Loyamba
, marichi 9
1. MADZI OCHIRITSA
a. Kodi ndi chifukwa cha cholinga chanji chimene anthu ambiri opuwala amapitira ku Yerusalemu? Yohane 5:2, 3.
b. Kodi ndi chikhulupiliro chanji chimene anthu anali nacho chokhuza thamanda la Betesida? Yohane5:4.
“Pa nthawi ina madzi athamanda limeneli amatakasidwa ndipo chimakhulupiliridwa kwambiri kuti chimenechi chinali chotsatira cha mphanvu za uzimu, ndi kuti winaaliyense amene angalowe mmadzimu koyambilira madziwo akatakasidwa, azachilitsidwa nthenda iliyonse imene iye alinayo. Mazana mazana aanthu odwala amakayendera kumalowa; koma khamu linali lalikulu zedi kotero kuti pamene madziwo atakasidwa amathamangira patsogolo, kuponda ndi mapazi awo azibambo, azimayi, ndi ana, ofooka kuposa iwo eni. Ambiri amatha kuyandikira pafupi ndi thamanda. Ambiri amene amakwaniritsa kufika pa thamandalo amafa ali mphepete. Makumbi anamangidwa pozungulira malo amenewa, kuti odwala azitha kutetezeka ku dzuwa la masana ndi kukuzizira kwa utsiku. Panali ena amene anagona mumakumbi amenewa, omakwawira mbali mwa thamandali tsiku ndi tsiku, kwa chabe ndi chiyembekezo cha kupeza thandizo.” – The Desire of Ages, p. 201.
c. Kodi kuyankhulana kwa pakati pa Yesu ndi munthu wina pa thamandapa kunayamba motani? Yohane 5:5-7
Lachiwiri
, Marichi 10
2. MITUNDU YOSIYANASIYANA YA KUPUWALA
a. Kodi ndi ntchito yanji yosatheka mwa umunthu imene Yesu anamulamulira munthu wopuwala kuti achite- nanga zotsatira zake zinali zotani? Yohane 5:8, 9 (mbali yoyamba).
“Yesu sanamufunse odwala ameneyu kuti akhale ndi chikhulupiliro mwa iye. Iye anangonena naye chabe kuti `tauka yalula mphasa yako, nuyende. ‘ Koma chikhulupiriro cha munthuyu chinagwira pa mawu amenewa minyewa ndi misempha iliyonse inatakasika ndi moyo watsopano, ndipo mchitidwe wa thanzi unabwera ku myendo yake yopuwala popanda funso iye anakhazikitsa mtima wake kuti amvere lamulo la Khristu, ndipo minofu yake inachita monga mwa chifuniro cha mtima wake. Pozuka ndi myendo yake, iye anazipeza yekha munthu wamphanvu.
“Yesu sanampatse iye chitsimikizo chilichonse cha thandizo la umulungu. Munthuyu akanatha kuima kumakaikira, ndikutaya mwayi wake umodzi wa kuchilitsidwa. Koma iye anakhulupilira mawu a Khristu, ndipo pakuchita mawuwo iye analandira mphanvu.” – The Desire of Ages, pp. 202-203.
b. Kodi ndi mukhalidwe lanji la uzimu mmene anthu amene achotsedwako kuchoka kwa Khristu amazipeza okha? Yesaya 1:5, 6; Aroma 7:24.
“Kudzera mu uchimo ife tadulidwa kuchoka ku moyo wa Mulungu. Miyoyo yathu ndi yopuwala. Mwa ife tokha tilibe ife kuthekera kwa kukhala moyo wachiyero monganso analili munthu opuwala kuti analibe kuthekera kwa kuyenda. Pali anthu ambiri amene amazindikira kusowa thandizo kwawo. Amene amafunitsitsa moyo wauzimu umene ungawabweretse iwo muchiyanjano ndi Mulungu; mwachabe amayesesa kuti awupeze iwo.” – Ibid; p 203.
c. Kodi ndi mankhwala anji okha amene angachilitse khalidwe limeneli? Machitidwe 9:34.
