Back to top

Sabbath Bible Lessons

Kuyenda ndi Yesu

 <<    >> 
LASABATA, OGASTI 22, 2026 Phunziro 8
Kukula mwa Khristu Vesi Loloweza: “Ndikakonzere iwo amene alira maliro m’zioni, ndi kuwapatsa chobvala kokometsa mmalo mwa phulutsa, mafuta akukondwa mmalo mwa maliro, chobvala cha matamando m’malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo achedwe mitengo ya chilungamo yakuiwoka Yehova, kuti iye alemekezedwe.” (Yesaya 61:3)
Zowerenga Zoonjezera:   Steps to Christ, pp.67—75. 
“Ndinu odalira pa Khristu, kuti muyende moyo wangwiro, monga nthambi ku phatha lake mukukula ndi kubereka zipatso’—Steps to Christ, p. 69.

1. GWELO LA KUKULA Loyamba , Ogasti 16
a. Ndimotani momwe malemba anafotokozera zokhuza kukula muchikhristu? Yesaya 61:3;1 Peter 2:2; Aefeso 4:14,15; Marko 4:26,27. “Palibe mzeru ndi luntha la munthu zomwe zingathe kutulutsa moyo mu zinthu zochepa za chilengedwe. Ndi kudzera m’moyo wokhawo umene Mulungu mwiniyekha amaupereka kuti zonse, kaya zomera kapena nyama, zikhale ndi moyo. Choncho ndikudzeranso m’moyo wochokera kwa Mulungu womwewo m'mene moyo wauzimu umabadwira m’mitima ya anthu.”—Steps to Christ, p .67 b. Ndichiyani chomwe chimaonetsera kudalira kwathu pa Khristu mukukula ndi kukhwima? Hoseya 14:5—7; 1 Akolinto 3:6,7. “Kudzera mu Mphatso yake yapamwamba ya Mwana wake Mulungu anakuta dziko lonse ndi mpweya wake wa chisomo chenicheni monga momwe mpweya ukutira dziko lonse lapansi. Onse amene amasankha kupuma mpweya wa moyowu adzakhala ndi moyo ndi kukula kufikira mu msinkhu wa abambo ndi amayi a mwa Yesu Khristu .Monga maluwa amatembenukira kudzuwa, kuti milezo ya kuwala ithandizire mukuonetsa bwino kukongola ndi maonekedwe ake, momwemonso ife tiyenera kutembenukira kudzuwa la chilungamo, kuti kuwala kwa kumwamba, kutiwalire, kuti khalidwe lathu lidzikula mofanana ndi Khristu.’—Ibid., p. 68.

