Back to top

Sabbath Bible Lessons

Kuyenda ndi Yesu

 <<    >> 
LASABATA, SEPTEMBA 19, 2026 Phunziro 12
Mmene Tingathanile ndi Kukaikila Vesi Loloweza: “Koma apemphe ndi chikhulupiliro, wosakakika konse pakuti wokaikayo afanana ndi pfunde la mnyanja lotengeka ndi mphepo ndikuwinduka nayo.” (Yakobo 1:6)
Zowerenga Zoonjezera:   Steps to Christ, pp. 105113 
“Mulungu samatipempha ife kuti tikhulupilire, popanda maumboni okwanira amene ife tingakhazikitsepo chikhulupiliro chathu.”—Steps to Christ, p. 105.

1. KODI KUKAYIKA NDI CHIYANI? Loyamba , Septemba 13
a. Ndichiyani chimene tikuyenera kukumbukira pamene tayesedwa kuti tidzisintasintha pakati pa chikhulupiliro ndi kukaikira? Yakobo 1:5-7. “Lonjezo la Mpulumutsi ndila kwa okhawo amene ali ofuna kutsatira ambuye mwanthunthu, Mulungu sakakamiza chifuniro cha wina aliyense; kotero Iye sangatsogolere iwo amene ali onyada kwambiri kukuphunzira, iwo amene amakhazikika mukutsatira kunjira za iwo eni. Kwa anthu amalingaliro awiri—iye amene amafuna kutsatira chifuniro chake, pamene akuzichula yekha kuti amachita chifuniro cha Mulungu—kwalembedwa, `Munthu ameneyu asaganize kuti azalandira kalikonse kuchokera kwa Mulungu.’ Yakobo1:7.”—Patriarchs and Prophets, p. 384. b. Ndichiyani chimene Ambuye wapereka ndi cholinga chogonjetsa kukaikira? Masalimo 119:105; Ahebri 11:1, 3, 6. “Chikhulupiliro chathu chiyenera kugonera pa maumboni, osati ku zoonetseredwa. Iwo amene akufuna kukaikira azakhala ndi mwayi pamene iwo amene amafuna kudziwa choonadi adzapeza maumboni ochuluka amene iwo angakhazikitsirepo chikhulupiliro chawo.”—Steps to Christ, p. 105.“Mulungu wapereka mu mawu ake umboni wokwanira wa khalidwe lake la umulungu. Choonadi chachikulu chimene chimakhuza chipulumutso chathu chinapelekedwa monveka bwino. Kudzera muthandizo la mzimu woyera, limene linalonjezedwa kwa onse amene akulifunafuna ilo mokhulupilika, munthu wina aliyense atha kuchizindikira choonadi ichi mwa iye yekha. Mulungu wapereka kwa anthu maziko olimba pamene angakhazikitsepo chikhulupiliro chawo.”—The Great Controversy, pp, 526,527

