Back to top

Sabbath Bible Lessons

Maphunziro AmBaibulo Apa Sabata

 <<    >> 
PHUNZIRO 6 SABATA, FEBULUWALE 8, 2025

KUYENDA KWA MZIMU WOYERA

VESI LOLOWEZA: “Ndipo monga Mose anakweza njoka mchipululu, chotero mwana wa munthu ayenera kukwezedwa; kuti yense wakukhulupilira akhale nawo moyo wosatha mwa iye” (Yohane3:14, 15).

“Yang’anani, O! yang’anani kwa Yesu ndikukhala ndi moyo.” Christian Education, p. 76.

Zowelenga Zoonjezera:   Christ’s Object Lessons, pp. 95-102

Loyamba , Feb 2

1. KUFUNSISISA KWA KHAMA

a. Kodi ndi funso lanji la Nikodemo limene likuwonesa kuti mtima wake unafewetsedwa? Yohane3:9.

“Yesu ananenetsa kwa Nikodemo: Simkangano womwe udzakuthandize mlandu wako; simtsutso womwe udzabweretse kuunika ku moyo. Ukuyenera kukhala ndimtima watsopano, apo ayi sungathe kuzindikira ufumu wa kumwamba. Siumboni waukuru womwe udzakubweretseni inu mumalo abwino, koma cholinga chatsopano, akasupe atsopano amachitachita. Muyenera kubadwa mwatsopano. Kufikira kusinthika uku kutachitika kupanga zinthu zonse zatsopano, maumboni amphanvu omwe angaonetsedwe akhala opanda ntchito. Chosowa chili mkati mwanu chilichonse chikuyenera kusinthidwa, apo ayi simungathe kuona ufumu wa Mulungu.

“Awa anali mawu ochititsa manyazi kwambiri kwa Nikodemu….Iye analibe malingaliro auzimu okwanira kuti azindikire thandauzo la mawu a Khristu. Koma mpulumutsi sanakumane ndi mtsutso ndi kutsutsana…

“Kuthwanima kwina kwa choonadi kunali kukulowa mmalingaliro amdindoyu. Mawu a Khristu anamudzadza iye ndi mantha, ndi kumutsogolera iye kuti afunsenso kuti, `Kodi zinthu zimenezi zingatheke bwanji? Ndikutsimikiza kwakukulu Yesu anayankha, ‘ Kodi uli mphuzitsi wa Israeli, ndipo sudziwa zinthu izi?’ Mawu ake anapereka kwa Nikodemo phunziro lakuti, mmalo mokumva kuphyetsedwa mtima ndi mawu omveka bwino a choonadi, ndikulorera kukhala ouma mtima, Iye anayenera kukhala ndi lingaliro lozichepetsa kwambiri la iye yekha chifukwa cha umbuli wake wauzimu. Komabe mawu aKhristu amalankhulidwa ndi ulamuliro otsindika,ndipo zonse, maonekedwe ndi mawu zinafotokoza chikondi choona chotero kwa iye, kotero kuti iye sanakhumudwitsike pamene anazindikira kusikisisa komwe iye ali nako.” – Testimonies to Ministers, pp. 368-369.


Lachiwiri , Feb 3

2. KUSINTHA KHALIDWE LENILENI

a. Kodi ndi muchiyani momwe Afarisi anali kudzikwedzera okha? Luka 18:9-12.

“Ayuda anali oyambirira kuitaniridwa ku munda wampesa wa Ambuye, ndipo chifukwa cha ichi iwo anali odzikwedza komanso odzilungamitsa. Zaka zawo zochuluka za utumiki iwo anazitenga ngati chowayenereza iwo kulandira mphoto yokulirapo koposa ena. Panalibe chinthu chokwiyitsa kwambiri kwa iwo kuposa kulengezetsa kuti amitundu anayenera kuloledwa kukhala ndi mwayi wofanana ndi iwo eni muzinthu za Mulungu.” – Christ’s Objects Lessons, p. 400.

b. Kodi Yesu anaonetsera bwanji ntchito ya mzimu woyera mumtima? Yohane 3:8.

