Kubvomereza Vesi Loloweza: "Wobisa machimo ake sadzaona mwai; koma wakuwabvomereza ndi kuwasiya adzachitiridwa chifundo" (Miyambo 28:13).
Zowerenga Zoonjezera:
Steps to Christ, pp. 37–41.
“Kuvomereza komwe kuli kutsanulidwa kuchokera mkati mwa moyo kumapeza njira yopita kwa Mulungu wachifundo chosatha.” — Steps to Christ, p. 38.
1. CHIFUNDO CHA MULUNGU Loyamba, Julayi 19
a. Pamene takhudzika ndi uchimo omwe tinachita, tikuyenera kuchita chiyani? Miyambo 28:13; Yakobo 5:16.“Zoyeneraza zoti munthu alandire chifundo cha Mulungu ndi zosavuta komanso ndi zolungama ndinso zanzeru. Ambuye safuna kuti tichite chinthu chinachake chopweteka ndi cholinga chakuti machimo athu akhululukidwe. Sitikuyenera kuyenda maulendo ataliatali komanso otopetsa, kapena kuchita mapemphero opweteka, kuti tipeze chivomerezo cha miyoyo yathu kwa Mulungu wakumwamba, kapena kuti atikhululukire machimo athu; koma iye amene avomereza machimo ake ndikuwasiya adzachitiridwa chifundo.”— Steps to Christ, p. 37.b. Kodi zimenezi zimafuna kuti tikhale ndi khalidwe lotani? Miyambo 15:33; 19:23; Masalmo 34:18.“Iwo amene sanadzichepetse pamaso pa Mulungu pozindikira kulakwa kwawo, sanakwaniritsebe mfundo yoyambirira ya kuvomereza. Ngati sitinachiteko kulapa koteroko komwe sichikuyenera kulapidwa, ndipo ngati sitinavomereze machimo athu modzichepetsa moona, komanso mwa mtima osweka, ndi kuda uchimo wathu, sitinafunefunepo chikhululukiro cha uchimo moona mtima; ndipo ngati sitinafunefunenepo, ndiye kuti sitinawupeze mtendere wa Mulungu. Chifukwa chokhacho chimene sitimakhululukidwa machismo omwe tanachita kale, ndi chakuti sitimafuna kudzichepetsa mitima yathu, komaso sitimafuna kugonjera ku zoyenerera za mawu a choonadi. Malangizo omveka bwino aperekedwa pankhani imeneyi. Kuvomereza tchimo, kaya kwa pagulu kapena mwa mtseri, kukuyenera kukhala kochokera pansi pa mtima, komanso kufotokozedwa momasuka.” —Ibid., pp. 37, 38
2. KUBVOMEREZA NDI KUKHULULUKA Lachiwiri, Julayi 20
a. Kodi timakhumudwitsanso ndani, pamene takhumudwitsa munthu wina? Masalmo 51:4.“Mtumwi akuti, ‘Muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupemphererane wina ndi m’nzake, kuti tichiritsidwe.' Yakobo 5:16. Vomerezani machimo anu kwa Mulungu, yekhayo amene angathe kukhululukira, ndi kuvomereza zolakwa zanu kwa wina ndi m’nzake. Ngati mwamukhumudwitsa m’nzanu kapena m’nansi wanu, mukuyenera kuvomereza zolakwa zanu, ndipo ndi udindo wake kukukhululukirani mwa ulere. Kenako mukuyenera kupempha chikhululukiro kwa Mulungu, chifukwa m’bale amene mwamuvulazayo mwini wake ndi Mulungu, ndipo pomuvulaza iye mwachimwira Mlengi wake ndi mombolo wake.”—Steps to Christ, p. 37.b. Ndi chifukwa chani tikuyenera kuwakhululukira ena? Mateyu 6:14, 15; Aefeso 4:32.“Iye yemwe sakhululuka ena amadula njira yokhayo yomwe iye akanalandirira chifundo chochokera kwa Mulungu. Tisalingalire kuti timalungamitsidwa posawakhululukira iwo omwe ativulazawo, chifukwa choti iwo sanabwere kwa ife kudzavomereza cholakwacho. Ndi udindo wawo, mosakayikiranso, kuti adzichepetse mu kulapa ndi kuvomereza; koma tikuyenera kukhala nawo mzimu wachifundo kwa iwo amene atilakwira, posatengera kuti avomereza zolakwa zawo kapena ayi. Posatengera kuti ativulaza bwanji ife, sitikuyenera kusunga mangawa athu ndi kudzimvera chisoni tokha chifukwa cha kuvulazidwa kwathu; koma pamene tikuyembekezera kukhululukidwa machimo athu otsutsana ndi Mulungu, tiyenera kuwakhululukira onse omwe atichitira zoipa.” —Thoughts From the Mount of Blessing, pp. 113, 114.c. Kodi ndi chayani chomwe chikuyenera kutiphunzitsa udindo wathu kwa anthu? 