Back to top

Sabbath Bible Lessons

Kuyenda ndi Yesu

 <<    >> 
LASABATA, Ogasti 8, 2026 Phunziro 6
Chikhulupiriro ndi Kubvomereza Vesi Loloweza: “Ndipo ndidzakupatsani mtima watsopano, ndi kulonga m'kati mwanu mzimu watsopano; ndipo ndidzachotsa mtima wamwala m'thupi, ndi kukupatsani mtima wamnofu” Ezekiele 36:26
Zowerenga Zoonjezera:   Steps to Christ, chapter 6, pp. 49–55. 
“Simungathe kuzitetezera machimo anu akale; simungathe kusintha mtima wanu ndi kudzipanga nokha kukhala woyera. Koma Mulungu walonjeza kukuchitiraniti izi zonse kudzera mwa Khristu.”—Steps to Christ, p. 51.

1. CHIKHULULUKIRO NDI MTENDERE Loyamba , Ogasti 2
a. Kodi ndi lonjezo lodabwitsa lanji la Mulungu la Chikhululukiro ndi mtendere? 1 Yohane 1:9 “Mukuona kuti moyo wanu wadzazidwa ndi kudzikonda ndi uchimo. Mukulakalaka kukhululukidwa, kuyeretsedwa, kumasulidwa. Chiyanjano ndi Mulungu, kufanana ndi Iye – Mungachite chiyani kuti muchilandire?“Ndi mtendere umene mukusowekera—Chikhululukiro cha Kumwamba ndi mtendere ndi chikondi m’moyo. Ndalama sizingagule ichi, luntha silingagule, nzeru siingachifikire; simungayembekeze, mwa kuyesetsa kwanu, kuchipeza. Koma Mulungu akupereka kwa inu monga mphatso, ‘opanda ndalama ndi opanda mtengo wake.’ Yesaya 55:1. Ndi chanu ngati mukufuna ndikutambasulira dzanja lanu ndikuchigwira ichi.”— Steps to Christ, p. 49. b. Kodi ndi lonjezo lina lotani lofunika limene lidzasanduliza umunthu kukhala munthu watsopano wogwirizana ndi Mulungu? Ezekieli 36:26. “Mwaulula machimo anu, ndi kuwachotsa mu mtima. Mwatsimikiza mtima kudzipereka nokha kwa Mulungu. Tsopano pitani kwa iye, ndikumupempha kuti akuchotsereni machimo anu ndi kukupatsani mtima watsopano. Ndiye khulupirirani kuti Iye amachita izi chifukwa Iye walonjeza. Ili ndi phunziro limene Yesu adaphunzitsa pamene Iye anali padziko lapansi, kuti mphatso imene Mulungu anatilonjeza ife, tiyenera kukhulupirira ife kuti tilandira, ndipo ndi chathu.”—Steps to Christ, pp. 49, 50.

