Loyamba
, Feb 9
1. BVUTO PAKATI PA WOPHUNZIRA
a. Kodi ndi funso lanji lomwe linabuka mwa ophunzira a Yohane ndi Ayuda? Yohane 3:25.
“Ophunzira a Yohane amayang’ana ndi nsanje pa kukula kwa kuchuka kwa Yesu. Iwo anali okonzekera kutsutsa ntchito yake, ndipo sipanadutse nthawi yaikulu iwo asanapedze chochitika. Funso linabuka pakati pa iwo ndi aYuda ngati mwina Ubatizo umathandiza kuyeretsa moyo kutchimo; Iwo amalimbikira kuti ubatizo wa Yesu umasiyana kwakukulu ndi wa Yohane. Mosachedwetsa iwo anali mumkangano ndi ophunzira a Khristu zokhuza kakonzedwe ka mawu oyenera kugwiritsidwa ntchito kuubatizo, komanso kumapeto kwake kuyenera kwa kubatiza kwa Yesu.” – The Desire of Ages,p. 175.
b. Kodi ndimotani momwe ophunzira a Yohane anaonetsera nsanje yawo kuntchito ya Khristu-ndipo ndiyankho lanji loyenera lomwe iye analipereka? Yohane 3:26, 27.
“Yohane mwachibadwa anali ndi zophophonya ndi zofowoka zomwe anthu amakhala nazo, koma kukhuza kwa chikondi chopatulika kunamusintha iye. Iye amakhala mumpweya wosaonongedwa ndiundekha komanso zikhumbokhumbo, ndimopitirira apo mpweya wa msanje. Iye samaonetsa kugwirizana ndikutsakhutisidwa kwa ophunzira ake, koma amaonetsera momwe iye amanvetsetsera mwabwinobwino ubale wake kwa Mesiya, ndimomwe mwachisangalaro iye anamulandilira Yemwe iye amamukonzera njira.” – Ibid., p. 179.
Lachiwiri
, Feb 10
2. UTUMIKI WA YOHANE
a. Kodi Yohane anaonetsera bwanji kuti iye anamvetsesa utumiki wake? Yohane 3:28, 29.
“Yohane anazifotokoza yekha monga bwenzi lomwe limachita ngati wamithenga pakati pa abwenzi otomerana, kukonzetsera njira ya ukwati. Pamene mkwati wamalandira mwatibwi wake, cholinga cha bwenzi chimakwanilitsidwa. Iye amasangalala muchimwemwe cha onse omwe iye analinawo mukukuza mgwirizano. Chotero Yohane anaitanidwa kuwalondolera anthu kwa Yesu. Ndipo chinali chimwemwe chake kuchitira umboni chipambano cha ntchito ya Mpulumutsi.” – The Desire of Ages, p. 179
b. Fotokozani ntchito ya Yohane- ndi yathu. Yohane1:23, 29.
“Poyang’ana mwachikhulupiriro kwa mpulumutsi, Yohane anakulitsidwa kufikira ku nsinkhu wakudzikanzidza yekha. Iye sanafune kukokera anthu kwa iye yekha, koma kukweza malingaliro awo pamwamba ndi pamwamba, kufikira iwo atapumula pa mwana wankhosa wa Mulungu. Iye mwini anali mawu okha ofuula mchipululu. Tsopano ndi chimwemwe iye anachilandira mwachifatso komanso mokondwa, kuti maso aonse atha kutembenukira kukuunika kwa moyo, “Onse omwe ali owona kumaitanidwe awo monga amithenga a Mulungu sadzafuna ulemu wakwa iwo okha. Chikondi chakwa wekha chidzamizidwa mu chikondi cha Khristu. Sipadzakhala makani olepheretsa ntchito yamtengo wapatali ya uthenga wabwino. Iwo adzazindikira kuti ndintchito yawo kuyankhula monga anachitila Yohane m’batizi, ‘onani mwana wankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo ladziko lapansi.’ Yohane1:29. Iwo adzakwedza Yesu, ndipo pamodzi ndi iye umunthu udzakwezedwa. ‘Atelo iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye woyera, ndikhala mmalo aatari ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali ndi mtima wozichepetsa ndi mzimu wosweka, kutsisimutsa mzimu wozichepetsa, ndikutsitsimutsa mtima wosweka.’Yesaya 57:15.” – Ibid.,pp.179,180.
“Musamafunefune kukondwa ndi ubwino wa inu nokha, koma funani kudziwa ndikuchita chifuniro cha Mulungu. Tiyeni aliyense azifunse, Kodi sindingalozere moyo wina wake kwa mwana wankhosa wa Mulungu, amene achotsa tchimo lake ladziko lapansi? Kodi sindingatonthoze wina wotaya chiyembekezo? Kodi sindingakhale njira yopulumutsira moyo wina kupita mu ufumu wa Mulungu? Tikufuna kuyenda kozama kwa mzimu wa Mulungu mmitima kuti tisakhale kokha ongokwanitsa kutetedza kwa ife tokha chovala choyela, koma kuti tithe kukopa ena kuti maina awo akathe kulembedwa m’buku lamoyo, osadzafufutidwamo.” – Historical sketches, p. 140.
