Loyamba
, Marichi 2
1. KUDZUTSA CHIDWI
a. Atatha kukhala masiku awiri ndi a Samaliya, kodi ndi kuti kumene Yesu anapita-nanga ndi ndani amene anakopeka ndi mbiri imeneyi? Yohane 4:43-46.
“Mbiri ya kubwereranso kwa Khristu ku Kana mwamsanga inafalikira mu Galireya monse ndipo inabweretsa chiyembekezo kwa odwala ndi osausika. Ku kapernamu mbiri imeneyi inakopa chidwi cha mkuru wa aYuda amene anali mdindo otumikira mfumu.” – The Desire of Ages, p. 196.
b. Kodi ndi chifukwa chiyani mdindo wa mkuruyi anapita kuti akakumane ndi Yesu? Yohane 4:47.
“Mwana wamwamuna wa mdindoyu amadwala nthenda yooneka yosachilitsika. Madotolo anamulephera ndi ndikumadikira basi kuti afe. Koma pamene bamboo ake anamva za Yesu, iye anatsimikizika zokapempha thanzizo kuchokera kwa iye.” – Ibid., p 197.
Lachiwiri
, Marichi 3
2. CHIDZINDIKIRO CHA KUKAYIKIRA
a. Fotokozani mmene Khristu anabvumbulutsira kusautsika kwa mkati mwa mtima wa mdindo wa mkulu amene anamupempha iye kuti amuchiritse mwana wake ku kaperenamu. Yohane 4:48.
“Mwanayo anali atadwalika zedi, ndipo panali mantha akulu, oti mwina sakhala moyo mpaka kufikira iye abwerenso, komabe mdindoyo anachimva kuti ndibwino akamufotokozere Khristu nkhaniyi maso ndi maso. Iye anayembekezera kuti mapemphero a tate akhoza kudzutsa chifundo cha Dokotala wamkulu.
“Atafika ku kana iye anapedza khamu lalikulu litamuzungulira Yesu. Ndi Mtima wankhawa iye anazipanikiza kufikira anafika pamaso pa mombolo. Chikhulupiriro chake chinazirara pamene iye anaona munthu chabe obvala zobvala za wamba wotuwa ndi wotopa ndi kuyendayenda. Iye anakaika ngati munthu ameneyu angathe kuchita chimene iye anabwera kudzamupempha iye; komabe iye anapedza mwayi woyankhulana ndi Yesu, namuuza iye chomwe anabwerera ndikumupempha mpulumutsi kuti atsagane naye kupita kunyumba kwake. komabe Yesu anaziwiratu nkhawa ya mdindoyu asananyamuke kunyumba kwake, Mombolo anaona kutsautsika kwake.
“Koma iye anadziwa kutinso tateyu, anali ndi zinthu zimene anazikhazikitsa mumtima mwake, zokhuzana ndi zoyenereza za kukhulupirira kwake mwa Yesu. Pokhapokha pempho lake ngati lingabvomerezedwe iye sangamulandire iye ngati Mesiya…
“Posatengela umboni wonse woti Yesu ndi khristu, wopemphathandizo anatsimikiza mtima kuti apange chikhulupiliro chake mwa khristu kukhala ndi choyenereza ngati iye angabvomeredwe pempho lake basi.” – The Desire of Ages, pp. 199-198.
b. Tikayesedwa kuti tifune zizindikiro, kodi ife tikuyenera kumakumbukira chiyani? Mateyu 12:38, 39.
“Khristu anapwetekedwa mumtima kuti anthu ake enieni, amene kwa iwo kunaperekedwa malembo opatulika, akulephera kumva mawu a Mulungu kuyankhulidwa kwa iwo mwa mwana wake.” – Ibid., p. 198.
“Anthu amafuna chizindikiro monganso mmasiku a Khristu. Koma Ambuye anawauza iwo kuti palibe chizindikiro chimene chikuyenera kuperekedwa kwa iwo. Chizindikiro chimene chikuyenera kuonekera tsopano komanso nthawi zonse ndiko kugwira ntchito kwa mzimu woyera mu mtima wa mphunzitsi kuti apange mawu kukhala okhuza monga momwe angathere. Mawu a Mulungu sinthano yokufa, youma koma mzimu ndi moyo. Satana sangakondenso chinthu china kwambiri kuposa kuchosa malingaliro aanthu kuchoka ku malembo kuti azifunafuna ndi kuyembekezera zinthu zina za kunja kwa Malemba kuti ziziwakomera iwo.” – Selected Messages, bk. 2, p. 95.
Lachitatu
, Marichi 4
3. MALINGALIRO OSIYANA
a. Fotokozani kusiyana pakati pa Ayuda ndi Asamaliya mokhuzana ndi chikhulupiliro chawo mwa Yesu. Marko6:2-6; Yohane 4:40-42.
