Loyamba
, Marichi 23
1. MIYOYO YANJALA
a. Kupatula ophunzira, kodi ndi ndani enanso amene anasagana naye Yesu pamene iye amaoloka nyanja ya Galileya isanafike paskha? Yohane 6:1, 2.
“Khristu anapita kumalo achinsinsi kukapuma ndi ophunzira ake, koma nthawi yopuma yabata yosowayi inasokonezedwa. Mwansangansanga ophunzira anaganiza kuti iwo apita kukapuma kumalo amene iwo sangasokonezedwe; koma khamu la anthu mwansanga nsanga pamene linayamba kusowa Mphunzitsi wa umulungu, iwo anafunsana, `Kodi ali kuti iye?’ ena mwa iwo anaona komwe Khristu ndi ophunzira ake analowela. Ambiri anayenda pa mtunda kuti akakumane nawo, pamene ena anatsatira ndi mabwato awo kudutsa pa Nyanja. Paskha anali pafupi kuti achitike, ndipo, kuchokera kutali ndi pafupi, magulu magulu a anthu apaulendo opita ku Yerusalemu anasonkhana kuti aone Yesu. Amachulukira chulukira kufikira anasonkhana amuna pafupifupi zikwi zisanu osawerenga ana ndi azimayi. Yesu asanafike pa gombe, khamu linali litasonkhana kale likumuyembekezera iye koma iye anafika mwakachetechete iwo osazindikira, ndipo anakhala kanthawi kochepa ndiophunzira ake ali paokha.” – The Desire of Ages, p. 364.
b. Fotokozani khalidwe la uzimu la anthu omwe anasonkhana pamenepa. Marko 6:34.
Lachiwiri
, Marichi 24
2. KUSAMALIRA ZOSOWA ZATHU
a. Kodi ndi chiyani chimene khristu mwachifundo anachizindikira kuti anthu akuchisowa-nanga ndi motani mmene iye anagwiritsira ntchito mwayi umenewu kuti ayese chikhulupiliro cha ophunzira wake Filipo? Yohane 6:3-6.
“Kuchokera pa phiri [Yesu] anayang’ana pansi pa khamu la anthu limene limayendayenda, ndipo mtima wake unatakasidwa ndi chifundo. Osokonezedwa monga momwe anariri, ndi wolandidwa kupuma kwake, Iye sanakwiye. Iye anaona chosowa chofunikira chachikulu chosoweka kulowelerapo kwake pamene amayang’ana anthu akubwera ndi kumabwerabe. Iye anakhuzika ndi chifundo ndi iwo chifukwa anali ngati nkhosa zopanda m’busa. Posiya malo ake opumulira, iye anapeza malo oyenera amene iye angathe kuwatumikira iwo. Iwo sanalandire thandizo lililonse kuchokera kwa Ansembe ndi atsogoleri; koma madzi amachiritso a Moyo amayenda kuchokera mwa Khristu pamene iye amaphunzitsa khamu njira ya chipulumutso…
“Tsikuli linaoneka kwa iwo monga kumwamba padziko lapansi, ndipo iwo samazindikira konse za kutalika kwa nthawi imene iwo anakhala osadya kanthu.