1 Petro 4:8; Aroma 13:8.“Muloleni Khristu, Moyo wa umulungu, akhale mwa inu, ndi kuti akavumbulutse za chikondi chochokera ku mwamba kudzera mwa inu, chomwe chingawutse chiyembekezo kwa anthu opanda chiyembekezo, ndikubweretsa mtendere wakumwamba ku mtima wosweka ndi uchimo. Pamene tikupita kwa Mulungu, chimenechi ndicho choyenerezo choti tichikwaniritse pamayambiriro pamene, kuti, polandira chifundo chochokera kwa Iye, timadzipereka tokha kuti tikawonetsere chisomo chake kwa ena.”—Ibid., pp. 114, 115.“Tchimo lathu lalikulu ndi kusowa kwa khalidwe la umunthu lochitirana kwa munthu mzathu. Ambiri amalingalira kuti akuwonetsera chilungamo cha Mulungu pomwe akulephereratu kuwonetsera kukoma mtima kwake ndi chikondi chake chachikulu. Kawirikawiri anthu amene iwo amakumana nawo mwaukali ndi mwa nkhanza amakhala ali pansi kulimbana ndi mayesero. Satana akulimbana nayo miyoyo imeneyi, ndipo mawu ankhanza, komanso opanda chisoni amawafooketsa ndi kuwapangitsa kuti agwere mu mphamvu ya wonyengayo.”—The Ministry of Healing, p. 163.
a. Kodi ndi machimo ati omwe akuyenera kuvomerezedwa poyera pamene ena akuyenera kubvomerezedwa kwa Mulungu yekha? Masalmo 32:5; Mateyu 5:23, 24.“Kuvomereza koona nthawi zonse kumakhala ndi khalidwe lachindunji, ndipo kumavomereza machimo ena ake. Iwo akhoza kukhala amtundu woti mkubweretsedwa kwa Mulungu yekha; akhozanso kukhala machimo omwe akuyenera kuvomerezedwa kwa anthu yemwe adavulazidwa chifukwa cha machimowo; kapena akhoza kukhala oti anachitidwa poyera, pa gulu la anthu, ndipo machismo otere ayenera kuvomerezedwa pagulunso. Koma kuvomereza konse kuyenera kukhala kolunjika, komanso komveka bwino, kuvomereza machimo eni eni omwe walakwitsa”—Steps to Christ, p. 38.“Tchimo la mtseri likuyenera kuvomerezedwa kwa Khristu, yemwe ali mkhalapakati yekhayo pakati pa Mulungu ndi munthu. . . . Tchimo lililonse ndi mlandu pamaso pa Mulungu, ndipo likuyenera kuvomerezedwa kwa Iye kudzera mwa Khristu. Tchimo lililonse lapoyera liyenera kuvomerezedwanso poyera.”—Gospel Workers, p. 216.b. Kodi cholinga cha kubvomereza koona ndi chani? 1 Samueli 12:19.“M'masiku a Samueli, Aisrayeli anapatuka kuchoka kwa Mulungu. Iwo anali akuvutika ndi zotsatira za uchimo; chifukwa choti anataya chikhulupiriro chawo mwa Mulungu, nataya kuzindikira kwa mphamvu ndi nzeru Zake zolamulilira mtunduwo, anataya chidaliro chawo cha kuthekera kwake kowateteza ndi kuvumbulutsa njira Yake. Iwo anamusiya wolamulira wamkulu wa chilengedwe chonse, ndi kufuna kulamulidwa monga momwe mafuko owazungulira analili. Iwo asadawupeze mtendere adavomereza motsimikiza kuti: ‘Pamwamba pa zoipa zathu zonse tinaonjezerapo choipa ichi, chakuti tinadzipemphera mfumu.’ 1 Samueli 12:19. Tchimo lomwelo limene iwo anakhudzika nalo linayenera kuvomerezedwa.”—Steps to Christ, pp. 38, 39.c. Ndi machitachita otani omwe akuyenera kuchitidwa patsogolo pa kuvomereza? Yesaya 1:16, 17; Ezekieli 33:15.