Back to top

Sabbath Bible Lessons

Kuyenda ndi Yesu

 <<    >> 
LASABATA, Ogasti 15, 2026 Phunziro 7
Yeso la Kukhala Ophunzira Vesi Loloweza: Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano. 2 Akorinto 5:17
Zowerenga Zoonjezera:   Steps to Christ 7, pp. 57—65 
“Khalidwe limaululidwa, osati ndi zochita zabwino nthawi zina kapena zochita zoipa nthawi zinanso, koma ndi zizolowezi zopitilira za mayankhulidwe ndi machitachita.”—Steps to Christ, pp. 57, 58.

1. NTCHITO YA MZIMU Loyamba , Ogasti 9
a. Kodi ndi phunziro lanji lomwe Khristu anaphunzitsa pakufotokoza ntchito ya Kutembenuka mtima? Yohane 3:5—8. “Munthu sangathe kunena nthawi yeniyeni kapena malo , kapena kulondoloza zochitika zolumikizana mu dongosolo la kutembenuka mtima ; koma izi sizionetsera kuti iye ndiosatembenuka….Monga Mphepo , imene sioneka , komabe zosatira zimaonekera komanso kumvedwa , ndi m’mene Ulili Mzimu wa Mulungu mu ntchito yake pa mtima wa munthu. Mphamvu imeneyi yakulenganso yomwe palibe diso la munthu lingathe kuona, imabereka moyo watsopano; imalenga munthu watsopano mu chifanizo cha Mulungu.” – Steps to Christ, p. 57. b. Kodi ndikusintha kotani komwe kudzaonekera mu moyo otembenuka moona? Aroma 12:9—18; 2 Akorinto 5:17. “Pamene sitingachite chilichonse chosintha mitima yathu kapena kudzibweretsa tokha muchiyanjano ndi Mulungu; Pamene sitikuyenera kuzidalira ife eni kapena ntchito zathu zabwino, miyoyo yathu idzaonetsera ngati chisomo cha Mulungu chikukhala mwa ife. Kusintha kudzaonekera mu khalidwe, zizolowezi ndi zofuna zathu. Kusiyana kudzaonekera mooneka bwino komanso motsimikizika chimene anali ndi chomwe ali…“Ndizoona kuti payenera kukhala khalidwe la kunja labwino pamaso pa anthu popanda mphamvu yatsopano ya Khristu. Chikondi cha chikoka ndi khumbo lofuna kukweza ena zingapangitse moyo wokhazikika m’makhalidwe abwino. Kuzipatsa ulemu kwathu kungatitsogolere ku kupewa maonekedwe oipa. Mtima wodzikonda sungachite zinthu zachifundo. Ndi mwanjira yanji, tsono, yomwe tingadziwire mbali yomwe ife tili?“ndi ndani ali ndi mtima? Ndi ndani amene malingaliro athu ali naye?” — Ibid., pp. 57, 58.

