Zopereka Za Sabata Loyamba
“Maphunziro oyambirira achinyamata kwambiri amaumba makhalidwe awo ku moyo.” – Testimonies for the Church, Vol. 3, 135.
Mawu ouzilidwa amafotokoza za machitachita achilimbikitso amene ‘misonkhano ya ana, kapena sukulu za ana aang’ono ophunzira Baibulo, zachitira ntchito yabwino. Maphunziro operekedwa amabwerezedwa ndi ana manyumba awo, ndipo amayi amaonesa chidwi chawo pomukonzekeretsa mwana mwaukhondo ku Sukulu. Ena ndi ana amakolo osakhala achikhulupiliro chathu.”-- Evangelisism, p. 583.
Malo ophunzirira a “Ana a Khalidwe” anakhazikitsidwa mu 2019 mu fagaras, mzinda wamphiri mu Romania. Ana apakati pa zaka ziwiri ndi zisanu akukulira mokongora pamenepa. Mophatikizirapo kuntchito zapadera zolingana ndi zaka, iwo amaphunzira nthano za m’baibulo, kupemphera, kuimba ndi kumupanga Mulungu kukhala bwenzi lawo. Mwauchichepere momwe iwo ali, iwo amamvetsetsa kuti Mulungu akutetezera ndipo iwo amaphunzira kumupempha iye thandizo kumavuto awo. Khalidwe lawo likumangika tsiku ndi tsiku. Mwachisomo cha Mulungu tingathe kuona kusinthika kowonekera mmiyoyo ya ana achichepere chifukwa cha tsogolo, ife tikufuna kuphunzitsa onse omwe zodutsamo za zinthu zawo sizikulolera ichi. Muchaka choyamba tinayamba ndi ana khumi ndi awiri 12; muchaka cha chinayi tinali ndi ana 32,31 a iwo ochokera kunja kwa mpingo. Panopa zochitika zikuchitiridwa mu zipinda 4 zomangidwa ndi likuru la union ya Romania, koma awa akuonetsera kukhala opanikizika pamene mapemphero ofuna kudzayamba ali opitilira malo athu. Mwa ichi, tikumvetsetsa kuti Mulungu akufuna ife kupitiliza komanso kukudza ntchito yodabwitsayi ndipo chotero ana ambiri abwere mukulumikizana nafe ndi mabanja awo ngati mkotheka. Chotero, mu 2021, gawo la malo linagulidwa kunja kwa mzinda ndipo tinapedza zilolezo zofunikira kuti tiyambe ntchito yakumanga. Tsopano madziko aikidwa kale. Tikuthokoza kwambiri kwa Mulungu pokhuza, mitima yaanthu ambiri mwa inu omwe akuthandiza ntchitoyi kufikira mulingo umenewo ndi inu nonse omwe mudzachite chomwechi mwaufulu moolowa manja tsopano. Ndimphanso zanu, mudzawapatsa ana omwe sakumziwa Mulungu mwayi obwera chifupi kwa iye ndikulandira maphunziro a chikhristu. Tikupempha kufuna kwabwino kwanu ndipo tasimikizika kuti inu simudzakhala chimodzimodzi, koma mudzatithandiza ife kubweretsa ntchito imeneyi ku chipambano chomalizitsa ndikutiikiza ife mmapempheronso.
Abale ndi Alongo anu kuchokera ku Union ya Romania