“Kodi ndi mwakhama motani mmene Afalisi amafunitsitsa kuonetsa umboni moonekera woonetsa khristu kuti ndiwachinyengo! Ndi motani mmene amayang’anitsitsa liwu lake lililonse, kufunafuna kuti apotoze ndi kutanthauza molakwika zoyankhula zake zonse, kunyada ndi kuweruziratu ndi zikhumbitso zinatseka njira iliyonse ya moyo kuumboni wa mwana wa Mulungu. Pamene iye poyera anazuzula zochimwa zawo ndi kumafotokoza kuti ntchito zawo zimachitira umboni woonetsera iwo kuti ndi ana a Satana, iwo mokwiya anamubwezera kuneneza uku ponena kuti, “kodi sitinanene choona kuti inu ndi msamaliya, ndi kuti muli ndi chiwanda.” – Selected Messages, bk.1,p. 70.
“Mpulumutsi anasiyanitsa kusakhulupilira kwamafunso koteleku ndi chikhulupiliro chophweka cha a Samariya, amene samafunsa chozizwa ndi chizindikiro. Mawu ake, umboni wosasusika wanthawi zonse wa umulungu wake, anali ndi mphanvu zokhuza zimene zimakafikira mmitima yawo. “ – The Desire of Ages, p. 198.
“Ngakhale [Yesu] anali muyuda, iye amalumikizana momasuka ndi Asamaliya, osasamala konse miyambo yachifalisi ya Ayuda yokhuzana ndi anthu onyozeka amenewa. Iye amagona mu nyumba zawo, nadya pa magome awo, ndipo anaphunzitsa mu misewu yawo. – The Acts of the Apostles, p. 19.
b. Fotokozani zomwe amadusamo ambiri mwa anthu amene amalankhula choonadi chalero kwa anthu ozinena a Mulungu mu mibado yonse. Yeremiya 20:8-11.
“Milandu yonse yomwe amaimbidwa khristu inapangidwa kuchokera muchinyengo. Chimodzimodzinso mu mlandu wa Stefano, ndi wa Paulo. Koma kufotokoza kosadalilika konse kumene kumapangidwa ku mbali yolakwa kuli ndi chikoka chifukwa pali anthu ambiri amene mitima yawo ndi yosayeretsedwa, amene amafunitsitsa kuti mawu amenewo akhale oona, oterewa nthawi zonse amakhala ndi chidwi choti alimbikitse bodza, cholakwa ndi chophophonya cha iwo amene amayankhula kwa iwo choonadi chosakondedwa.
“Sizikuyenera kudabwitsika ife konse pamene malingaliro oipa alandilidwa mwachangu monga ngati choonadi chosakaikitsa ndi iwo amene ali ndi khumbo la bodza. Wosusa khristu kawiri ndi kawiri amasokonezedwa ndi kukhazikitsidwa chete kudzera mu mzeru za mawu ake; komabe iwo anali ofunitsitsa kumvetsera mpheketsera iliyonse, ndi kumapedza mawu ena kuti amukore iye kawiri ndi mafunso osusa.” – Selected Messages, bk. 1, pp. 70, 71.
Lachinayi
, Marichi 5
4. PEMPHO MODZICHEPETSA
a. Pamene chikhulupiriro cha mdindo wolemekezeka chinagwira zolimba pa Khristu kodi ndi motani mmene iye anabwerezera pempho lake? Yohane 4:49.
“Monga kuthwanima kwa kuwala, mawu a Mpulumutsi kwa mdindo olemekezeka anaika poyera za mumtima mwake. Iye anaona kuti zolinga zake mukufuna yesu zinali zaundekha. Chikhulupiliro chake choipa chinaonekera kwa iye mukhalidwe lake lenileni. Mwa nkhawa yaikulu iye anazindikira kuti kukaika kwake kukhoza kutaikisa moyo wa mwana wake. Iye anazindikira kuti anali pamaso pa yekhayo amene amatha kuwerenga malingaliro, kwa iye amene zinthu zonse ndi zotheka … Chikhulupiriro chake chinagwira zolimba pa Khristu monga anachitira Yakobo, pamene amalimbana ndi ngelo, iye analira, `Sindizakuleka iwe kuti umuke, ukapanda kundidalitsa ine.’ Geneses 32:26.” – The Desire of Ages, p. 198,
b. Kodi ife tikuyenera kuphunzira chiyani kuchokera ku zomwe Yesu anachita mmalo mopita kunyumba ya mdindo olemekezeka? Yohane 4:50.
