Back to top

Sabbath Bible Lessons

Maphunziro AmBaibulo Apa Sabata

 <<    >> 
PHUNZIRO 12 SABATA, MARICHI 22

ULAMULIRO WA MWANA WAMUNTHU

VESI LOLOWEZA: “Pakuti monga Atate ali ndi moyo mwa iye yekha, momwemonso anapatsa mwana kukhala ndi moyo mwa iye yekha; ndipo anampatsa iye mphanvu yakuchita mlandu pakuti ali mwana wa Munthu”(Yohane 5:26,27).

“Ulamuliro wanga, [Yesu] anati,wakuchitila ntchito imene inuyo mukundineneza Ine, ndiwoti Ine ndine mwana wa Mulungu, Mmodzi ndi Iye muchilengedwe, muchifuniro, ndi mucholinga. Muntchito zake zonse za chilengedwe ndi chisamaliriro, ndimagwirizana ndi Mulungu.” – The Desire of Ages,p. 208.

Zowelenga zoonjezera:   Thoughts from the Mount of the Blessing, pp. 123-129. 

Loyamba , Marichi 16

1. OFANANA NDI MULUNGU

a. Pambali pa kuchilitsa munthu wopuwala pa dzuwa lasabata, ndichifukwa china chitinso chimene Ayuda anadanira ndi Yesu? Yohane 5:17, 18.

“Yesu anazinena kukhala ndi ulamuliro wofanana ndi Mulungu…

“Mtundu wonse wa Ayuda umamuchula Mulungu kuti Atate wawo, chotelo iwowo sakanakwiyitsidwa kwambiri chotelo ngati Khristu akanazionetsera yekha kuti ali ndi chibale chofanana chotele ndi Mulungu. Koma iwo anamuimba mlandu wakuchita mwano, kuonetsera kuti iwo amumvetsetsa iye kuti akuzinena yekha mulingaliro lapamwamba.” – The Desire of Ages, pp. 207-208.

b. Kodi ndimotani mmene Khristu anasimikizira ulamuliro wa malamulo a Mulungu pamwamba pa miyambo ya anthu? Mateyu 15:1-9, 13.

“Adani awa akhristu analibe zotsutsa zina zilizonse zoti athe kukwanitsa kutsutsa choonadi chimene iye amachibweretsa mosindika kuchikumbumtima chawo. Iwo amangofotokoza chabe za miyambo ndi malamulo awo, ndipo zimenezi zimaoneka zofooka ndizopanda pake pamene zikufanizilidwa ndi mfundo zimene Yesu amazipeleka kuchokera mumalembo a Mulungu ndi muzochitikachitika zosalekeza za chilengedwe.” – Ibid., p. 208.


Lachiwiri , Marichi 17

2. UMODZI NDI ATATE

a. Kodi ndimotani mmene Yesu anafotokozera ubale wake ndi Atate? Yohane 5:19, 20.

b. Kodi ndiulamuliro ndi mphanvu zanji zochokera kwa Atate zimene Khristu analengeza kuti iyenso alinazo? Yohane 5:21-23.

“Ansembe ndi atsogoleri anaziika iwo okha monga oweludza oti azitsutsa ntchito za Khristu, koma iye anazilengezetsa yekha kukhala oweludza wawo, ndi oweludza wadziko lonse lapansi. Dziko lapansi linaperekeka kwa Khristu, ndipo kudzera mwa iye kwakhala kukubwela mdalitso winaulionse wochokela kwa Atate kupita kumtundu wakugwa wa Anthu. Iye anali mombolo mmbuyo monsemu monganso analiri atabwela ndi kukhala munthu. Pomwepo pomwe chimo linapezeka, Pomweponso panali mpulumutsi. Iye anapeleka kuunika ndi moyo kwaonse, ndipo molingana ndimuyeso wakuunika komwe kunapelekedwa, wina aliyense azaweluzidwa. Ndipo iye amene anapeleka kuunika, iye amene wakhala akuutsatila moyo ndi kuchonderera kwa chifundo, kufunafuna kuti aupindule iwo kuchokera kuuchimo kupita kuchiyelo, ndimmodzi yemweyo mkhala pakati ndi oweludza wake.” – The Desire of Ages,p. 210.

c. Fotokozani kusintha kwa khalidwe kumene kumachitika pamene ife tikuzindikira kuti khristu ndioweludza wathu. Aroma2:1-3; Mateyu 7:1.

