Back to top

Sabbath Bible Lessons

Kuyenda ndi Yesu

 <<    >> 
LASABATA, SEPTEMBER 12, 2026 Phunziro 11
Mwayi wa Pemphero Vesi Loloweza: “Koma iwe popemphera, lowa m’chipinda chako, nutseke chitseko chako, nupemphere Atate wako ali m’tseri, ndipo Atate wako wakuona m’tseri adzakubwezera iwe” (Mateyu 6:6).
Zowerenga Zoonjezera:   Steps to Christ, pp.93–104. 
“Pemphero ndilo kutsegulira mtima kwa Mulungu monga ngati kwa bwenzi. Osati kuti ndizofunikira kuti timudziwitse Mulungu chimene ife tiri, koma kuti zitithandize kuti timulandire Iye. Pemphero silimamupangitsa Mulungu kuti atsikire kwa ife, koma limatikweza ifeyo kwa Iye.”—Steps to Christ, p. 93.

1. WOPEMPHA WAMKULU Loyamba , Septemba 6
a. Monga Mwana wa munthu, ndi chiyani chomwe Yesu anachipeza kukhala chofunikira? Luka 5:16; Marko 6:46. “Onani Mwana wa Mulungu akuwerama m’pemphero kwa Atate Wake! Ngakhale ali Mwana wa Mulungu, amalimbitsa chikhulupiriro chake mwa pemphero, ndipo mwa kulumikizana ndi Kumwamba amatenga mphamvu yolimbana ndi zoipa komanso kutumikira zosowa za anthu. Monga Mbale Wamkulu wa mtundu wathu, Iye amadziwa zosowa za awo amene pozingidwa ndizofooka, komanso pokhala m’dziko la uchimo ndi mayesero, amafunabe kumutumikira. Iye amadziwa kuti atumiki amene amawawona kukhala ndikuthekera kowatumiza kukatumikira ndi anthu ofooka ndi olakwitsa; koma kwa onse amene amadzipereka kwathunthu kuntchito yake, Iye amalonjeza kuwapatsa thandizo lakumwamba. Chitsanzo cha Iye mwini ndi chitsimikizo kuti kupemphera moona mtima, mosalekeza kwa Mulungu mwa chikhulupiriro—chikhulupiriro chimene chimatsogolera kukudalira Mulungu kwathunthu ndi kudzipereka kotheratu kuntchito yake—chidzalimbika kubweretsa kwa anthu thandizo la Mzimu Woyera mu nkhondo yolimbana ndi uchimo.”—Gospel Workers, p. 511. b. Ndimotani momwe kachitidwe ka kapemphero ka Khristu kakukhalira chitsanzo kwa ife? Marko 1:35; Luka 6:12. “Yesu mwini, pamene anali kukhala pakati pa anthu, nthawi zambiri anali kukonda kupemphera.”—Steps to Christ, p.93.

