 5:39; Yesaya 34:16.“Mulungu amalankhula nafe m’Mawu ake. Mmenemu tiri ndi mabvumbulutso omveka bwino a khalidwe lake, mmene amachitira ndi anthu, komanso ntchito yayikulu ya chiwombolo.”—Steps to Christ, p. 87.b. Ndi chiyani chomwe chiyenera kumachitidwa tsiku ndi tsiku ndi aliyense yemwe akukhumba kukula mukulimbika ndi mphamvu za Mulungu? Yohane 6:53, 63; Akolose 3:1, 2.“Mutu wa chiombolo ndi womwe angelo amalakalaka kuyang'anamo; idzakhala sayansi ndi nyimbo ya owomboledwa m’mibadwo yosatha ya muyaya. Kodi sikoyenera kuti zilingaliridwe ndi kuphunziridwa mosamalitsa tsopano? Chifundo chosatha ndi chikondi cha Yesu, nsembe yoperekedwa chifukwa cha ife, zimayitanitsaa kusinkhasinkha mozama ndimosamalitsa kwambiri. Tiyenera kukhazikika pa khalidwe la Muomboli wathu wokondedwa ndi Mtetezi. Tiyenera kusinkhasinkha za ntchito ya Iye amene anabwera kudzapulumutsa anthu ake ku machimo awo.”—Ibid., pp. 88, 89.c. Kodi tingatengere bwanji Mawu a Mulungu m’mitima yathu?? Mateyu 4:4; 2 Timoteyo 2:15.“Palibe amene ali ndi mzimu woyamikira chiphunzitso chake amene angawerenge ndime imodzi ya m’Baibulo popanda kupezamo mfundo yothandiza. Koma chiphunzitso chamtengo wapatali cha Baibulo sichiyenera kupezedwa mwa apo ndi apo kapena osaphunzira. Dongosolo lake lalikulu la chowonadi silimaperekedwa kotero kuti lizindikiridwe ndi woŵerenga wofulumira kapena wosasamala. Chuma chake chambiri chili pansi kwambiri, ndipo chingapezeke kokha mwa kufufuza mwakhama ndi kuyesetsa kosalekeza. Choonadi chimene chimapanga chinthu chachikulu chiyenera kufufuzidwa ndi kusonkhanitsidwa, ‘kuno pang’ono, ndi ukonso pang’ono.’ Yesaya 28:10.“Pamene afufuzidwa motero ndi kusonkhanitsidwa pamodzi, adzapezedwa kukhala oyenererana bwino lomwe. Uthenga uliwonse ndi chowonjezera ku china, uneneri uliwonse ndi kufotokozera kwa wina, chowonadi chirichonse ndi chitukuko cha chowonadi china. Mitundu ya chuma cha Chiyuda imafotokozedwa momveka bwino ndi uthenga wabwino. Mfundo iriyonse m'mawu a Mulungu ili ndi malo ake, mfundo iliyonse imakhala nayo. Ndipo dongosolo lathunthu, m’kapangidwe ndi kachitidwe kake, limapereka umboni kwa Mlembi wake. Mapangidwe oterowo palibe malingaliro a munthu aliyense koma a Wopandamalire yekha amene angathe kukhala nawo kapena kuwamvetsetsa.”—Education, pp. 123, 124.
5. KUPHUNZIRA BAIBULO Lachisanu, Septemba 3
a. Ndi chiyani chimene chinabweretsa chitonthozo ndi thandizo kwa Yeremiya pa nthawi yake yovuta? Yeremiya 15:16.“Palibe chinthu chomwe chimathandiza kwambiri kulimbitsa nzeru kuposa kuphunzira Malemba Opatulika. Palibe bukhu loposa lomwe liri ndi mphamvu zokweza maganizo, kupatsa mphamvu malingaliro, monga chowonadi chachikulu ndi cholemekezeka cha Baibulo. Zikanakhala kuti Mawu a Mulungu akuphunziridwa monga momwe zinayenera kumakhalira, anthu akanakhala ndi maganizo otambalala, khalidwe lolemekezeka, ndi cholinga chokhazikika zomwe ndizosowa masiku ano.”—Steps to Christ, p. 90.“Iye amene amapereka chidwi chachikulu ku Malemba Opatulika, kudzera mupemphero adzakhala ndi kumvetsetsa kwabwino komanso chiweruzo cholimba, monga ngati kuti potembenukira kwa Mulungu wafika pa mlingo wapamwamba wa nzeru.”—Mind, Character, and Personality, vol. 1, p. 95.b. Ndi motani momwe Malemba Opatulika ayenera kuphunziridwira? Nanga ndi chiyani chomwe chiyenera kuyamba kuphunzira Baibuloko kusanachitike? Masalimo 119:9, 11, 16.“Choonadi cha Mulungu, monga golide, sichimakhala nthawi zonse powonekera; chikuyenera kupezeka kokha kudzera mu kuganiza mozama ndi kuphunzira.”—Gospel Workers, p. 76.“Monga wokumba migodi amapezera mizere ya miyala yamtengo wapatali yobisika pansi pa nthaka, choteronso amene amafufuza Mawu a Mulungu mosalekeza ngati chuma chobisika adzapeza chowonadi chamtengo wapatali kwambiri, chomwe ndichophimbika kwa munthu aliyense wofufuza mosasamala. Mawu owuziridwa, posungidwa ndi kuganiziridwa mumtima, adzakhala ngati mitsinje yotuluka ku kasupe wa moyo.Baibulo siliyenera kuphunziridwa popanda kupemphera. Tisanatsegule masamba ake tiyenera kupempha chiwalitsiro cha Mzimu Woyera, ndipo tidzapatsidwa. . . . Angelo ochokera kudziko la kuwala adzakhala ndi iwo amene kudzera mukudzichepetsa kwa mtima wawo amafuna chitsogozo cha kumwamba.”—Steps to Christ, p. 91.