Back to top

Sabbath Bible Lessons

Maphunziro AmBaibulo Apa Sabata

 <<    >> 
PHUNZIRO 3 SABATA, JANUWALE 18, 2025

UKWATI KU KANA

VESI LOLOWEZA: “Chilichonse chimene anena kwa inu, chitani” (Yohane 2:5, gawo lomaliza).

“Yesu anayamba ntchito yokonzanso poyandikirana mwa chifundo kwambiri ndi umunthu.”— The Desire of Ages, p. 150.

Zowelenga Zoonjezera:   The Desire of Ages, pp. 144-153
  Messages to Young People, pp. 403-418 

Loyamba , Jan 12

1. CHIYAMBI CHA UTUMIKI WA KHRISTU

a. Kodi Yesu anayambira kuti utumiki wake padziko lapansi? Yohane 2:1, 2.

“Yesu sanayambe utumiki Wake ndi ntchito ina yaikulu pamaso pa a Sanhendrini ku Yerusalemu. Pamsonkhano wa pakhomo m’mudzi waung’ono wa ku Galileya mphamvu Yake inaperekedwa kuonjezera chisangalalo cha phwando laukwati. Kotero Iye anasonyeza chifundo chake ndi anthu, ndi chikhumbo chake chotumikira ku chisangalalo chawo. M'chipululu cha mayesero Iye mwini adamwa chikho cha tsoka. Iye anabwera kudzapatsa anthu chikho cha m’dalitso, mwa dalitso Lake kuti ayeretse ubale wa moyo wa umunthu.”— The Desire of Ages, p. 144.

b. Kodi chinachitika n'chiyani phwando laukwati lisanathe? Yohane 2:3.

“[Mariya] ankafunitsitsa kuti [Yesu] atsimikizire kwa anthu kuti Iye analidi Wolemekezeka wa Mulungu. Iye amkayembekeza kuti pakhoza kukhala mwayi kuti Iye achite chozizwa pamaso pawo.

“Unali mwambo wa nthawiyo kuti mapwando aukwati apitirire masiku angapo.Pa nthawiyi, phwandolo lisanathe kunapezeka kuti vinyo watha. Zimenezi zinachititsa kuti anthu asokonezeke maganizo komanso kuti anong’oneze bondo. Zinali zachilendo kuti vinyo athe pazochitika za zikondwerero, ndipo kusapezeka kwake kunkaoneka ngati kuperewera kwa kuchereza alendo.”— Ibid., pp. 145, 146.


Lachiwiri , Jan 13

2. KHRISTU NDI AMAYI AKE

a. Kodi amayi ake a Khristu ananena chiyani, ndipo yankho Lake linali lotani? Yohane 2:3, 4.

“[Kuchokera pa Yohane 2:4] Yankho limeneli, lodzidzimutsa monga momwetikuwonera ife, silinasonyeze kunyoza kapena mwano. Mayankhulidwe a Mpulumutsi kwa amayi Ake anali ogwirizana ndi mwambo wakumeneko. Kayankhidwe kotere kankagwiritsidwa ntchito kwa anthu amene amafunika kuchitiridwa ulemu. Mchitidwe uliwonse wa moyo wapadziko lapansi wa Khristu unali wogwirizana ndi lamulo limene Iye mwini anapereka, 'Lemekeza atate wako ndi amako.' Eksodo 20:12. Pamtanda, m’macitidwe ake otsiliza a cifundo kwa amayi ake, Yesu analankhulanso nawo mofanana, pamene amawapereka ku chisamaliro cha wophunzira wake wokondedwa koposa. Ponse pawiri pa phwando laukwati ndi pamtanda, chikondi chosonyezedwa mu kamvekedwe ka mau ndi mmayang’anidwe ndi mmachitidwe zinatanthauzira mawu Ake.”— The Desire of Ages, p. 146.

b. Kodi amayi a Khristu ananena chiyani kwa anthu amene anali kutumikira—ndipo kodi mawu amenewa akugwiranso ntchito motanikwa ife lerolino? Yohane 2:5.

“[Otsatira a Khristu] ayenera kukhala amphamvu mowonjezereka m’kulengeza choonadi pamene akuyandikira ku ungwiro wa chikhulupiriro ndi chikondi cha pa abale awo. Mulungu wapereka chithandizo chaumulungu pazochitika zonse zadzidzidzi zomwe chithandizo cha umunthu sichingathe kuyerekezedwa. Iye amatipatsa Mzimu Woyera kutithandiza mu vuto lililonse, kulimbitsa chiyembekezo chathu ndi chitsimikizo, kuunikira malingaliro athu ndi kuyeretsa mitima yathu. Iye akutanthauza kuti zipangizo zokwanira zidzaperekedwa kuti igwiridwe ntchito ya mapulani ake. Ndikukuuzani kuti mufunefune uphungu kwa Mulungu. Mufunefuneni ndi mtima wonse, ndipo ‘chilichonse chimene anena kwa inu, chitani. Yohane 2:5.”— Testimonies for the Church, vol. 6, pp. 414, 415.

c. Kodi Yesu anauza wotumikira pa ukwatiwo kuti achite chiyani? Yohane 2:6-8.

