Back to top

Sabbath Bible Lessons

Kuyenda ndi Yesu

 <<    >> 
LASABATA, OGASTI 1, 2026 Phunziro 5
Kudzipereka Vesi Loloweza: “Ndipo mudzandifunafuna Ine, ndi kundipeza, pamene mundifuna ndi mtima wanu wonse.” (Yeremiya 29:13).
Zowerenga Zoonjezera:   Steps to Christ, pp. 43–48
“Ndizosatheka kuti ife mu mphamvu zathu kuchirimika mu nkhondoyi; ndipo chirichonse chomwe chimatichotsa malingaliro athu kwa Mulungu, chilichonse chomwe chimatitsogolera ife ku kudzikuza, kapena kudzidalira patokha, ndithu chimenecho chikukonzetsera njira ya kugwa kwathu. Mfundo yaikulu ya Buku lopatulika ndi kuphunzitsa kusadalira mphamvu za munthu koma kulimbikitsa kudalira mphamvu za Mulungu.”—Patriarchs and Prophets, p. 717.

1. NKHONDO YOLIMBANA NDI UNDEKHA Loyamba , Julayi 26
a. Kodi Paulo anafotokoza bwanji za nkhondo yachikhristu ndi zida zake zofunikila pa nkhondoyi? Aefeso 6:12–18. “Satana analimbana ndi Khristu pogwiritsa ntchito mayesero ake owopsa komanso ovuta zedi kuwazindikira, komabe anakanika mu mkangano uliwonse. Nkhondo zimenezo zidamenyedwa m’malo mwathu; zigonjetso zimenezo zimatithandiza ife kuti tigonjetse. Khristu adzapereka mphamvu kwa iwo aomwe akuyifunafuna. Palibe munthu amene angathe kugonjetsedwa ndi Satana popanda munthuyo mwini kulorera. Woyesayo alibe mphamvu zolamulira chifuniro cha munthu kapena kuwukakamiza munthu kuti achimwe. Satana angathe kukhumudwitsa munthu, koma sangathe kumuyipitsa munthu. Angathe kuyambitsa zowawa, koma sangathe kumudetsa munthu. Choonadi chakuti Khristu anagonjetsa chikuyenera kuwalimbikitsa omutsatira ake molimbika mtima kuti ayimenye nkhondo mwamphamvu yolimbana Satana komanso uchimo.”—The Great Controversy, p. 510. b. Kodi ndi kuti komwe Satana akuyesetsa kuti apeze ulamuliro kotheratu? Miyambo 4:23. “Monga momwe munthu ‘asinkhasinkha mu mtima mwake, ali wotere.’ Miyambo 23:7. Mtima ukuyenera kukonzedwanso ndi chisomo cha umulungu, apo ayi kukhala kwa chabe kufunafuna chiyero cha moyo. Iye amene amayesera kumanga khalidwe labwino, ndi lolungama popanda chisomo cha Khristu, akumanga nyumba yake pam’chenga wogwedezeka. Nyumbayo idzagwetsedwa ndithu mu mkuntho wamphamvu wa mayesero.”—Patriarchs and Prophets, p. 460.