2. PEMPHERO LA KHRISTU Lachiwiri , Septemba 7
a. Kodi Yesu anawaphunzitsa ophunzira ake kuti adzipemphera motani? Luka 11:1–4. “Pamene Yesu anali padziko lapansi, anaphunzitsa ophunzira ake mmene angamapempherere. Iye anawatsogolera iwo kuti adzipereka zosowa zawo za tsiku ndi tsiku kwa Mulungu, ndi kutaya pa Iye nkhawa zawo zonse. Ndipo chitsimikizo chimene anawapatsa chakuti mapemphero awo adzamveka, ndi chitsimikizonso ngakhale kwa ife. . . .Iye ndi m’bale wathu mu zofooka zathu, ‘anayesedwa m’njira zonse monga ifenso;’ koma monga wopanda tchimo, chikhalidwe chake chinakana zoipa; Iye anapirira nkhondo ndi kuvutika kwa mtima m’dziko la uchimo. Umunthu wake unapanga pemphero kukhala chofunikira komanso mwayi. Iye anapeza chitonthozo ndi chisangalalo polankhulana ndi Atate ake. Ndipo ngati Mpulumutsi wa anthu, Mwana wa Mulungu, anaona kufunikira kwa pemphero, koposa kotani ife anthu ofooka ndi ochimwa tikuyenera kuwona kufunikira kwa kupemphera mwakhama ndi mosalekeza?”— Steps to Christ, p.93, 94. b. Ndimotani momwe Baibulo likufotokozera za kudzipereka kwa Khristu, komanso chifukwa chimene izi zinali zofunikira kwambiri? Yesaya 50:4; Aheberi 2:10; 5:7–9. “Pamene umunthu unali pa Iye, anadzimva kusowekera mphamvu kwake kuchokera kwa Atate wake. Anali ndi malo apadera opempherako. Ankakonda kulumikizana ndi Atate wake m’malo chete a kumapiri. Munchitidwe umenewu, moyo wake woyera wa umunthu unalimbikitsidwa kuti athe kugwira ntchito ndi kupirira mayesero omwe angathe kukumana nawo. Mpulumutsi wathu amadziwa zofooka ndi zosowa zathu, chifukwa kuti anakhala wopempha, wopemphera usiku wonse, kufunafuna mphamvu zatsopano kuchokera kwa Atate ake, kuti akatulukire wolimbikitsidwa ndi wokonzeka kugwira ntchito ndi kupirira mayesero. Iye ndi chitsanzo chathu m’zinthu zonse.”— Testimonies for the Church, vol. 2, pp. 201, 202.“Ndinaona kuti palibe ngakhale m’modzi mwa achinyamata makumi awiri amene amadziwa chimene chipembedzo chochitachita chiri. Amadzitumikira okha koma nkumadzitchula atumiki a Khristu; koma ngati tsoka limene liri pa iwo siliwonongedwa, posachedwapa adzazindikira kuti mphotho ya olakwa ndi yawo. Ponena za kudzikana kapena nsembe chifukwa cha choonadi, apeza njira yosavuta yopitirira zonsezi. Mmalo momadandaulira mwakhama ndi misozi ndi kulira mwamphamvu kwa Mulungu kuti apeze chisomo chakukhululukira ndi mphamvu kuchokera kwa Iye yopewera mayesero a Satana, achipeza kukhala chosafunikira kuti akhale owona ndi odzipereka; akuwona kuti akhoza kukhala bwino popanda zimenezi. Khristu, Mfumu ya ulemerero, ankachoka yekha nthawi zambiri kupita kumapiri ndi kumalo a chipululu kukapemphera kwa Atate wake; koma munthu wochimwa, amene mwa iye mulibe mphamvu, amaganiza kuti angakhale moyo popanda pemphero lowirikiza.”— Ibid., vol. 1, p. 504, 505.