2. ZINSINSI ZA KUMWAMBA Lachiwiri , Septemba 14
a. Kodi tingafotokoze motani za zinsinsi zimene Mulungu sanazifotokoze? Dentelonomo 29:29; Yobu 38:4—11. “Mawu a Mulungu, monga khalidwe la Olemba wa umulungu, amafotokoza zinsinsi zimene sizingamvetsetsedwe mwanthunthu ndi zolengedwa zokhala ndi malire. Kulowa kwa uchimo mudziko, kusandulika kwa Khristu m’thupi la umunthu, kubadwa kwake, kuuka ndi maphunziro ena ambiri operekedwa m’Buku Lopatulika, ndi zinsinsi zokuya zomwe mzeru zaumunthu sizingakwanitse kufotokozera kapena kumvetsetsa modzadza. Koma tilibe chifukwa chokaikira mawu a Mulungu chifukwa sitingathe kumvetsetsa zinsinsi za machitachita Ake.”—Steps to Christ, p. 106.“Mulungu samakakamiza anthu kugonjetsa kusakhulupilira kwawo. Pamaso pawo pali kuunika ndi mdima, choonadi ndi bodza. Zili kwa iwo kusankha chimene iwo angachilandire. Malingaliro a munthu anapatsidwa mphanvu zosiyanitsira chabwino ndi choipa. Mulungu anapanga kuti munthu asamapenge chisankho kuchokera mummene thupi lake likumvera, koma kuchokera mu kulemera kwa maumboni, mosamalitsa kufananiza lemba ndi lemba. Pokhala kuti Ayuda anaika pambali tsankho lawo ndi kufananiza ulosi wolembedwa ndi Mfundo zimene zinaonetsera moyo wa Yesu, iwo akanazindikira chiyanjano chokongola pakati pa ulosi ndi kukwanilisidwa kwake mu moyo ndi utumiki wa m’galileya wodzichepetsayu.“Ambiri akunamizidwa lero munjira yofanana ndi yomwe Ayuda ananamizidwira. Aphuzitsi achipembezo amawelenga Baibulo mukuunika kwa chiziwitso cha iwo eni ndi miyambo, ndipo anthu fufuza malemba mwa iwo eni, ndikuweluza kwa iwo eni kuti choonadi ndi chiyani; komano iwo amagonjera ku chiweruzo cha atsogoleri awo, ndi kusiya miyoyo yawo mmanja mwa azitsogoleri awo. Kulalikira ndi kuphuzitsa kwa mawu Ake ndi njira imodzi yokha imene Mulungu anaidzodza mukufalitsa choonadi Chake; koma tikuyenera kubweletsa chiphuzitso munthu aliyense kumuyeso wa malemba opatulika.”— The Desire of Ages, pp.458, 459. b. Kodi zimazindikirika motani mu Buku Lopatulika kuti pali zinthu zina zovuta kuzimvetsetsa? 2 Petro 3:16. “Kuvuta kwa Malemba Opatulika kwakhala kukugwiritsidwa ntchito ndi achikunja ngati mfundo yotsutsa Baibulo; koma kutali ndi izi, kumapanga umboni wamphanvu wa kuuziridwa kwake kwa umulungu. Koma ngati malemba samafotokozera za Mulungu koma icho chimene ifeyo tingathe kuchimvetsetsa mosavuta; Ngati ukulu ndi mphanvu Zake zikanamvetsetsedwa ndi malingaliro okala ndi malire, kutere Baibulo likana lopanda umboni wachindunji wa ulamuliro wa Umulungu. Maphunziro a ulemerero ndi chinsinsi ofotokozedwa mmalemba akuyenera kuutsa chikhulupiriro mwa iwo monga mawu a Mulungu.”—Steps to Christ, p. 107,

3. KUOPSA KWA MTIMA WOSAKHULUPILIRA Lachitatu , Septemba 15
a. Kodi choopsa choziwika bwino kwa okhulupirira mumasiku ano otsiliza ndi chiyani? Ahebri 3:12; 2 Timoteo 4:3, 4. “Pamene Mulungu akutumiza kwa anthu machenjezo ofunikira kwambiri kotelo kuti uthengawu ukuonetsedwa ngati ukulalikidwa ndi Angelo opatulika owuluka pakatikati pa mlengalenga, Iye akufuna munthu aliyense wodzazidwa ndi mphanvu zakulingalira awulandire uthengawu. Chiweluzo choopsa chonenedwa motsutsana ndi kupembeza chilombo ndi fano lake (Chibvumbulutso 14:9—11), chidzatsogolera onse ku kuphunzira mwa mwakhama ulosi kuti aphunzire kuti chizindikiro cha chilombo ndi chiyani, nanga ndimotani tingapewere kuchilandira ichi. Koma magulu aanthu akupewetsa makutu awo kuchoka kukumvetsera choonadi ndipo akutembenukira ku nthano za chabe. Mtumwi Paulo anafotokoza, mukuyang’ana mmatsiku omalidza: “Nthawi idzafika imene sadzalora chiphuzitso cholamitsa.” 2 Timoteo 4:3. Nthawi imeneyo yafika tsopano modzaza. Khamu laanthu silikufuna choonadi cha m’Baibulo, chifukwa chimatsutsana ndi mtima wa uchimo, wokonda dziko lapansi; ndipo Satana akupereka chinyengo chimene iwo achikonda.”—The Great Controversy, pp. 594, 595. b. Ndichiyani chinaloseledwa zamakhalidwe la magulu awiri mumasiku otsiliza? Danieli 12:10; Chibvumbulutso 22:11. “Mulungu adzakhala ndi anthu padziko lapansi ochirikiza Baibulo, ndi Baibulo lokha basi, kukhala monga muyeso wa ziphuzitso zonse ndi maziko akukozanso konse. Maganizo a anthu ophunzira, Mfundo za sayansi, chikhulupiriro kapena mfundo za mabungwe a mpingo, zochuluka ndi zogawanika monga mipingo imene ziimira, mawu a gulu—osati mmodzi kapena onse aizi ziyesedwe monga umboni wa kapena wotsutsana ndi mfundo iliyonse ya chikhulupiriro cha chipembezo. Tisanavomereze chiphunzitso kapena lamulo lililonse, tiyenera kufunsa kuti kodi ‘Atero Ambuye’ pochirikiza chiphunzitsocho.”—Ibid.,p 595.“Kuunika kwatsopano kudzabvumbulutsidwabe mu mawu a Mulungu kwa iye amene akukhala mukulumikizana ndi dzuwa lachilungamo. Pasapezeke wina aliyense kufika kumapeto kuti palibe choonadi china chimene chingabvumbulutsidwe. Akhama, ofunafuna choonadi mwapemphero adzapeza miledzo yapamwamba yakuunika kuti ikawalabe kuchokera mmawu a Mulungu. Khamu la miyala ya mtengo wapatali siinamwazidwebe imene ikuyenera kusonkhanitsidwa pamodzi kuti ikakhale chuma cha otsala a anthu a Mulungu. Komano kuwala sikuperekedwa kuti kukhale mphamvu ya mpingo chabe, koma kuti kukawalire kwa iwo amene ali mumdima.”—Counsels on Sabbath shool work, p. 34