2. KUKHALA CHOLENGEDWA CHA TSOPANO Lachiwiri , Ogasti 10
a. Kodi ndi chipatso chanji chomwe chimabadwa mwa iwo odzazidwa ndi Mzimu Woyera? Agalatiya 5:22, 23. “Iwo amene amakhala cholengedwa chatsopano mwa Khristu Yesu amabala zipatso za Mzimu. . . Zinthu zimene ankadana nazo kale tsopano amazikonda, ndipo zimene ankakonda kale tsopano amadana nazo. Odzikuza ndi odzikweza amakhala ofatsa ndi otsika mu mtima. Achabe ndi amwano amakhala aulemu ndi osadzionetsera. Oledzera amakhala odziletsa, ndipo owononga amakhala oyera mtima. Miyambo yachabe ndi mafashoni a dziko lapansi amayikidwa pambali. Akhristu sadzafunafuna ‘kukongoletsa kwa kunja,’ koma ‘munthu wobisika wa mtima, mu chovala chosaola, cha mzimu wofatsa ndi wachete.’ 1 Petro 3:3, 4.”—Steps to Christ, pp. 58, 59.“Chikoka cha Mzimu Woyera ndi moyo wa Khristu mwa munthu . Sitimuwona Khristu kapena kulankhula naye, koma Mzimu wake woyera ali pafupi ndi ife pamalo alionse. Amagwira ntchito mwa aliyense amene amalandira Khristu. Onse amene amadziwa kupezeka kwa Mzimu amaonetsera zipatso za Mzimu—chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kufatsa, kuchita zabwino, chikhulupiriro.”—SDA Bible Commentary [E. G. White Comments], vol. 6, p. 1112. b. Kodi ndi Umboni wanji wa kulapa kwenikwenii? Ezekieli 33:14, 15. “Palibe umboni wa kulapa kwenikweni pokhapokha ngati kulapako kwabweretsa kukozanso kwa moyo. Ngati munthu abwezera chowinda, abweza zomwe anaba, avomereza machimo ake, ndi kukonda Mulungu ndi anzake, wochimwa akhoza kukhala wotsimikiza kuti wadutsa kuchokera ku imfa kupita ku moyo.“Pamene ife, monga anthu ochimwa ndi ophophonya, timabwera kwa Khristu ndi kutenga nawo mbali m’chisomo chake chachikhululukiro, chikondi chimatumphuka mu m’mtima. Katundu aliyense amakhala wopepuka, chifukwa goli limene Khristu amapereka ndi lopepuka. Udindo umakhala chisangalalo, ndipo kudzipereka nsembe kumakhala chimwemwe. Njira imene kale inkaoneka ngati yakutidwa ndi mdima, imakhala yowala ndi kuwunika kwa Dzuwa la Chilungamo.“Ukoma wa khalidwe la Khristu udzawoneka mwa otsatira ake. Chinali chisangalalo chake kuchita chifuniro cha Mulungu. Chikondi kwa Mulungu, ndi changu cha ulemerero wake, zinali mphamvu yoyendetsera moyo wa Mpulumutsi wathu. Chikondi chinakongoletsa ndi kukweza zochita zake zonse. Chikondi ndi cha Mulungu. Mtima wosakonzetseredwa sungayambitse kapena kubala chikondi. Chimapezeka mu mtima okha umene Yesu amaulamulira. ‘Tikonda ife, chifukwa anayamba Iye kutikonda.’ 1 Yohane 4:19. Mu mtima umenene wakonzedwanso ndi chisomo cha Mulungu, chikondi chimakhala mfundo yoyendetsera machitachita. Chimasintha khalidwe, chimayendetsa zilakolako, chimalamulira malingaliro, chimagonjetsa maudani, ndi kukweza zikhumbitso. Chikondi chimenechi, chikakhala m’moyo, chimakometsa moyo ndi kufalitsa chikoka chosinthira kwa onse ozungulira.”— Steps to Christ, p. 59.

3. ZOLAKWIKA ZIWIRI Lachitatu Ogasti 11
a. Kodi ndi Zolakwikwa ziti zowopsa zimene ambiri amene amadzitcha Akhristu amazivomereza? Afilipi 3:9; Aroma 10:3; Yakobo 2:17. “Pali zolakwa ziwiri zimene ana a Mulungu—makamaka amene angobwera kumene kuyamba kudalira chisomo chake—ayenera kusamala nazo kwambiri.Choyamba, chimene tafotokoza kale, ndi kuyang’anira ku ntchito zawo, kapena kudalira zomwe angachite, Kuzibweretsa okha muchiyanjano ndi Mulungu. Iye amene akuyesera kukhala woyera mtima mwa ntchito zake zokha posunga lamulo, akuyesera zosatheka. Zonse zimene munthu angachite popanda Khristu zimakhala zodetsedwa ndipo kuzikonda ndi tchimo. Ndi chisomo cha Khristu chokha, kudzera mwa chikhulupiriro, chimene chingatipangitse ife kukhala oyera mtima.“Cholakwika china, chomwe ndichowopsa mofanana, ndi kulingalira kuti chikhulupiriro cha mwa Khristu chimamasula munthu ku kusunga lamulo la Mulungu; kuti popeza mwa chikhulupiriro chokha timakhala nawo otenga mabli m’chisomo cha Khristu, zochita zathu zilibe ntchito pa chipulumutso chathu.”—Steps to Christ, pp. 59, 60. b. Kodi lonjezo la pangano latsopano limasonyeza bwanji kuti chisomo cha Khristu sichimatimasula ku kumvera lamulo la Mulungu? Aheberi 8:10; 10:16. “Lamulo la Mulungu ndi chisonyezo cha khalidwe lake lenileni; ndi chithunzi cha mfundo yayikulu ya chikondi, ndipo ndiwo maziko a ulamuliro wake kumwamba ndi padziko lapansi. Ngati mitima yathu yasinthidwa muchifanizo cha Mulungu, ngati chikondi chaumulungu chadzalidwa m’moyo, kodi lamulo la Mulungu silidzachitika m’moyo? Pamene mfundo ya chikondi yadzalidwa mu mtima, pamene munthu wasinthidwa kuti akhale ngati chithunzi cha amene anamupanga, lonjezo la pangano latsopano limakwaniritsidwa [Ahebri 10:16]. Ndipo ngati lamulo lalembedwa mu mtima, kodi silidzatsogolera moyo? Kukhala omvera—utumiki ndi kudzipereka kwa chikondi—ndizo chizindikiro chenicheni cha kukhala ophunzira.”— Ibid., p. 60“Mulungu amafuna panopa chimodzimodzi ndi chimene anafunira kwa oyera awiri mu Edeni, kumvera kwangwiro ku zofuna zake. Lamulo lake limakhala chimodzimodzi mu mibado yonse. Muyezo wa chilungamo waukulu umene unaperekedwa mu Chipangano Chakale sunatsitsidwe mu Chatsopano. Si ntchito ya Uthenga Wabwino kufooketsa zofuna za lamulo loyera la Mulungu, koma kubweretsa anthu pamene angathe kusunga malamulo ake.Chikhulupiriro mwa Khristu chimene chimapulumutsa moyo sichili monga chimene ambiri amachifotokoza. ‘Khulupirirani, khulupirirani,’ ndi kulira kwawo; ‘khulupirirani mwa Khristu yekha, ndipo mudzapulumutsidwa. Ndi zimene muyenera kuchita.’ Pamene chikhulupiriro chenicheni chimadalira Khristu mokwanira pa chipulumutso, chidzatsogolera ku kumvera kwathunthu lamulo la Mulungu.”—SDA Bible Commentary [E. G. White Comments], vol. 6, p. 1073.