“Mapeto ake tsiku linafika madzulo. Ndipo dzuwa linali kulowa kumadzulo, komabe anthu anakhalabe pamalopo. Yesu anatumikira tsiku lonse popanda kudya kapena kupumula. Nkhope yake imaoneka yotopa komanso anali ndi njala, ndipo ophunzira anamupempha iye kuti aleke kutumikira kwake. Koma iye sakanakhonza kuzipatula yekha kuchoka ku khamu limene limazipanikiza kwa iye…
“Iye amene anaphunzitsa anthu njira imene angapezere mtendere ndi chimwemwe anali wolingalira zedi za zosowa zawo za kuthupi monganso zosowa zawo za uzimu. Anthu anali otopa ndi olema ndi kukomoka. Panali azimayi amene anali ndi makanda mmanja mwawo komanso ana achichepere amene amazendewera kumasiketi awo. Ambiri anali ataimilira kwa maola ambiri…
“Ambiri anali ochokera kutali, ndipo anali asanadye kanthu kalikonse kuyambira mmamawa. Kumizinda ndi midzi yozungulira iwo akanatha kukagula zokudya….Koma Yesu anati, `Apatseni kudya ndiinu’ ndipo kenako, potembenukira kwa Filipo, iye anamufunsa iye, ‘kodi tidzagula kuti mikate kuti adye awa?’ Koma ananena ichi kuti ayese chikhulupiliro cha ophunzira ameneyu.” – The Desire of Ages,pp. 364, 365.
b. Kodi yankho la Filipo linali lotani? Yohane 6:7.
“Filipo anayang’ana pa khamu lalikulu lomwe linali pamenepa, ndipo analingalira momwe chinalili chosatheka kuwapatsa iwo chakudya chokwanira kukhutitsa njala ya khamu lotere. Iye anayankha kuti mikate yokwana malupiya atheka mazana awiri siili yokwanira kugawira iwo ngakhale kuwagawanitsa pang’onopang’ono, kotero kuti aliyense athe kukhala ndi kochepa.” – Ibid.
Lachitatu
, Marichi 25
3. CHINACHILICHONSE CHOMWE CHINALIPO
a. Kodi ndi chidziwitso chanji chimene Andreya anachipereka kwa Yesu- nanga kodi ndi chiyani chimene Ambuye anawalamulira ophunzira kuti achite? Yohane 6:8-10.
“Yesu anafunsa kuti kodi ndi chakudya chochuluka bwanji chimene chingapedzeke pagulu pamenepo. Pali nyamata pano, ananenanso Andreya, `Amene ali nayo mikate isanu yaberere, ndi tinsomba tiwiri, koma nanga izi zifikira bwanji ambiri otere?’ Yesu anapempha kuti zimenezi zibwerestedwe kwa iye. Kenako anawauza ophunzira kuti awakhalitse anthu pansi pa udzu mmagulu amakumi asanu kapena zana, kuti pakhale dongosolo, ndi kuti onse athe kuchita umboni kuchomwe iye amafuna kuti achichite.” – The Desire of Ages, p. 365.
b. Fotokozani ndandanda wa zimene Khristu anachita kuti achulukitse zakudya-nanga kodi ndi maphunziro anji amene ife tingathe kuphunzira kuchokera ku chimenechi? Mateyu 14:19; Marko 6:37-41; Yohane 6:11.
“Yesu sanafune kuti akope anthu kupita kwa iye kudzera mukuwapatsa zofuna zawo za manyado. Kukhamu lalikulu limenelija, lotopa ndi lanjala chifukwa cha tsiku lalitali, lodzala ndi zosangalasa chakudya chophweka chinali chitsimikizo cha mphanvu zake komanso chisamaliro chake cha chifundo kwa iwo mu zinthu zophweka zammoyo. Mpulumutsi sanalonjeze osatira ake zinthu zamanyado za dziko lapansi; akhoza kukhala anthu osauka; koma mawu ake alonjeza kuti zosowa zawo zizapatsidwa, ndiponso iye analonjeza icho chimene chili chabwino kwambiri kuposa chuma cha dziko lapansi- chitonthonzo cha kupezeka kwake kwa iye mwini kwa iwo.” – The Ministry of Healing, pp.47,48.
“Mu chozizwitsa ichi Khristu analandira kuchokera kwa Atate; iye napereka kwa ophunzira ake nagawira kwa anthu, ndipo anthu anagawana wina ndi mzake. Chotero onse amene alumikizidwa kwa Khristu azalandira kuchokera kwa iye mkate wa Moyo, naugawira iwo kwa ena. Ophunzira ake ndiye njira imene inakhazikitsidwa yolumikizira Khristu ndi anthu.” – Ibid., p.49.
c. Ndi za phunziro lanji la utumiki woona limene ife tikukumbutsidwa pamenepa? Yesaya 16:6.