2. MOYO KUDZERA MWA YESU Lachiwiri , Ogasti 3
a. Kodi Yesu anauza wakufa ziwalo ku Betesida kuti achite chiyani, ndipo ife tingaphunzirepo chiyani pa zimene zinachitikazi? Yohane 5:1—9. “Tiyeni titembenukire ku nkhani ya wakufa ziwalo wa ku Betesida.Wovutika wosaukayo analibe thandizo; anali asanagwiritseko ntchito miyendo yake kwa zaka makumi atatu kudza zisanu ndi zitatu. Koma Yesu anamuuza kuti, ‘Nyamuka, yalula mphasa yako, nuyende.’ Munthu wodwala akanatha kunena , ‘Ambuye ngati mundichiritsa, ndidzamvera mawu anu.’ Koma, ayi, iye anakhulupirira mawu a Khristu, anakhulupirira kuti anachiritsidwa, ndipo anachita khama nthawi yomweyo; anafuna kuyenda, nayendadi. Iye anachita pa mawu a Khristu, ndipo Mulungu anapereka mphamvu. Anachiritsidwa.”— Steps to Christ, p. 50.“Yesu sanamutsimikizire kuti Mulungu amuthandiza. Munthuyo akanatha kuima ndikukayikira, ndikutaya mwayi wake umodzi wochiritsidwa. Koma iye anakhulupirira Mawu a Kristu, ndipo m’kuchita mwa iwo analandira mphamvu.“Kupyolera mu chikhulupiriro chomwecho tidzalandira machiritso auzimu. Mwa uchimo ife tinadulidwa kuchoka ku moyo wa Mulungu. Miyoyo yathu ndiyakufa. Mwa ife tokha sitingathe kukhala moyo wachiyero monga momwe munthu uja analiri wopanda mphamvu wosakhoza kuyenda. Pali ambiri omwe amazindikira kusowa thandizo kwawo, ndi amene amalakalaka moyo wauzimu omwewo umene udzawabweretse mu m’gwirizano ndi Mulungu; akungolimbikira mwachabe kuupeza. Pothedwa nzeru amafuula kuti, ‘munthu wosauka ine! adzandilanditsa ndani m’thupi la imfa iyi? Aroma 7:24. Lolani anthu okhumudwa awa, ovutikirawa ayang'ane m'mwamba. Mpulumutsi akuweramira pa ogulidwa ndi mwazi Wake, akunena ndi chikondi chosaneneka ndi chisoni, ‘Kodi ukufuna kuchiritsidwa?’ Iye akukuitanani kuwuka mu thanzi ndi mtendere.”— The Desire of Ages, p. 203. b. Kodi wochimwa akulonjezedwa chiyani kudzera mwa Khristu? 2 Mbiri 7:14; Hoseya 14:4 “Simungathe kuzitetezera machimo anu akale; simungathe kusintha mtima wanu ndikuzipanga nokha kukhala woyera. Koma Mulungu walonjeza kuti adzakuchitirani zonsezi kudzera mwa Khristu. Inu khulupilirani lonjezoli. Wululani machimo anu ndikuzipereka nokha kwa Mulungu. Funani kumutumikira Iye. Mofanana ndi momwe mukuchitira izi, Mulungu adzakwaniritsa Mawu ake kwa inu. Ngati mukhulupirira lonjezo—kukhulupirira kuti mwakhululukidwa ndi kuyeretsedwa—Mulungu amapereka chowonadi; wachiritsidwa monga momwe Khristu anapatsa wakufa ziwalo mphamvu yoyenda pamene munthuyo anakhulupirira kuti iye anachiritsidwa. Zili choncho ngati mukhulupirira.“Musadikire kuti mumve kuti mwachiritsidwa, koma nenani kuti, ‘Ndikukhulupirira; zili choncho, osati chifukwa ndikumva choncho, koma chifukwa Mulungu walonjeza.’ ” — Steps to Christ, p. 51.

3. KUBVOMEREZEDWA MWA WOKONDEDWA Lachitatu , Ogasti 4
a. Pamene Yesu walandiridwa ngati Mpulumutsi, kodi chimachitika ndi chiyani ku machimo akale? Aroma 3:24, 25; 5:1, 9, 10. “Yesu anati, ‘Zinthu zirizonse mukazipemphera ndi kuzipempha, khulupirirani kuti mwazilandira, ndipo mudzakhala nazo.’ Marko 11:24 . Pali chifukwa ku lonjezo ili—kuti tipemphere monga mwa chifuniro cha Mulungu. Koma ndi chifuniro cha Mulungu kutiyeretsa ife ku uchimo, kutipanga ife kukhala ana ake, ndi kutipangitsa ife kukhala ndi moyo woyera. Choncho tikhoza kupempha madalitso amenewa, ndi kukhulupirira kuti tazilandira, ndi kuthokoza Mulungu kuti tazilandira. Ndi mwayi wathu kupita kwa Yesu ndi kuyeretsedwa, ndi kuima pachilamulo opanda manyazi kapena chisoni.”— Steps to Christ, p. 51. b. Kodi wokhulupirira ali ndi kaimidwe kotani pamaso pa Mulungu? Aroma 8:1. “Pamene moyo wa Mkhristu udzakhala wodzicepetsa, suyenera kukhala wachisoni ndi kuzinyazitsa. Ndi mwayi wa aliyense kuti akhale ndi moyo kuti Mulungu amuvomereze ndi kumudalitsa. Si chifuniro cha Atate wathu wakumwamba kuti tikhale otsutsidwa nthawi zonse ndi mdima. Palibe umboni wa kudzichepetsa kwenikweni pakupita ndi mutu utaweramitsidwa pansi komanso mtima wodzaza ndi maganizo aundekha. Tikhoza kupita kwa Yesu ndi kuyeretsedwa, ndi kuyima pa chilamulo opanda manyazi ndi chisoni.”— The Great Controversy, p. 477.“Pamene tidzipereka tokha kwathunthu kwa Mulungu, ndi kukhulupirira kwathunthu, mwazi wa Khristu umatsuka ku machimo onse. Chikumbumtima chikhoza kumasulidwa kukutsutsidwa. Kupyolera mu chikhulupiriro mu mwazi wake, onse akhoza kukhala angwiro mwa Yesu Khristu. . . . Sitiyenera kuda nkhawa ndi zomwe Khristu ndi Mulungu amaganiza za ife, koma zimene Mulungu amaganiza za Khristu, wolowa m’malo mwathu. Inu muli wolandiridwa mwa Wokondedwa.”—Selected Messages, bk. 2, pp. 32, 33 c. Kodi ndi kusintha kotani kumene kuyenera kuzindikirika ndi onse omwe adalowa mu pangano la ubale ndi Mulubgu ili? 1 Petro 1:18, 19; 1 Akorinto 6:19; 20; Agalatiya 3:26. “Kuyambira tsopano simuli a inu nokha, munagulidwa ndi mtengo wake.” ( 1 Petro 1:18, 19 ) Kupyolera mu mchitidwe wopepuka uwu wa kukhulupirira Mulungu, Mzimu woyera wabala moyo watsopano mu mtima mwanu. Ndinu mwana wobadwira mubanja la Mulungu, ndipo Iye amakukondani monga momwe amakondera Mwana wake.”— Steps to Christ, pp. 51, 52.