3. MWAYI WA PEMPHERO Lachitatu , Septemba 8
a. Kodi Yesu anasonyeza motani mtima wa Atate wake pa zosowa za anthu? Mateyu 6:6; 7:7–11. “Atate wathu wa kumwamba akuyembekezera kutipatsa ife chidzalo cha madalitso ake. Ndi mwayi wathu kumwa mochuruka pa kasupe wa chikondi chopanda malire. N’zodabwitsa motani kuti ife timangopemphera pang’ono! Mulungu ndiwokonzeka komanso wofunitsitsa kumva pemphero loona la ana ake odzichepetsa kwambiri, koma pali kunyalanyaza kwakukuru kowonekeratu kumbali yathu kumuuza Mulungu zosowa zathu. . . .“Mulungu ndi wanzeru kwambiri kotero kuti salakwitsa, ndipo ndi wabwino kwambiri kotero kuti sangakanize chinthu chabwino kwa iwo oyenda molungama. Potero musaope kumukhulupirira, angakhale musakuwona yankho la pemphero lanu nthawi yomweyo. Khulupirirani lonjezo lake losatsutsika lakuti, ‘Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu.’”—Steps to Christ, pp. 94, 96. b. Ndi chiyani chimalepheretsa mapemphero athu kumvedwa ndi Ambuye? Masalimo 66:18; Miyambo 28:13. “Malingaliro athu akhoza kuwoneka kuti ali kwa Mulungu; tikhoza kumalingalira pa ntchito zake, chifundo chake, ndi madalitso ake; koma zimenezi mukunena moona, sizitanthawuza kulumikizana naye. Pofuna kulankhulana ndi Mulungu, tiyenera kukhala ndi zoti timuwuze zokhudza moyo wathu weniweni.. . .“Ndichiyani chimene Angelo akumwamba angaganize zokhuza anthu osowa thandizo, amene ali pachiwopsezo choyesedwa, pamene mtima wa Mulungu wa chikondi chopanda malire ukukhumba kuwathandiza, wokonzeka kuwapatsa zambiri kuposa zimene iwo angapemphe kapena kuganiza, chonsecho iwo amangopemphera pang’ono chabe komanso ali ndi chikhulupiriro chochepa kwambiri? Angelo amakonda kugwada pamaso pa Mulungu, iwo amakonda kukhala pafupi naye. Iwo amaona kuti kulumikizana ndi Mulungu ndicho chimwemwe chawo chachikulu; chonsecho ana a padziko lapansi, amene akusowekera kwambiri thandizo limene Mulungu yekha ndiye angapereke, amaoneka okhutitsidwa kuyenda popanda kuwala kwa Mzimu wake, yemwe ndiye bwenzi la kupezekapo kwake.“Mdima wa woipayo umakuta onse amene amanyalanyaza kupemphera. Mayesero onong’oneza a mdani amawatsogolera iwo ku uchimo; ndipo zonsezi zimachitika chifukwa iwo sakugwiritsa ntchito mwayi womwe Mulungu wawapatsa muchikhazikitso cha kumwamba cha pemphero.. . .“Ngati timasekelera zoyipa mumitima mwathu, ngati tikukakamilira ku tchimo lirilonse lodziwika, Ambuye sadzatimvera; koma pemphero la munthu wolapadi ndi wosweka mtima limalandiridwa nthawi zonse. Pamene zolakwa zonse zodziwika zakonzedwa, tikhoza kukhulupilira kuti Mulungu adzayankha mapemphero athu. Kuyenedwa kwathu sikungatibvomereze ku chifundo cha Mulungu; ndi kuyenera kwa Yesu kokha komwe kudzatipulumutse, mwazi wake ndiwo udzatitsuke; komabe tiri ndi ntchito yoti tichite pokwaniritsa zinthu zofunika kuti tilandiridwe.”—Ibid., pp.93–95.

4. PEMPHERO LOPAMBANA Lachinayi , Septemba 9
a. Ndi zinthu zofunika ziti za pemphero lopambana poyerekeza ndi pemphero lofooka komanso losagwira ntchito? Ahebri 11:6; Maliko 11:24. “Tikapanda kulandira zinthu zomwe tinapempha pa nthawi yomwe tinapemphera, tikuyenera kukhulupilirabe kuti Ambuye wamva ndipo adzayankha mapemphero athu. Ife tiri olakwa ndipo sitimawona patali, kotero kuti nthawi zina timapempha zinthu zomwe sizingatipatse madalitso, ndipo Atate wathu wa kumwamba mwachikondi amayankha mapemphero athu potipatsa zomwe zingatipindulitse kwambiri—zomwe ife tokha tingafune ngati tingawone zinthu zonse momwe ziliri ndi maso owunikiridwa ndi Mulungu. Pamene mapemphero athu akuoneka ngati sakuyankhidwa, tiyenera kukakamira ku lonjezo; chifukwa nthawi yoyankha idzafika ndithu, ndipo tidzalandira dalitso lomwe tikulisowa kwambiri.”—Steps to Christ, p. 96. b. Pofuna kuti pemphero limvedwe ndi Ambuye, kodi tiyenera kukhala ndi mzimu wotani? Mateyu 6:12; Maliko 11:25, 26. “Tikamabwera kupempha chifundo ndi madalitso kwa Mulungu tiyenera kukhala ndi mzimu wachikondi ndi wokhululuka mumtima mwathu. Tingapemphere bwanji kuti, ‘Mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso tiakhululukira amangawa athu,’ chonsecho tikukhalabe mu mzimu wosakhululuka? Mateyu 6:12. Ngati tikufuna kuti mapemphero athu amvedwe, tiyenera kukhululukira ena mofanana ndi mmene ifeyo tikufunira titakhululukidwira.”—Ibid., p. 97. c. Ndichiyani chomwe tiphunzire kuchokera ku pemphero la Eliya lopemphelera mvula? 1 Mafumu 18:41–45. “Mnyamata wa Eliya anali kuyang’anira pamene Eliya anali kupemphera. Kasanu ndi kamodzi anabwerera kuchokera pa kuyang’anira, akunena kuti, Palibe kanthu, palibe mtambo, palibe chizindikiro cha mvula. Koma mneneriyo sanagonje ndi kukhumudwa. Anapitiriza kudzisanthula moyo wake kuti awone ngati panalipo pena pake pomwe analakwira Mulungu, anabvomereza machimo ake, ndipo potero anapitiriza kudzichepetsa pamaso pa Mulungu, uku akuyang’anirabe chizindikiro chakuti pemphero lake liyankhidwe. Pamene ankafufuza mtima wake, ankawoneka kukhala woperewera kwambiri, kwa iye yekha komanso pamaso pa Mulungu. Zinawoneka kwa iye mwini kuti anali chabe, ndipokuti Mulungu ndiye anali zonse; ndipo pamene anafika pa mfundo yodzikana yekha, ndikukakamilira kwa Mpulumutsi monga mphamvu yake yokha ndi chilungamo chake, yankho linabwera.”—The SDA Bible Commentary, vol. 2, p. 1035.

