Uthenga Wabwino Malinga ndi Yohane (GA WO LACHIWIRI) << >> MAWU OTSOGOLERA Zolembela za uthenga wabwino molingana ndi Yohane zinalembedwa patsogolo pa mabuku ena atatu authenga wabwino (wochedwa ndandanda wa mauthenga abwino), koma mkatikati mwa dzaka 100 zoyambilira. Muzaka za mma 1900, otsutsa Baibulo anayesela kuti akane kuti bukhuli linalembedwa isanafike AD 150, chotelo kuyetsera kuchosa choona choti mtumwi Yohane ndiye amene analemba bukuli. Otsutsawa amanena kutinso mubuku limeneli mumaonekela mzeru za otumbatumba a Gnostic Filosofe ndipo chotelo sizingatheke kuti lilembedwe isanafike nthawi imene mzeru zimenezi zinakhala chiopsezo chachikulu kuchikhulupiriro. (Gnosticism ndi mzeru za filosofe ndi dongosolo la chipembezo lakagulu kochepa kakalekale kamene kamanena kuti chiziwitso osati chikhulupiliro ndiye mfundo yofunikila kuchipulumutso.)Lingaliro losokoneza limeneli kwanthawi yaitali lakhala likukanidwa. Mosiyana ndi zimenezi, maumboni a ponseponse akuchitira umboni za kukhalapo kwa bukhu lachinayi la uthenga wabwino ndi kulemekezedwa kwakukulu komwe anthu akhala alinako ku bukhuli ngakhale muzaka za mma A.D. 115. Umodzi mwa maumboni amenewo anabwera kudzera mu kupedzeka kwa chidutswa cha papyrusi, kokhala ndi mavesi ochepa a Yohane (chaputala 16, vesi 31-33, 37, 38), amene amadziwika ndi dzina lotiRylands Papyrus amene amachedwa P52, amene analembedwa A.D 125. Kachiduswa kameneka, kamene kanapezeka ku dziko la Egupto kumayambiriro kwa zaka za mma 200, amatengedwa ngati umboni wogwirika wa kufalikira ndi ukalekale wa bukhu lachinayi la uthenga wabwino. Ophunzira ochuka wa chipangano chatsopano Adolph Deissmann akutsimikizira kuti: “Misuso yambiri yokhuzana ndi kupezeka kochedwa kwa bukhu la uthenga wabwino wa Yohane mwachangu zizafota ndi kuuma monga mtengo munyumba yotentha kwambiri. Ife kuno ku Rylands Papyrus tili ndi zolembera zina zimene ndi umboni kuti Uthenga wabwino wa Yohane sunayambe mu zaka za mma 200, koma kuti zolembera zimenezi zinafika kale ku Egypto. Kulembedwa kwa Uthenga wabwino chotero kukuyenera kuikidwa muzaka zoyambirira zambuyo.” – Deutsche Allgemeine Zeitung, Dec. 3, 1935. Zolembela za Yohane sizinangotumikila kokha kucholinga chapadela pakati pa akhristu oyambilira; zakhala zikubweletsa chitsogozo cha uzimu, thandizo, ndichilimbikitso kwa otsatila a Khristu, okhala pansi pazochitika zosiyanasiyana kupyola mumibadomibado. Ambuye “ali ndi kuunika kumene kuli kwatsopano kwa ife, komabe ndikwamtengo wapatali kwambili, kuunika kwakalekale koti kuwalire kuchokela kumawu achoonadi. Tili ndi milezo chabe yakuunika kumene kuyenela kubwela pa ife. Ife sitikugwiritsa ntchito kwambiri kuunika kumene Ambuye anatipatsa ife kale, ndipo pakutelo ife tikulephera kulandira kuunika koonjezera; ife sitikuyenda muukunika kumene kunapelekedwa kale kwa ife. “Timazichula ife tokha kuti ndiife anthu osunga malamulo, koma sitikuzindikila kuya ndikukula kwa mfundo za lamulo la Mulungu; Ife sitimazindikila khalidwe lake lopatulika. Ambiri amene amazinena kukhala aphuzintsi achoonadi, alibe chiziwitso chenicheni cha zimene iwo akuchita Mukuphuzitsa lamulo laMulungu, chifuka choti iwo alibe chiziwitso cha moyo cha Ambuye Yesu Khristu.”-Selected messages,BK. 1, pp. 401,402. Tilole kuti kuphunzira kopitilira kwa uthenga uwu wabwino zitithandize ife kumuziwa Yesu bwino! Agawo la sabata sukulu aku General Comference << >>