4. KUYENDA NDI KHRISTU Lachinayi , Ogasti 5
a. Kodi wokhulupirira ayenera kukhala ndi makhalidwe otani? Akolose 2:6. “Tsopano popeza mwadzipereka kwa Yesu, musabwerere m’mbuyo, musazitengere kutali ndi Iye, koma tsiku ndi tsiku muzinena kuti, ‘Ine ndine wa Khristu; Ndadzipereka ndekha kwa Iye;’ ndipo mpempheni kuti akupatseni Mzimu Wake ndi kukusungani mwa chisomo Chake. Monga momwe zilili pakudzipereka nokha kwa Mulungu, ndi kumukhulupirira Iye, kuti mukhale mwana Wake, kotero muyenera kukhala mwa Iye. Mtumwiyo akuti, ‘Chifukwa chake monga munalandira Kristu Yesu Ambuye, yendani mwa Iye.’ Akolose 2:6 .“Ena akuwoneka kuti akuganiza kuti ayenera kukhala pa chitetezero, ndipo ayenera kutsimikizira Ambuye kuti iwo akonzedwanso, iwo asanatenge madalitso Ake. Koma iwo akhoza kutenga madalitso a Mulungu ngakhale tsopano. Iwo ayenera kukhala nacho chisomo Chake Mzimu wa Khristu, kuthandiza zofowoka zawo, kapena sangathe kukaniza zoipa. Yesu amakonda kuti ife tibwere kwa Iye monga ife tiri, ochimwa, opanda thandizo, odalira. Ife tingabwere ndi kufooka kwathu konse, kupusa kwathu, uchimo wathu, ndi kugwa pa mapazi Ake mu kulapa. Ndi ulemerero Wake kutizungulira ife m'manja mwa chikondi chake ndikumanga mabala athu, kutisambitsa kutichotsera zodetsa zonse.”— Steps to Christ, p. 52. b. Ndi thandizo lanji lokonzedweratu ku zophophonya zomwe zimachitika mu dongosolo lakuphunzira? 1 Yohane 2:1, 2. “Chotsani kukayikira kuti malonjezo a Mulungu sanakonzedwere inu. Ndi a aliyense wolapa moona. Mphamvu ndi chisomo zaperekedwa kudzera mwa Khristu kuti zibweretsedwe ndi angelo otumikira ku moyo uliwonse wokhulupilira. Palibe amene ali ochimwitsitsa mpaka kuti sangapeze mphamvu, chiyero, ndi chilungamo mwa Yesu, amene adawafera iwo. Akuyembekezera kuwavula iwo zobvala zawo zamabanga ndi zodetsedwa ndi uchimo, ndikuwaveka iwo miinjiro yoyera ya chilungamo; Iye akuwalamula kuti akhale ndi moyo osafa ayi.” –Ibid., pp. 52, 53 c. Fotokozani m’mene timalimbikitsidwira paulendowu. 1 Yohane 1:7; Agalatiya 5:16, 17, 25. “Iwo amene akuyenda m’njira zanzeru alinso m’masautso, ali opambana chimwemwe; pakuti Iye amene moyo wawo umkonda ayenda pambali pawo wosaoneka. Pa Kukwera kulikonse amazindikira momveka bwino kukhudza kwa dzanja Lake; ku masitepe aliwonse kunyezimira kwa ulemerero wochokera kobisika kumagwera pa njira zawo; ndipo nyimbo zawo za matamando, zokwera kwambiri, zimakwera mpaka kulumikizana ndi nyimbo za angelo pamaso pa mpando wachifumu.”— Thoughts from the Mount of Blessings, p. 140.