2. KHALIDWE LATHU LOSOWA THANDIZO Lachiwiri , Ogasti 17
a. Ndi mfundo zanji zofunikira zimene Mbuye wathu anatambasulira kwa ophunzira ake iye asanamalidze utumiki wake wa dziko lapansi? Yohane 15:4—7. “Ambiri amaganiza kuti akhodza kuchita mbali ya ntchito zina pa iwo okha. Iwo anadalira mwa Khristu kuti machimo awo akhululukidwe, koma tsopano ndi mphamvu zawo zokha akuyetsera kuti akhale angwiro. Koma kuyesera kulikonse kwa mtundu uwu kumalephera. Yesu anati, popanda ine, simungathe kuchita kanthu. Kukula kwathu mu chisomo, chisangalaro chathu, kupindula kwathu zonse zimadalira pakulumikizana kwathu ndi Khristu. Pokhala mwa Iye tsiku ndi tsiku, ola ndi ola, timakula mwa chisomo. Iye sioyamba yekha, komanso wotsiriza wachikhulupiliro chathu. Ndi Khristu amene ali woyamba, wotsiliza ndi wa nthawi zonse. Iye ayenera kukhala ndi ife, sipokhapokha poyamba pokha ndi mapeto antchito yathu ayi, komanso mu khwelero lililonse la njira.”—Steps to Christ, p.69.“Ngati muli ofuna kuphunzira kufatsa ndi kuzichepetsa mtima mu sukulu ya Khristu, Iye moona azakupatsani mpumulo ndi mtendere. Ndi chobvuta kwambiri kusiya chifuniro chanu chomwe ndi njira zanu. Koma mukaphunzira kutero mudzapeza mpumulo ndi mtendere. Kunyada, undekha ndi zikhumbitso zanu zikuyenera kugonjesedwa; zifuniro zanu zikuyenera kumezedwa mu chifuniro cha Khristu. Choncho moyo wonse udzakhala monga nsembe yozipereka ya chikondi chosatsithika. Machitidwe ndi mawu anu zonse zidzaonetsera chikondi. Monga moyo wa mpetsa umafalikira kudutsira mu nthambi zikulizikulu kenako kufika pansi pa nthambi zing’onozing’ono, mpakana m’masamba akusonga, momwemonso chisomo ndi chikondi cha Khristu chimayaka ndi kukhazikika m’moyo, chimatumiza mphanvu zake kukafalikira ku mbali zonse za thupi lonse, ndi kulamulira machitachita a thupi ndi malingaliro.”—The SDA Bible Commentary [E.G. White comments] vol.5,pp.1091.1092. b. Kodi chinsinsi chakukula mwa Khristu ndichiyani? Akolose 2:6; Ahebri 10:38. “Munazipereka nokha kwa Mulungu kuti mukhale wake modzadza, kumtumikira ndi kumumvera Iye, ndipo munatenga Khristu monga mpulumutsi wanu. Simungathe kuchita chozitetezera machimo anu mwa inu nokha kapena kusintha mtima wanu, koma pakuzipereka nokha kwa Mulungu, mumaonetsa chikhulupiliro kuti Iye mwa Khristu Yesu anachita zonse izi chifukwa cha inu. Mwachikhulupiliro mumakhala aKhristu, ndipo mwa chikhulupiliro mumakula mwa Iye. Kudzera mukupereka ndi kulandira muyenera kupereka zonse, mtima wanu, chifuniro chanu, utumiki wanu, kuzipereka nokha kwa Iye mukumvera zofuna zake zonse; ndipo muyenera kuzitengera zonse, Khristu, wodzala ndi m’dalitso wonse, kukhala mumtima mwanu, kukhala mphamvu yanu, chilungamo chanu, nthandizi wanu wamuyaya kuti akupatseni inu mphamvu zakumvera.”—Steps to Christ, pp, 69,70

3. KUDZIPEREKA TSIKU NDI TSIKU Lachitatu , Ogasti 18
a. Kodi ndi udindo wanji woyambilira wa ana a Mulungu pamene akuyamba tsiku lirilonse? Masalimo 5:3. “Dziperekeni nokha kwa Mulungu mamawa, chipangeni ichi kukhala ntchito yanu yoyambilira. Lolani kuti pemphero lanu likhale lotele, “Ambuye nditengeni ine monga m'mene ndiliri ndikuika mzeru zanga zonse pamapazi anu. Ndigwiritseni ntchito muutumiki wanu mukhale mwa ine, ndipo lolani ntchito zanga zilembedwe mwa inu. Ichi chikhale chochitika cha tsiku ndi tsiku. Mamawa ulionse ziperekeni nokha kwa Mulungu pa tsiku limenelo pelekani dongosolo lanu kwa Iye kuti zikatengedwe kapena kupelekedwa monga momwe chipambano chake chingalozere. Ndi mwa tsiku ndi tsiku momwe mungapelekere moyo wanu m’manja a Mulungu, ndipo moyo wanu uzaumbidwa mochulukira pa moyo wa Khristu.”—Steps to Christ, p. 70. b. Ndi kuitanira kwanji kumene Khristu akukulitsa tsiku ndi tsiku? Mateyu 11:28, 29. “Kukhala moyo wanu mwa Khristu ndiko kukhala moyo wosapuma. Sipakuyenera kukhala kuzimva kokwanilisidwa, koma pakuyenera kulumikizana, chidaliro cha mtendere. Chiyembekezo chanu sichiri pa inu nokha; chili mwa Khristu. Zofooka zanu zimalumikizana ku mphanvu zake, kupanda chiziwitso kwanu kumalumikizana ndi mzeru zake, kulephera kwanu kulumikizana ndi kupilira kwake kwapamwamba. Tsopano simukuyenera kuziyang’anira pa inu nokha, musalore malingaliro anu akhazikike pa undeka, koma yang’anani pa khristu, lolani malingaliro anu akhazikike pa chikondi chake, pakukongola kwa ungwiro, za khalidwe lake. Khristu mukuzikaniza kwake, Khristu mukuzichepetsa kwake, Khristu muungwiro ndi kupatulika kwake, Khristu muchikondi chake chapamwamba, izi ndizo mfundo za maphunziro oti azilingalilidwa m’moyo. Ndi kudzera mukumukonda Iye, kuphunzira kwa Iye, kudalira modzaza pa Iye, kuti mumasandulika kukhala ofanana naye.”—Ibid.,pp.70, 71. c. Kodi phata lenileni lokhalira ndi mtendere wammalingaliro ndi chiyani? Yesaya 26:3, 4; 30:15. “Onse angamutenge Khristu pa mawu ake, ndi kupereka miyoyo yawo kuti aisunge, kupereka miyoyo yawo kudongosolo lake, adzapedza mtendere ndi bata. Palibe chakudziko lapansi chingawapangitse iwo kukhala achisoni pamene Khristu mukupezeka kwa akuwapanga iwo kukhala amsangala. Mukubvomereza zochitika mumakhala mpumulo wa ngwiro… Miyoyo yathu itha kumaoneka yosowa chiyembekezo; koma pamene tizipereka tokha kwa wamkulu, kwa ogwira ntchito wamzeru, Iye azabweletsa njira ya moyo ndi khalidwe zimene zidzakhale za kuulemelero wake.“Kumwamba kumayambira pamene kudzera mwa Yesu timalowa mpumulo wake. Timayankha kukuitanira kwake, Idzani, phunzirani kwa ine, ndipo mukubwela kumeneku timayamba moyo wamuyaya.”—The Desire of Ages, p. 331.