“Pafupi ndi khomo panali mitsuko yamadzi isanu ndi umodzi ikuluikulu yamyala, ndipo Yesu anawuza atumiki aja kuti aidzaze ndi madzi. Izo zinachitidwa. Ndiye pamene vinyo anafunidwa kuti agwiritsidwe ntchito nthawi yomweyo, Iye anati, 'Tengani tsopano, ndipo mupite nawo kwa kazembe wa phwando.' M’malo mwa madzi amene zotengerazo zinadzazidwa, munatuluka vinyo.”— The Desire of Ages, p. 148.


Lachitatu , Jan 14

3. VINYO WA KHRISTU

a. Pamene vinyo anaperekedwa kwa anthu, kodi kazembe wa phwandolo analankhula chiyani? Yohane 2:9, 10.

“Kazembe wa phwando komanso oitanidwawo sankadziwa kuti vinyo watha. Atalawa yemweotumikirawo anabweretsa, Kazembe wa mphwandoyo adazindikira kutivinyoyo anali opambana kwambiri kuposaamene iye adamwapo kale, ndipo ndiwosiyana kwambiri ndi yemwe analandira kumayambiriro kwa phwando.”— The Desire of Ages, p. 148.

b. Kodi ndi mtundu wanji wa vinyo amene Khristu anapeleka? Yesaya 65:8.

“Vinyo amene Khristu anapereka paphwando, ndi amene anapereka kwa ophunzira monga chizindikiro cha mwazi wake, anali madzi ofinyidwa ku mphesa. Mneneri Yesaya akunena za zimenezi pamene akunena za vinyo watsopano ‘m’tsango,’ nati, ‘Musamuwononge; pakuti m’menemo muli dalitso. Yesaya 65:8....

“Vinyo wosasasa amene Iye anapereka kwa oitanidwa paukwati anali chakumwa chokoma ndi chotsitsimusa. Zotsatira zake zinali kupangitsa kukoma kwake kukhala kogwirizana ndi chilakolako chachakudya chopatsa thanzi.”—Ibid., p. 149.

c. Kodi Malemba amati chiyani za vinyo wosasa? Miyambo 20:1; 23:29-35.

“Anali Khristu amene m’Chipangano Chakale anapereka chenjezo kwa Aisrayeli, ‘Vinyo achita chiphwete, chakumwa chaukali chisokosa; wosochera nazo alibe nzeru.’ Miyambo 20:1. Ndipo Iye mwini Sadapereke chakumwa choterocho. Satana amayesa anthu kuti azigwiritsa nchito zinthu zomwe zingasokoneze kulingalira ndi kufooketsa malingaliro auzimu, koma Khristu amatiphunzitsa kubweretsa chikhalidwe chonse pansi pa kumvera. Moyo wake wonse unali chitsanzo cha kudzikana yekha. Kuti athetse mphamvu ya chilakolako cha chakudya, Iye anavutika m’malo mwathu chiyeso choopsa kwambiri chimene anthu angapirire. Anali Khristu amene analamula kuti Yohane M’batizi asamwe vinyo kapena chakumwa choledzeretsa. Iyenso ndi Yemwe adapereka lamulo lofanana ndi lomweli kwa mkazi wa Manowa. Ndipo anatemberera munthu amene adzaika botolo ku milomo ya mnansi wake. Khristu sanatsutsane ndi chiphunzitso Chake.”— Ibid.


Lachinayi , Jan 15

4. CHITSANZO CHA KHRISTU PA ZACHISANGALALO.

a. Kodi ndi zolinga zotani zimene zinakwaniritsidwa kudzera muzinthu ziwiri kupezekapo kwa Khristu ndi chozizwitsa Chakepaphwando laukwati, ngakhale kwa ife lerolino? Yohane 2:11.

“Khristu amadziwa zinthu zonse; Iye anayang’ana kupyola mumibado kufikira ku m’nthawi yathu ino, ndipo anaona mmene zinthu zidzakhalire kumapeto kwa mbiri ya dziko. Iye anaona anthu zikwizikwi akuwonongeka chifukwa chakumwa vinyo ndi zakumwa zoledzeretsa. Pang’ono ndi pang’ono dziko lidzafika mumkhalidwe wofanana ndi umene unali m’masiku a chigumula chisanachitike. Koma kumwamba kwakweza chizindikiro chachenjezo, kuti anthu atenge chenjezo, ndi kugwirizana ndi Mulungu kuti adziteteze. Iye watipatsa zitsanzo za kudziletsa kotheratu, ndipo wapereka malangizo amene, ngati atsatiridwa, padzatulukapo kulengedwa ndi kusungidwa kwa nyonga, luso, ndi chipambano cha ana athu.”— The Signs of the Times, April 16, 1896.

b. Fotokozani mtundu wakhalidwe losisimusa umene Khristu anausonyeza mu utumiki Wake wonse. Mateyu 11:29.

