Chikondi cha Mulungu kwa Munthu Vesi Loloweza: “Taonani chikondi chimene Atate watipatsa, kuti titchedwe ana a Mulungu; chifukwa chake dziko lapansi silitidziwa ife, chifukwa silinam’dziwe Iye” (1 Yohane 3:1).
Zowerenga Zoonjezera:
Steps to Christ, pp. 9–15.
“Mulungu ndi chikondi. Monga kuwala kwa dzuwa, chikondi ndi kuwala ndi chimwemwe zimatuluka kuchokera kwa Iye kupita ku zolengedwa Zake zonse.”—Thoughts from the Mount of Blessing, p. 77.
1. MULUNGU NDI CHIKONDI Loyamba, Juni 2
a. Ndi umboni wotani wa chikondi cha Mulungu womwe waperekedwa kwa anthu? Eksodo 34:6, 7; Yona 4:2 (gawo lomaliza); Yeremiya 31:3.“Mawu a Mulungu amavumbulutsa khalidwe Lake. Iye mwini walengeza chikondi Chake chosatha ndi chifundo Chake. Pamene Mose anapempha, ‘Ndionetseni ulemerero Wanu,’ Yehova anayankha, ‘Ndidzapititsa ukoma Wanga wonse pamaso pako.’ Eksodo 33:18, 19. Uwu ndi ulemerero Wake. Ambuye anadutsa pamaso pa Mose, nati, ‘Yehova, Yehova Mulungu, wachifundo ndi wachisomo, woleza mtima, ndi wodzala ndi ubwino ndi choonadi, wosungira chifundo anthu zikwi, wokhululukira mphulupulu ndi zolakwa ndi uchimo.’ Eksodo 34:6, 7. Iye ndi ‘wosakwiya msanga, ndi wachifundo chachikulu,’ ‘chifukwa Iye akondwera ndi chifundo.’ Yona 4:2; Mika 7:18.”—Steps to Christ, p. 10.b. Kodi cholinga cha Mulungu potumiza Mwana wake chinali chiyani? Mateyu 11:27; Yohane 14:8, 9.“Satana anatsogolera anthu kuganiza kuti Mulungu ali ngati munthu amene khalidwe lake lalikulu ndi loweruza mwankhanza—yemwe ndi woweruza wankhanza, wokongoza ngongole mopanda chilungamo ndi mwankhanza. Iye amayerekezera Mlengi ndi munthu amene akuyang’ana ndi maso ansanje kuti azindikire zolakwa ndi zolakwitsa za anthu, kuti awapatse chilango. Yesu anabwera kudzakhala pakati pa anthu kuti achotse mdima umenewu, mwa kuonetsera chikondi chosatha cha Mulungu.”—Ibid., p. 11.
2. NTCHITO YA YESU Lachiwiri, Juni 29
a. Kodi Yesu anafotokozera bwanji za ntchito yake ya padziko lapansi? Luka 4:16–18.“[Kuchokera pa Luka 4:18] Iyi inali ntchito ya [Yesu]. Iye anayendayenda akuchita zabwino ndi kuchiritsa onse omwe anali oponderezedwa ndi Satana. Kunalibe midzi yonse kubuura kwa matenda m'nyumba iliyonse, chifukwa Iye anadutsamo ndi kuchiritsa odwala awo onse. Ntchito yake inapereka umboni wa kudzozedwa kwake kwaumulungu. Chikondi, chifundo, ndi kukoma mtima zinaonekera mu chochita chilichonse cha moyo wake; mtima wake unakhala wachifundo kwa ana a anthu. Iye anatenga chibadwa cha munthu, kuti afikire zosowa za munthu. Osauka kwambiri komanso odzichepetsa sanaope kumuyandikira. Ingakhale ana aang'ono ankakopeka naye. Iwo ankakonda kukwera pa mawondo ake ndikuyang'ana nkhope yowalabadirayo, yokoma mtima ndi chikondi.”—Steps to Christ, pp. 11, 12.“Yesu anaona mwa munthu aliyense munthu amene ayenera kupatsidwa kuyitanira ku ufumu Wake. Iye anafika pa mitima ya anthu mwa kupita pakati pawo ngati munthu amene amawafunira zabwino. Iye anawafunafuna m’misewu ya anthu onse, m’nyumba za anthu, m’mabwato, m’sunagoge, m’mphepete mwa nyanja, ndi pa phwando la ukwati. Iye anakumana nawo pa ntchito zawo za tsiku ndi tsiku, ndipo anasonyeza chidwi mu zochitika zawo za tsiku ndi tsiku. Iye anapereka malangizo ake m’nyumba, kubweretsa mabanja m’nyumba zawo pansi pa chikoka cha kukhalapo Kwake kwaumulungu. Chifundo chake champhamvu chinathandiza kukopa mitima. Nthawi zambiri ankapita kumapiri kukapemphera payekha, koma izi zinali kukonzetsera ntchito Yake pakati pa anthu omwe anali ndi moyo wotanganidwa. Kuchokera nthawi imeneyi Iye ankatuluka kudzathandiza odwala, kulangiza osadziwa, ndi phwanya maunyolo a akapolo a Satana.”