Back to top

Sabbath Bible Lessons

Maphunziro AmBaibulo Apa Sabata

 <<    >> 
PHUNZIRO 9 SABATA, MARICHI 1, 2025

KUBADWA KWA MTUMIKI

VESI LOLOWEZA: “Kodi simunena inu, kuti yatsala miyezi inai, ndipo kudza kumweta? Onani ndinena kwa inu,kwezani maso anu, nimuyang’ane m’minda, kuti mwayera kale kufikira kumweta” (Yohane 4:35).

“Yesu anayamba kugumula khoma lolekanitsa pakati pa ayuda ndi Amitundu, ndikulalikira chipulumutso kudziko lapansi. Ngakhale anali muyuda, Iye amasakanikirana mwaufulu ndia Samaliya, kuthetsa myambo ya chifarisi ya mtundu wake.” – The Desire of Ages, p. 193.

Zowelenga zoonjezera:   Testimonies for the Church, Vol. 5, pp. 182-187 

Loyamba , Feb 23

1. MOYO WATSOPANO, ZOKHUMBA ZATSOPANO

a. Atamuzindikira Yesu ngati Mesiya, kodi mzimayi waku samariya anachita chiyani mwachangu? Yohane 4:28, 29.

“Mzimayi anazazidwa ndi chimwemwe pamene iye amanvetsera ku mawu a khristu. Bvumbulutso lodabwitsa linali pafupifupi likulamulira. Posiya msuko wake wamadzi, iye anabwerera ku mzinda, kupitisa uthenga kwa ena. Yesu anadziwa chifukwa chomwe iye anapitira. Kusiya msuko wake wamadzi kunayankhula mosalakwitsa monga kuchotsatira cha mawu ake, linali khumbo losasewera la moyo wake kutenga madzi amoyo; ndipo anaiwala chiwiya chake kumadzi, iye anaiwala ludzu lampulumutsi, lomwe iye amafunika kulisamalira. Ndipo mtima wosefukira ndi chimwemwe, iye anafulumizitsidwa pa njira yake, kukapereka kwa ena kuunika kwamtengo wapatali komwe iye anakulandila.” – The Desire of Ages, p. 191.

b. Kodi ndichiyani chomwe anthu okhala mu Sukali anachita pamene iwo anamva umboni wa mzika mzawo? Yohane 4:30.

“Mawu amzimayi anakhuza mitima yao. Panali mafotokozedwe atsopano pa nkhope pake, kusinthika mmaonekedwe ake onse. Iwo anali ofunitsisa kukaona Yesu.” – Ibid.


Lachiwiri , Feb 24

2. ZOKOLOLA NDI OMWETA

a. Pamene Yesu anaona anthu okhala ku Sukali akubwera, kodi iye analankhula chiyani kwa ophunzira ake? Yohane 4:37-38.

“‘Iye wakumweta alandira kulipira,’ Iye anatero, ‘ndipo asonkhanitsira zobala ku moyo wosatha; kuti wofesayo akakondwere pamodzi ndi womwetayo pakuti momwemo chonenacho chiri choona, wofesa ndi wina, womweta ndi winanso.’ Apa khristu anatchula utumiki wopatulika operekedwa ndi Mulungu kwa onse omwe alandira uthenga wabwino. Iwo akuyenera kukhala amithenga ake amoyo. Iye akufuna utumiki wawo wapayekhapayekha. Ndipo kaya tadzala kapena tamweta, tikugwirira ntchito Mulungu. Wina afesa mbewu; wina asonkhanitsa zokolola; ndipo onse ofesa ndi omweta alandira kulipira. Onse akondwera pamodzi muchobwezera cha ntchito yawo.” – The Desire of Ages, pp. 141, 192

b. Kodi chotsatira cha umboni wa mzimayi wokhuza Khristu chinali chiyani- ndipo tingaphunzirepo chiyani kuchokera ku zotsatira zamphanvu zomwe unali nawo? Yohane 4:39.

“Pamene talumikizidwa kwa Khristu, timakhala ndi malingaliro a khristu. Chiyero ndi chikondi chimawalira mu khalidwe, chifatsondi choonadi zimalamulira moyo. Zofotokoza zonse za maonekedwe a nkhope zimasintha. Khristu kukhazikika mmoyo amaikamo mphanvu zosinthira, ndipo machitidwe akunja amachitira umboni ku mtendere ndi chimwemwe zomwe zikulamulira mkati. Timamwa muchikondi cha Khristu, monga nthambi zimatenga zakudya ku mpesa. Ngati talumikizidwa mwa Khristu, ngati nyewa ndi mnyewa talumikizana ndi mpesa wamoyo, tidzapereka umboni wa chenicheni pobereka zolemera zofanana za chipatso cha moyo. Ngati talumikizana ndi kuunika, tidzakhala njira za kuunika, ndipo mmau ndi ntchito zathu tidzaonetsera kuunika kudziko lapansi….