2. KUYITANA KOCHOKERA KUMWAMBA Lachiwiri , Julayi 27
a. Kodi ndi chani chomwe chikuyenera kutayidwa ndi cholinga chakuti tikhale ophunzira ake a Khristu? Luka 14:33; Mateyu 6:24. “Podzipereka tokha kwa Mulungu, tiyenera kusiya zonse zomwe zingatilekanitse ife ndi Iye. Chifukwa chake Mpulumutsi akuti, [kuchokera pa Luka 14:33]. Chilichonse chomwe chingawuchotse mtima kwa Mulungu chikuyenera kutayidwa. Chuma ndi fano la anthu ambiri. Chikondi cha ndalama, khumbo lofuna chuma, ndi unyolo wagolide womwe umawamangirira anthu kwa Satana. Kutchuka komanso ulemu wa dziko lapansi zimapembedzedwa ndi gulu lina la anthu. Moyo wa mtambasale, komanso ufulu wosakhala ndi udindo uliwonse ndi fano la ena. Koma ma unyolo a ukapolowa akuyenera kuphwasulidwa. Sitingakhale theka limodzi kwa Ambuye ndi theka linanso ku dziko lapansi. Sitili ana a Mulungu pokhapokha ngati sititakhala ana ake kwathunthu.”—Steps to Christ, p. 44. b. Kodi ndi kuyitana kuti kwa umulungu komwe Ambuye akupereka kwa onse amene akufuna moyo watsopano ndi mtima watsopano? Yesaya 1:18; Yeremiya 29:13; Yakobo 4:7–10. “Ulamuliro wa Mulungu, suli ngati monga momwe Satana amawuwonetsera, kuti ndi wokhazikidwa pa kugonjera mosazindikira, kapena ulamuliro wopanda nzeru. Ulamulirowu umakopa nzeru ndi chikumbumtima. . . . Mulungu samakakamiza chifuniro cha zolengedwa zake. Iye sangalandire ulemu womwe superekedwa mwa ufulu komanso mwanzeru. Kugonjera kokakamizidwa kokha kutha kulepheretsa kukula kwenikweni kwa malingaliro komaso kwa khalidwe; kugonjera kotereku kutha kumupangitsa munthu kukhala chinthu chongolamulildwa mopanda ufulu wosankha. Chimenecho sicholinga cha Mlengi. Iye amafuna kuti munthu, yemwe ndi ntchito yayikulu ya mphamvu yake ya kulenga, akafikile pamlingo wosinthika wapamwamba womwe iye angathe kuufikira. Mulungu amayika pamaso pathu madalitso apamwamba omwe amafuna atatibweretsera ife kudzera mu chisomo chake. Iye akutiyitana ife kuti tidzipereke kwa Iye, kuti Iye akachite chifuniro chake mwa ife. Zili kwa ife kusankha kumasulidwa ku ukapolo wa uchimo, kuti tigawane nawo ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.”— Ibid., pp. 43, 44.“Khristu anawonetsedwa ngati mpulumutsi wa anthu. Anthu samayenera kumadalira mu ntchito za iwo eni, ndi mu chilungamo cha iwo eni, kapena mwa iwo okha mu njira ina iliyonse, koma mwa mwana wa Nkhosa wa Mulungu amene achotsa machimo a dziko lapansi. Woyimira Atate anavumbulutsidwa mwa Iye. Kuyitana kunaperekedwa kudzera mwa Iye, kuti ‘Tiyeni tsono, tiweruzane,’ atero Yehova: ngakhale zoyipa zanu ziri zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale ziri zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa woti mbu.’ Kuyitana kumeneku kukufikiranso momveka bwino kwa ife lero lino. Musalole kuti kunyada, kapena kudzikuza, kapena kudzilungamitsa kuti kulepheretse wina aliyense kuvomereza machimo ake, kuti alandire lonjezano.”—Fundamentals of Christian Education, p. 239.

3. KHRISTU ANAPEREKA ZONSE Lachitatu , Julayi 28
a. Kodi ndi chani chomwe chamupatsa Khristu ufulu wowatengera ana Ake kumwamba? Akolose 1:14; Ahebri 7:25. “Mkati mwa m'dima woopsa, womwe unkawoneka kuti unasiyidwa ndi Mulungu, Khristu anachotsamo madontho omaliza a mu chikho cha tsoka la anthu. Mu maola owopsa amenewo, Iye anadalira pa umboni wokuvomereza kwa Atate Wake womwe unaperekedwa kwa Iye m’buyomo. Iye ankadziwa bwino khalidwe la Atate Wake; Iye anamvetsa chilungamo Chake, chifundo Chake, ndi chikondi Chake chachikulu. Mwa chikhulupiriro Iye anapumula mwa Iye, amene chinali Chimwemwe chake kumumvera. Ndipo monga mukugonjera Iye anadzipeleka Yekha kwa Atate, lingaliro losiiyidwa mu chikondero cha Atate Wake linachotsedwa. Mwa chikhulupiriro, Khristu anali wogonjetsa.”—The Desire of Ages, p. 756.“Mu mphatso ya Yesu, Mulungu anapereka kumwamba konse. Kutengera malingaliro a munthu, nsembe yotereyi inali kutaya chabe. Mu malingaliro a munthu, dongosolo lonse la chipulumutso ndi kutaya chifundo komanso zinthu zofunikira. Kudzikana komanso kudzipereka nsembe kwa mtima wonse zimatipeza kwina kulikonse. Khamu lakumwamba lingayang’ane modabwitsika ndi banja la anthu lomwe likukana kukwezedwa komanso kudzadzidwa ndi chikondi chopanda malire, chomwe chawonetsedwa mwa Khristu. Kotero angafuule niti, Chifukwa chani kutaya kwakukulu kotereku?“Koma chitetezero cha dziko lotayika chinayenera kukhala chodzaza, chochuluka, komano chokwanira. Msembe ya Khristu inali yochuluka kwambiri kufikira moyo wina uliwonse womwe Mulungu adawulenga. Sikukanatheka kuyikidwa malire kuti chiwerengero cha omwe angalandire Mphatso yayikuluyo chisapitirire. Anthu onse sanapulumutsidwe; komabe dongosolo la kuwombola si kutaya chabe chifukwa choti silikukwaniritsa zonse zomwe ukoma mtima wake waperekedwera. Payenera kukhala zokwanira komanso zotsala.”—Ibid., pp. 565, 566. b. Kodi Yesu amafuna chani kwa onse amene akufuna kukhala ana ake ndi kufuna kulandira Mzimu wake? Miyambo 23:26. “[Yesu] akuyembekezera mwachifundo kuti amve kuvomereza kwa a anthu osochera, ndi kulandira kulapa kwawo. Iye amayang'ana kubwezera kwa chiyamiko kuchokera kwa iwo, monga momwe mayi amayang'anira kumwetulira kochokera kwa mwana wake wokondedwa. Mulungu wamkulu amatiphunzitsa ife kumutchula Iye Atate. Iye akufunitsitsa kuti ife timvetsetse momwe mtima wake umatifunira mwakhama, komanso mwachifundo mu mayesero ndi mu masautso athu onse.”— Gospel Workers, p. 210.“Kodi timataya chani, tikapereka zonse? Mtima wodetsedwa ndi uchimo, kuti Yesu awuyeretse, nawutsuke ndi mwazi wake, ndi kutipulumutsa kudzera mu chikondi chake chosayerekezeka. Komabe anthu amaganiza kuti ndi zovuta kutaya zonse! Ndili ndi manyazi pomva zomwe izi zikulankhulidwa, ndili ndi manyazi kulemba zimenezi.”—Steps to Christ, p. 46.