5. CHIKONDI CHA ATATE CHOWOMBOLA Lachisanu , Ogasti 6
a. Kodi zofunikira kuti tivomerezedwe ndi Mulungu ndi chiyani? Yesaya 55:7; 44:22. “Mulungu samachita nafe monga anthu okhala ndi malire amachitirana wina ndi mnzake. Zolingalira zake ndizo za chifundo, chikondi, ndi chifundo chachikulu.”— Steps to Christ, p. 53.“Aliyense amene pansi pa chidzudzulo cha Mulungu adzachepetsa moyo wake ndi kuvomereza ndi kulapa, monga Davide adachitira, akhale ndi chitsimikizo kuti chiyembekezo chilipo. Aliyense amene avomereza mwa chikhulupiriro malonjezo a Mulungu, adzapeza chikhululuko. Ambuye sadzataya konse munthu ngakhale m’modzi wolapa moona.”— Patriarchs and Prophets, p. 726. b. Kodi maganizo enieni a Atate wathu wakumwamba ndi otani kwa onse amene ataya njira? Ezekieli 18:32; Luka 15:18—20. “Satana ndi wokonzeka kuba zitsimikizo zodalitsika za Mulungu. Iye akufuna kutenga kuwala kulikonse kwa chiyembekezo ndi mlezo uliwonse wa kuwala kuchokera ku moyo; koma inu musamulole kuchita ichi. Musamatchera khutu kwa woyesayo, koma muzinena kuti; ‘Yesu anafa kuti ine ndikhale ndi moyo. Amandikonda, ndipo safuna kuti ndionongeke. . . . Fanizo likukuuzani momwe wosochera adzalandiridwire: ( Luka 15:18—20 )“Koma ngakhale fanizo ili, lachifundo ndi lokhudza mtima momwe liririmu, silinafikire kufotokoza mokwana chifundo chosatha cha Atate wakumwamba. Yehova ananena kudzera mwa mneneri wake kuti: ‘Ndakukonda iwe ndi chikondi chosatha: chifukwa chake ndakukoka iwe ndi kukukomera mtima.’ Yeremiya 31:3. Pamene wochimwa akali kutali ndi nyumba ya Atate, kuononga chuma chake mu dziko lachilendo, mtima wa Atate ukulakalaka pa iye; Ndipo Kulakalaka kulikonse komwe kungadzutsidwe m'mitima mwawo kukubwerera kwa Mulungu, ndi kuchonderera kofatsa kwa Mzimu Wake, kumukopa, kumupempha, kukokera wosokera ku mtima wa Atate wake wachikondi.”— Steps to Christ, pp. 53, 54.

MAFUNSO OBWEREZA PAWEKHA Lachisanu n’chimodzi , Ogasti 7
1. Kodi ndichiyani chimalowa m’moyo womwe machimo ake akhululukidwa? 2. N’chifukwa chiyani wakufa ziwalo wa ku Betesida anakwanitsa kuyenda mwadzidzidzi? 3. Tikalandira Khristu kukhala Mpulumutsi wathu, kodi ndilonjezo lanji limene lili lathu? 4. Kodi chinsinsi cha kuyenda mopambana ndi Khristu n'chiyani? 5. Longosolani kusiyana pakati pa njiru ya Satana ndi chikondi chowombola cha Atate.
 <<    >>