Loyamba
, Feb 16
1. YESU MU SUKARI
a. Paulendo wake wopita ku Galileya, kodi ndi kuti komwe Yesu ndi ophunzira ake anaima? Yohane 4:6.
“Pamene Yesu anakhala pambali pa chitsime, Iye anafooka ndi njala komanso ludzu, ndipo tsopano dzuwa lausana linaombela pa iye. Ludzu lake linakulirakulira poganizira zakudzidzirila, madzi otsitsimutsa omwe anayandikira, komabe osafikilika kwa iye chifukwa iye analibe chingwe ngakhale chitin chotungila, ndipo chitsime chinali chokuya. Gawo la Umunthu linali pa iye, ndipo iye anadikirira kuti wina abwere kudzatunga.” – The Desire of Ages, p. 183.
b. Kodi ndindani yemwe anabwera kuchitsime ndipo ndikukoma mtima kwanji komwe Yesu anakupempha kwa iye- ndipo ndi chiyani chimene tikuyenera kuphunzira ku zimenezi? Yohane 4:7.
“Udani pakati pa Ayuda ndi a Samariya unapewetsa Mzimayi kuti apereke chifundo kwa Yesu: Koma mpulumutsi anafunafuna kupeza mfungulo kumtima uwu, Ndipo ndichikondi chobadwa nacho cha umulungu, Iye anapempha kukondera osati kupatsidwa. Kupereka kwa chikondi kukanatha kukanidwa ; koma chidaliro kudzutsa chidaliro.Mfumu yakumwamba inadza ku moyo osowa abwenziwu, kupempha utumiki ku dzanja lake. Iye amene anapanga Nyanja, amene amalamulira madzi ozamitsitsa, amene anatsegula akasupe ndi modutsa mwake adziko lapansi, anapumula kukutopa kwake pachitsime cha Yakobo, ndipo anadalira pa chikondi cha mlendo kumphatso ngakhale ya madzi akumwamba.” – Ibid. p.184.
Lachiwiri
, Feb 17
2. MADZI A OSIYANA AMTUNDU WINA
a. Kodi Yesu anaitanitsa bwanji chidwi cha mzimayi kumphatso ya chipulumutso? Yohane 4:10.
“Madzi omwe Khristu amatanthaudza anali bvumbulutso la chisomo chake mmawu ake; mzimu wake, chiphunzitso chake, zili ngati kasupe okwaniritsa kumoyo wina ulionse. Kasupe wina aliyense kumene iwo azapite azatsimikizira kukhala osakhutiritsa. Koma mawu achoonadi ali odzidzilira ngati misinje, anathandauridwa ngati madzi aku lebano, omwe nthawi zonse amakwaniritsa. Mwa Khristu ndimodzadza ndi chimwemwe kunthawi zanthawi.” – Testimonies to Ministers, p. 390.
b. Kodi mzimayi anayankha chiyani ku chopereka cha Khristu? Yohane 4:11, 17.
“Kumvetsetsa kwa mzimayi sanadziwe tanthaudzo la Khristu; Iye amayerekedza kuti iye amanena za chitsime chomwe chinalipo pamaso pawo.” – The Spirit of Prophecy, Vol. 2, pp. 140, 141.
c. Kodi Yesu anasiyanitsa bwanji pakati pa mtundu umodzi wa madzi ndi wina ndipo ndimotani, momwe uthengawu ukuyenera kutidalitsira ifenso? Yohane 4:14, 14, Chibvumbulutso 22:17.
“Tikuyenera kukulitsa chikondi ndi chiyamiko, tikuyenera kuyang’ana kwa Yesu ndikukhala otsinthika kufanana ndi iye. Mapeto a izi adzakhala kulimbika koonjezeredwa, chiyembekezo, kupilira ndi kulimba mtima. Tidzamwa madzi amoyo omwe Khristu amanena kwa mzimayi wakusamaria. Iye anati; ‘ukadadziwa mphatso ya Mulungu ndi iye amene alikunena ndi iwe, undipatse ine ndimwe, ukadapempha iye, ndipo akadakupatsa madzi amoyo….Yense wakumwako madzi amene ine ndidzampatsa sadzamva ludzu nthawi zonse; koma madzi amene ine ndidzampatsa adzakhala mwa iye kasupe wa madzi otumphukira ku moyo wosatha.’ Madzi awa akuimirira moyo wa Khristu, ndipo moyo ulionse ukuyenera kukhala nawo awa kudzera mu kubwera kukulumikizana kwa moyo ndi Mulungu. Kenako chidaliro, chodalitsika, chodzichepetsa choyamika zidzakhala mfundo zokhazikika mmoyo. Mantha osakhulupilira adzachotsedwa ndipo padzakhala chikhulupiriro cha moyo. Tidzalingalira khalidwe la iye amene anatikonda ife koyambilira.” – Testimonies to Ministers, p. 226.