4. KUDZIPEREKA KWATUNTHU Lachinayi , Julayi 29
a. Kodi khumbo lalikuru la Paulo kwa okhulupirira linali chiyani? Aroma 12:1; 1 Atesalonika 5:23. “Ngakhale zinenedwa kwa Israyeli wakale, mawu awa alinso ndi phunziro kwa anthu a Mulungu m’masiku ano. Pamene mtumwiyo anandaulira abale ake kuti apereke matupi awo ‘nsembe yamoyo, yopatukika, yokondweretsa Mulungu,’ iye anakhazikitsa mfundo za chiyeretso chenicheni. Sikuti chimenechi ndi chiphunzitso chabe, kapena malingaliro chabe, kapena mtundu wamawu chabe, koma ndi mfundo yamoyo, yogwira ntchito, mu moyo watsiku ndi tsiku. Mfundoyi imafuna kuti zizolowezi zathu za madyedwe, mamwedwe, ndi mavalidwe zikhale zotetezera thanzi lathu la thupi, thanzi la malingaliro, ndi thanzi la makhalidwe abwino, kuti tipereke kwa Ambuye matupi athu, osati chopereka choyipitsidwa ndi zizolowezi zolakwika, koma ‘nsembe yamoyo, yopatukika, yokondweretsa Mulungu.’”— The Sanctified Life, pp. 27, 28.“Tikuyenera kudzipereka tokha ku utumiki wa Mulungu, ndipo tikuyenera kuyesetsa kupereka pafupifupi chopereka changwiro mukuyesetsa kwathu konse. Mulungu sadzakondwera ndi chochepereka chilichonse chotsika kuposa chabwino chomwe ife tingapereke. Iwo amene amkonda Iye ndi mtima wonse, adzafunitsitsa kumupatsa Iye utumiki wabwino zedi wa moyo, ndipo nthawi zonse iwo adzakhala akuyesetsa kubweretsa mphamvu zawo zonse za umunthu kuti zikagwirizane ndi malamulo omwe adzalimbikitsa kuthekera kwawo kochita chifuniro chake.”—Patriarchs and Prophets, pp. 352, 353. b. Pamene khamu la anthu linamva nkhani ya Petro pa tsiku la Pentekoste, kodi ndi chiyani chomwe chidalemetsa mitima yawo? Machitidwe 2:37, 38. “[Khamulo] linamva ophunzira akunena kuti anali Mwana wa Mulungu amene anapachikidwa uja. Ansembe komanso olamulira ananjenjemera. Kusweka mtima ndi chisoni chachikulu zinawakhudza anthuwo. “Analaswa mtima mwawo, natitu kwa Petro ndi atumwi enawo, ‘Tidzachita chani amuna inu, abale?” Mkati mwa iwo omwe amkawamvetsera ophunzirawo panali Ayuda odzipereka, omwe anali owona mtima mu chikhulupiriro chawo. Mphamvu yomwe inatsogolera mawu a mlalikiyo inawatsimikizira kuti Yesu analidi Mesiya. . . .“Petro anawatsimikizila anthu okhudzikawo kuti anakana Khristu chifukwa choti ananamizidwa ndi ansembe komanso ndi owalamulira; ndi kuti ngati akanapitirizabe kuyang’ana kwa anthu awa kuti apeze uphungu, ndi kuyembekezera kuti iwo amuvomereze Khristu, iwo eni asanachite zimenezo, sangathekumulandira Iye. Amuna amphamvu amenewa, ngakhale ankadzinenera kuti ndi a umulungu, anali ndi cholinga chofuna chuma ndi ulemerero wa dziko lapansi. Samkafuna kubwera kwa Khristu kuti alandire kuunika.”—The Acts of the Apostles, pp. 43, 44.