—The Desire of Ages, p. 151.b. Ngakhale kuti anali wodzaza ndi chikondi ndi chifundo, kodi ndi chitsanzo chotani cha kukhulupirika kwa Khristu mu kudzudzula zolakwika? Yohane 9:39–41; Mateyu 21:12, 13.“Yesu sanapondereze mawu amodzi a choonadi, koma nthawi zonse ankawanena mwachikondi. Ankachita zinthu mwanzeru kwambiri komanso molingalira, chidwi cha chifundo mu kulumikizana ndi anthu. Iye sanali wamwano, sanalankhule mawu amphamvu mosayenera, sanamvetse ululu wosafunikira kwa munthu wokhudzika. Iye sanadzudzule kufooka kwa anthu. Analankhula choonadi, koma nthawi zonse mwachikondi. Anadzudzula chinyengo, kusakhulupirira, ndi kusayeruzika; koma misozi inali m’mawu Ake pamene ankalankhula mawu ake odzudzula mwamphamvu. . . Munthu aliyense anali wamtengo wapatali m’maso mwake. Ngakhale kuti nthawi zonse ankadzionetsera ulemu waumulungu, anawerama ndi ulemu waukulu kwa membala aliyense wa banja la Mulungu. Mwa anthu onse Iye anaona miyoyo yogwa yomwe cholinga chake chinali kuipulumutsa.”—Steps to Christ, p. 12.
3. MOYO WODZIKANA WEKHA Lachitatu, Jui 30
a. Ndi katundu wolemera wotani amene Mpulumutsi wathu ananyamula panthawi ya moyo wake padziko lino lapansi? Yesaya 53:5–7; Luka 2:48, 49.“Yesu ananyamula udindo waukulu woopsya wopulumutsa anthu. Iye ankadziwa kuti pokhapokha ngati pakhala kusintha kwakukulu pa mfundo ndi zolinga za mtundu wa anthu, onse adzatayika. Uyu anali katundu wa moyo Wake, ndipo palibe amene akanatha kuyamikira katundu amene anali pa Iye. Mu umwana, unyamata, ndi ukulu wake, Iye ankayenda yekha. Komabe, kunali kupezeka kumwamba kungokhala chabe pamaso pake. Tsiku ndi tsiku Iye ankakumana ndi mayeso ndi mayesero; tsiku ndi tsiku ankakumana ndi choipa, ndipo anaona mphamvu ya choipa pa iwo amene ankafuna kuwadalitsa ndi kuwapulumutsa. Komabe sanalephere kapena kukhumudwitsidwa.“Mu zinthu zonse Iye analondoloza zofuna zake kukukwaniritsa ntchito Yake. Iye analemekeza moyo Wake mwa kupanga chilichonse cha moyo wake kukhala chogonjera chifuniro cha Atate Wake. Pamene Iye ali mnyamata, amayi Ake, atamupeza mu sukulu ya arabi, anati, 'Mwana, wativutitsiranji chonchi?' Iye anayankha— ndipo yankho Lake ndilo mfundo yaikulu ya ntchito Yake ya moyo—'Munali kundifunafuna chifukwa chiyani? Simudziwa kuti ndiyenera kukhala m'ntchito ya Atate Wanga?'“Moyo wake unali wodzipereka msembe nthawi zonse. Iye analibe pokhala m'dziko lino, kupatulapo pamene kukoma mtima kwa abwenzi kunamupatsa Iye monga wapaulendo. Iye anabwera kudzakhala moyo wosaukitsitsa m’malo mwathu, ndi kuyenda ndi kugwira ntchito pakati pa osowa ndi ovutika. Wosazindikirika komanso wosalemekezedwa, Iye anayenda kupita ndi kutuluka pakati pa anthu omwe Iye anawachitira zambiri.”— Gospel Workers, pp. 42, 43.b. Kodi kufalikira kwa chikondi chachikulu cha Mulungu kumatiphunzitsa chiyani za Atate wathu wakumwamba? Yohane 3:16; 1 Yohane 4:9, 10.