Back to top

Sabbath Bible Lessons

Maphunziro AmBaibulo Apa Sabata

 <<    >> 
PHUNZIRO 4 SABATA, JANUWALE 25, 2025

YESU MU KACHISI

VESI LOLOWEZA: “Koma Yehova ali M’kachisi wake wopatulika; ndipo dziko lonse lapansi likhale chete pamaso pake” (Habakuku 2:20).

“Malo a mpingo akuyenera kukhala ndi ulemu wopatulika.”— Testimonies for the Church, Vol. 5, p. 494.

Zowelenga zoonjezera:   Testimonies for the Church, vol. 5, pp. 491-500

Loyamba , Jan 19

1. KACHISI ADETSEDWA

a. Fotokozani momwe zinalili mu kachisi wa kuYerusalemu pomwe Khristu amayamba utumiki wake. Yohane 2:13, 14.

“Pa chaka, Myuda aliyense amayenera kupereka theka la masekeli ngati ‘dipo la moyo wake’….... pambali pa izi ndalama zambiri zinalinso kuperekedwa ngati zopereka za ufulu, kuti zisungidwe ku thumba losungiramo la m’kachisi. Ndipo kunali kuti ndalama zonse za kunja zinayenera kutsinthidwa kupita ku malupiya otchedwa masekeli a m’kachisi, omwe anali olandirika pa ntchito ya utumiki wa m’kachisi. Kusintha ndalamako kudatsekula makomo ku khalidwe la chinyengo ndi lolanda, ndipo izi zidakulira kufika pochotsa ulemu, ndipo izi zinali ngati njira zopezera ndalama kwa asembe.

“Ogulitsawo amawonjezera mitengo yogulitsira nyama namagawana phindu lake ndi asembe komanso atsogolerii, omwe mukutero amazilemeretsa okha mmmalo mwa anthu.”—The Desire of Ages, p. 155.

b. Kodi izi zinakhudza bwanji utumiki wa m’kachisi? Ezekieli 22:26 (mbali yotsiriza).

“Mu nthawi ya paskha, nsembe zambiri zinali kuperekedwa, ndipo ndalama za zogulitsa za m’kachitsi zinali zambiri koposa. Zotsatira zake pamakhala chisokonezo, malo mwa kachisi opatulika wa Mulungu, malowo anayamba kukhala ngati mtsika wa nyama chifukwa cha phokoso la nyama. Munali phokoso la kunenelera malonda, kulira kwa ng’ombe, nkhosa, nkhunda pamodzi ndi kulira kwa malupiya ndi mikangano yoonetsa kusamvesetsana pa malonda. Chisokonezochi chinali chachikulu kotero kuti opembeza amasokonezedwa, ndipo mawu omwe amayenera kupita kwa wa Mwambamwamba anali kumizidwa mu phokoso lomwe linali m’kachisimo.”—Ibid.


Lachiwiri , Jan 20

2. ULEMU M’NYUMBA YA MULUNGU

a. Kodi Mulungu amawatenga motani malo omwe Iye amaonetsera kupedzeka kwake--ndipo langizo lake loyamba linali lotani pa Phiri la Sinai? Ekisodo 3:1–5; 19:12, 13.

“pamene Ambuye adatsikira pa Phiri la Sinai, malowo adayeretsedwa ndi kupezeka kwake….ili ndi phunziro kuti paliponse pomwe Mulungu amapezeka malowo amakhala oyera”—The Desire of Ages, pp. 155, 156.

b. Kodi Yesu anachita chiyani kutsatira pa kuipitsidwa kwa kachisi? Yohane 2:15, 16.

“Pamene Yesu analowa m’kachisi, adayang’ana ponseponse. Adaona malonda achinyengo. Adaona nkhawa za osauka, omwe amaganiza kuti popanda kukhetsa mwazi palibe kukhululukidwa ku machimo awo. Adaona bwalo la kunja litasandulika malo ochitira malonda odetsedwa. Malo opatulika adasandulika malo ochitira malonda.”—Ibid., p. 157.

“Akutsika pa makhwerelo, adakweza mwamba nkwapulo wa zingwe zomwe zinaunjikidwa polowera. Iye adalamulira ogula kuti achoke pa malo akachisiwo. Mu nthawi yoyamba Iye adagubuduza matebulo otsinthirapo ndalama mwa mphavu ndi mosanyengelera. Malupiya anataika pansi akuchita phokoso. Palibe yemwe anamufusa za ulamuliro wakewu. Yesu sadawakwapule ndi nkwapu koma ka nkwapu komwe kadali m’manja mwake kamaoneka ngati lupanga la moto. Akulu akulu a m’kachisi, alembi, mavenda ndiso ogulitsa ng’ombe, pamodzi ndi nkhosa ndi abulu awo, anathawa pa malowo kuopa kuweruzidwa ndi kupezeka kwake.”—Ibid.,p. 158.

c. Kodi kuyeretsedwa kwa kachisi ndi Yesu kumatanthauzanji? Malaki 3:1–3.