“Kuvomereza sikudzalandiridwa ndi Mulungu popanda kulapa moona mtima ndi kukonzanso. Pakuyenera kukhala kusinthika kotheratu m'moyo; chilichonse chomukhumudwitsa Mulungu chikuyenera kuchotsedwa. Ichi chidzakhala chotsatira chenicheni chomva chisoni ndi uchimo.” — Ibid., p. 39.“Moyo uliwonse wotembenuka mtima, monga Zakeyu, udzawonetsera kulowa kwa Khristu mumtima mwake posiya machitidwe osalungama, omwe akhala ukudziwika nawo m'moyo wake. Monga mkulu wa msonkho, moyowo udzapereka umboni wa kuona mtima kwake kudzera mu kubwenzeretsa.”—The Desire of Ages, p. 556
4. KUOPSA KODZILUNGAMITSA Lachinayi, Julayi 22
a. Pamene Ambuye anamufunsa Adamu ndi Hava za tchimo lawo, kodi iwo anawonetsera bwanji kuti silinali vuto lawo kwenikweni? Genesis 3:12, 13.“Adamu sakanatha kukana kapena kudzikanira za tchimo lake; koma m'malo mosonyeza kukhudzika mtima, iye anayesa kuyika mlandu wake pa mkazi wake, moteronso pa Mulungu Mwini: ndipo Iye anati, ‘Mkazi amene Inu munandipatsa kuti akhale nane anandipatsa ine chipatso cha mtengowo, ndipo ndinadya.’”—Patriarchs and Prophets, p. 57.“Adamu ndi Hava atadya chipatso choletsedwa, iwo anagwidwa ndi mantha komanso manyazi. Pamayambiliro lingaliro lomwe anali nalo linali la momwe angalikanire tchimo lawo ndi kuthawa chilango choopsa cha imfa. Pamene Ambuye anawafunsa za tchimo lawo, Adamu anayankha, poyika mlanduwo mbali imodzo pa Mulungu ndi mbali ina pa bwenzi lake. ‘Mkazi amene Inu munandipatsa kuti akhale nane anandipatsa ine chipatso cha mtengowo, ndipo ndinadya.’ Ndipo Mkaziyo anayika mlandu wake pa njoka, nati, ‘Njoka inandinyenga ine, ndipo ndinadya.’ Genesis 3:12, 13. Chifukwa chani munapanga njoka? Ndi chifukwa chani munayilola kuti ibwere mu Edeni? Awa anali mafunso omwe amatanthawuza mukuwiringura kwake chifukwa cha tchimo lake, kotero kuti amamuyimba Mulungu mlandu pa kugwa kwawo.”—Steps to Christ, p. 40.b. Ndi chifukwa chani kudzilungamitsa kumapangitsa kuti kuvomereza kusakhale kopindulitsa? Yobu 9:20; Luka 16:15.“Mzimu wodzilungamitsa unayambira mwa atate wamabodza ndipo wakhala ukuonetseredwa ndi ana amuna ndi akazi onse a Adamu. Kuvomereza kwa dongosolo ili sikumatsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu, ndipo sikudzalandiridwa kwa Mulungu. Kulapa kwenikweni kudzamutsogolera munthu kunyamula mlandu wake yekha ndi kuwuvomereza mopanda bodza kapena chinyengo.”—Ibid., p. 40.“Tisayesere kuchepetsa mlandu wathu podzikanira tchimo. Tivomereze mlingo umene Mulungu alionera tchimo, ndi kuti tchimolo ndi lalikuludi. Kalvari yekha angavumbulutse za koopsa ndi kuyipa kwa tchimo. Tikanawusenza mlandu wathu tokha, ukanatiphwanya. Koma m'modzi wosachimwayo watenga malo athu; ngakhale kuti sanayenera kutero, Iye wanyamula mphulupulu zathu. ‘Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi olungama Iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chili chonse.’ 1 Yohane 1:9. Chowonadi chaulemerero! —olungama ku lamulo lake lomwe, komanso olungamitsa onse amene akhulupirira mwa Yesu. ‘Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a cholowa chake? Iye sasunga mkwiyo wake ku nthawi yonse, popeza akondwera nacho chifundo.’ Mika 7:18.”— Thoughts from the Mount of Blessing,116.