“Nsembe yaikulu iyi sinapangidwe kuti ipange mumtima mwa Atate chikondi pa munthu, osati kuti Iye afune kupulumutsa. Ayi, ayi! ‘Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero kuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha.’ Yohane 3:16. Atate amatikonda, osati chifukwa cha dipo lalikulu, koma Iye anapereka dipo chifukwa amatikonda. Khristu anali njira yomwe Iye akanatha kutsanulira chikondi chake chopanda malire pa dziko lochimwa. ‘Mulungu anali mwa Khristu, kuyanjanitsa dziko lapansi kwa Iye mwini.’ 2 Akorinto 5:19. Mulungu anazunzika ndi Mwana wake. Mu ululu wa Getsemane, imfa ya pa Kavale, mtima wa Chikondi Chopanda malire chinalipira mtengo wa chiwombolo chathu.” — Steps to Christ, p. 13.
4. WOLOWA M'MALO NDI DIPO LATHU Lachinayi, Julayi 1
a. Kodi maziko a chipulumutso cha miyoyo yathu ndi chiyani? 1 Akorinto 1:30; Machitidwe 16:31.“O, Khristu anali ndi njala ndi chikhumbo chachikulu chotani nanga cha moyo kuti apulumutse chomwe chinatayika! Thupi lopachikidwa pamtanda silinachepetse umulungu Wake, mphamvu Yake ya Mulungu yopulumutsa kudzera mu nsembe ya anthu, onse omwe angalandire chilungamo Chake. Pofa pamtanda, Iye anasamutsa mlandu kuchokera kwa munthu wochimwa kupita kwa Wolowa m'malo wake wa umulungu kudzera mu chikhulupiriro mwa Iye monga Mombolo wake. Machimo a dziko lolakwa, omwe m'chifaniziro akuimiridwa ngati 'ofiira ngati kapezi,' adawerengedwa kwa dipo la umulungu.”—This Day With God, tsamba 236.b. Kodi Khristu anachita chiyani kuti atipulumutse chomwe chili choposa khama kapena nzeru za munthu? Yohane 10:17; Aroma 5:6–8.“'Atate wanga wakhala akukukondani inu kwambiri kotero kuti amandikondanso Ine koposa chifukwa chopereka moyo wanga kuti ndikuwomboleni. Pokhala Wolowa m'malo mwanu ndi dipo lanu, popereka moyo wanga, potenga mangawa anu, zolakwa zanu, ndimakondedwa ndi Atate wanga kwambiri; pakuti ndi nsembe Yanga, Mulungu akhoza kukhala wolungama, komanso wolungamitsa iye amene akhulupirira Yesu.'“Palibe wina koma Mwana wa Mulungu amene akanatha kutipulumutsa; pakuti Iye yekha amene anali pachifuwa cha Atate ndiye akanatha kumulengeza Iye. Iye yekha amene ankadziwa kutalika ndi kuya kwa chikondi cha Mulungu ndiye akanatha kuchiwonetsa. Palibe china chocheperapo kupatula nsembe yopanda malire yoperekedwa ndi Khristu m'malo mwa munthu wochimwa yomwe ikanatha kusonyeza chikondi cha Atate kwa anthu otayika.”—Steps to Christ, p. 14.c. Kodi Yohane akanachitira umboni chiyani za wotiyimira pampando wachifumu wa Mulungu? 1 Yohane 1:1–3.“Pali ochepa okha amene amazindikira khalidwe loipa la uchimo, ndipo amamvetsetsa kukula kwa chiwonongeko chomwe chabwera chifukwa cha kuswa lamulo la Mulungu. Mwa kufufuza dongosolo lodabwitsa la chiwombolo chobwezeretsa wochimwa ku chifaniziro cha makhalidwe abwino a Mulungu, tikuona kuti njira yokhayo yopulumutsira munthu inapangidwa kudzera mukudzipereka msembe, ndi kudzitsitsa kosayerekezeka ndi chikondi cha Mwana wa Mulungu. Iye yekha ndiye anali ndi mphamvu yomenya nkhondo ndi mdani wamkulu wa Mulungu ndi munthu, ndipo, monga wolowa m'malo mwathu ndi dipo lathu, Iye wapereka mphamvu kwa iwo amene amamugwira Iye ndi chikhulupiriro, kuti akhale ogonjetsa m'dzina Lake, komanso kudzera mu ubwino Wake. ” — Christian Education, p. 112.
