Back to top

Sabbath Bible Lessons

Maphunziro AmBaibulo Apa Sabata

 <<    >> 
PHUNZIRO 5 SABATA, JANUWALE 25, 2025

YESU NDI NIKODEMO

VESI LOLOWEZA: “Yesu anayankha nati kwa iye, Indetu, Indetu, ndinena ndi iwe, ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuona ufumu wa Mulungu” (Yohane3:3).

“Kasupe wa mtima ayenera kuyeretsedwa msinje usanakhale oyera. Iye amene akuyetsa kupita kumwamba posunga malamulo, akuyesa chosateka.” – The Desire of Ages, p. 172

Zowelenga zoonjezera:   Steps to Christ, pp. 67-75

Loyamba , Jan 26

1. MUNTHU WOTCHUKA AFUNAFUNA YESU

a. Kodi Nikodemu anali ndani, nanga ndi motani mmene amaoneledwa mmaso mwa anthu? Yohane 3:1, 10.

“Nikodemo anali ndi udindo waukulu wodalilika mufuko la chiyuda. Anali ndi maphunziro apamwamba, ndi matalenti akhalidwe lapamwamba osati lachisawawa, ndipo anali membala olemekezeka munkhosolo ya dziko…Ngakhale anali wachuma, ophunzira, ndi olemekezeka, iye anakhala okopeka mtima mwadzidzidzi ndi munthu wodzichepetsa waku Nazareti.” – The Desire of Ages, p. 167.

“Anali Mfalisi weniweni wodzitsata, ndi womazitamandira iye mwini pa ntchito zake zabwino. Ndipo iye amatamandidwa ponseponse pa ntchito zake zabwino ndi zachifundo zimene amathandizira nazo mautumiki akukachitsi, ndipo amadzimva kukhala opindula kukondela kwa Mulungu.” –Ibid., p. 171

b. Kodi ndi ola liti limene Nikodemo ananyamuka ndi kukakumana ndi Yesu? Yohane3:2 (mbali yoyamba).

“Pakhala ndi kudzindikira pa kafukufuku yemwe anafunsa zokhudzana ndi malo amene Mpulumutsi angakapumile muphiri la azitona, iye anadikilira mpakana mzinda utakhala bata, ndipo kenako anayamba kumutsaka iye.” – Ibid. p.168.


Lachiwiri , Jan 27

2. KUKAMBILANA KWA MSELI

a. Kodi ndi chani chimene chikuonetsa kumvetsetsa kwa chikondi kwa Khristu mukumulandira mlendo wake mu maola otaika kwambiri autsiku? Masalmo 31:20, 21.

“[Nikodemo] anafunitsitsa zedi kukambilana ndi Yesu, komano anazibitsa posamafuna iye moonekela.Zikanakhala zinthu zochotsa ulemu kwambiri kuti mtsogoleri wa chiyuda aziphatike yekha molumikizana ndi mphunzitsi wosachuka. Ndipo ulendo wake ukanakhala kuti unadziwika ndi gulu la chisanihedrini, zikanamuputira iye mavuto achitonzo ndi kutsalidwa. Iye analingalira kuti akumane naye mwa chinsinsi, anachita izi potengela kuti ngati angapiteko moonekela, anthu ena akhonza kutsatira chitsanzo chake.” – The Desire of Ages, p. 168.

b. Fotokozani mmene Nikodemo anayambila kukambilana kwake ndi Yesu? Yohane 3:2.

“Nikodemo anazimva kukhala ndi mantha achilendo, pamaso pa Khristu, ndipo anayesetsa kudzibitsa pansi pa kuzilimbitsa ndi ulemu. Iye anati, `Mphuzitsi,’ ‘ Ife timadziwa kuti inu ndi Mphuzitsi ochokela kwa Mulungu: popedza palibe munthu amene angachite zozizwa zotele zimene inu mukuchita, pokhapokha ngati Mulungu sali ndi iye.’ Kudzera mukulankhula za mphatso zotsowa za khristu monga Mphunzitsi, komanso ndi mphanvu zake zodabwitsa zochitila zozwizwa, iye amaona kuti akukonza njira yoti akhale ndi kulankhulana naye kwabwino. Mawu ake anakonzedwa kuti awonetse ndi kuitanitsa chidaliro; komano amaonetsa muzenizeni zake kusakhulupirira. Iye samamubvomereza Yesu kuti ndi Mesiya, amangoti ndi mphunzitsi chabe ochokela kwa Mulungu.” – Ibid.

c. Kodi ndi ganizo lanji limene Khristu mwadzidzidzi anadabwitsa nalo Nikodemo? Yohane 3:3.