“Yesu anali ndi mphatso yaikulu kuti aipereke. Iye amafuna, osati kungomuchilitsa mwanayo chabe koma kuti ampange mdindo ameneyu ndi apanyumba ake onse kukhala ogawana nawo madalitso a chipulumutso, ndi kuyatsa nyali mu kaperenamu, amene posachedwa akhale munda womwe iye azigwiramo ntchito zake. Koma mdindo wolemekezekayu akuyenera kuzindikira chosowa chake kaya iye asanayambe kufuna chisomo cha khristu. Mdindo ameneyu amaimirira anthu ambiri a mudziko lake. Iwo anali ndi chidwi mwa Yesu koma ndi zolinga za undekha. Iwo amayembekezera kulandira phindu lapadera kuchokera ku mphanvu zake, ndipo iwo anakhazikitsa chikhulipiliro chawo mu kupatsidwa kukondeledwa kumeneku kwa zinthu zakanthawi. Koma iwo samazindikira konse za nthenda yawo ya uzimu ndipo samaona konse chosowa chawo cha chisomo cha Umulungu…
“Mpulumutsi sangazichotse konse kuchoka kumoyo umene ukukangamira kwa iye, kuchonderera chosowa chake chachikulu. Mdindo wolemekezekayu anachoka pamaso pa mpulumutsi ndi mtendere ndi chimwemwe zimene iye sanayambe wakhala nazo mbuyo monsemu. Sanangokhulupilira kokha kuti mwana wake achilitsidwa, koma ndi chidaliro champhanvu iye anakhulupirira mwa khristu monga mombolo.” – Ibid.,pp. 198,199.
“Ife tonse timafunitsitsa mayankho achangu ndi achindunji amapemphero athu,ndipo timayesedwa kuti tigwetsedwe mphwayi pamene mayankho achedwa kapena abwera munjira imene sitimayiyembekeza. Koma Mulungu ndi wamzeru zonse ndi wabwino kwambiri kuti amayankha mapemphero athu nthawi zonse munthawi yomweyo ndi munjira yomweyo mmene tikufunira. Iye azachita zambiri ndi zabwino kwa ife kuposa kungokwaniritsa zofuna zathu zonse… Zochititika izi zimene zimayesa chikhulupiliro ndi zakuubwino wathu.” – The Ministry of Healing,pp. 230,231.
Lachisanu
, Marichi 6
5. MACHIRITSO NDI CHIPULUMUTSO
a. Kodi ndi munjira yanji mmene Yesu anachilitsira mwana wa mdindo wolemekezeka? Yohane4:51-53. Kodi choona ichi chikutikumbutsa ife chiyani? Aefeso3:20-21.
“Pa mphindi yomweyo imene chikhulupiliro cha Atate chinagwira chitsimikizo choti, mwana wako ali ndi moyo, chikondi cha Umulungu chinakhuza mwana amene amafayo.” – The Desire of Ages, p. 199.
“Pa Mphindi yomweyo anthu amene amayang’anira amene anali pa mbali pa mwana amene anali pafupi kufayu kunyumba ku kapenamu anaona kusintha kodabwitsa ndi kwachangu. Mthunzi wa imfa unachotsedwa kuchoka pankhope pa wodwalayo kuocha kwa thupi kunachoka ndipo mmalo mwake kubwereranso kwa nthanzi kwa pumphu. Maso ofooka anawalitsidwa ndi chiziwitso cha mzeru, ndipo mphanvu zinabwerera ku thupi lofooka ndi lodwalika. Palibe chizindikilo china chilichonse cha nthenda yake chomwe chinasalira pa mwanayu. Thupi lake lotentha linasandulika lofewa ndi lanthete, ndipo mwakachetechete anagona tulo labata. Nthenda inamuleka iye pakatikati pa usana. Banja lonse linadabwitsika, ndipo chimwemwe chawo chinali chachikulu.” – Ibid.
b. Kodi ndi motani mmene Yesu amayankhulira kwa aliyense amene akuchonderera thandizo? Mateyu11:28-30.
“Mpulumutsi sangachoke kuchoka kumoyo umene ukukangamira kwa iye kuchonderera chosowa chake chachikulu.” – Ibid., p. 198.
“Kodi inu mukuzinva mumtima kuti chifukwa choti ndi inu ochimwa simungayembekezere kulandira mdalitso kuchoka kwa Mulungu? Kumbukirani kuti Khristu anabwera kudziko lapansi kudzapulumutsa ochimwa. Tilibe kenakalikonse kotiyamikira ife kwa Mulungu; pempho limene ife tingathe kulipereka tsopano komanso nthawi zonse ndi khalidwe lathu losoweratu thandizo, limene likupangitsa mphanvu zake zoombola kukhala chosowa chachikulu. Posiya kuzidalira tokha konse, tikhoza kuyang’ana ku mtanda wa kavale ndi kunena kuti; “Mmanja mwanga mulibe chopereka chilichonse chimene ndikuchibweretsa ndikungokangamira ku mtanda wanu basi.” – The Ministry of Healing, p. 65.
Lachisanu ndi chimodzi
, Marichi 1
6. MAFUNSO OBWEREZA PAWEKHA
1. Kodi ndi chifukwa chiyani kawirikawiri aneneri salandiridwa bwino kwawo?
2. Kodi ndi mawu anji amdindo amene akuonetsera kusakhulupilira kwake?
3. Kodi ndi motani mmene Khristu anachitira ku kusakhulupilira kwa anthu?
4. Kodi ndi ndani amene anaonetsera chikhulupiliro chachikulu mwa Yesu- Ayuda kapena aMitundu?
5. Kodi Yesu akulonjeza chiyani kwa onse amene abvomereza kuitana kwake?