5. KUBVOMEREZA POYELA Lachisanu, Julayi 23
a. Kodi Paulo anavomereza bwanji tchimo lake modzichepetsa komanso mwachindunji? Machitidwe 26:10, 11.“Zitsanzo m’mawu a Mulungu za kulapa kwenikweni ndi kudzichepetsa zimawonetsera mzimu wa kuvomereza, womwe mulibemo chodzikanira cha uchimo kapena kuyesera kudzilungamitsa. Paulo sanafune kudziphimba yekha; Iye anapenta uchimo wake ndi mtundu wake wodetsetsa, sanayese kuwuchepetsa mlandu wake. [kuchokera pa Machitidwe 26:10, 11].”—Steps to Christ, p. 41.b. Kodi Paulo adanena kuti chani mu kalata wake woyamba wa kwa Timoteo? 1 Timoteo 1:15.“Mwa ife tokha sitingathe kuona chilichonse koma kufooka kokha, palibe chotiyenereza ife kwa Mulungu, ndipo Satana amatiuza kuti zilibe phindu; patokha sitingathe kuchiritsa makhalidwe athu oyipa. Pamene tikuyesela kubwera kwa Mulungu, m'dani amatinong'oneza kuti, kupemphera sikopindulitsa kwa inu; kodi inu simunachite choyipa chija? Kodi inu simunamuchimwire Mulungu ndi kuwononga chikumbumtima chanu? Koma tikhoza kumuza m’danyo kuti, ‘mwazi wa Yesu Khristu mwana Wake umatisambitsa kutichotsera uchimo wonse.’ 1 Yohane 1:7. Pemene tikudzimva kuti tachimwa ndipo sitingathenso kupemphera, imeneyo ndiyo nthawi yoyenera kupemphera. Kaya tingachite manyazi motani ndi kudzimva kuchepetsetsa kwambiri, komabe tiyenera kupemphera ndi kukhulupirira. [kuchokera pa 1 Timoteo 1:15]. Chikhululukiro. . . ndi mphatso yoperekedwa kwa ife, ndyokhala nacho chilungamo chopanda banga cha Khristu, maziko ake popeleka.”—Thoughts from the Mount of Blessing, pp. 115, 116.c. Kodi ndi chani chomwe Mulungu walonjeza, tikavomereza machimo athu? 1 Yohane 1:9.“Mtima wodzichepetsa ndi wosweka, wogonjetsedwa ndi kulapa kwenikweni, udzayamikira chinachake cha chikondi cha Mulungu ndi mtengo wa Kalvari; ndipo monga momwe mwana amavomerezera kwa atate wake wachikondi, momwemonso moyo wolapadi udzabweretsa machimo ake onse pamaso pa Mulungu. Ndipo kwalembedwa, [kuchokera pa 1 Yohane 1:9].”—Steps to Christ, p. 41.