“Yesu anayamba ntchito yokonzanso kudzera mukubwera chifupi mwa chifundo ndi anthu. Pamene Iye amasonyeza kulemekeza kwambiri lamulo la Mulungu, anadzudzula khalidwe lodzionetsera la Afalisi, ndipo anayesa kumasula anthu ku malamulo opanda nzeru amene anawamanga. Iye ankafuna kuphwanya zotchinga zomwe zinkalekanitsa magulu osiyanasiyana a anthu, kuti Iye akhoze kubweretsa anthu pamodzi monga ana a banja limodzi. Kupezeka kwake paphwando laukwati kunalinganizidwira kukhala sitepe lakukwaniritsa ichi.”— The Desire of Ages, p. 150.

“Yesu anadzudzula kudzikonda m’njira zonse, komabe anali ndi chikhalidwe chotha kulumikizana ndi anthu. Iye anavomereza kucherezedwa ndi magulu onse, kuyendera nyumba za olemera ndi osauka, ophunzira ndi osadzindikira, ndi kufuna kukweza maganizo awo kuchokera ku mafunso a zinthu zawamba za mmoyo kupita ku zinthu zauzimu ndi zamuyaya. Iye sanapereke chilolezo cha chitayiko, ndipo panalibe mthunzi wa makhalidwe a dziko umene unaipitsa khalidwe Lake; komabe adakondwera ndi zochitika za chisangalalo chopanda zoipa, ndipo mwa kupezeka Kwake adavomereza kusonkhanako. Ukwati wa Ayuda unali chochitika chochititsa chidwi, ndipo chimwemwe chake sichinali chosakondweretsa kwa Mwana wa munthu. Kudzera mu kupezeka pa phwando limeneli, Yesu analemekeza ukwati monga dongosolo laumulungu.”— Ibid., pp.150, 151.


Lachisanu , Jan 16

5. KUYANJANA KWA MACHEZA KWABWINO

a. Kodi tiyenera kuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Khristu chimene chimamusiyanitsa Iye mosiyana ndi atsogoleri achipembedzo amasiku Ake? Miyambo 18:24.

“Utumiki wa Khristu unali wosiyana kwambiri ndi wa akulu Achiyuda. Kulemekeza kwawo kwa chikhalidwe ndi miyambo kunawononga ufulu weniweni wa kuganiza kapena kuchitapo kanthu. Iwo anakhala ndi mantha osalekeza omaopa kudetsedwa. Kuti apewe kuyanjana ndi ‘odetsedwa,’ amadzipatula, osati kwa amitundu okha, komanso kwa anthu ambiri a mtundu wawo, osafuna kuwapindulira kapena kuwapindura kukhala abwenzi awo. Kudzera mu kulimbikira za nkhani zimenezi, iwo anachepetsa malingaliro awo ndi kufupikitsa njira ya moyo wawo. Chitsanzo chawo chinalimbikitsa kudzikuza ndi kusalolerana pakati pa magulu onse a anthu.”— The Desire of Ages, p. 150.

b. Kodi cholinga chathu chikhale chiyani m'mayanjano onse? Miyambo 11:30.

“Titha kuwonetsa chidwi zikwi chaching'onochingono m'mawu achikondi ndi mukuyang’ana kwachifundo, zomwe zidzawaliranso pa ife. Akhristu osaganizira ena amaonesera kudzera mukunyozera kwawo zaena kuti sali olumikizana ndi Khristu. Ndi zosatheka kukhala mu umodzi ndi Khristu koma kukhala opanda chifundo kwa ena ndi kuiwala za ufulu wawo.

“Tonse tiyenera kukhala mboni za Yesu. Mphamvu ya chiyanjano, yoyeretsedwa ndi chisomo cha Khristu, iyenera kukuzidwa mu kupindula miyoyo kwa Mpulumutsi. Lolani kuti dziko liziona kuti sitili otangwanika ndi chisamaliro cha ife eni mwa undekha, koma kuti Ife timakhumba ena kugawana nafe madalitso ndi mwayi. Awonetseni kuti chipembedzo chathu sichimatipangitsa kukhala opanda chifundo kapena ofuna zathu zokha. Lolani onse amene amadzinenera kuti apeza Khristu atumikire monga Iye anachitira pothandiza anthu. Sitiyenera konse kupereka ku dziko malingaliro abodza akuti Akhristu ndi anthu achisoni, osasangalala.”— The Adventist Home, p. 428.


Lachisanu ndi chimodzi , Jan 17

6. MAFUNSO OBWEREZA PAWEKHA

1. Fotokozani zipatso zauzimu zobalidwa kudzera mu chozizwitsa cha Khristu ku Kana.

2. Fotokozani ubale umene unalipo pakati pa Khristu ndi amayi Ake.

3. N’chifukwa ciani kazembe wa phwandolo anaonetsa kudabwa?

4. Kodi ndi vinyo wotani amene moyenerera amaimira mwazi wa Khristu?

5. Pamapwando, kodi tiyenera kukumbukira chiyani pa chitsanzo cha Yesu?

 <<    >>