“Ophunzira anabweretsa kwa Yesu zonse zimene iwo anali nazo; koma iye sanawaitane kuti akhale pansi nadye. Iye anawalamulira iwo kuti apereke chakudyacho kwa anthu. Chakudya chinachulukirachulukira mmanja mwake ndi mmanja mwa ophunzira, pomatenga kuchokera kwa Khristu, sizimatha. Nkhokwe yaing’onoyi inali yokwanira kwa onse. Pamene khamu lonse linamaliza kudya, ophunzira anadya ndi Khristu, chakudya chamtengo wapatali, choperekedwa kuchokera kumwamba.” – Ibid.
Lachinayi
, Marichi 26
4. UKOMA WA KUGAWANA
a. Kodi tikuyenera kuphunzirapo chiyani kuchokera ku langizo lalikulu limene Yesu analipereka atatha kudyetsa khamu? Yohane 6:12, 13.
“Pamene mitanga ya zakudya zotsara inatoleledwa, anthu analingalira za abwenzi awo amene anali kunyumba. Iwo amafunanso anzawo agawane nawo mkate umene Khristu anaudalitsa. Zomwe zinali mmitanga imeneyi zinagawidwa pakati pa khamu lomwe linali ndi khumbo loti ligawiridwe, ndipo iwo anapita nazo kumadera onse ozungulira.”-The Desire of Ages, p. 368.
“Yesu analamulira ophunzira ake ‘sonkhanitsani makombo kuti kasatayike kanthu.’ Yohane 6:12. Mawu awa ali ndi tanthauzo lalikulu kuposa kungoika zakudya mumitanga. Phunziroli ndi lambali ziwiri. Pasamakhale kutayika kwa chilichonse. Tisamalore kutaya mwayi ulionse. Tisamanyozere china chilichonse chimene chingathe kupindulira munthu –lolani kuti kena kalikonse kasonkhanitsidwe kamene kangathandize kupeputsa zosowa za anthu anjala a kudziko lapansi. Ndi kusamalitsa komweku tikuyenera kumayamikira mkate ochokera kumwamba kuti ukhutitse zosowa za moyo. Kudzera muliwu linalililonse la Mulungu tikuyenera kukhala. Chinachilichonse chimene Mulungu anayankhula mmawu ake sichikuyenera kutayika. Ngakhale liwu limodzi limene limakhuza chipulumutso chathu chamuyaya sitikuyenera kulinyozera, liwu limodzi silikuyenera kugwa pansi osasamalidwa.” – The Ministry of Healing, p. 48
b. Ngakhale zitamaoneka ngati zosakukomera kapena zosatheka, kodi ndi makhalidwe anji a chikhristu amene ife tikulamuliridwa kuti tiwakudze? Yesaya 58:6-8; 1 Petro 4:9.
“Mu chazizizi chilichonse tikuyenera ife kumapempha thandizo kuchokera kwa iye amene ali ndi zinthu zamuyaya pamaso pake…
“Pamene ife tikuona zosowa za osauka, osazindikira, osauka,kodi ndi kangati kamene mitima yathu imakhumudwa, timafunsa kuti, kodi zingathandize chiyani mphanvu zathu zofooka ndi chuma chathu chochepa kuti zithandize zosowa zazikulu zotere? Kodi sitikuyenera kudikira munthu wina wake amene ali ndi kuthekera kwakukulu kuti atsogolere ntchito kapena bungwe lina lake lithandize izi? Khristu akuti; `Apatseni iwo kuti adye’; gwiritsani chuma,nthawi ndi kuthekera, zimene muli nazo. Bweresani mikate yanu kwa Yesu.