“Mphepo imanveka munthambi za mitengo, kugwetsa masamba ndi maluwa; chonsecho ndiyosaoneka, ndipo palibe munthu amadziwa komwe ikuchokera kapena komwe ikupita. Choteronso ndintchito ya Mzimu woyera pamtima. Sizizngafotokozedwe konse kuposa momwe mphepo ingayendere. Munthu sangathe kutchula nthawi yeniyeni kapena malo enieni, kapena kuzindikira zochitika zonse za mundondomeko yakusinthika; koma ichi sichimamusonyeza iye kukhala osasinthika. Kudzera mwa mthenga monga mpepo yosaoneka, Khristu amagwira ntchito mokhazikika pamtima.” – The Desire of Ages, p. 172.

c. Kodo ndimotani momwe chithuzithunzi cha umulungu chimakhazikitsidwira mumtima? Yesaya 30:21; Yeremiya 42:3 ; Mateyu16:17.

“Pang’ono ndi pang’ono, mwinanso mosadziwika kwa ochirandira, chilimbikitso chimachitidwa kuti chiusendezere moyo kwa khristu. Izi zimatha kukhala zolandira kuzera mukukangamira pa iye, kudzera mukuwerenga malembo kapena kudzera mukunvetsera mawu kuchokera kwa mlaliki wamoyo. Mwadzidzi, pamene mzimu akubwera ndi kudandaulira kwakukuru kwa chindunji, moyo mwachimwemwe umazipereka okha kwa Yesu. Mwa ambiri ichi chimatchulidwa kusinthika kodabwitsa; koma chimakhala chotsatira cha kudandaulira kwa nthawi yaitali kwa mzimu wa Mulungu-ndondomeko yochitidwa modekha.”—Ibid.

“Bvomerezani mitima yanu kuti ifewetsedwa ndi kugonjetsedwa ndi mzimu wa Mulungu. Lolani mmoyo youma ngati myala isukunuke pansi pakugwira ntchito kwa mzimu woyera.” – Letters and Manuscripts, Vol. 12, Letter 53, 1897.


Lachitatu , Feb 4

3. UMBONI WAKUBADWA MWATSOPANO

a. Kodi ndimotani momwe kugwira ntchito kwa mkati kwa mzimu woyera kumaonetsedwera kunja? Agalatiya 5:22-25.

“Pamene mphepo payokha iliyosaoneka, imatulutsa zotsatira zomwe zimaoneka komanso kunvedwa. Chomwecho ntchito yamzimu pa moyo idzazibvumbulutsa yokha mmachitachita alionse aiye amene wanva mphanvu yake yopulumutsa. Pamene mzimu wa Mulungu watenga ulamuliro wa mtima, umasintha moyo. Malingaliro auchimo amachotsedwa, machitachita oipa amadzudzulidwa; chikondi, kudzichepetsa ndi mtendere zimatenga malo amkwiyo, msanje ndi kulimbana. Chimwemwe chimatenga malo a kukhumudwa, ndipo maonekedwe a nkhope amaonetsera kuunika kwa kumwamba.” – The Desire of Ages, p. 173.

b. Kodi ndiliti lomwe munthu amalandira mdalitso wakusinthika? Aroma 10:9, 10, 1 Yohane 1:9.

“Palibe munthu amaona dzanja lomwe limanyamula zothodwetsa, kapena kuona kuunika kukutsika kuchokera kumabwalo akumwamba. Mdalitso umabwera pamene mwachikhulupiriro moyo wazipereka okha kwa Mulungu. Tsopano mphanvu imeneyo yomwe palibe maso a munthu angathe kuiona imalenga munthu watsopano mchifaniziro cha Mulungu.” – Ibid.

“Ngati muli ndi mzimu woyera kuumba komanso kukonza mtima wanu tsiku ndi tsiku, tsopano mudzakhala ndikunvetsetsa kopatulika kozindikira khalidwe la ufumu wa Mulungu. Nikodemo analandira chiphuzitso cha Khristu ndipo anakhala wokhulupilira owona.” – Testimonies to Ministers, pp. 369-370.

c. Kodi Khristu akuionetsa motani ndondomeko imeneyi? Mateyu 13:33.