“Mmalo molandira moni waulemu oteleyu, Yesu anaika maso ake pa iye wolankhulayo, monga ngati kuwelenga moyo wake wonse. Ndipo kudzera mu nzeru zake zopandamalire iye anaona munthu pamaso pake wofunafuna choonadi. Ndipo iye anadziwa cholinga chakuyendeledwa kotele, ndipo ndi khumbo lofuna kukudza kukhudzika kumene kunali pa malingaliro a iye amene amamunvetsera, Iye anangolankhula mwa chindunji, ndi kunena mwakachetechete, komano mwa chikondi, `Indetu, Indetu, ndinena ndi iwe, ngati munthu sabadwa mwa tsopano, sakhonza kuona ufumu wa Mulungu.’ Yohane 3:3.

“Nikodemu anabwera kwa Ambuye poganizira kuti alowe mukukambirana ndi iye, komano Yesu anaika poyera mfundo za madziko achoonadi.” – Ibid, pp. 168-171.


Lachitatu , Jan 28

3. KUBADWA MWATSOPANO

a. Kodi ndi motani mmene Nikodemo anayankhila ku zimene Khristu anamuuza kuti akusoweka- ndipo monga iye, kodi ndi chifukwa chani ife tonse tikusoweka chochitika chakubadwanso mwatsopano? Yohane3:4-8.

“Chitsanzo cha kubadwanso mwatsopano, chimene Yesu anachigwiritsa ntchito, sichinali chosaziwikiratu kwa Nikodemo. Anthu otembenuka ndi kupita kuchikhulupiriro cha a Israeli kawirikawiri amafanizidwa ndi ana oti angobadwa kumene. Chotelo iye samayenera kunva mawu a Khristu ndi kuwatenga ngati ndi ongosewela achibwana. Komano chifukwa cha chibadwidwe chake chabwino chokhala mu Israeli, Iye amadziona yekha kukhala ndi malo otsimikizika muufumu wa Mulungu. Iye amadzinva yekha kukhala otsasowa kusinthika, ndi chifukwa chake anali odabwa pa mawu a mpulumutsi. Iye anakhumudwa chifukwa choti mawu anali kufotokoza pafupifupi za iye. Kunyada kwa mfalitsi kunali kulimbana ndi khumbo loona la kufunafuna choonadi. Iye anadabwa kuti ndi chifukwa chani Khristu analankhula naye monga anachitilamu, posalabadira za udindo wake monga mtsogoleri mu Israeli.

“Podabwitsika ndi udindo umene anali nawo, iye anamuyankha Khristu mmawu ozadzidwa ndi kusiyana ndi zimene khristu amanena, nati`Kodi munthu, angabadwe bwanji iye atakula kale? Monga anthu ena onse ambiri pamene choonadi chodula moyo wakale chabweretsedwa kuchikumbumtima, iye amaonetsera chilungamo choti munthu wachibadwa samalandira konse zinthu za Mzimu wa Mulungu. Mumakhala mulibe mwaiye kanthu kalikonse kamene kamavomera ku zinthu za uzimu; popedza zinthu zauzimu zimazindikilika mwa uzimu.

“Komano Mpulumutsi samayankha ndi chitsutso kuchitsutso ayi. Iye anakwedza mkono wake mwapadera, ndi mwaulemu mwakachetechete, iye anatsindikidza choonadi mu mtima pamodzi ndi chitsimikizo chachikulu, `Indetu, Indetu, ndinena ndi iwe, ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi mwa Mzimu, sangakhoze konse kulowa muufumu wa Mulungu.” – The Desire of Ages, p 171.

b. Kodi ndi liti komanso ndi motani mmene munthu angabadwenso mwa tsopano? Yohane 1:12, 13.