Lachitatu
, Feb 11
3. MPHATSO YA MZIMU
a. Kodi unyinji wa anthu unachita nawo bwanji uthenga wa Khristu? Yohane 3:32.
“Ophunzira a Yohane anayankhula kuti anthu onse akubwera kwa Khristu; Koma ndi masomphenya a bwino Yohane anati, `Palibe munthu akulandira umboni wake;’ chotero wochepetsetsa anali okonzeka kumulandira iye ngati opulumutsa ku tchimo. Koma ‘iye amene analandira umboni wake anaikapo chizindikiro chake kuti Mulungu ali owona.’ Yohane 3:33.” – The Desire of Ages, p. 181.
b. Ndikwandani komwe mphatso ya mzimu woyera ikuperekedwa? Yohane 3:34.
“Tingathe kulandira kuunika kwa kumwamba pokhapokha ngati tikufuna kutaya undekha. Sitingathe kuzindikira khalidwe la Mulungu, kapena kumlandira Khristu mwachikhulupiriro, pokhapokha titalorera kubweretsa muukapolo lingaliro lililonse kukumvera kwa Khrsitsu. Kwa onse omwe achita ichi Mzimu woyera umaperekedwa kwa iwo opanda muyeso. Mwa Khristu‘chikhalira chizalo cha Umulungu mthupi, ndipo muli odzadzidwa mwa iye.’ Akolose 2:9, 10, R. V.” – Ibid.
c. Ndimotani momwe mfungulo wakulandirila muyeso waukulu wa mzimu woyera unabvumbulutsidwira mopitilira mmalemba? Yohane 14:15-17; Machitidwe 5:32.
“Sitikuyenera kumangoyankhula kokha kuti ndimakhulupilira koma kuchita choonadi. Ndikudzera mukutsatira kuchifuniro cha Mulungu mmawu athu, mmayendedwe athu, mukhalidwe lathu, zomwe zimachitira umboni kulumikizana kwathu ndi iye. Nthawi iliyonse pamene wina wasiya tchimo, lomwe liri kuphwanya kwa lamulo, moyo wake udzabweretsedwa kukufanana ndi lamulo, mukunvera kwangwiro. Iyi ndintchito ya mzimu woyera. Kuunika kwa mawu owerengedwa mosamalitsa, mawu achikumbumtima,kuyesesa kwa mzimu woyera,zimabereka mumtima chikondi chenicheni cha Khristu, yemwe anazipereka yekha nsembe yapumphu kuombola munthu yense, thupi,moyo ndi mzimu. Ndipo chikondi chimaonetsedwa mukunvera. Mzere osiyanitsa udzaonekera bwinobwino ndikusiyanitsa pakati pa onse omwe amakonda Mulungu ndikusunga malamulo ake, ndi onse omwe samamkonda iye ndiosasamala malemba ake.” – Testimonies for the Church, Vol. 6, p. 92.
Lachinayi
, Febuluwale 12
4. MTENGO WA UBATIZO
a. Ndichifukwa chiyani chili chofunikira kumvetsetsa khwerero lomwe tikulitenga chifukwa cha Khristu pamene tapanga chiganizo chobatizidwa? Yohane 3:36.
“Kuchotsapo Khristu, ubatizo monga utumiki wina ulionse, uli mwambo opanda phindu.” –The Desire of Ages, p. 181.
“Sipakusowekera mtsuso monga wakuti kaya ubatizo wa Khristu kapena wa Yohane umayeretsa ku tchimo. Ndichisomo cha Khristu chomwe chimapereka moyo ku moyo.” -Ibid.
“Ndikudzela mwa Khristu mokha momwe umuyaya ungapezedwe. Yesu anati: ‘ Iye wokhulupirira pa mwana ali nawo moyo wosatha: ndipo iye amene sakhulupirira mwana alibe moyo.’ Yohane3:36. Munthu wina aliyense angathe kubwera mukukhala nawo m’dalitso limeneli lopanda mtengo ngati iye angazagwirizane ndi zoyenereza. ‘Kwa iwo amene afunafuna ulemelerondi ulemu ndi chisaonongeko, mwa kupilira pa ntchito zabwino, azabwezera moyo wosatha.’ Aroma 2:7.” – The Great Controversy, p. 533.