“Mabwalo a kachisi ku Yerusalemu, ozadzidwa ndi malonda onyasa odetsedwa, amaimirira kachisi wa mtima, odetsedwa ndi zikhumbitso zoipa komanso malingaliro osalungama. Poyeretsa kachisi kuchosa ogulitsa ndi ogula aku dziko, Yesu adaonetsa cholinga chake choyeretsa mtima kuuchotsera zodetsa – za m’dziko, zilakolako za thupi, zizolowezi zoipa zomwe zimaononga moyo.”—Ibid.,p. 161.


Lachitatu , Jan 21

3. KUPEZEKA KWA MULUNGU

a. Kodi cholinga cha Mulungu pokhazikitsa kachisi pakati pa anthu ake chidali chiyani? Ekisodo 25:8.

“Kachisi yemwe adamangidwa kuti Mulungu akhalemo, adapangidwa kuti akhale phunziro kwa Israeli ndiso ku dziko. Kuyambira nthawi zosayamba, chinali cholinga cha Mulungu kuti cholengedwa chilichonse chikhale mokhalamo Mlengi kuyambira serafi woyera ndi wowala mpakana munthu.”—The Desire of Ages, p. 161.

b. Kodi n’chifukwa chiyani okhulupirira akutengedwa kukhala kachisi wa Mulungu? Ndipo tikuyenere kuchitanji mwa mtima wonse kuti kachisiyu akhalebe wopatulika? 1 Akorinto 3:16, 17; Yesaya 57:15.

“Chifukwa cha uchimo, munthu adaleka kukhala kachisi wa Mulungu. Wodetsedwa ndi kuonongedwa ndi zoipa, mtima sunathenso kuvumbulutsa ulemelero wa umulungu. Koma kudzera mu umulungu wa mwana wa Mulungu, cholinga cha kumwamba chikukwaniritsidwa. Mulungu amakhala mwa anthu, ndipo kudzera mu chisomo chake chopulumutsa mtima wa munthu umakhalanso kachisi wake.”—Ibid.

“Ngati timakhulupirira kuti chimaliziro cha zinthu zonse chili pafupi, ‘kodi tikuyenera kukhala anthu otani? Mu mayankhulidwe a chiyero ndi umulungu.’

“Moyo uliwonse womwe umakhulupirirachoonadi mopanda chinyengo udzakhala mu ntchito zomwezo. Onse adzakhala oona ndi okhulupirika, ndi osatopa pogwira ntchito yobwezera miyoyo kwa Khristu. Pamene choonadi chadzalidwa ndi kuzika midzu m’mitima yawo, pamenepo adzafunanso kuti achidvale m’mitima ya wena. Choonadi kwambiri chikumasungidwa m’mabwalo akunja. Chibweretseni icho mkati mwa mtima, chichite ufumu m’menemo ndi kulamulira moyo. Mawu aMulungu akuyenera kuphunziridwa ndi kumveredwa, ndipo moyo udzapeza mpumulo, mtendere ndiso Chimwemwe, ndipo udzlimbikitsidwa mu zakumwamba; koma pamene choonadi chaikidwa pambali m’moyo, m’mabwalo akunja, moyo sutenthesedwa ndi Malawi a moto ochokera ku ukoma wa Mulungu.”

“Kwa ambiri chipembezo cha Khristu, chikumangochitidwa kwa masiku ena, kapena muzochitika zina ndipo mu nthawi ndi zochika zina chimaikidwa pambali ndi kunyozeledwa. Mfundo za choonadi sizikuyenera kugwira ntchito kwa maola ochepa okha monga pa sabata, kapena mu ntchito zochepa zachifundo, koma chikuyenera kubweretsedwa m’moyo kuti chitsuke ndi kuyeretsa khalidwe.”— Testimonies for the Church, vol. 5, p. 547.


Lachinayi , Jan 22

4. KUYERETSEDWA KWA KACHISI WA MOYO

a. Kodi tikuyenera kuzindikira chiyani za kulephera kwathu kwa kuyeretsa kachisi? Yeremiya 2:22; Yobu 14:4.

“Palibe munthu pa yekha angathe kuchotsa kuipa kwake komwe kwamanga nthenje mu mtima mwake.”—The Desire of Ages, p. 161.

b. Kodi ndi chinsisi chanji chomwe chimatiimitsa pamaso pa Mulungu woyera ndi mtima woyeretsedwa? Ezekieli 36:25–27; Zakariya 3:3–5.