“Iye amene akuzipereka kukhala ndi Mzimu wakuneneza ali ndi mlandu wachimo lalikulu kupotsera iye amene iye akumuneneza, popedza iye sakungochita chabe chimo lomwelo, koma akuphatikizira ku ilo chinyengo ndikutola zifukwa.

“Khristu ndi muyeso woona wokha wa khalidwe, ndipo iye amene amaziika yekha pamwamba monga muyeso wa ena akuziika yekha pamalo pa Khristu. Ndipo popedza Atate `anapereka kuweludza konse kwa mwana’ (Yohane 5:22), Iye amene amaziika yekha kuti aziweludza zolinga za ena kawilinso akuukila udindo wa mwana wa Mulungu. Ozinena kukhala oweludzawa ndi otsutsa ena akuziika okha kumbali yawokana Khristu, `amene atsutsana nazo nadzikuza pazonse zochedwa Mulungu, kapena zopembezeka; kotelo kuti iye wakhala pansi kukachitsi wa Mulungu, nazionetsera kuti ali Mulungu.’2Atesalonika 2:4.” – Thoughts from the Mount of Blessings, pp.125,126.

“Ife sitingathe kuwelenga mtima. Ife eni olakwa, sindife oyenela kukhala pansi ndi kumaweluza ena. Anthu amalire akhoza kuweludza zooneka zokha zakunja. Kwa iye yekha amene amaziwa zinsisi zimene zimatsogolera machitachita, amenenso amachita ndi anthu mwachifundo ndi mwachikondi,ndi amene anapatsidwa mphanvu yakuweludza moyo wina ulionse.” – Ibid., p. 124.


Lachitatu , Marichi 18

3. CHISIMIKIZO CHA MTENGO WAPATALI

a. Kodi ndi chisimikizo chanji chimene chapatsidwa kwa okhulupilira aliyense odzipereka kwa Khristu? Yohane 5:24.

“Mukulamula kulikonse ndimulonjezo lilonse la mmawu a Mulungu ndimphanvu, moyo weniweni wa Mulungu, pkumene kudzera mmenemo kulamulako kudzakwanilitsidwa ndi lonjezo kukwanilitsidwa. Iye amene mwachikhulupiliro akulandira mawu akulandira moyo weniweni ndi khalidwe la Mulungu.” – Christ`s Object Lessons, p. 38.

“Ntchito yayikulu imene anachitilidwa ochimwa amene wadetsedwa ndikukhala ndi chilema ndizoipa ndi ntchito yakulungamitsidwa. Kudzera mwa iye amene amalankhula choonadi iye amalengezetsedwa kuti ndiolungama. Ambuye amaika pa okhulupilira aliyense chilungamo cha Khristu ndikumulengeza iye kuti ndiolungama pamatso pa chilengedwe chonse. Iye amasamusira machimo ake kwa Khristu, amene ndimlowa mmalo, chikole, ndi dipo la ochimwa. PaKhristu iye amaika mphulupulu ya moyo wina ulionse umene wakhulupirira `ameneyo sanaziwa uchimo anamuyesera uchimo mmalo mwathu kuti ife tikhale chilungamo cha mulungu mwa iye.’(2 Akolinto 5:21)…

“Ngakhale monga ochimwa momwe tilili pansi pakutsutsidwa ndi lamulo, komabe Khristu kudzera mukunvera kwake kumene anakuonetsera ku Lamulo, iye amanenera ku moyo wolapa kuyenera kwa chilungamo cha iye mwini. Kuti tipedze chilungamo cha Khristu, ndichofunikira kwa ochimwa kuti aziwe tanthauzo la kulapa kumene kumabweretsa kusintha mmalingaliro, muuzimu ndi mmachitidwe. Ntchito yakusinthika ikuyenera kuyambira mumtima, ndikuonetsera mphanvu zake mugawo lililonse la munthu; koma munthu alibe kuthekera kwakuyambitsa kulapa kotere, Ndipo angakhale nako kudzera mwa Khristu yekha basi, amene ‘anakwera kumwamba, ndikukamanga amsinga, ndikukapatsa mphatso kwa anthu.’ ” – Selected Messages, bk. 1, pp. 392, 393.

b. Kodi ndimaudindo anji aumulungu amene Khristu anabvumbulutsa kuti alinawo? Yohane 5:25-29.