“Pakuyang’anitsitsa timakhala osinthika; ndipo pamene tikulingalira pa ungwiro wa khalidwe lakumwamba, tidzakhumba kukhala osinthika apumphu, ndiokonzedwanso muchifaniziro cha ungwiro wake. Ndikuzera mwachikhulupiriro mwa mwana wa Mulungu momwe kusinthika kumachitika mukhalidwe, ndipo mwana wa mkwiyo amakhala mwana wa Mulungu. Iye amadutsa kuchoka ku imfa kupita kumoyo iye amakhala mu uzimu ndipo amadzindikira zinthu za uzimu. Mzeru za Mulungu zimawalira malingaliro ake, ndipo iye amaona zinthu zodabwitsa kuchokera mmalamulo ake. Pamene munthu wasinthika ndi choonadi, ntchito ya kusinthika kwa khalidwe imapitilira.” – Selected Messages, bk. 1, pp. 337-338.


Lachitatu , Feb 25

3. KUPEPEZEKA KWA YESU MU SAMARIYA

a. Kodi ndipempho lanji lomwe anthu aku Samaliya analipereka kwa Yesu- ndipo chifukwa chiyani? Yohane 4:40.

b. Fotokozani chotsatira cha nthawi yakukhala kwa Khristu mu Samariya. Yohane 4:41.

“Mmawu oyankhulidwa kwa mzimayi pachitsime, mbewu yabwino, inadzalidwa, ndipo ndimofulumira motani momwe zokolola zinalandiridwa. Anthu aku Samariya anabwera ndikuzamunva Yesu, ndikukhulupilira mwa iye. Pozinga mozungulira iye pachitsime, iwo anamudzadza iye ndi mafunso, ndipo mokondwera analandira kufotokozera kwake kwa zinthu zambiri zomwe zinakhala zophimbika kwa iwo. Pamene iwo amamvetsera, nkhawa zao zinayamba kuchoka. Iwo anali ngati anthu amumdima waukulu kusatira mlezo wodabwitsa wakuunika kufikira iwo atapeza usana.. Koma iwo sanakhutitsidwe ndi mkumano waufipiwu. Iwo anali chidwi choti amve zambiri, ndikukhalanso ndi abwenzi awo kudzamvetsera kwa mphunzitsi wodabwitsayu. Iwo anamuitanira iye ku mzinda wawo; kwa matsiku awiri iye anakhala mu Samariya, ndipo ambiri ena anakhulupirira pa iye.”--The Desire of Ages, p. 192.

“Khristu anabvumbulutsa Mulungu kwa ophunzira ake munjira yakuti anachita mmitima yawo ntchito yapadera, yotere yonga yomwe iye wakhala akudandaulira ife kuti timlole kuichita mmitima yathu. Pali ambiri omwe, akukhalanso kwambiri pa zolembedwa, ataya chiyang’aniro cha mphanvu zamoyo za chitsanzo cha Mpulumutsi. Iwo ataya chiyang’aniro cha iye monga, wantchito wozikaniza yekha,wodzichepesa. Chomwe iwo akusowa ndikuyang’ana kwa Yesu. Tsiku lililonse tikusoweka kubvumbulutsidwa kwatsopano kwa kupedzeka kwake.” -Reflecting Christ, p. 302.

c. Kodi a Samariya ambiri anayankhula chiyani atatha kumlandira Yesu monga Mesiya? Yohane 4:42.

“Afalisi ananyoza kuzichepetsa kwa Yesu. Iwo ananyozera zozizwa zake, ndikupempha chizindikiro kuti iye anali mwana wa Mulungu. Koma a Samariya sanafunse chizindikiro, ndipo Yesu sanachite zozizwa pakati pawo, kupatula mukubvumbulutsa zinsinsi za moyo wake kwa mzimayi pachitsime. komabe anthu ambiri anamlandira iye. Muchimwemwe chatsopano iwo anati kwa Mzimayi, ‘Tsopano takhulupirira, Osati chifukwa cha kulankhula kwako; pakuti tanva tokha ndipo tidziwa kuti uyudi ndithu ndi Khristu, Mpulumutsi wa dziko lapansi.” – The Desire of Ages, pp. 192-193.


Lachinayi , Feb 26

4. MPHANVU YA UNENERI

a. Kodi ndi pauneneri wanji pomwe a Samariya anakhazikitsa chikhulupiriro chawo mwa Mesiya olonjezedwa? Genesis 49:10.

“A Samariya anakhulupilira kuti Mesiya anayenera kubwera monga mpulumutsi, osati kwa Ayuda okha, koma kudziko lapansi. Mzimu woyera kuzera mwa Mose analosera iye ngati mneneri wotumizidwa kuchokera kwa Mulungu. Kuzera mwa Yakobo chinakhala chikulankhulidwa kuti kwa iye anthu akuyenera kusonkhanira; ndipo kudzera mwa Abraham kuti mwa iye mitundu yonse yadziko lapansi ikuyenera kudzadalitsidwa. Pa malemba amenewa, anthu aku Samariya anakhazikitsa chikhulupiriro chawo mwa Mesiya. Mfundo yakuti Ayuda amatanthauzira molakwika aneneri obwera pambuyo, kumakhulupirira za ulemerero wakubwera kwa Khristu kwachiwiri kumakusokoneza ndi koyamba, zitsogolera a Samariya kusiya zolembedwa zopatulika zonse kupatula zomwe zinaperekedwa kudzera mwa Mose. Koma pamene Mpulumtsi amachotsa zothandauzira zabodzazi, ambiri analandira mauneneri osatira komanso mawu a Khristu mwiniwake okhuza ufumu wa Mulungu.” – The Desire of Ages, p. 193.

b. Kodi tingaphunzire chiyani lero kuchokera kuchoona chakuti Asamariya anali otsegukira modabwitsa ku choonadi? Mlaliki 11:4, 5.