4. KULINGALIRA KUMATHANDIZA PA KUSINTHA Lachinayi , Ogasti 19
a. Kodi zotsatira ndizanji pamene tiloza malingaliro athu kukhazika pa Yesu mmalo momaziyang’ana tokha? 2 Akolinto 3:18. “Pamene tiyang’ana mosalekeza pa Yesu ndi diso lachikhulupiriro, tidzalimbikitsidwa. Mulungu adzapanga bvumbulutso lapamwamba kwa onse akumva njala ndi ludzu la Iye. Iwo adzapedza kuti Khristu ndi Mpulumutsi wa munthu aliyense payekha. Pamene iwo akudya pa mawu ake, adzapedza kuti ndi moyo ndi mzimu. Mawu amaononga khalidwe lachibadwa, khalidwe lakudziko, ndi kukhazikitsa moyo watsopano mwa Yesu Khristu, mzimu woyera umabwera m’moyo monga mtonthonzi. Kudzera mu mphanvu zotsinthira za chisomo chake, chithunzithunzi cha Mulungu chimaonekera mwa ophunzira, Iye amakhala cholengedwa chatsopano. Chikondi chimatenga malo achiwawa, ndipo mtima umalandira chifanizo cha Umulungu.”—The Desire of Ages, p. 391.“Pamene malingaliro akhazikika pa undekha, iwo amachosedwa kwa Khristu, yemwe ndi gwelo la mphanvu ndi moyo. Ndi cholinga cha satana kuti chidwi chichoke kwa Mpulumutsi ndi kutipewetsa kulumikizana ndi kupereka moyo kwa Khristu. Zosangalatsa za mdziko, chisamaliro cha moyo ndi zovuta ndi zisoni, zolakwa za ena kapena zolakwa za iwe mwini ndi zophophonya, izi zonse iye adzafuna kutembenuzira malingaliro awo. Simukuyenera kulumikizana ndi zotengela zake. Ambiri amene ali ndi chikumbumtima chabwino ndinso amene ali ndi khumbo lokhala okondweretsa Mulungu Iyenso adzawatsogolera kukukhazikika mu zolakwitsa zawo ndi zofooka, ndi munjira imeneyi kuwalekanitsa iwo kwa Khristu amene amayembekezera kupeza chiyembekezo . Sitikuyenera kupanga undekha kukhala gwelo lathu ndi kukhazikika munkhawa ndi mantha za momwe tidzapulumutsidwire. Zonse izi zimachosa miyoyo kuchoka ku gwelo la mphamvu zathu. Perekani ndi kusunga miyoyo yanu kwa Mulungu ndi kudalira kwa iye. Lankhulani ndi kulingalira za Yesu. Lolani undekha uchotsedwe mwa Iye.”— Steps to Christ, pp. 71, 72. b. Ndi chiyani tingaphunzireko kuchokera mukusintha komwe kunabwela pa akuphunzira atatha iwo kukhala pamodzi ndi Khristu muutumiki wake wa tsiku ndi tsiku? Machitidwe 4;13. “Mukupenyerera pa (Yesu) timasandulika kukhala muchifanizo chake kuchoka kuulemerero kupita kuulemerero monga mwa mzimu wa Ambuye.’ 2 Akolinto 3:18.“Ndimomwemonso mene ophunzira oyambilira anapezera kufanana ndi mpulumutsi wawo wokondedwa. Pamene ophunzirawo amanva mawu a Yesu, iwo amaona kusowekera kwawo kwa Iye. Iwo amaganiza, iwo apeza, iwo amamutsatira iye. Iwo anali ndi iye mnyumba, pa gome, mukuyandikana, m'maminda, iwo anali ndi iye monga ophunzira ndi mphuzitsi tsiku ndi tsiku kulandira kuchokera pa milomo yake chiphuzitso cha choonadi chopatulika. Iwo amamuyang’ana Iye monga akapolo kwa mbuye wawo, kuphunzira udindo wawo, ophunzira amenewo anali amuna onga zotengela zofooka monga tilili ife. Yakobo 5:17. Iwo anali ndi nkhondo yofanana yolimbana ndi tchimo. Iwo amasowekela chisomo chofanana kuti ayende moyo wangwiro.”— Ibid., pp.72,73.