“Mpulumutsi akuwelamira pa amene anagulidwa ndi mwadzi wake, ndi kunena ndi chifundo ndi chikondi chosaneneka, `ufuna, kuchiritsidwa kodi? Iye akukulamulirani inu kuti dzuka mwa thanzi ndi mtendere. Musadikire kuti muzimve mumtima kuti mwachiritsidwa. Khulupilirani mawu ake, ndipo azakwaniritsidwa. Ikani chifundo chanu ku mbali ya Khristu. Chifuniro choti mutumikira iye, ndipo mukuchita monga mwa mawu ake inu muzalandira mphanvu kaya ndi khalidwe loipa lanji, chikhumbokhumbo chachikulu chimene kudzera mukuchita kwa nthawi yaitali chikumanga zingwe thupi ndi moyo, Khristu ndi wothekera ndi ofunitsitsa ku pulumutsa. Iye adzapereka moyo ku moyo umene uli okufa mu uchimo.’ Aefeso2:1. Iye azamasula kuti akhale amfulu ansinga mukufgooka ndi masoka ndi maunyolo a chimo.” – Ibid.
Lachitatu
, Marichi 11
3. KUYENDA MMOYO WATSOPANO
a. Kodi ndimotani mmene Khristu amatithandizira ife kuti tigonjetse? Aefeso 2:1-6
“Munthu mwachibadwa amakondwera kutsatira malingariro asatana, ndipo iye sangathe kumukaniza mwachipambano mdani woopsa ameneyi pokhapokha Khristu, mgonjetsi wamphanvu, akhala mwa iye, natsogolera zikhumbokhumbo zake, ndikumpatsa iye mphanvu…Satana amaziwa bwino kwambiri kuposa anthu aMulungu mphanvu zimene iwo angakhale nazo zomugonjesera iye pamene mphanvu zawo zili mwa Khristu. Pamene iwo mozichepetsa achonderera thandizo kwa mgonjesi wamphanvu, okhulupirira ofooketsetsa wachoonadi, wodalira modzadza mwa Khristu, angathe mwachipambano kumlaka Satana ndi khamu lankhondo lake lonse.” – Testimonies for the church,Vol. 1, p. 341.
“Tikuyenera kuphunzira za Khristu. Tikuyenera ife kuziwa chimene iye ali kwa onse amene iye wawaombola. Tikuyenera kuzindikira kuti kudzera muchikhulupiriro mwa iye ndimwayi wathu kukhala otenga nawo mbali khalidwe la umulungu, ndipo kotelo kuthawa chibvundi chimene chili mudziko lapansi kudzera muchilakolako. Kenako ife timayelesedwa kuchokera kuuchimo onse, zilema zonse za khalidwe. Sitikufunika ife kulekerera khalidwe limodzi lauchimo…
“Pamene ife tikutenga nawo mbali khalidwe la umulungu zizolowezi za chibadwa ndizotengela za zoipa timadulidwako kuchokera kukhalidwe, ndipo ife timapangidwa mphanvu zamoyo timapangidwa kukhala mphanvu zabwino kuubwino. Nthawi zonse kuphunzira za mphuzitsi wa umulungu, tsiku nditsiku otenga nawo khalidwe lake, ife timagwirizana ndi Mulungu mukugonjetsa mayesero asatana. Mulungu amagwira ntchito, ndiponso munthu amagwira ntchito, kuti munthu athe kukhala mmozi ndiKhristu monga khristu ali amodzi ndi Atate. Kenako ife timakhala pamodzi ndi Khristu mmabwalo akumwamba. Malingaliro amapumula ndi mtendere ndi chitsimikizo mwa Yesu.” – The Review and Herald April 24, 1900.
b. Fotokozani mtendere umene umabwera kudzera mumphanvu zochokera mwa Khristu. Aroma 8:3-6.