Lachitatu
, Feb 18
3. MADZI AMOYO
a. Kodi mzimayi wakusamariya anaonetsa bwanji kuti iye samamvetsetsabe mawu a Khristu? Yohane 4:15.
“Chisomo chakumwamba chomwe ndi iye yekha yemwe angachipereke, chilingati madzi amoyo, kuyeretsa, kutsitsimutsa ndi kulimbikitsa moyo.
“Yesu sanapereke lingaliro lakuti kumwa kamodzi kokha kwa madzi amoyo ndikokwaniritsa wolandira. Iye amene walawa chikondi cha Khristu adzafunafunabe choonjezera; koma sadzafuna chinthu china. Kulemera, Ulemu, ndizokondweretsa za dziko sizizamukopa iye. Kulira kokhazikika kwa mtima wake ndikokuti, zina za iye. Ndipo iye amene wabvumbulutsa ku moyo kufunikira kwake akudikirira kukhutitsa njala ndi ludzu lake. Katundu ndi zodalira zonse za munthu zidzalephera. Mathamanda onse adzaumitsidwa, dzithapwi zonse zidzauma; koma mpulumutsi wathu ndi kasupe wosaphwa. Tingathekumwa, ndikumwanso, ndipo tidzapeza nthawi zonse madzi atsopano. Iye amene khristu akhala mwa iye ali ndimkati mwake kasupe wamadalitso- chitsime cha ‘madzi a moyo chotumphukira kumoyo wosatha.’ Kuchokera ku kasupe ameneyu iye atha kutunga mphanvu ndi chisomo chokwaniritsa ku zosowa zake zonse.” – The Desire of Ages, p. 187.
b. Monga mzimayi wakusamariya ndi apaulendo mchipululu mu Exsodo, kodi ndimotani momwe ife kawirikawiri timalephera kuzindikira chisomo chodabwitsa chomwe chimayenda kuchokera mwa Khristu? Masalmo 78:15, 16, 20 (mbali yoyamba); 114:7, 8.
“Mose anamenya tanthwe, koma anali mwana wa Mulungu yemwe, anaphimbika mumtambo,amene anaima pambali pa Mose, ndikupangitsa madzi opatsa moyo kuti ayende. Osati Mose ndi akuluakulu okha, koma msonkhano wonse womwe unaima patali, unaona ulemelero wa Ambuye; koma zikadakhala kuti mtambo wachotsedwa, iwo akanaphedwa ndi kuwala kowopsa kwa Iye amene anali mkatimo.” – Patriarchs and prophets, p. 298.
“Chisomo cha Khristu chopezeka mmawu ake nthawi zonse chimayankhulabe ku moyo. Kumuimilira iye monga chitsime cha madzi amoyo kutsitsimutsa moyo wa ludzu. Ndimwayi wathu kukhala ndi mpulumutsi wamoyo, wopirira. Iye ndi gwero la mphanvu za uzimu zozalidwa mkati mwathu, ndipo chikoka chake chidzasefukira ndi kuyenda kudzera mmawu ndi mmachitachita, kutsitsimutsa onse okhala mumpweya wachikoka chathu, kubereka mwa iwo zikhumbokhumbo ndi kufunitsitsa kwa chilimbikitso komanso ungwiro, kwa chiyero komanso mtendere, komanso kwa chimwemwe chomwe sichimabweretsa chisoni pamodzi ndi icho. Ichi ndichotsatira cha mpulumutsi wokhala mkati.” – Tetsimonies to Ministers, p. 390.
Lachinayi
, Feb 19
4. YESU AYAMBA KUBVUMBULUTSA CHOMWE ALI
a. Kodi ndi nkhani yanji yatsopano yomwe Yesu anaibweretsa mukuyankhulana kwake ndi Mzimayi wakusamaliya –ndipo ndimotani momwe iye anayankhira? Yohane 4:16, 17 (Mbali yoyamba).
“Yesu tsopano mwachangu anatembenuza zokambirana. Moyo uwu usanalandire mphatso yomwe iye amafuna kuipereka, iye anayenera kubweretsedwa kukuzindikira tchimo lake ndi mpulumutsi wake. Iye anati kwa iye, ‘pita kamuitane mwamuna wako, nudze kuno.’ Iye anayankha, ndilibe mwamuna’; Chotero iye anayembekezera kupewa mafunso onse olozera mu chimenecho.” – The Desire of Ages, p. 187.
b. Kodi Yesu anayamikira motani yankho lake- ndipo ichi chikutikumbutsa ife chiyani zokhuza zonse zomwe iye akudziwa zokhuza wina aliyense wa ife? Yohane 4:17 (mbali yotsiliza) 18; Masalimo139:7, 8, 11, 12.
“Ukulu wa Mulungu uli kwa ife wovuta kuumvetsetsa. ‘ Mpando wa chifumu wa Ambuye uli m’mwamba(masalmo11:4); Komabe kuzera mwa Mzimu wake iye amapezeka paliponse. Iye ali ndichiziwitso chosabisika cha, ndi chidwi chachikulu, cha ntchito zonse za dzanja lake.”-Education, p. 132.