“Chifukwa choti iye analawa matsautso ndi mayetsero aanthu, ndipo amamvetsetsa kufooka ndi machimo anthu; Chifukwa choti mmalo mwathu iye analimbana ndikugonjetsa Satana, Ndipo azachita molungama ndi mwachifundo ndimoyo ulionse umene mwadzi wake wa iye yekha unakhesedwa kuti ukapulumutse-chifukwa cha ichi, mwana wa munthu anasankhidwa kuti akapeleke chiweludzo.” – The Desire of Ages, p. 210.

“Khristu ndiovekedwa ndi mphanvu zakupatsa moyo kuzolengedwa zonse.” – Selected Messages, bk. 1. p. 249.


Lachinayi , Marichi 19

4. YESU PHATA LENILENI LAMALEMBO

a. Kodi ndi motani mmene Khristu anafotokozera chifukwa cha kusakhulupirira kwa Ayuda? Yohane 5:37, 38.

“Mmalo mopepetsa chifukwa cha machitidwe amene iwo amadandaula, kapena kufotokoza cholinga chake mukuchita ichi,Yesu anatembenukira kwa atsogoleri, ndipo onenezedwa anakhala oneneza. Iye anawadzuzula iwo za kuuma kwa mitima yawo, ndikusazindikira kwawo kwa malemba. Iye anafotokoza kuti iwo akana malembo a Mulungu, monganso mmene iwo amukanira iye amene Mulungu anamutuma.” – The Desire of Ages, p. 211.

b. Kodi ndi chifukwa chiyani aYuda amalephera kuzindikira malembo? Yohane 5:39, 40.

“Musamba lililonse, kaya mbiri, kapena lamulo, kapena uneneri, malembo achipangano cha kale ndi owalitsidwa ndi ulemerero wa Mulungu. Monga mmene zinaliri malamulo khumi, dongosolo lonse la chiyuda unali uneneri odzadza wa uthenga wabwino. Kwa Khristu `aneneri onse amuchitira umboni.’ Machitidwe10:43. Kuyambira kulonjezo limene linapelekedwa kwa Adamu kufikira kupyola munthawi ya akuluakulu achikhulupiliro ndikwa oweludza, kuunika kwa ulemerero kwa kumwamba kunaonetsera poyela mapadzi ampulumutsi. Aneneri anaona nyenyezi yaku Beterehemu, Silo amene azabwere, pamene zinthu za msogolo zimadutsa pamaso pawo mundanda wodabwitsa wa chinsinsi. Munsembe iliyonse imfa ya Khristu imaonetsedwa. Mu mtambo ulionse wazofukitsa chilungamo chake chimakwela. Kudzera mulipenga lililonse lachikondwerero dzina lake limaveketsedwa. Muchophimba chodabwitsa cha chinsinsi chochititsa mantha chakumalo opatulikitsitsa ulemerero wake umakhalako.

“Ayuda anali anthu amene amasunga malembo, ndipo amalingalira kuti kudzera muchidziwitso chawo cha pamwamba chamalembo iwo alinawo moyo wosatha. Koma Yesu anati, ` Mulibe inu mawu ake akukhala mwa inu.’ Pokana Khristu mmawu ake, iwo anamukana iye pamaso. `simukudza kwa ine,’ iye anatelo, `Kuti mukhale nawo moyo.’

