Back to top

Sabbath Bible Lessons

Maphunziro AmBaibulo Apa Sabata

 <<    >> 
PHUNZIRO 2 SABATA, JANUWALE 11, 2025

MWANAWANKHOSA WA MULUNGU

VESI LOLOWEZA: “Iye anatsenderezedwa, koma anazichepetsa yekha osasegula pakamwa pace; ngati nkhosa yosogoleredwa kukaphedwa, nndi ngati mwana wa nhosa amene ali du pamaso pa omsenga, motero sanatsegula pakamwa pace” (Yesaya 53:7).

“Lolani wochimwa wolapayo akhazikitse maso ake pa ‘Mwanawankhosa wa Mulungu, amene achotsa chimo lace la dziko lapansi.”— The Faith I Live By, p. 107.

Zowelenga Zoonjezera:   The Desire of Ages, pp. 132-143

Loyamba , Jan 5

1. UMBONI WA YOHANE MBATIZI

a. Kodi Yohane M’batizi analengeza chiyani zokhudza Yesu? Yohane 1:15-18.

b. Kodi Yohane anadzizindikiritsa yekha bwanji kwa atsogoleri achipembedzo? Yohane 1:19-23. Kodi ndi ulosiwotani umene iye anakwaniritsa—ndipo tikulimikizana nawo bwanji ulosiwu? Yesaya 40:3-5.

“M’gawo lililonse la mbiri ya dziko lapansi Mulungu wakhala ali ndi mabungwe akekuti apititse patsogolo ntchito Yake, imene iyenera kuchitidwa m’njira Yake yoikika. Yohane M’batizi anali ndi ntchito yapadera, imene iye anabadwira ndi imene anaikidwirako—ntchito yokonza khwalala la Ambuye....

“[Utumiki wake wa m’chipululu] unali kukwaniritsidwa mosazembaitsakwa ulosi kochititsa chidwi koposa.”— The Southern Watchman, March 21, 1905.

“Ambuye anapatsa [Yohane M’batizi] uthenga wake. Kodi anapita kwa ansembe ndi olamulira ndi kuwafunsa chilolezo kuti akalengeze uthenga umenewu?— Ayi, Mulungu anamuchotsa kwa iwo kuti asatengeke ndi mzimu ndi chiphunzitso chawo. Iye anali liwu la wofuula m’chipululu [Yesaya 40:3–5]. Uwu ndiwo uthenga womwe uyenera kuperekedwa kwa anthu athu; tiri pafupi ndi kumapeto kwa nthawi, ndipo uthenga ndi wakuti, Konzani khwalala la Mfumu; sonkhanitsani miyala; kwezani muyezo kwa anthuwo. Anthu ayenera kudzutsidwa. Ino si nthawi yofuula mtendere ndi chitetezo.”—Selected Messages, bk. 1, p. 410.


Lachiwiri , Jan 6

2. UTUMIKI WODZIPEREKA NSEMBE

a. Pamene Yesu anadza kwa Yohane kudzabatizidwa, kodi Yohane anaonetsera Iye motani ndi kuchitira umboniza ntchito yake kwa anthu? Yohane 1:29, 34. Kodi ndi ulosi wanji umene unakwaniritsidwa? Yesaya 53:4-7.

“Khristu anali Mumbolo wa munthu pa chiyambi cha dziko monga alili lero. Asanaveke umulungu wake ndi umunthu ndi kubwera ku dziko lathu lapansi, uthenga wabwino unaperekedwa ndi Adamu, Seti, Enoke, Metusela, ndi Nowa. Abrahamu m’Kanani ndi Loti ku Sodomu analengeza uthengawo, ndipo kuchokera ku mibadwo kufikira mibadwo ina amithenga okhulupirika analengeza Wakudzayo. Miyambo ya chuma cha Ayuda idakhazikitsidwa ndi Khristu Mwiniwake. Iye anali maziko a dongosolo lawo la nsembe zoperekedwa, choimira chachikulu cha utumiki wawo wonse wachipembedzo. Mwazi okhetsedwa monga nsembe imapelekedwa kuimira nsembe ya Mwanawankhosa wa Mulungu. Zopereka zonse zomwe zinali mthuzi zinakwaniritsidwa mwa Iye” — Christ’s Object Lessons, p. 126.

b. Kodi Yohane anamufotokoza motani Yesu kwa ophunzira ake? Yohane 1:35, 36. Kodi mawu ake anawakhudzabwanji, nanga n'chiyani chinachitika patsogolo pake mmoyo wake? Yohane 1:37.