“Angelo akumwamba amafufuza ntchito yomwe yaikidwa mmanja aanthu, ndipo pamene pali kuchoka kumfundo zachoonadi, ‘kuperewera’ kumalembedwa mu mbiri.” – Child Guidance, p. 155.
“Lamulo la Mulungu limafikira zokumva muntima ndi zolingalira, komanso mmachitachita akunja limabvumbulutsa zinsinsi za mumtima, kuonetsera kuwala pazinthu zisanakwaniridwe mumdima. Mulungu amadziwa lingaliro lililonse cholinga chilichonse, dongosolo lililonse, ndi ganizo lililonse. Mabuku a kumwamba amasunga machimo omwe akanachitidwa pakanakhala kuti pali mwayi. Mulungu adzabweretsa ntchito iliyonse muchiweruzo, ndi zinthu zonse zachinsinsi. Mwalamulo lake iye amayeza khalidwe la munthu aliyense. Monga wojambula waluso amasamutsa kuika pa nsalu yokhutala maonekedwe ankhope chotero maonekedwe a khalidwe la munthu wina aliyense amasamusilidwa kumabuku akumwamba. Mulungu ali ndi chithunzi changwiro cha khalidwe la munthu wina aliyense ndipo chithunzi chimenechi iye amachifanizira ndi malamulo ake. Iye amabvumbulutsa kwa munthu zolakwitsa zomwe zadetsa moyo, ndikuitatsa pa iye kulapa ndi kubwerera kuchoka kuuchimo.” – The SDA Bible Commentary [E.G White Comments], Vol. 5, p. 1085.
Lachisanu
, Feb 20
5. YESU WAZIBVUMBULUTSA YEKHA MONGA MPULUMUTSI
a. Kodi ndi chiyani chimene mzimayi wa pachitsime uja mapeto ake anachizindikira zokhuza Yesu? Yohane 4:19. Kodi kuzindikiraku kunali kokwanira?
“Omvetsera ananjenjemera. Zanja lodabwitsa linabvundukula masamba a mbiri ya moyo wake, kubweretsa poonekera icho chimene iye anayembekezera kuchisunga mobisa mpaka kalekale. Kodi Iye anali ndani kuti angathe kuwerenga zinsinsi za moyo wake? Tsopano munabwera mmalingaliro ake malingaliro a umuyaya, a chiweruzo cha mtsogolo, pamene zonse zomwe zikubisidwa tsopano zidzabvumbulutsidwa mukuunika kwake. Mukuwala kwake, chikumbumtima chinazutsidwa.
“Iye sanakane kanthu; koma iye anayesesa kupewa zonenapo kanthu za nkhaniyi yosalandiridwa. Ndikulemekeza kwakukulu iye anati, ‘Abuye ndizindikira kuti muli mneneri.’ Tsopano, kuyembekezera kukhazikitsa chete kususika, iye anatembenukira kumfundo ya mkangano wachipembezo. Ngati uyu anali mneneri motsimikidzika iye akanapereka kwa iye malangizo okhuza nkhani zimenezi zomwe zinali mkangano wa nthawi yaitali.” – The Desire of Ages, pp. 187-188.
b. Pamene mzimayi anaonetsa chikhulupiriro mukubwera kwa Mesiya, kodi Yesu anayankhula chiyani kwa iye? Yohane 4:25, 26.
“Kuitanira kwa uthenga wabwino sikukuyenera kuchepetsedwa pansi, ndikuperekedwa kwa osankhika ochepa okha, omwe ife tikuganiza kuti zizatipatsa ife ulemu ngati iwo ataulandira iwo. Uthenga ukuyenera kuperekedwa kwa onse. Kulikonse komwe mitima yatseguka kulandira choonadi, Khristu ali wokonzeka kuulangiza iwo. Iye amabvumbulutsa kwa iwo Atate, ndi kupembedza kolandilika kwa iye amene amawerenga mtima. Chifukwa cha izi iye amagwiritsa ntchito mafanizo kwa iwo, monga kwa mzimayi wa kuchitsime, Iye akuti, ‘Ine wakulankhula nawe ndine amene.” – The Desire of Ages, pp. 194.
Lachisanu ndi chimodzi
, Feb 21
6. MAFUNSO OBWEREZA PAWEKHA
1. Kodi ndichifwa chiyani Yesu sanachite konse chozwizwa kudzichitira iye mwini?
2. Kodi Yesu anagwiritsa ntchito thandizo lanji kumtsogolera mzimayi wakuSamariya ku uthenga wabwino?
3. Kodi Ambuye akulankhula chiyani zokhuza madzi amoyo?
4. Ndichifukwa chiyani Khristu anatchula moyo weniweni wa Mzimayi wa ku Samariya?
5. Tchulani lonjezo lophatikizana ndi kubwera kwa Mesiya.