“Ubatizo ndi kulengeza kopatulika kwambiri kwa kusiya dziko lapansi. Onse omwe anabatizidwa mmaina atatu a Atate, mwana ndi mzimu woyera, mukulowa kwawo mmoyo wawo wa chikhristu amalengeza poyera kuti iwo asiyana nawo utumiki wa Satana ndipo akhala mamembala a banja lachifumu, ana a mfumu ya kumwamba.” – Testimonies for the Church, Vol. 6, p.91.
b. Fotokozani mawu ochitisa mantha a Yohane m’batizi omwe akuonetsera kuya kwa kudzipereka kwamoyo kwenikweni komwe kumaonetseredwa kudzera muubatizo? Luka 3:7, 8.
“Yohane anaika mkhwanga ku midzu ya mtengo. Iye amadzudzula tchimo mosaopa zotsatira,ndi kukonzera njira mwana wankhosa wa Mulungu.
“Herodi anakhuzika pamene iye amanvetsera maumboni amphanvu otchulidwa ndi Yohane, ndipo ndichidwi chachikulu iye anafunsa chomwe iye akuyenera kuchita kuti akhale ophunzira wake. Yohane anadziwa nkhani yakuti iye akufuna kukwatira mkazi wa mchimwene wake, pomwe mwamuna wake anali moyo, ndipo mokhulupirika amamuuza Herodi kuti ichi sichinali chololedwa mmalamulo.” – Early Writings, p. 154.
“Yohane m’batizi anakumana ndi tchimo ndikudzudzula koonekera mwa anthu antchito zapansi komanso mwa anthu amaudindo apamwamba. Iye analankhula choonadi kwa mafumu ndi anthu olemekezeka, kaya iwo amva kapena achikana icho. Iye amayankhula mwachindunji kwa munthu.” – Selected Messages, bk. 2, p. 149.
Lachisanu
, Feb 13
5. NJIRA YA MZERU
a. Pakuzindikira kuti Afarisi anali kuyesesa kubweretsa kulimbana pakati pa yohane ndi iye mwini, kodi Yesu anachita chiyani? Yohane 4:1-3.
“Yesu anadziwa kuti [Afalisi] anali kuyesesa kukonza zolimbana pakati pa ophunzira ake ndi a Yohane. Iye anadziwa kuti mphepo inali kusonkhana yomwe itha kuchotsa mmodzi wa aneneri aakuru kwambiri omwe sanaperekedwepo kudziko lapansi. Pofuna kupewa zochitika zonse zosamvetsetseka kapena ndewu, iye anasiyiratu ntchito yake, ndikuchoka ku Galireya. Ifenso, pamene tiri ozipereka kuchoonadi tikuyenera kuyesesa kupewa zonse zomwe zingatsogolere kukusagwirizana ndi mkangano. Chifukwa paliponse pamene izi zabuka, zimathera kukutaya miyoyo. Paliponse pamene chochitika chachitika chochititsa mantha kuti chiyambitsa mpatuko, tikuyenera kutsatira chitsanzo cha Yesu ndi cha Yohane m’batizi.” – The Desire of Ages, p. 181.
b. Kodi tikuyenera kuphunzirapo chiyani kuchokera kukhalidwe la Yohane ku kuthetsa vuto? Yohane 3:30.
“Monga ophunzira a Yohane, ambiri amazimva kuti kupambana kwa ntchito kumadalira pa ogwira ntchito oyambirira. Chidwi chimakhazikidwa pa munthu mmalo mwa kumwamba, nsanje imalowapo, ndipo ntchito ya Mulungu imasiidwa. Munthu yemwe mosasamala walemekezedwa amayesedwa kukukondwerera kuzidalira yekha. Iye samazindikira chidaliro chake pa Mulungu. Anthu amaphuzitsidwa kudalira pa munthu kuti awatsogolere, ndipo pakutero iwo amagwa mukulakwitsa, ndikutsogoleredwa kuchoka kwa Mulungu.
“Ntchito ya Mulungu siikuyenera kukhala ndichithunzi ndi chizindikiro chamunthu. Nthawi ndi nthawi Ambuye adzabweretsa amithenga osiyanasiyana, omwe kuzera mwa iwo cholinga chake chingazakwaniritsidwe mwabwino. Odala ali iwo omwe akufuna kuti undekha uchepetsedwe, kuyankhula pamodzi ndi Yohane m’batidzi, ‘Iye ayenera kukula koma ine ndichepe.’ ” – Ibid., p. 182.
Lachisanu ndi chimodzi
, Feb 14
6. MAFUNSO OBWEREZA PAWEKHA
1. Kodi ndi chifukwa chiyani ophunzira a Yohane anakhala ansanje ndi ntchito ya Khristu?
2. Kodi Yohane analengeza chiyani kwa ophunzira ake?
3. Ndikucholinga chanji chomwe mphatso ya Mzimu woyera inaperekedwa?
4. Kodi ubatizo umakwaniritsa bwanji cholinga chake chenicheni?
5. Kodi ndichiyani chomwe Yesu ndi Yohane anachita pamene iwo anazindikira choopsa cha kulimbana pakati pa ophunzira awo?