“Ngakhale kuti zomwe mulinazo sizingathe kukhala zokwanira kudyetsa zikwizikwi, zikhoza kukwanira kudyetsa mmodzi. Mumanja a khristu zimenezo zikhoza kudyetsa ambiri. Monga ophunzira, perekani zimene mulinazo; Khristu azachulukitsa mphatso imeneyo. Iye azabwezera mphoto kukudalira koona kophweka mwa iye. Icho chimene chimaoneka chochepa zedi chizakhala phwando lalikulu.” – Ibid., pp. 49, 50.
Lachisanu
, Marichi 27.
5. MLENGI WATHU NDI WOTITHANDIZA IFE
a. Kodi ndi makhalidwe odabwitsa anji a Mulungu amene ife sitikuyenera kumawaiwala? Masalmo37:25, 26; Afilipi 4:19.
“Ndi chisomo cha Mulungu mu zinthu zazing’ono chimene chimazipanga izo kukhala zokwanira. Dzanja la Mulungu litha kuzichulukitsa izo kukhala mazanamazana. Kuchokera ku zomwe alinazo. Iye akhoza kuyala gome Muchipululu. Kudzera mu kukhuza kwa dzanja lake iye akhoza kuchulukitsa zinthu zochepa ndi kudzipanga izo kukhala zokwanira kwaonse. Ndi mphanvu zake zimene zinachulukitsa mikate ndi ufa mmanja a ana a aneneri…
“Pamene Yesu analamurira ophunzira ake kuti apatse khamu zoti adye, iwo anayankha kuti, `Ife tilibe mikate koma isanu yokha ndi nsomba ziwiri, kapena timuke ndikukagulira anthu awa onse zakudya.’ Luka 9:13. Kodi zinthu zimenezi zinali chiyani pa gulu lalikulukulu?
“Phunziro limeneli ndi la ana a Mulungu mu m’bado ulionse. Pamene Ambuye wapereka ntchito kuti igwiridwe, musalore munthu wina aliyense ayime ndi kumafunsa za mzeru imene ili mukulamula, kapena zotsatira zomwe zingathe kukhalapo za kuyesesa kwawo kuti amvere. Zinthu mmanja a anthu zikhoza kuoneka zochepa kuti sizingakwanire kukwaniritsa chosowacho; koma mmanja mwa Ambuye zizaoneka kuti ndi zambiri koposa….
“Kukula kwa kumvesesa kwa ubale wa Mulungu kwa onse amene iye anawagula ndi mphatso ya mwana wake, chikhulupiriro chachikulu mukupita patsogolo kwa ntchito yake pa dziko lapansi- ichi ndi chosowa chachikulu cha mpingo lero. Musalore wina aliyense azitaya nthawi mukumafotokoza za kuchepa kwa chuma chawo chomwe chikuoneka. Zooneka zikhoza kukhala zosapasa chiyembekezo, koma mphanvu ndi chidaliro mwa Mulungu zizabweretsa chuma, Mphatso imene yabweretsedwa kwa iye ndi chiyamiko ndi pemphero lopempherera mdalitso lake, Iye azaionjezera monga momwe iye anaonjezerera zokudya zimene zinaperekedwa kwa ana a aneneri ndi khamu lotopa.” – Prophets and Kings, pp. 241-243.
Lachisanu ndi chimodzi
, Marichi 28
6. MAFUNSO OBWEREZA PAWEKHA
1. Fotokozani malingaliro aanthu mmene amamvesera mawu a Khristu.
2. kodi ndi motani mmene ambuye anaperekera thandizo ku zosowa zawo zakuthupi?
3. kodi ndi chiyani chimene ife tikuphunzirapo kuchokera ku mmene Khristu anasungira khamu mwadongosolo?
4. Kodi ndikuyenera kukumbukira chiyani ndikamakakamizika mumtima kuti, “Apatseni iwo kuti adye.”?
5. Chulani nthawi zimene chisamaliro cha Mulungu kwa inu mwapaderadera chinaonekera.