Back to top

Sabbath Bible Lessons

Maphunziro AmBaibulo Apa Sabata

 <<    >> 
  Sabata, Febuluwale 1, 2025

Zopereka Za Sabata Loyamba

Sitingafunse za nkhondo, ndi mbiri za nkhondo, ngozi zoopsa kwambiri, chilala, madzi otsefukira, mphepo ya mkuntho, zibvomerezi, moto, ndi miliri zikuchulukira pa dziko lonse lapansi ndi changu chachikulu kwambiri- zonsezi zili zongokwanitsa maulosi a m’Baibulo amene timawawerenga. Zoonadi, mungozi zonsezi, tikhonza kumaona bwino lomwe za kuyandikira kwa Mulungu kudza ku dziko lapansi. Anthu ochuluka zikwi zikwi amazunzika kwambiri ndi zovuta zoopsazi, ndipo chifukwa chazimenezi akuitanira chithandizo chosiyanasiyana kuchokera kwa akazembe a Yesu Khristu kuti apereke mankhwala ochilitsa a ku giliyadi.

Mavuto opweteka kwambiri awa, A gawo loona umoyo wabwino wa anthu la ku GC lakhala likugawa madalitso amene amaperekedwa kuchokela mu chuma cha zopereka zathu chimene chimatumizizdwa ndi inu, abale athu odzungulira pa dziko lonse. Zoperekazi zimatumizidwa mu njira yapadera ypawekha kuti ikafikile zotsowazi, komanso kudzera mu njira ya zopereka za pa Sabata loyamba. Okondedwa abale ndi alongo zopereka zanu zakhala zikutumikira monga thandizo kwaiwo amene analuza pokhala pawo mu ngozi zachilengedwe zogwa mwazizizi; zakhala zikuthandizira zokudya kwa mabanja ambiri mazana mazana ndi kutsamalira ana amasiye ndi akazi amasiye, powafikitsira chitsamaliro ndi chithandizo kwa iwo. Zopereka zimenezi zakhala zikuthandizira makolo mukupedza mbewu zoti adzale ndi kumadyetsa mabanja awo kapena kuyamba business yaing’ono ndi kuti anthu ambiri osawelengeka achikhulupiriro chathu azitha kupedza mwayi opedza ndalama ndi ntchito imene kwa iwo ikanakhala yotsatheka kupedzeka kwaiwo.

Tithokoze Mulungu kuti mu nthawi ino ya mabvuto, anthu ambiri akhala akukhudzika kuti ayike zopereka zawo pa guwa la Nsembe la Ambuye. Mmalo mwa iwo amene akuthandizidwa, tikukuthokozani kwambiri zedi!

Komano ngakhale zili chomwechi, zotsowazi sizimatherapo mmalo mwake, zikuchu-lukila kwambiri tsiku ndi tsiku, chotelo zopeleka zanu zimathandiza kwakukulu zedi.

“Mtanda wa khristu ukudandaulira kuolowa manja kwa otsatila aliyense wa Mpulumutsi odala. Mfundo imene ikuonetseredwa apapa ndi yopereka, pakupereka. Zinthu izi, pochitika mmafuno abwino ndi muntchito za moyo wa chikhristu.” – Counsels on Stewardship, P. 14.

Lero pamene mukupereka zopereka zanu zapadera za Sabata loyamba, chonde chitani mwakuthekera kwanu kuti mulemekeze Mulungu wanu. Kaya ndi zochepa kapena ndi zambiri, zonsezo zikhonza kuchita mbali yake yaikulu. Kuchokera ku chuma cha chikondi chogawidwachi, tidzakhala tikupitiliza kugwawa madalitso kwa abale athu pa dziko lonse lapansi. “Iye amene amapereka kwa anthu amakhala akudalitsa ena, ndipo amakhala adalitsikanso iye mwini kumuyeso wambiri” (Ibid., p. 13) Ambuye Mulungu wathu akudalitseni kopotsa!

Kuchokera ku nthambi yoona za umoyo wa anthu ku likulu la mpingo

 <<    >>