Zopereka Za Sabata Loyamba
Dziko la Paraguay ndi dziko lopanda lozunguliriridwa ndi maiko osiyanasiyana ku South America, linacita malire ndi Argentina, Bolivia, ndi Brazil. Chiwerengero cha anthu ndi pafupifupi 6.1 miliyoni, 96.1% ndi omwe amati ndi Akhristu (88.3% Chikatolika ndi 7.8% zipembedzo zina za chikhristu); 2.6% amati ndi osapembeza, ndipo otsalawo ndi a zipembedzo zina kapena sanazitchule. Chuma cha dziko chimakhazikika pa ulimi makamaka wa soya—ndipo pazaka 50 zapitazi, Paraguay yakuzanso kwambiri makampani opanga magetsi ochokera kumadzi. Mamembala oyamba a SDA Reform Movement anafika kuno kuchokera ku Hungary m’ma 1940 ndipo ntchito inakula kwambiri m’ma 1950 kudzera m’mautumiki a ukopotala ndipo pambuyo pake m’ma 1970 kupyolera muzamishonale wanchito za machiritso. Panopa tili ndi gulu lodabwitsa la mamembala okhulupirika mu mizinda ikuluikulu. Kwa zaka zambiri tinali ndi chipatala chachilengedwe chomwe chinkagwira ntchito mumzinda waukulu wa Asunción, kutipangitsa ife kuthekera kwa kugawana uthenga wabwino ndi miyoyo yambiri ndi Kuphunzitsa moyo waanthu otsala a Mulungu. Ndi thandizo la Mulungu ndi gulu lathu la akatswiri lotcedwa inter disciplinary, tikuyembekeza kutsitsimutsa chipatalachi—koma tsopano kuti chigwire ntchito yofikira anthu mumzinda, ndi m’midzi kuti akwaniritse lamulo la umulungu lakuti: “‘Chokani mizinda. Khazikitsani zinyumba zanu, masukulu anu, ndi maofesi kutali kuchokera pakati pa anthu.’ ”—Selected Messages, bk. 2, p. 357.
Poganizira masomphenya amenewa, tinapeza malo kumudzi wina wokongola kwambiri m'dera la Paraguarí, pafupifupi 66 km. (41 miles) kuchokera kulikulu. Tili kale ndi malo opatulika ndi opembedza pa malowa, koma ichi ndi chiyambi chabe. Cholinga ndi kukhazikitsa malo ochitira zinthu zosiyanasiyana, malo okhala ndi zipatala zoyambira, sukulu ya tchalitchi, tchalitchi, ndi a malo opangira mabizinesi odzipezera okha chakudya chaumoyo.
Tikupempha abale athu padziko lonse kuti atithandize kukhala owolowa manja kuti tichikwaniritse cholinga ichi. Kugwirizana kwanu kudzapereka chilimbikitso chatsopano cha gawo lomaliza lofunika kumaliza ntchitoyi. Tikudalira mu mphamvu ndi chisomo chodabwitsa cha Mulungu ndipo tili otsimikiza kuti Yehova adzadalitsa kuyesetsa kwa anthu athu onse padziko lonse lapansi kulimbikitsa ndi kukulitsa kulalikira uthenga mu dera lino la munda wake wamphesa.
Abale ndi alongo anu ochokera ku filudi ya Paraguay