“Atsogoleri aYuda amawelenga ziphuzitso za aneneri zokhuzana ndi ufumu wa Mesiya; koma iwo amachita ichi, osati ndikhumbo loona lakuti adziwe choonadi, koma ndicholinga choti apedze maumboni olimbikitsira ziyembekedzo zawo za undekha. Pamene Khristu anabwera munjira yosiyana ndi mmene iwo amayembekezera, iwo sanathe kumulandira iye; ndipo ndi cholinga chozilungamitsa okha, iwo anayestetsa kuti aonetsere umboni kuti iye ndiwachinyengo. Pamene kamodzi iwo anaika mapadzi awo munjira imeneyi, zinali zophweka kuti Satana alimbikitse kutsutsa kwawo komutsutsa Khristu. Mawu omwewo amene amayenera kulandilidwa ngati umboni wa umulungu wake amatanthauziridwa momutsutsa iye. Chotelo iwo anatembenudza choonadi cha Mulungu kukhala bodza.” – Ibid.,pp. 210, 212.


Lachisanu , Malichi 20

5. ULEMELERO WA MULUNGU

a. Kodi ndi chiyani chimene chinasogolera Ayuda kuti akane Yesu ndikufuna aphuzitsi abodza? Yohane 5:41-44.

“Yesu anati, `Sindilandira ulemu kuchokera kwa anthu.’ Sichinali chikoka cha aSanihedrin, sichinali chibvomerezo chawo chimene iye amachifuna. Iye sakadatha kulandira ulemu kuchokera kukuyamikira kwawo. Iye anali ovekedwa ndi ulemu ndi ulamuliro wa kumwamba. Ngati iye akanakhala kuti amachifuna chimenechi, angelo akanatha kubwera ndikuzampatsa iye ulemu; kawirinso atate anachitira umboni za umulungu wake. Koma chifukwa cha kuubwino wawo, kuubwino wadziko limene iwowo anali atsogoleri ake, iye anafunitsitsa atsogoleri a Ayuda kuti adzindikire khalidwe lake, ndikulandira madalitso amene iye anabwera kudzawapatsa iwo.

“ `Ndaza ine mudzina la atate wanga, ndipo simundilandira ine; akadza wina mudzina lake la iye mwini koma iyeyo muzamulandira.’ Yesu anabwera kudzera muulamuliro wa Mulungu,anali ndi chithunzithunzi chake, anakwanilitsa mawu ake, ndikufunafuna ulemerero wake; komabe iye anali osalandilidwa ndi atsogoleri a Israeli; koma pamene ena adzabwere, omanamizira khalidwe la Khristu, koma omadzazidwa ndi chifuniro cha iwo eni ndikumafunafuna ulemerero wa iwo eno, iwo adzalandiridwa. Nanga chifukwa chiyani? Chifukwa iye amene amafunafuna ulemerero wa iye mwini amakopa khumbo lakufuna kudzikweza wekha mwa ena. Kukopa kotele Ayuda azakukondwerera, iwo azatha kulandira mphuzitsi wabodza chifukwa choti iye amayamikira mwabodza kunyada kwawo kudzera mukubvomeredza malingaliro awo okondedwa ndi miyambo yawo. Koma chiphuzitso cha Khristu sichimabvomelezana ndi mfundo zawo. Chinali cha uzimu, ndipo chimafuna kupereka nsembe undekha; chotelo iwo sanathe kuchilandira icho. Iwo sanali ozolowelana ndi Mulungu, ndipo kwa iwo mawu ake kudzera mwa Khristu anali mawu a Mlendo.

“Kodi chinthu chomwechi sichikubwelezedwa mmatsiku athu? Sipali ambiri, Ngakhale atsogoleri azipembedzo amene akuumitsa mitima yawo kulimbana ndi mzimu woyera, kuchipanga kukhala chosatheka kwa iwo kudzindikira mawu aMulungu? Kodi iwo sakukana mawu a Mulungu, kuti azitha kusunga myambo yawo?.” – The Desire of Ages, pp. 212, 213.


Lachisanu ndi chimodzi , Marichi 21

6. MAFUNSO OBWEREZA PAWEKHA

1. Kodi ndi ulamuliro ndi kuyenera kwanji kumene Khristu akunena kuti ali nawo?

2. Kodi ndi ubale wanji umene wakhala ulipo pakati pa Khristu ndi Atate?

3. Kodi ndi mphanvu zanji zopereka moyo zimene Khristu ali nazo?

4. Fotokozani Yohane 5:39.

5. Fotokozani zotsatira za mtundu wachiyuda kukana Khristu monga Mesiya.

 <<    >>