“Mwana aliyense amakhala moyo Kudzera mmoyo wa atate wake. Ngati inu muli mwana wa Mulungu, wobadwa kudzera mwa mzimu wake, mumakhala moyo wodzera mmoyo wa Mulungu…[ndipo]Moyo wa Khristu umaonekera mmoyo kudzera mu` thupi lathu la kufa’[2Akolinto4:11]. Moyo umenewo umene uli mwa inu udzatulutsa khalidwe lomwelo ndikuonetsera ntchito zomwezo monga unachitila mwa Khristu. Motelo inuyo mudzakhala muchiyanjano ndi lemba lina lililonse lalamulo lake; pakuti `malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo.’Masalmo19:7, mwatanthauzo. Kudzera muchikondi `choikika chake chakulamulo’ chizakwanilitsidwa mwa ife, `amene sitiyendayenda monga mwa thupi koma monga mwa mzimu.’ Aroma 8:4” – Thoughts from the Mount of Blessings, p.78.
Lachinayi
, Marichi 12
4. MKWIYO WA AFALISI
a. Posalabadira mdalitso umene unapelekedwa kwa opuwala, kodi ndichifukwa chiyani afalisi anakwiya kwambiri? Yohane 5:9 (gawo lomaliza), 10.
“Pamene opuwala ochilitsidwayo anathamanga mwa changu kumapita ndi kuyenda kwa mphanvu ndimastepe omasuka,kumayamika Mulungu ndi kumakondwerera mumphanvu zake zatsopano zomwe anazipedza, iye anakumana ndi Afalisi ambiri,ndipo mwachangu anawauza iwo zakuchilitsidwa kwake. Iye anadabwitsika pakusasamala kumene iwo anali nako pomvetsera kunkhani yake.
“Ndikhope zakugwa anamudula iye pakamwa, pomufutsa chifukwa chiyani iye ananyamula mphatsa yake patsiku lasabata. Iwo mwamkwiyo anamkumbutsa iye kuti sichololeka kwa iye kusenza katundu patsiku la Ambuye. Muchisangalaro chake munthuyu anaiwala kuti tsikuli linali lasabata; komabe iye samachinva mumtima kususika pa kumvera lamulo la iye amene anali ndi mphanvu zotere zochokera kwa Mulungu. Iye molimba mtima anayankha kuti, `Iye amene anandichilitsa, yemweyu anati kwa ine, yalula mphasa yako, nuyende.` Ndipo iwo anamufunsa iye kuti ndi ndani amene anachichita ichi koma iye samamdziwa kuti ndi ndani. Atsogoleri amenewa amadziwa bwinobwino kuti ndi mmodzi yekha wakhala akuzionetsera yekha kuthekera kwa kuchita chozizwa chimenechi; koma iwo amafunitsitsa umboni wachindunji woti ndi Yesu, kotero kuti iwo akathe kumuimba mlandu iye kuti ndi wophwanya sabata. Mukuweruza kwawo iye sanangophwanya kokha lamulo mu kuchiritsa munthu pa tsiku la sabata komanso wachita chinthu choipitsitsa mu kulamulira iye kuti anyamule mphasa yake.” – The Desire of Ages, pp. 203-204
b. Kodi Ayuda analipanga Sabata kukhala chiyani? Mateyu 23:4.
“Ayuda anapotozeratu lamulo kotero kuti analipanga ilo kukhala gori la ukapolo. Zofuna zawo zopanda tanthauzo zinakhala manong’onong’o pakati pa maiko ena. Makamaka sabata linachingilidwa ndi zolesa zopanda tanthauzo zambirimbiri. Kwa iwo silinali losangalatsa; tsiku loyera la Ambuye, lolemekezeka. Alembi ndi Afalisi anapanga kusunga kwake cholemetsa chosapilirika. Muyuda samaloledwa kusonkha moto kapena kuyasa kandulo pa Sabata. Zotsatira zake anthu amadalira anthu amitundu muzochitika zambiri zimene myambo yawo imawaletsa iwo kudzichitira iwo eni. Iwo samaonetsera kuti ngati machitidwe awa ali uchimo, iwo amene akugwiritsa ntchito ena kuti achite zimenezo ndi olakwa chimodzimodzi ngati kuti achita ntchito zimenezo iwo eni. Iwo amaganiza kuti chipulumutso chinali cha Ayuda basi, ndipo khalidwe la anthu ena onse, pokhala lopanda chiyembekezo ndi kale, silingaipitsidwenso. Koma Mulungu sanapereke malamulo amene sakuyenera kumveredwa ndi onse. Malamulo sakubvomereza zoletsa zosamveseseka kapena zaundekha.”–Ibid., p. 204.