4. CHIPULUMUTSO MPHATSO YAULERE Lachinayi , Ogasti 12
a. Kodi ndichiyani chomwe chikuyembekezereka kwa anthu amene akufuna moyo wosatha? 1 Yohane 5:2, 3; 1 Akorinto 7:19. “Ngati mudzipereka kwa [Khristu], ndi kumuvomereza kuti ndi Mpulumutsi wanu, ngakhale moyo wanu ukhale wodzazidwa ndi machimo, chifukwa cha Iye mudzawerengedwa ngati olungama. Khalidwe la Khristu lidzayimirira m'malo mwa khalidwe lanu, ndipo mudzavomerezedwa pamaso pa Mulungu ngati kuti simunachimwepo.Kuposera apo, Khristu amasinthanso mtima. Amakhala mu mtima mwanu mwa chikhulupiriro. Muyenera kusunga m’gwirizano uwu ndi Khristu mwa chikhulupiriro ndi kupereka mosalekeza chifuniro chanu kwa Iye; ndipo pamene mukuchita izi, Iye adzagwira ntchito mwa inu kuti mukhale ndi chikhumbo ndi kuchita mogwirizana ndi chifuniro chake. Chifukwa chake munganene kuti, ‘Koma moyo umene ndiri nao tsopano m’thupi, ndiri nao m’chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.’ Agalatiya 2:20. Ndipo Yesu ananena kwa ophunzira ake, ‘Pakuti wolankhula si ndinu, koma Mzimu wa Atate wanu akulankhula mwa inu.’ Mateyo 10:20. Ndipo ndi Khristu Wogwira ntchito mwa inu, mudzawonetsa mzimu womwewo ndi kuchita ntchito zabwino zomwezo ntchito za chilungamo, kumvera.“Choncho tilibe kanthu mwa ife tokha komwe tingadzitamandire nako. Tilibe maziko a kudzikwenza. Maziko athu okhawo a chiyembekezo ali mu chilungamo cha Khristu chimene chimaperekedwa kwa ife, ndi mwa icho chimene chimapangidwa ndi Mzimu wake kugwira ntchito mwa ife ndi kudzera mwa ife.”— Steps to Christ, pp. 62, 63. b. Ngakhale Ambuye wapanga njira kuti aliyense apeze chipulumutso, n’chifukwa chiyani ena amalephera kupeza njira imeneyo? Aefeso 2:8, 9; Machitidwe 4:12; Aroma 9:30–33. “M’malo moti chimasule munthu ku kumvera, ndi chikhulupiriro chokha chimene chimatipatsa gawo mu chisomo cha Khristu, chimene chimatipatsa mphamvu kuti tikhale omvera…“Chikhulupiriro chotchedwa cha mwa Khristu chomwe chimavomereza kumasulidwa kwa anthu ku udindo wokhala omvera kwa Mulungu, sichikhulupiriro, koma kudzikuza. ‘Pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiriro.’ Koma ‘chikhulupiriro, ngati chili chopanda ntchito, ndi chakufa.’ Aefeso 2:8; Yakobo 2:17. Yesu ananena za Iye mwini asanabwere padziko lapansi kuti, ‘Kuchita chikondwero chanu kundikonda, Mulungu wanga; Ndipo malamulo anu ali m’kati mwa mtima mwanga.’ Masalimo 40:8. Ndipo asanakwere kumwamba analengezanso kuti, ‘Ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m’chikondi chake.’ Yohane 15:10. Malemba amanena kuti, ‘Ndipo umo tizindikira kuti tamzindikira iye, ngati tisunga malamulo ake. . . . Iye wakunena kuti akhala mwa Iye, ayeneranso mwini wake kuyenda monga anayenda Iyeyo.’ 1 Yohane 2:3–6. ‘Chifukwa Khristu anavutika chifukwa cha ife, kutisiyira chitsanzo, kuti muyenera kutsatira mapazi ake.’ 1 Petro 2:21.”—Ibid., pp. 60–62.