“Yakobo anali wopalamula pa zomwe anamuchitira Esau; koma adalapa. Tchimo lake linakhululukidwa ndi kusukudwa; ndipo anatha kupirira pa nthawi yomwe Mulungu anazivumbulutsa kuzionetsera kwa iye. Koma anthu amaonongedwa pamene abwera pamaso pa Mulungu mwadala akukakamirabe zoipa zawo. Pakudza kwa Khristu kachiwiri oipa adzathedwa ndi mzimu wa mkamwa mwake,’ ndi kuonongedwa ndi kuwala kwa kudza kwake.’ 2 Atesalonika 2:8. Kuunika kwa ulemerero wa Mulungu, kumene kumapereka moyo kwa olungama, kudzapha ochimwa.”

“Mu nthawi ya Yohane m’batizi, Khristu anali kuti aonekere monga mvumbulutsi wa khalidwe la Mulungu. Ndipo kukhala kwake kunali kuti kuonetsere uchimo wa anthu. Pamene anali kufuna kuti machimo awo ayeretsedwe ndi pomwe amagwirizana naye. Oyera mtima okha ndi omwe angaime naye.”—Ibid., p. 108.

“Khristu yekha ndi yemwe angathe kuyeretsa kachisi. Koma sadzakakamiza kuti alowe. Sabwera mu kachisi monga ngati wakale uja; koma akuti, ‘taona ndaima akhomo ndio ndigogoda: munthu akamva mawu anga nakatsekula chitseko, ndizdzakhala mwa iye.’ Chibvumbulutso 3:20. Sadzakhala kwa tsiku limodzi lokha; Iye akuti, ‘ndidzakhala mwa iwo ndikuyendayenda mmwemo….. ndipo adzakhala anthu anga.’ ‘Adzachotsa zoipa zathu; ndi kuzitaya pansi pa nyanja.’ 2 Akorinto 6:16; Mika 7:19. Kupezeka kwake kudzayeretsa ndi kupatula moyo, kuti ukhale kachisi wa moyo wopatulikira Ambuye, ndi mokhalamo Mulungu mwa mzimu.’ Aefeso 2:21, 22.”—Ibid.,pp. 161, 162.

“Pamene Yesu adakali kutumikira m’kachisi m’mwamba, adakalibe kutumikira mpingo pa dziko kudzera mwa mzimu wake.”—Ibid.,p. 166.


Lachisanu , Jan 23

5. KUYERETSA KACHISI LERO

a. Kodi ndi motani momwe Mulungu amawawerengerera mulandu atsogoleri a anthu ake amene amapeputsa malo a nyumba yake yopatulika? Habakuku 2:20; Ezekieli 44:23.

“Malo akachisi wa Mulungu akuyenera kukhala opatulika. Koma pofuna kupeza phindu zonsezi zinaiwalidwa.’’

“Asembe ndi atsogoleri anaitanidwa kukhala omuilira Mulungu ku dziko lonse; adayenera kuti azudzulepo za kuonongedwa kwa kachisi. Adayenera kupereka kwa anthu chitsanzo cha nzeru ndi chifundo.”—The Desire of Ages, p. 156.

“Ndizoona ndithu kuti ulemu wa mkachisi wa Mulungu watha. Zinthu ndi malo opatulika sizikulemekezedwanso; woyera ndi wamkulukulu sakuyamikidwa….. Mulungu adapereka malamulo, angwiro ndi acindunji kwa anthu ake akale. Kodi khalidwe lake latsintha? Kodi Iye si ndiye Mulungu wa mphamvu ndi wamkulu olamulira kumwamba? Kodi sizingakhale zabwino kuti kawirikawiri tiziwerenga malangizo omwe aheberi adapatsidwa ndi Mulungu, kuti ife amene tili ndi kuunika kuti titengereko ulemu wa m’kachisi wa Mulungu?”—Testimonies for the Church, vol. 5, pp. 495, 496.

b. Fotokozani chipambano chomwe chimapezeka mu mphamvu za Khristu. Mateyu 5:8; 1 Yohane 3:1–3.

“Ndikuitanira wina aliyense yemwe amati ndi mwana wa Mulungu kuti asaiwale choonadi chachikulu chotere, kuti tikufunika mzimu wa Mulungu m’kati mwathu kuti tikalowe m’mwamba, ndi ntchito ya Khristu kunja kwathu kuti atipatse chilolezo pa cholowa chamuyaya.”—Testimonies to Ministers, p. 442.


Lachisanu ndi chimodzi , Jan 24

6. MAFUNSO OBWEREZA PAWEKHA

1. Kodi ndi ndani omwe anali otsogolera malonda oipa m’kachisi?

2. Kodi tikuyenera kukhala ndi ganizo lotani pamene tikudza pamaso pa Mulungu?

3. Fotokozani kufunika kwa uzimu komwe kachisi wa ku Yerusalemu adayenera kukhala nawo.

4. Kodi Khristu amalenegeza chiyani poyeretsa kachisi?

5. Kodi kachisi wathu wa mtima woipa angayeretsedwe bwanji

 <<    >>