Lachisanu
, Marichi 13.
5. SABATA NDI CHOLINGA CHAKE
a. Kodi Khristu amagwirizana bwanji ndi lamulo la Mulungu komanso ndi Sabata? Yesaya 42:21.
“Yesu anabwela kudzakwedza lamulo ndi kulipanga ilo kukhala lolemekezeka. Iye samachepetsa kulemekezeka kwake, koma kulikweza ilo…Iye anabwera kuzamasula zosafunikira zolemetsa kuchoka ku Sabata zimene zimalipanga ilo kukhala themberero mmalo mwa mdalitso.” – The Desire of Ages, p. 206.
b. Kodi ndi chiyani chimene chikuyenera kapena chimene sichikuyenera kuchitidwa pa tsiku la Sabata? Eksodo 20:8-11.
“Pakati pa anthu osausika amene anali pa thamanda [Khristu] anasankha munthu wobvutikitsisa kuti agwiritse ntchito mphanvu zake zochilitsa, ndipo analamula munthu kuti anyamule mphasa yake kudutsa mu mzinda ndi cholinga choti afalitse ntchito yaikulu imene inachitidwa pa iye. Ichi chikhoza kuutsa mafunso okhuzana ndi kuti kodi choyenera kuchitidwa pa Sabata ndi chiyani, ndipo chikhoza kutsegula njira kuti iye azuzule zoletsa za Ayuda zokhuza tsiku la Ambuye, ndi kulengeza za kutha kwa myambo yawo.
“Yesu anafotokoza kwa iwo kuti ntchito yakuthandiza osausika inali yogwirizana ndi lamulo la Sabata. Ndi yogwirizana ndi ntchito ya angelo a Mulungu amene nthawi zonse amakwera ndi kusika pakati pa kumwamba ndi dziko lapansi kukatumikira anthu obvutika…
“Munthunso ali ndi ntchito yoti ayigwire mutsiku limeneli. Zofunikira za moyo zikuyenera kuchitidwa, odwala akuyenera kusamalilidwa, zosowa za osowa zikuyenera kuperekedwa. Sazatengedwa kukhala opanda mulandu iye amene amanyozera kuthandiza osausika pa sabata. Tsiku loyera lopuma la Mulungu linapangidwa chifukwa cha Munthu, ndipo ntchito za chifundo ndi zogwirizana bwino ndi cholinga chake. Mulungu samafuna kuti zolengedwa zake zisausike ndi ululu ngakhale mkamphindi umene angathe kuthandizidwa pa Sabata kapena pa tsiku lina.” – Ibid., pp. 206,207.
Lachisanu ndi chimodzi
, Marichi 14
6. MAFUNSO OBWEREZA PAWEKHA
1. Kodi ndi chikhulupiriro chanji chimene chinali ponseponse chokhuzana ndi thamanda la Betsida.
2. Kodi ndi odwala wanji wapadera amene anakopa chidwi cha Khristu.
3. Kodi ndi motani mmene kupuwala kwathu kwa uzimu kungachilitsidwire?
4. Kodi ndi chiyani chimene chinakwiyitsa Ayuda kwambiri chokhalana ndi kuchilitsidwa kozwizwitsaku?
5. Kodi ndi ntchito zanji zimene zili zogwirizana ndi lamulo la Sabata?