“Chotupitsa chosungidwa mu ufa chimagwira ntchito mosaoneka kubweretsa choumbidwa pasi pa ndondomeko yake yakufufumitsa chotero chotupitsa cha choonadi chimagwira ntchito mwachinsinsi, mwakachetechete, mokhazikika, ku kusintha moyo. Zokonda zachibadwa zimafewetsedwa ndi kugonjetsedwa malingaliro atsopano, zolinga zatsopano zimadzalidwa. Muyeso watsopano wa khalidwe umakhazikitsidwa- moyo wa Khristu. Malingaliro amasinthidwa; mphanvu zimazutsidwa kukugwira ntchito munjira yatsopano. Munthu samavekedwa ndi mphanvu zatsopano, koma mphanvu zomwe analinazo zimayeretsedwa. Chikumbumtima chimadzutsidwa. Timadzazidwa ndi makhalidwe omwe amatiyenereza ife kuchita utumiki kwa Mulungu.” – Christ’s Object Lessons, pp. 98, 99.


Lachinayi , Feb 5

4. KULONGOSOLA KODZIWIKA BWINO

a. Kodi Yesu analongosola bwanji kupachikidwa kwake komwe kuchitike posachedwa? Yohane 3:14, 15.

“[Potengera Yohane3:14,15] Apa panali pabwalo pomwe Nikodemo amapadziwa pwinobwino. Chizindikiro cha njoka yamkuwa yokwezedwa zinampanga iye kumvesesa bwino utumiki wa mpulumutsi. Pamene anthu a Israeli anali kufa ndi ululu wa njoka za moto, Mulungu anatsogolera Mose kupanga njoka yamkuwa, ndikuika iyo pamwamba mkatikati mwa nsonkhano. Tsopano liwu linamveka kuzungulira msasa wonse kuti onse omwe angayang’ane pa njoka yamkuwa akhala ndi moyo. Anthu amadziwa bwino kuti mwa iyo yokha njoka yamkuwa inalibe mphanvu ya kuwathandiza iwo. Inali chizindikiro cha Khristu. Monga chifaniziro chinapangidwa mofanana ndi njoka zoononga chinakwezedwa pamwamba kumachilitso awo, chotero mmodzi opangidwa mchifaniziro chathupi lauchimo anayenera kukhala mpulumutsi wawo. Aroma8:3.Ambiri a Israeli amautenga utumiki wa zinsembe ngati uli ndi ubwino mwa iwo okha owamasula iwo kutchimo. Mulungu amakhumba kuwaphunzitsa iwo kuti zinalibe mphanvu zoposa njoka yamkuwa. Unali wotsogolera malingaliro awo kwa mpulumutsi. Kaya kumachilitso a mabala awo kapena kukukhululukidwa kwa machimo awo, iwo sakanatha kuzichitira kanthu kena kalikonse kiwo wa okha koma kuwonetsa chikhulupiliro chawo mumphatso ya Mulungu. Iwo anayenera kuyang’ana ndikukhala ndi moyo.” – The Desire of Ages, pp. 174-175.

b. Ngakhale panali thandizo kodi ndichifukwa chiyani ena amafa? 1 Akolinto 10:9; Ahebri 3:12.

“Ambiri a AIsraeli samaona thandizo mumankhwala omwe kumwamba kunasankha. Anthu okufa ndi ena oti akufa anawazungulira iwo,ndipo iwo anadziwa kuti, popanda thandizo lakumwamba, imfa yawo inaliyotsimikizika; koma iwo amapitilizabe kudandaula zilonda zawo, ululu wawo, imfa yawo yotsimikizika, kufikira mphamvu zawo zimatha,ndipo maso awo anachita khungu, pamene iwo akanatha kupedza machilitso achanguchangu.” – Patriachs and Prophets, p. 432.

c. Ngati tikufuna kupulumutsidwa, kodi tikuyenera kuyang’ana kuti? Ahebri 6:19, 20.