5. LONJEZO KWA IFE Lachisanu , Ogasti 20
a. Ndi lonjezo lanji limene Yesu analisiya kwa omutsatira ake mukukumana ndi zovuta za udani wa mdzikoli? Mateyu 28:20 “Pamene khristu amakwera kumwamba, chikumbumtima cha kupezeka kwake chinali pakati pawo pamodzi ndi otsatira ake. Kunali kupezeka kwa payekha, kodzaza ndi chikondi ndi kuunika. Yesu, mpulumutsi anayenda ndi kulankhula ndi kupemphera ndi iwo. Iye amene analankhula za chiyembekezo ndi chitonthozo m’mitima yawo, pamene uthenga wa mtendere unakali pa milomo yake, anachotsedwa pakati pawo kupita kumwamba, ndi kumveka kwa mawu ake kunabwelelanso pakati pawo pomwe khamu la Angelo limamulandira Iye, ndikuti “Ine ndili pamodzi ndi inu kufikira kumapeto nthwi ya dziko lapansi;” mateyu28:20.”—Steps to Christ, pp. 73.74. b. Ndi malangizo anji ofunikira amene Yesu anawasiira ophunzira ake chotelo kuti akazindikire choyenera kuchita munthawi ya kusowa? Yohane16:23,24; 14:16—18. “Pamene anasonkhana pamodzi khristu atakwela kumwamba iwo anali othekera kukupereka zosowa zawo kwa atate mudzina la Yesu…Iwo anakweza manja awo achikhulupiliro pamwamba ndi pambamba ndi wotsutsa wamkulu, Aroma8:34. Tsiku la pentecositi linawabweletsa iwo mukupezeka kwa mtonthonzi amene khristu analankhula za iye, “Iye adzakhala ndi inu;” ndipo Iye analankhulanso kuti, “Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Wokhulupilira ine, ntchito zimene ndicita adzachita zoposa izi; chifukwa ndipita ine kwa Atate. Yohane 14:12; 6:7. Ndi kudzera mwa mzimu woyera, momwe Khristu akuyenera mopitilira kukhala m’mitima ya ana ake. Kulumikizana kwake kumakhala chifupi kwambiri kuposera m’mene anali ndi iwo mwakuthupi; kuunika, ndichikondi ndi mphanvu zokhalira mwa Khristu zinaonetsedwa kudzera mwa iwo, chotelo kuti anthu, mukuyang’ana modabwitsika; anatenga chiziwitso kwa iwo kuti iwo anakhalapo ndi Yesu.’ Machitidwe4:15.’—Ibid.,pp. 74, 75.

MAFUNSO OBWEREZA PAWEKHA Lachisanu n’chimodzi , Ogasti 21
1. Pamene tikukula monga ngati zomela, chifukwa chiyani tikusowekera thandizo lochokera kumwamba? 2. Monga zomera zimasowekera mibvumbi ndicholinga chokula muuzimu? 3. Ndichiyani chimapangitsa kuzipereka kwa tsiku ndi tsiku kukhala kofunikira kwa ife aliyense payekha payekha? 4. Chifukwa chiyani Mulungu ali ndi khumbo kwa ife mukuchotsa undekha pa Yesu nthawi zonse. 5. Ndi lonjezo lanji limene lingakhale mu zenizeni tsiku ndi tsiku mmoyo wa Okhulupilira aliyense?
 <<    >>