“Kudziko lonse lapansi Abambo ndi Amayi akuyang’ana mwachidwi kumwamba. Mapemphero ndi misodzi ndi mafunso zokwera kuchokera mmiyoyo yofunafuna kuunika, chisomo, mzimu woyera. Ambiri ali pa gombe la ufumu, kudikirira chabe kusonkhanisidwira mkati.” – The Acts of the Apostle, p.109

c. Kodi ndichiyani chomwe anthu amakhala pamene iwo moonadi alandira Khristu? Perekani chitsanzo. Marko 5:18-20; 7:31-37.

“Mzimu wa Khristu udzayambisa mwa munthu zonse zomwe zidzakometse khalidwe ndikulemekedza umunthu. Udzammanga munthu, ku ulemerero wa Mulungu muthupi, mmoyo ndi mzimu. Ndipomiyoyo yomwe yakhala inachepetsedwa ndi kupitisidwa pansi kukhala zida za Satana kudzera mumphanvu ya Khristu akusinthikabe kukhala amithenga a chilungamo, ndikutumizidwa chitsogolo ndi mwana wa Mulungu kuyankhula za zinthu zazikulu zomwe Ambuye wachita kwa iwo ndi chifundo choonetsedwa pa iwo.” – The Desire of Ages, p. 341.


Lachisanu , Feb 27

5. ATUMIKI ACHIKHRISTU

a. Kodi ndimaphunziro anji amene Ife tikuphunzira kuchokera kwa mzimayi waku Samariya? 1 Yohane 1:1-3, 2 Akolinto 5:14 (mbali yoyamba).

“Nthawi yomweyo pamene iye anapeza mpulumutsi Mzimayi wa ku Samariya anabweretsa ena kwa iye. Iye anazionesa yekha mtumiki wamphanvu kwambiri kuposa ophunzira a iye mwini. Ophunzira sanaone kanthu mu Samariya chosonyeza kuti unali munda wolimbikitsa. Malingaliro awo anakhazikika pantchito yaikulu yoyenera kuchitidwa mtsogolo. Iwo sanaone kuti ufulu owazungulira iwo zinali zokolora zoyenera kusonkhanitsidwa. Koma kudzera mwa mzimayi yemwe iwo amamunyoza, mzinda wonse unabweretsedwa kumunva mpulumutsi. Iye ananyamulira kuunika kwa anthu amziko nthawi yomweyo.

“Mzimayi uyu akuimilira kugwira ntchito kwa chikhulupiriro chochitachita mwa khristu. Ophunzira aliyense oona amabadwa mu ufumu wa Mulungu monga mtumiki. Iye amene wamwa madzi amoyo amakhala kasupe wa moyo. Wolandira amakhala opereka. Chisomo cha Khristu mmoyo chili ngati kasupe wamadzi muchipululu, otungidwa mpaka kutsitsimutsa onse, ndikuwapangitsa onse omwe ali okonzeka kuonongeka kufuna kukumwa madzi amoyo.” – The Desire of Ages, p. 195.

b. Kodi chochitika chimenechi chingatilimbikitse ife bwanji lero? Mlaliki 11:6

“Sitikusoweka kupita kumalo achilendo kukakhala atumiki a Mulungu. Onse otizungulira ife ali minda. ‘Yoyera yokonzeka kukumweta,’ ndipo aliyense amene angafune angathe kusonkhanitsira ‘zobala ku moyo wosatha.’ Mulungu akuitanira ambiri mu Battle creek omwe akufa kuuzimu waulesi kuti apite komwe ntchito yawo ikusowekela muntchito yake. Tulukani mu Buttle Creek, ngakhale ichi chitafunikira msembe yapadera. Pitani kwinakwake kuti mukakhale mdalitso kwa ena. Pitani komwe mungakalimbikitse mpingo wina wofooka. Gwiritsani ntchito mphanvu zomwe Mulungu wakupatsani inu.” – Testimonies for the Church, Vol. 5, p. 187.


Lachisanu ndi chimodzi , Feb 28

6. MAFUNSO OBWEREZA PAWEKHA

1. Kodi mzimayi anachita chiyani pamene iye anaona Yesu monga mpulumutsi yekhayo?

2. Fotokozani chomwe chikutanthauza kuti minda yayera yokonzeka kukholola.

3. Kodi ndimatsiku angati omwe Yesu anakhala ndi a Samariya?

4. Kodi ndiumboni wanji omwe a Samariya anapereka okhuza Yesu?

5. Chimachitika ndichiyani kwa anthu nthawi yomweyo pamene iwo amlandira Yesu ku miyoyo yawo?

 <<    >>