“Mulungu anakondetsetsa dziko lapansi, chotelo kuti iye anapereka mwana wake obadwa yekha, ndi kuti munthu akathe kulumikizana ndi Mulungu. Kudzera mukuyenera kwa Khristu iye akhoza kubwezeletsedwanso kwa Mlengi wake. Mtima wake ukuyenera kukonzedwanso ndi chisomo cha umulungu; iye akuyenera kukhala ndi moyo watsopano ochokera kumwamba. Kusintha uku ndiko kubadwa mwa tsopano, kumene ngati sikuchitika, Yesu anati, `munthu sadzakhonza kuona ufumu wa Mulungu.” –The Great Controversy, p. 467.

“Kudzera muchochitika chophweka cha kukhulupilira Mulungu, Mzimu Woyera umatenga malo amoyo watsopano mmoyo mwanu. Mumakhala monga ngati mwana wobadwa mubanja la Mulungu, ndipo iye amakukondani inu monga amamukondera mwana wake.”-Steps to Christ, p 52


Lachinayi , Jan 29

4. KUYERETSEDAWA NDI KUBADWANSO

a. Kodi ndi chiyani chimene chimaonetsera kuyeretsa ndi kukonzanso kumene kumadza ndi kubadwanso mwatsopano? Mariko16:16 (mbali yoyamba).

“Mphanvu yotsintha ya Mulungu imatha kusintha zidzolowezi zobadwa nazo ndi zotengela kwa ena; popedza chipembedzo cha Yesu ndi chokwedza. `kubadwanso’ kumatanthauza kusinthika, kubadwa mwatsopano mwa Khristu Yesu.” – The Adventist Home, p. 206.

“Khristu anapanga ubatizo kukhala chidzindikilo cholowela muufumu wake wa uzimu. Iye anapanga ichi kukhala chinthu chofunikira chimene anthu onse akuyenela kuchivomeleza ngati amakhumba kuti adzizdzindikilidwa monga okhala pansi pa ulamuliro wa Atate, Mwana, ndi Mzimu woyera. Munthu asanayambekupedza malo okhala mu mpingo, asanathe kudutsa pakhomo polowera pa ufumu wa uzimu wa Mulungu, iye akuyenela kaye kuti alandile kutsindika kwa dzina la umulungu loti, `Ambuye ndiye chilungamo chathu.’ Yeremiya 23:6.

“Ubatizo ndi kukana kopatulika kolikana dziko lapansi. Iwo amene anabatizidwa mu maina atatau a Atate, Mwana ndi Mzimu Woyera, pakulowa kwawo moyo wachikhristu amalalikira poyera kuti iwo atsiya kutumikila Satana ndipo akhalano ziwalo za ufumu wopatulika wolemekedzeka, ana a Mfumu ya kumwamba. Iwo amakhala amvera kulamula koti; `Tulukani ndi kupatuka pakati pawo ndi kukhala apadera… ndi kutsakhudza konse kanthu kosakonzeka.’ Ndipo kwaiwo kumakwanilitsidwa lonjedzo loti; `Ndipo ine ndizakulandilani inu, ndipo ndizakhala Atate kwa inu, ndipo inu mudzakhala ana anga aamuna ndi akazi, atelo Ambuye wa mphanvu zonse.’ 2 Akolinto 6:17, 18.” – Testimonies for the Church, Vol. 6,p. 91.

b. Kodi ndi chiyani chimene chinanenedwa zokhuzana ndi kuipa kwa khalidwe lathu lachibadwa ndi dongotsolo la Mulungu lotisintha ife? Yohane 3:6; Yeremiya 17:9, Aefeso 5:26, 27.

“Ndizosatheka kwa ife, ndi mwaife tokha, kuti tikathawe mu zenje la uchimo mmene ife tinamilamo. Mitima yathu ndi yoipa, ndipo sitingaisinthe tokha… maphunziro, chikhalidwe, kuchita kwa chifuniro, kuyesetsa kwa munthu, zonsezi zili ndi malo ake othekela, komano apa pokha ndi zopanda mphanvu konse. Zikhonza kutulutsa khalidwe looneka lolondola kunjaku, komano sizingasinthe mtima; sizingakhonze kuyeletsa akasupe amoyo. Pakuyenera kukhala mphanvu yomagwira ntchito kuyambira mkati, moyo watsopano ochokela kumwamba, anthu asanatembenuke kuchoka kuuchimo ndi kupita ku chiyero. Mphanvu zimenezo ndi Khristu. Chisomo chake chokha ndi chimene chingafulumizitse zochitika zopanda moyo za moyo,ndi kuzibweretsa kwa Mulungu, ku chiyero.” – Steps to Christ, p. 18.