5. YESU ANALIPIRA DIPO Lachisanu, Julayi 2
a. Kodi n’chiyani chinapangitsa Khristu kukhala woyenera kulipira dipo la chiwombolo chathu? 1 Petro 1:18, 19; Ahebri 5:8, 9.“Mtengo wolipidwa kutiwombola, nsembe yopanda malire ya Atate wathu wakumwamba popereka Mwana wake kuti atifere, iyenera kutipatsa ife malingaliro apamwamba a zomwe tingakhale kudzera mwa Khristu. Monga tauziridwa ndi mtumwi Yohane poona kutalika, kuzama, ndi kukula kwa chikondi cha Atate kwa mtundu wowonongeka, anadzazidwa ndi kuyamikira ndi ulemu; ndipo, polephera kupeza chilankhulo choyenera chofotokozera ukulu ndi kukoma mtima kwa chikondi ichi, anaitana dziko lonse kuti lichione… . . . Ndi mtengo wanji umene izi zimaika pa munthu! Kudzera mu kuchimwa ana a munthu amakhala akapolo a Satana. Kudzera mu chikhulupiriro mu nsembe yotetezera ya Khristu ana a Adamu akhoza kukhala ana a Mulungu. Mwa kutenga khalidwe la umunthu, Khristu amakweza mtundu wa anthu. Anthu okugwa amaikidwa komwe, kudzera mu kulumikizana ndi Khristu, iwo angakhaledi oyenerera kutchedwa ‘ana a Mulungu.’ ” —Steps to Christ, p. 15.b. Ndi mawu ati omwe mtumwi Yohane anagwiritsa ntchito pofotokoza kukula kwa chikondi cha Mulungu? 1 Yohane 3:1, 2.“Chikondi choterechi chilibe chofanana nacho. Ana a Mfumu yakumwamba! Lonjezo lamtengo wapatali! Mutu wa kusinkhasinkha kwakukulu! Chikondi chosayerekezeka cha Mulungu ku dziko lomwe silinamukonde Iye! Lingaliroli lili ndi mphamvu yogonjetsa moyo ndipo limabweretsa malingairo mu ukapolo ku chifuniro cha Mulungu. Pamene tikuphunzira kwambiri khalidwe la Mulungu mu kuwala kwa mtanda, timaona kwambiri chifundo, kukoma mtima, ndi chikhululukiro zikugwirizana ndi kupanda tsankho ndi chilungamo, ndipo timazindikira bwino kwambiri maumboni osawerengeka a chikondi chomwe chilibe malire ndi chifundo choleza choposa chifundo cha mayi kwa mwana wake wopanduka.” —Ibid.
1. Fotokozani makhalidwe ofunikira kwambiri a khalidwe la Mulungu.2. Kodi Yesu anaulula bwanji khalidwe la Mulungu ali padziko lapansi?3. Kodi ntchito ya Khristu inakhudza bwanji zisankho zake?4. Mwa kukhala mlowa m'malo wathu, kodi Yesu amaphunzitsa maphunziro otani?5. Fotokozani mphatso yomaliza ya Khristu m'malo mwathu.