“Tsiku lotsatira lake [patsogolo pa ubatizo wa Khristu], pamene ophunzira awiri anaimirira pafupi naye, Yohane anamuonanso Yesu ali pakati pa anthu. Kachiwirinso nkhope ya mneneriyo inawalitsidwa ndi ulemerero wochokera kwa Osaonekayo, pamene anafuula, ‘Taonani Mwanawankhosa wa Mulungu!’ Mawuwa anasangalatsa kwambiri ophunzirawo. Sanawamvetse bwino lomwe. Kodi dzina limene Yohane anamupatsa—‘Mwanawankhosa wa Mulungu’ linkatanthauza chiyani? Yohane mwiniyo anali asanafotokoze. Atamusiya Yohane, iwo anapita kukafunafuna Yesu.”— The Desire ofAges, p. 138.

“Yohane anauza ophunzira ake kuti Yesu ndiye Mesiya wolonjezedwayo, Mpulumutsi wa dziko lapansi. Pamene ntchito yake inali kutha, anaphunzitsa ophunzira ake kuyang’ana kwa Yesu, ndi kum’tsatira monga Mphunzitsi Wamkulu. Moyo wa Yohane unali wachisoni komanso wodzikana. Iye analengeza za kudza koyamba kwa Khristu, koma sanaloledwe kuchitira umboni zozizwitsa Zake, ndi kusangalala ndi mphamvu yosonyezedwa ndi Iye. Pamene Yesu anayenera kudzikhazikitsa monga mphunzitsi, Yohane anadziwa kuti iye mwini ayenera kufa. Liwu lake silinkamveka kawirikawiri, kupatula m’chipululu. Moyo wake unali wosungulumwa. Sanamamatire ku banja la atate wake, kuti asangalale ndi chiyanjano chawo, koma anawasiya kuti akwaniritse ntchito yake.”— Early Writings, p. 154.


Lachitatu , Jan 7

3. OPHUNZIRA OYAMBIRIRA A YESU

a. Kodi ena mwa ophunzira oyambirira a Yesu anali ndani? Mateyu 4:18, 21. Kodi anasonyeza chidwi chotani mwa Khristundipo kusonkhana kwawo koyamba ndi Iye kunali kwakutali motani? Yohane 1:38, 39.

“M’modzi wa awiriwo [amene anatsatira Yesu] anali Andreya, mbale wake wa Simoni; winayo anali Yohane mlaliki. Amenewa anali ophunzira oyambirira a Khristu. Mosonkhezeredwa ndi chisonkhezero chosaletseka, iwo anatsatira Yesu—ofunitsitsa kulankhula naye, komabe anachita mantha ndi kukhala chete, otayika mu lingaliro lofunikira kwambiri lakuti, ‘Kodi ameneyu ndi Mesiya?”

“Yesu anadziwa kuti ophunzirawa anali kumutsatira. Iwo anali zipatso zoyamba za utumiki Wake, ndipo munali chisangalalo mu mtima wa Mphunzitsi waumulungu pamene miyoyo imeneyi inalabadira chisomo Chake. Koma popotoloka adafunsa yekha, Mufuna chiyani? Iye Ankawasiya ndi ufulu obwerera m’mbuyo kapena kulankhula za chikhumbo chawo.

“Pa cholinga chimodzi chokha anali kuzindikira. Kukhalapo kumodzi kunadzaza malingaliro awo. Iwo anafuula kuti, ‘Rabi,... kodi mumakhala kuti?’ Mu kuyankhulana kwachidule panjira iwo sanathe kulandira zomwe iwo amazilakalaka. Iwo anafuna kukhala okha ndi Yesu, kukhala pa mapazi ake, ndi kumva mawu ake....