“Zotsatira zoopya za tchimo zngathe kuchotsedwa pokhapokha kuzera muthandizo lomwe Mulungu analikhazikitsa. Aislaeli amapulumutsa miyoyo yawo poyang’ana pa njoka yokwezedwa. Kuyang’ana kemeneko kumaphatikizilapo chikhulupiriro. Iwo amakhala ndi moyo chifukwa amakhulupirira mawu a Mulungu, ndikudalira mu njira zomwe zinabweresedwa kumachilitso awo. Chotero wochimwa atha kuyang’ana kwa Khristu ndikukhala ndi moyo. Iye amalandira chikhulukiro kuzera muchikhulupiriro mu nsembe yotetezera… Khristu ali ndi mphanvu komanso njira mwa iye yekha yochizira ochimwa wolapa.” – Ibid., p. 431.


Lachisanu , Feb 6

5. KUIKA MASO ATHU MOKHAZIKIKA

a. Kodi ndiphunziro lanjilimene patapita nthawi linamvetsetsedwa ndi Nikodemo lomwe tikusoweka kulitenga- ndikulisunga nthawi zonse mmalingaliro? Aefenso 2:8; Luka 13:20, 21.

“Kawirikawiri funso limabwera, chifukwa chiyani, tsopano, pali anthu ambiri, ozitchula okhulupirira mawu a Mulungu, omwe mwa iwo simukuoneka kukonzanso mmawu, muuzimu ndi mukhalidwe? Nduchifukwa chiyani kuli ambiri omwe sangathe kupirira kutsutsa kuzolinga ndi madongosolo awo, omwe amaonesa kupsa mtima kodetsedwa, komanso omwe mawu awo ali aukali, ozitamandira,ndi okwiya? Pamaoneka mmoyo mwawo chikondi chomwechomwecho cha undekha zizolowezi zomwezo za kuzikonda, mkwiyo omweomwewo ndi mawu okalipa, zomwe zimaoneka mmoyo wa anthu akudziko. Pali kudzikudza kowonekera, komwenso kwakhazikika mmakhalidwe akuthupi, makhalidwe omwewo amphulupulu kukhala ngati choonadi sichikuziwikilatu kwa iwo. Chifukwa ndichakuti iwo sanatembenuke. Iwo alibe chotupitsa chobisidwa cha choonadi mumtima mwawo. Sichinapatsidwe mwayi wochita ntchito yake. Zizolowezi komanso zikhalidwe zawo zachibadwa za zoipa sizinaperekedwebe kumphanvu zake zosintha. Miyoyo yawo imabvumbulutsa kusowekera kwa chisomo cha Khristu, kusakhulupirira mumphanvu zake zosintha khalidwe.

‘Chikhulupiriro chimadza pakumva, ndi kumvetsera kumawu a Mulungu.’ Aroma 10;17. Malemba opatulika ali chida champhanvu mukusinthika kwa khalidwe. Khristu anapemphera, ‘ patulani iwo mchoonadi mawu anu ndichoonadi.’ Yohane17:17. Ngati aphunziridwa ndikumveredwa, mawu a Mulungu amagwira ntchito mumtima, kugonjetsa khalidwe lililonse losapatulidwa. Mzimu woyera amabwera kutsutsa za tchimo, ndipo chikhulupiriro chomwe chimatumphuka mumtima chimagwira ntchito mwachikondi kwa Khristu, kutifananitsa ife mthupi,moyo ndi mzimu kuchifaniziro chake. Tsopano Mulungu angathe kutigwiritsa ntchito ife kuchita chifuniro chake. Mphanvu zomwe tinapatsidwa zimagwira ntchito kuyambira mkati kufikira kunja, kutitsogolera ife kuyankhula kwa ena choonadi chomwe chinayankhulidwa kwa ife.” – Chirst Object Lessons, pp. 99,100.


Lachisanu ndi chimodzi , Feb 7

6. MAFUNSO OBWEREZA PAWEKHA

1. Kodi khalidwe lalikulu la afarisi linali lanji mmatsiku a Khristu.

2. Fotokozani momwe ife timabadwiranso kuchifaniziro cha Khristu.

3. Ndimotani momwe kusinthika kwa mtima kumaonetseredwa?

4. Fotokozani choimilira cha njoka yokwezedwa.

5. Kodi fanizo la chotupitsa likubvumbulutsa bwanji kukula muchisomo cha Mulungu?

 <<    >>