4. CHOYAMBITSA KUKAIKA CHENICHENI Lachinayi , Septemba 16
a. Kodi tingasiyanitse bwanji pakati pa chofunikira ndi chosafunikira? 2 Akolinto 13:5; Tito 3:9—11. “Pamene Mulungu wapeleka umboni okwanira wa chikhulupiliro, Iye sadzachotsa zozikanira zonse zopangitsa munthu kuti asakhulupilire. Onse oyang’ana kuli mbedza kuti akakolekeko kukaikira kwawo adzaipedza. Ndipo onse okana kulandira ndi kumvera mawu a Mulungu kufikira chikaiko chonse chitachotsedwa, ndipo palibenso mwayi ulionse wa kukaikira, iwo sazafika ku kuunika.”—The Great Controvesy, p. 527. b. Kodi ndi mdalitso wanji udzafike pa odzichepetsa? Yakobo 4:6,10; 1 Petro 5:6, 7. “ ‘Zosowa zonse zinaperekedwa, njala ya moyo wanga inakwaniritsidwa; ndipo tsopano Baibulo kwa ine ndi chibvumbulutso cha Yesu khristu. Kodi mukufunsa kuti mchifukwa chiyani ndimakhulupirira Yesu? Chifukwa choti Iye ali kwa ine mpulumutsi wa umulungu. Chifukwa chiyani ndimakhulupilira Baibulo? Chifukwa ndalipedza kuti ndi mawu a Mulungu ku moyo wanga.’ Titha kukhala ndi mboni mwa ife eni kuti Baibulo ndi loona, kuti Khristu ndi mwana wa Mulungu. Tikudziwa kuti sitikutsatira malingaliro opanda pake.”—Steps to Christ, p. 112. c. Ndimotani mtumwi Paulo akufotokozera zodutsamo za moyo za okhulupilira tsopano ndinso mtsogolo? 1 Akolinto 13:12. “Mmoyo uno tingayambe kuzindikira chabe mutu wodabwitsa wa chiombolo. Ndi kuzindikira kwathu kochepaku tiyenera kulingalira moona manyazi ndi ulemerero, moyo ndi imfa, chilungamo ndi chifundo, zimene zinakumana mu mtanda; komabe mukutambasula kwambiri kwa mphamvu zathu za malingaliro sitingakwanitsebe kumvetsetsa kufunikira kwake modzadza. Kutalika ndi kufupika, kuzama ndi mukukula, kwa chikondi cha Mulungu zimazindikilika mochepetsetsa. Dongosolo la chipulumutso silingamvetsetsedwe modzadza, ingakhale pamene oomboledwa adzaziona momwe iwo amaoneredwa ndikuziwa mmene iwo amadziwidwira; koma kupyola mu mibadwo yamuyaya choonadi chatsopano cidzakhalabe chikutambasuka ku malingaliro odabwa ndi achimwemwe.”—The Great Controversy, p. 651.“Mwachikhulupiliro titha kuona kutsogolo ndi kumvetsetsa chowinda cha Mulungu mukukula kwa mzeru, mphanvu za umunthu kulumikizana ndi umulungu, ndipo mphanvu iliyonse ya moyo kubweletsedwa mu kulumikizana mwachindunji ndi phata lakuunika. Tingathe kukondwera kuti zonse zomwe zimatibvutitsa ife pazimene Yehova amachita zizapangidwa kukhala zosabvuta, zinthu zobvuta kuzimvetsetsa tidzapeza kufotokozera kwake mu nthawi imeneyo; ndipo pamene mzeru zathu zofooka zimapeza chisokonekero chokhachokha ndi malonjezo osweka, tidzaona ungwiro weniweni ndi chiyanjano chokongola. [1 Akolinto 13:12]’”—Steps to Christ, pp.112, 113.