5. KUPIRIRA MUKUPEMPHERA Lachisanu , Septemba 10
a. Kodi atumwi akupereka malangizo otani ofunika okhudza pemphero? 1 Petro 4:7; Afilipi 4:6. “Pali kufunikira kwa khama mkupemphera; musalole chirichonse kuti chikusokonezeni. Yesetsani kwambiri kuti kulumikizana pakati pa Yesu ndi moyo wanu zisaleke. Funani mwayi uliwonse wopita kumalo amene mapemphero amachitikira. Iwo amene akufunadi kulumikizana ndi Mulungu amapezeka pa msonkhano wopemphererako, okhulupirika kuchita udindo wawo ndipo ali ndi changu chofuna kulandira madalitso onse amene angawapeze. Amagwiritsa ntchito mwayi uliwonse wodziyika okha pamalo amene angathe kulandira mizere ya kuwala kochokera kumwamba.”—Steps to Christ, p. 98. b. Monga kholo lirilonse, kodi Ambuye amayembekezera kuti ana Ake achita chiyani? Luka 11:10, 13; Yohane 14:13, 14. “‘M’dzina Langa,’ Khristu anauza ophunzira Ake kuti adzipemphera. M’dzina la Khristu omutsatira Akeonse amkuyenera kuyima pamaso pa Mulungu. Kupyolera mu mtengo wake wa nsembe yomwe inaperekedwa chifukwa cha iwo, iwowa ali ofunikira kwambiri pamaso pa Ambuye. Chifukwa cha chilungamo cha Khristu chochokera kwa Iye, iwowa amawerengedwa kukhala anthu amtengo wapatari. Chifukwa cha Khristu, Mulungu amakhululukira iwo amene amamuopa Iye. Samawona kuipa kwa wochimwa mwa iwo. Amaona mwa iwo chifaniziro cha Mwana Wake, amene iwo amakhulupirira.”—The Desire of Ages, p. 667.“Palibe nthawi kapena malo amene sipoyenera kupereka pemphero kwa Mulungu. Palibe chomwe chingalepheretse kukweza mitima yathu mu mzimu wa pemphero lowona. Pakati pa khamu la anthu mumsewu, pakati pa kugwira ntchito, tingatumize pemphero kwa Mulungu ndi kupempha chitsogozo cha kumwamba, monga Nehemiya anachitira pamene anapempha pamaso pa Mfumu Artaxerxes. Malo a pemphero angapezeke kulikonse kumene tiri.”—Steps to Christ, p. 99.

MAFUNSO OBWEREZA PAWEKHA Lachisanu n’chimodzi , Septemba 11
1. Ndi chitsanzo chiti cha kupirira m’pemphero chomwe chaperekedwa kwa okhulupirira onse? 2. Ndi ulosi uti womwe ukuwonetsa kufunika kwa pemphero m'mawa uliwonse? 3. Kodi chofunikira choyamba cha pemphero lopambana ndi chiyani? 4. N’chifukwa chiyani tiyenera kupitiriza kupemphera pamene tikadali kudikirirabe yankho? 5. Fotokozani tanthauzo lenileni la kupemphera m’dzina la Yesu.
 <<    >>