Back to top

Sabbath Bible Lessons

Maphunziro AmBaibulo Apa Sabata

 <<    >> 

MAWU OTSOGOLERA

Chaka chino, tiphunzira magawo anayi akotala pa buku la UthengaWabwino waYohane. Chifukwa cha kudzichepetsa, mlembi wa Uthenga Wabwino wachinayi sakudzizindikiritsa yekha, ndipo samadzitchula kuti ndi mmodzi wa ophunzira awiri amene anatsatira Yesu poyamba (Yohane 1:37). M’malo mwake, iye ananena kuti “wophunzira wina,” “wophunzira ameneyo,” “wophunzira... amene anamkonda,” “wophunzira amene Yesu anamkonda,” ndi “wophunzira amene akuchitira umboni za izi” (Yohane 18:15; 19:26; 21:20, 23, 24). Mfundo yakuti ophunzira ena otchuka amatchulidwa ndi mayina pamene dzina la Yohane silinatchulidwe, ikuwoneka kuti ikusonyeza kuti iye ayenera kuti anali mlembi wauthenga wa bwinowo.

Malingana ndi Mzimu wa Wachinenero, mlembi wa Uthenga Wabwino wachinayi anali Yohane, “wophunzira amene Yesu anamkonda.” Iye anali mmodzi wa ophunzira atatu amene anaona ulemerero wa Kristu pa phiri la kusandulika ndi zowawa Zake m’munda atangotsala pang’ono kumangidwa. Moyo wake uli chitsanzo chapadera chosonyeza mmene mphamvu ya Mulungu ingasinthire kotheratu “mwana wa bingu” kukhala munthu wa chikondi ndi wozindikira mwakuya.

“Yohane anamamatira kwa Kristu monga mpesa umakangamirira kumzati wolemekezeka. Chifukwa cha Mbuye wake anapyola muzoopsa zabwalo la milandu ndi kukayandikira pa mtanda, ndipo pa uthenga wa kuti Khristu wauka, anathamangira kumanda, mu changu chake anapotsa ngakhale Petro wopupuluma.

“Chikondi chodalira ndi kudzipereka kopanda undekha zosonyezedwa m’moyo ndi mukhalidwe la Yohane zimapereka maphunziro amtengo wapatali kumpingo Wachikristu. Yohane mwachibadwa analibe kukongola kwakhalidwe kumene kunaonekera kudzera mu zimene zinamuchitikira pambuyo pake. Mwachibadwa anali ndi zilema zazikulu. Iye sanali kokha wonyada, wodzikuza, ndi wofuna ulemu, komanso anali wopupuluma, ndi waukali povulazidwa. Iye ndi mbale wake ankatchedwa ‘ana a bingu.’ Kupsa mtima koipa, khumbo la kubwezera, mzimu waoneneza, zonse zinali mwa wophunzira wokondedwayu. Koma pansi pa zonsezi Mphunzitsi waumulunguyo anazindikira mtima wachangu, wowona mtima, ndi wachikondi. Yesu anadzudzula kudzikonda kumeneku, kukhumudwitsa zokhumba zake, kuyesa chikhulupiriro chake. Koma Iye anamuululira chimene moyo wake unkalakalaka—kukongola kwa chiyero, mphamvu yosintha ya chikondi.”— The Acts of the Apostles, p. 539, 540.

Maulamuliro onse akale amanena kuti Uthenga Wabwino wa Yohane unalembedwa ku Efeso cha m’ma A.D. 90 kapena mbuyo mwake. Wophunzirayu anaikidwa m’mbiya yamafuta owira ndikupulumuka imfa m’njira yozizwitsa, ndipo pambuyo pake anakaikidwa kuchisumbu cha Patmo (Chivumbulutso 1:9). Pamenepo iye analemba Chivumbulutso. Kulowa kwa Nerva pampando wachifumu (AD 96) kunamupangitsa kuti abwerere ku Efeso, kumene chimakhulupiriridwa kuti anapitirizabe kukhala mpaka imfa yake mu ulamuliro wa Trajan (AD 98-117).

Mzimu wa Khristu utsogolere maphunziro athu a mukotala lino, ndi kukhudza mitima yathu poyankha ku chikondi chake!

A gawo la sabata skulu a ku General Conference

 <<    >>