5. CHOLINGA CHA MULUNGU KWA ANTHU AKE Lachisanu , Septemba 17
a. Ndimunjira yanji yozindikirika imene Yehova wakhala akutambasula mawu ake munthawi ino pamene chimalidziro chili pafupi? Chibvumbulutso 10:2, 6, 7. “Buku lomwe linasindikizidwa chidzindikiro silinali buku la Chibvumbulutso, koma gawo la ulosi wa Danieli limene limakhudzana ndi matsiku otsiliza. . . [Kuchokera pa Daniel 12:4.] Pamene bukuli linasegulidwa, kulengezedwa kunachitika, “Sipadzakhalaso nthawi.” (Onani Chibvumbulutso 10:6.) Buku la Danieli tsopano ndilosasindikizidwaso, ndi chibvumbulutso chopangidwa ndi Khristu kwa Yohane chizafika kwa onse okhala pa dziko lapansi. Kudzera mukuchuluka kwa chidziwitso anthu akuyenela kukonzetseredwa kuima mu tsiku la mvula yamasika.”—Selected Messages, bk. 2, p. 105.“Ambiri anakhazikitsa lingaliro loti buku la chibvumbulutso ndi buku losindikizidwa, ndipo iwo sadzapereka nthawi yawo ndi kuwelenga zinsinsi zake. Iwo akulankhula kuti iwo ayenera kukhazikitsa chiyang’aniro pa ulemerero wa chipulumutso, ndikuti zinsinsi zobvumbulutsidwa kwa Yohane pa chisumbu cha patimo ndi chosafuna chidwi chawo kuposa izi. Koma Mulungu samalitenga bukuli kukhala lotere. . . .“Buku lachibvumbulutso limatsegula ku dziko lapansi zimene zakhalapo, zimene ziripo, ndi chimene chidzabwere; ndimachenjezo a athu amene chimalidziro chadziko lapansi chawafikira. Liyenera kuwelengedwa ndimantha a ulemu…“Ambuye mwini anabvumbulutsira kwa mtumiki wake Yohane zinsinsi za buku la Chibvumbulutso, ndipo Iye anapanga kuti liyenera kusegulidwa kukuwelengedwa ndi onse. Mubuku limeneli mukutambasulidwa zochitika zimene kunthawi ino zinadutsa, ndi zina zopatsa chidwi za muyaya zimene zikuchitika motidzungulira ife; maulosi ena aiwo sanafike pokwanilitsidwa modzadza kufikira kutsekedwa kwa nthawi, pamene mkangano waukulu omaliza pakati pa mphanvu za kumidima ndi kalonga wakumwamba kuzachitika.”—The SDA Bible Commentary [E.G. White comments], vol. 7, p. 954. b. Kodi okhulupilira ayenera kuchita chiyani pakuwelenga malemba? 2 Timoteo 2:15; Yohane 7:17.

MAFUNSO OBWEREZA PAWEKHA Lachisanu n’chimodzi , Septemba 18
1. Ndikhalidwe lanji limene tiyenera kukhala nawo ndicholinga chomvetsetsa choonadi? 2. Fotokozani chifukwa chiyani simalemba onse amene angamvetsetsedwe. 3. Chifukwa chiyani ambiri samafuna kulandira choonadi cha m’baibulo? 4. Ndichiyani chimene iwo onse amene amafuna kukaikira nthawi zonse amapedza? 5. Chifukwa chiyani kufuna kumvera kulikofunikira kukumvetsetsa choonadi?
 <<    >>