5. KUPITIRIZA KUDZIPEREKA Lachisanu , Julayi 30
a. Ndi chani chomwe chimabweretsa kukhudzika kuti tidzipereke kwathunthu kwa Ambuye ndi kutha kuwonetsera chifaniziro cha Khristu? Afilipi 2:12, 13. “Mulungu sakukuuzani kuti mudzichita mantha kuti Iye adzalephera kukwaniritsa malonjezo Ake, kapena kuti kuleza mtima Kwake kudzatopa, kapena kuti chifundo Chake chidzaperewera. Chitani mantha kuti chifuniro chanu mwina sichidzagonjera ku chifuniro cha Khristu, kuti makhalidwe anu obadwa nawo ndi zizolowezi zanu zingadzalamulire moyo wanu. ‘Pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe chifukwa cha kukoma mtima kwake ndiye Mulungu.’ Chitani matha kuti mwina undekha udzalowerera pakati pa moyo wanu ndi Mphunzitsi wamkulu. Chitani mantha kuti mwina chifuniro chanu chidzawononga cholinga chachikulu chomwe Mulungu anafuna kuchikwaniritsa kudzera mwa inu. Chitani mantha mukudalira mu mphamvu zanu, chitani mantha mukuchotsa dzanja lanu mu dzanja la Khristu ndi kuyesa kuyenda mu njira ya m’moyo popanda kupezekapo Kwake kosatha.”—Christ’s Object Lessons, p. 161. b. Ndimotani momwe kukhazikika mu chikhulupiriro ndi kudzipereka kwathunthu ku mfundo zoyenera kungachirikizidwire? Agalatiya 2:20; Mateyu 16:24, 25. “Iwo amene akufuna kulandira dalitso la kuyeretsedwa akuyenera koyambirira kuphunzira tanthauzo la kudzipereka msembe. Mtanda wa Khristu ndiwo mzati wapakati womwe pa pachikidwapo ‘ulemerero wolemera woposa waukulu kwambiri ndi wosatha.'”—The Acts of the Apostles, p. 560.“Simungathe kuwusintha mtima wanu, simungathe pa nokha kupeleka chikondi cha mtima wanu kwa Mulungu; koma mungathe kusankha kumutumikira Iye. Mutha kumupatsa Iye chifuniro chanu; Kenako adzagwira ntchito mwa inu kuti mufune ndi kuchita mogwirizana ndi zomukondweretsa Iye. . . .“Kudzera mu kugwiritsa ntchito bwino chifuniro chanu, kusinthika kwaphumphu kudzachitika m’moyo wanu. Popereka chifuniro chanu kwa Khristu, mumadzigwirizanitsa ndi mphamvu yomwe ili pamwamba pa maulamuliro ndi phamvu zonse. Mudzakhala ndi mphamvu yochokera kumwamba yoti ikulimbitseni, kotero kuti kudzera mu kudzipereka kosalekeza kwa Mulungu mudzapangidwa kukhala ndi moyo watsopano, ingakhalenso moyo wa chikhulupiriro.”—Steps to Christ, pp. 47, 48.

MAFUNSO OBWEREZA PAWEKHA Lachisanu n’chimodzi , Julayi 31
1. Kodi chofunika ndi chani kuti tikapambane mu nkhondo yolimbana ndi m’dani wa miyoyo yathu? 2. Kodi nkhondo yeniyeni ndiiti kuti tikamugonjetse m'dani wogonjetsedwa kale? 3. Kodi tingaphunzirepo chani kuchokera mu mphatso ya Khristu ya chipulumutso chathu? 4. Kodi cholinga cha Mulungu kwa okhulupirira n’chani, kuthupi ndi ku uzimu? 5. Ngati chifuniro chathu chikugwirizana ndi chifuniro cha Mulungu, ndi chani chomwe chidzachitike tsiku ndi tsiku?
 <<    >>