“Ngati Yohane ndi Andireya anakakhala ndi mzimu wosakhulupirira wa ansembe ndi olamulira, iwo sakadapezeka monga ophunzira pa mapazi a Yesu. Iwo akadabwera kwa Iye monga otsutsa, kudzaweruza mawu Ake. Motero ambiri amatseka chitseko cha mwayiwamtengo wapatali kwambiri. Koma sizinali choncho ndi ophunzira oyambirirawa. Iw anavomera ku kuitana kwa Mzimu Woyera mu ulaliki wa Yohane M’batizi. Tsopano anazindikira mawu a Mphunzitsi wakumwamba. Kwa iwo mawu a Yesu anali odzaza ndi kutsitsimutsa ndi choonadi ndi kukongola. Kuunikira kwaumulungu kunatsanuliridwa pa chiphunzitso cha Malemba Achipangano Chakale. Mitu yambiri ya choonadi inaonekera m’kuunika kwatsopano.”— The Desire of Ages, pp. 138, 139.

b. Kodi ophunzira oyambirira anachita chiyani atangokumana ndi Yesu? Yohane 1:41, 42.

“Andireya ankafuna kugawa chimwemwe chimene chinadzaza mtima wake. Popita kukafunafuna mbale wake Simoni, anafuula kuti, ‘Tamupeza Mesiya’. Simon sanadikirire kuti amuitanireso kachiwiri. Iye anamvanso kulalikira kwa Yohane Mbatizi, ndipo anafulumira kupita kwa Mpulumutsi.”—Ibid., p. 139.


Lachinayi , Jan 8

4. KUTHETSA KUWERUZIRATU

a. Fotokozani zimene zinachitika pamene Yesu anaitana wophunzira wotsatira kuti amutsatire Iye. Yohane 1:43-45.

“Filipo anamvera lamulolo, ndipo pomwepo anakhalanso wantchito wa Khristu. Filipo anamuitana Natanayeli.”— The Desire of Ages, p. 139.

b. Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Khristu anachita pogonjetsa kukaikira kwa Natanayeli? Yohane 1:46-49.

“Pamene Natanayeli anayang’ana Yesu, iye anakhumudwa. Kodi munthu ameneyu, amene anali ndi zizindikiro za kuvutika ndi kusauka, angakhale Mesiya? Komabe Natanayeli sakanatha kusankha kumkana Yesu, chifukwa uthenga wa Yohane unamuthandiza kukhudzika mtima.

“Panthawi imene Filipo anamuitana iye, Natanayeli anali atachoka n’kupita kutchireko kuti akasinkhesinkhe zimene Yohane analengeza komanso za maulosi onena za Mesiya. Iye anapemphera kuti ngati amene analengezedwa ndi Yohane anali mpulumutsi, ichi chidziwike kwa iye, ndipo Mzimu Woyera unakhala pa iye ndi chitsimikiziro chakuti Mulungu anayendera anthu Ake ndi kuwadzutsira iwo nyanga ya chipulumutso....

“'Yesu anayankha nati kwa iye, Filipo asanakuitane iwe, pokhala iwe pansi pa mkuyu, ndinakuona iwe.'

“Zinali zokwanira. Mzimu wa Mulungu umeneunachitira umboni Natanayeli m’pemphero lake lapayekha pansi pa mkuyu tsopano unalankhula naye m’mawu a Yesu.Ngakhale anali kukaikira, ndi kugonjera ku tsankho, Natanayeli anadza kwa Khristu ndi chikhumbo chowona chofuna choonadi, ndipo tsopano chikhumbo chake chinakwaniritsidwa. Chikhulupiriro chake chinaposa cha iye amene anamubweretsa kwa Yesu. Iye anayankha nati, ‘Rabi, Inu ndinu Mwana waMulungu; Inu ndinu Mfumu ya Isiraeli.’