5. KUKHALA MWA CHIKHULUPIRIRO Lachisanu , Ogasti 13
a. Kodi mtumwi Paulo ankakhala bwanji moyo wachipambano? 1 Akorinto 15:30, 31. “Muyenera kusunga kulumikizana uku ndi Khristu mwa chikhulupiriro ndi kupereka mosalekeza chifuniro chanu kwa Iye; ndipo pamene mukuchita izi, Iye adzagwira ntchito mwa inu kuti mukhale ndi chikhumbo ndi kuchita mogwirizana ndi chifuniro chake.”— Steps to Christ, pp. 62, 63.“Khristu, m’thupi lake la umunthu, anapanga khalidwe labwino kwathunthu, ndipo khalidwe limenelo akufuna kutipatsa ife. ‘Zolungama zathu zonse ziri ngati chovala chodetsedwa.’ Yesaya 64:6. Chilichonse chimene tingachite tokha chimakhala chodetsedwa ndi tchimo. Koma Mwana wa Mulungu ‘anawonekera kuti achotse machimo athu; ndipo mwa Iye mulibe tchimo.’ … Khristu anali womvera ku zofuna zonse za lamulo. Iye ananena za Iye mwini, ‘Kuchita chikondwero chanu kundikonda, Mulungu wanga; Ndipo malamulo anu ali m’kati mwamtima mwanga.’ Masalimo 40:8. … Mwa kumvera kwangwiro Iye wapanga kuti zikhale zotheka kwa aliyense kumvera malamulo a Mulungu. Pamene tidzipereka tokha kwa Khristu, mtima umayanjanitsidwa ndi mtima wake, chifuniro chimaphatikana ndi chifuniro chake, maganizo amakhala pamodzi ndi maganizo ake, malingaliro amakhala osungidwa mwa Iye; timakhala m’moyo wake. Ichi ndi chimene chimatanthauza kuvala zovala za chilungamo chake.”—Christ’s Object Lessons, pp. 311, 312. b. Kodi ndi chimwemwe chotani chomwe wolemba masalimo anachionetsera m’moyo wake? Masalimo 119:97. “Pamene tikulankhula za chikhulupiriro, pali kusiyana komwe tiyenera kukukumbukira. Pali mtundu wa chikhulupiriro chomwe chili chosiyana kwathunthu ndi chikhulupiriro chenicheni. Kukhalapo ndi mphamvu ya Mulungu, choonadi cha mawu ake, ndi mfundo zoona zimene ngakhale Satana ndi makamu ake sangathe kuzikana pa mtima. Baibulo limanena kuti ‘ziwanda zimakhulupiriranso, ndipo zimanthunthumira,’ koma ichi sichikhulupiriro. Yakobo 2:19. Pamene palibe kungokhulupirira mawu a Mulungu, koma kupereka chifuniro kwa Iye; pamene mtima waperekedwa kwa Iye, pamene chikondi chakhazikitsidwa pa Iye, pamenepo pali chikhulupiriro—chikhulupiriro chimene chimagwira ntchito mwa chikondi ndi kuyeretsa moyo. Mwa chikhulupiriro chimenechi mtima umasinthidwa kukhala chithunzi cha Mulungu.”— Steps to Christ, p. 63.

MAFUNSO OBWEREZA PAWEKHA Lachisanu n’chimodzi , Ogasti 14
1. Fotokozani umboni wa kutembenuka mtima. 2. Kodi kusiyana pakati pa munthu wakale ndi munthu watsopano ndi kotani? 3. Fotokozani zoopsa ziwiri zimene tiyenera kupewa m’moyo wathu wauzimu. 4. Pamene tikukhala m’chisomo, kumvera kumaikidwa malo anji? 5. Ndi malingaliro, zilakolako komanso zolinga zotani zimene zimakondedwa pamene Khristu akukhala mu mtima?
 <<    >>