Lachisanu , Jan 30

5. MOYO WATSOPANO NDI MACHITACHITA ATSOPANO

a. Kodi ndi uthenga wanji pambuyo pake atumwi amayenela kuulemba okhuzana ndi kusintha kumene kumadza molingana ndi kubadwanso mwatsopano? Agalatiya 2:20; 1 Yohane 2:15-17.

“Mphanvu zotsintha za Mulungu zimasintha zizolowezi zachibadwa ndi zotengela; popedza chipembezo cha Yesu ndi chokwedza. `Kubadwanso’ kumatanthauza kubadwanso mwatsopano mwa khristu Yesu.” – The Adventist Home, p. 206.

“[Paulo] anasimikiza mu mtima kuti ngati malingaliro aanthu akanabweretsedwa kukudzindikila nsembe yodabwitsa imene inapangidwa ndi wolemekezeka wa kumwamba, kuzikonda ndi undekha wonse zikanathamangitsidwa kuchoka mumitima yawo. Iye akulondolera malingaliro koyambilira kuudindo umene Khristu anali nawo kumwamba, mu nyumba ya Atate wake; Ndipo mtumwi akumuonetsera iye pamwamba, mu nyumba ya Atate wake; ndipo mtumwi akumuonetsera iye pambuyo pake kuti anatula pansi ulemelero wake, ndi kuzipereka Yekha mwachifuniro kumakhalidwe onse azochitika zozichepetsa amakhalidwe aumunthu, ndi kutenga maonekedwe akapolo, ndi kukhala onvera kufikila imfa, ndipo imfa yake yochititsa manyazi ndi yachitonzo, yonvetsa chisoni zedi, ndi yowawa zedi-imfa yapamtanda. Kodi akhristu angathe kulingalira za chionetsero chodabwitsachi cha chikondi cha Mulungu kwa munthu popanda kukhala ndi nthumadzi ya chikondi ndi kukhala ndi lingaliro loganiza za choona choti ife sindife ayife tokha? Mbuye wotele sakuyenela kutumikilidwa kudzela mukukakamizidwa, muchitsiliro, ndi muzolinga a undekha.” – Testimonies for the Church, Vol. 4, p. 458.

“Ndikulankhulani monga Khristu analankhulira kwa Nikodemo; `Ukuyenera kubadwanso mwatsopano.’ Iwo amene amalamulilidwa ndi Khristu mkati mwa mtima mwawo amanva kusakhala ndi khumbo lotsatira zochitika zozionetsera za dziko lapansi. Ndipo iwo amatengera kulikonse muyeso wa mtanda, ndi kumachitila umboni nthawi zonse za mfundo za pamwamba ndi zabwino kupotsera iwo amene zochitika za dziko zawadya moyo. Mavalidwe athu, pokhala pathu, machezedwe athu, zonsenzi zikuyenera kuchitila umboni za kuzipereka kwathu kwa Mulungu. Kodi ndi mphanvu zotani zimene zikanawatsata iwo amene akamazinva kuti analeka zonse chifukwa cha Khristu.” – Ibid, Vol. 5, p. 189.


Lachisanu ndi chimodzi , Jan 31

6. MAFUNSO OBWEREZA PAWEKHA

1. Chifukwa cha ntchito zake zabwino kodi ndi motani mmene Nikodemo amazionera yekha?

2. Kodi ndi motani mmene Nikodemo anachitila pamaso pa Khristu?

3. Kodi zimatanthauza chiyani kukhala “Obadwanso”?

4. Kodi ndi motani mmene kubadwanso mwatsopano kumachitikira?

5. Kodi ndi kusintha kotani kwa khalidwe kumene kumadza chifukwa cha kubadwanso mwatsopano, ndipo chifukwa chiyani?

 <<    >>