“Natanayeli akanadalira arabi kuti amutsogolere, sakadamupeza Yesu. Ndikudzera mu kuzionera yekha ndi kuweluza yekha kumene kunampanga Iye kukhala wophunzira. Chotero kwa ambiri lerolino amene tsankho limawalepheretsa kuchita zabwino. Zotsatira zikanakhala zosiyana motani nanga ngati ‘anakadza ndi kudzawona’!

“Pamene iwu akudalira chitsogozo cha olamulira a anthu, palibe amene adzafike ku chidziwitso chopulumutsa cha choonadi. Mofanana ndi Natanayeli, tiyenera kuphunzira mawu a Mulungu patokha, ndi kupemphera kuti mzimu woyera utiunikire. Iye amene anaona Natanayeli pansi pa mtengo wa mkuyu adzationa ife m’malo obisika a pemphero. Angelo ochokera ku dziko la kuunika ali pafupi ndi awo amene modzichepetsa amafunafuna chitsogozo chaumulungu.”—Ibid., pp. 139–141.


Lachisanu , Jan 9

5. KUMWAMBA KOTSEGUKA

a. Kodi Khristu anamulonjeza chiyani Natanayeli—ndipo nchifukwa chiyani? Yohane 1:50, 51.

“[Potengera Yohane 1:50, 51.] Apa Khristu moonekeratu akunena kuti, M’mphepete mwa Yordano miyamba inatseguka, ndipo Mzimu anatsikira pa Ine monga nkhunda. Chochitika chimene chija chinali chizindikiro chabe kuti ndine Mwana wa Mulungu. Ngati mukhulupirira mwa Ine chomwecho, chikhulupiriro chanu chidzafulumizitsidwa. Mudzaona kuti kumwamba kwatseguka, ndipo sikudzatsekedwa konse. Ndatsegulira inu. Angelo a Mulungu akukwera, akusenza mapemphero a osowa ndi opsinjika mtima mkupititsa kwa Atate wakumwamba, ndi kutsika, kubweretsa madalitso ndi chiyembekezo, kulimba mtima, chithandizo, ndi moyo kwa ana a anthu.”— The Desire of Ages. pp. 142, 143.

b. Kodi chimachitika ndi chiyani pamene tamulandira Khristu? Yohane 4:14; Chivumbulutso 22:17.

“Pamene wina walandira chowonadi m’chikondi cha choonadichi, adzasonyeza ichi mwa kukopa kwa kachitidwe kake ndi kamvekedwe ka mawu ake. Iye amadziwikitsa zimene iye mwini anazimva, kuziona, ndi kuzigwira za mawu a moyo, kuti ena akhale ndi chiyanjano ndi iye mwa chidziwitso cha Khristu. Umboni wake, wochokera ku milomo yokhudzidwa ndi khala lamoto la pa guwa la nsembe, uli choonadi ku mtima womvera, ndipo umagwira ntchito ya chiyeretso pa khalidwe....

“Mulungu akanatha kufikira cholinga chake populumutsa ochimwa popanda thandizo lathu; koma kuti ife tikhale ndi makhalidwe ngati a Khristu, tiyenera kutenga nawo gawo mu ntchito yake. Kuti tilowe mu chisangalalo Chake—chisangalalo cha kuona miyoyo yawomboledwa ndi nsembe Yake—tiyenera kutenga nawo mbali mu ntchito Zake za chiombolo chawo.”—Ibid., p. 142.


Lachisanu ndi chimodzi , Jan 10

6. MAFUNSO OBWEREZA PAWEKHA

1. N’cifukwa ciani Yohane M’batizi anaitanidwa kukakhala ku chipululu?

2. Kodi tingatsatire bwanji moyo wa Yohane Mbatizi pa moyo wathu?

3. Kodi tingaphunzire chiyani kuchokera kwa Yohane ndi Andireya atakumana ndi Yesu?

4. Kodi chilengezo choyambirira cha Natanayeli chingatilimbikitse motani?

5. Kodi chimasonyeza m’chiyani ngati chikhulupiriro changa mwa Khristu ndi chenicheni kapena ayi?

 <<    >>