Back to top

Sabbath Bible Lessons

Uthenga Wabwino Malinga ndi Yohane (GA WO LACHIWIRI)

 <<    >> 
PHUNZIRO 7 SABATA, MEYI 17, 2025

KUUNIKA KOKANIDWA – KAPENA KOWUNIKIRIDWA?

VESI LOLOWEZA: “Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndizaopa yani?” (Masalimo 27:1).

“Khristu ndi kuunika, kumene kumawalira munthu wina aliyense amene amadza mu dziko lapansi.’ Yohane 1:9.Monga mmene kudzera mwa Khristu munthu wina aliyense amakhala ndi moyo, chotelonso kudzera mwa Iye moyo ulionse umalandira miledzo ina yake yakunika ya umulungu.”- Education, p. 29.

Zowelenga zoonjezera:   Testimonies for the Church, vol. 7, pp. 18–28

Loyamba , Meyi 11

1. KUUNIKA KOLOSELEDWA

a. Kodi ndi motani mmene Mzimu Woyera umafotokozera za Yesu kudzera mwa Yesaya? Yesaya 49:6.

b. Kodi ndi motani mmene Simioni anamuzindikirira Yesu pa nthawi imene iye anabweretsedwa kukachisi kuti adzapatulidwe - Nanga kodi zimenezi zingatipangitse ife kulingalira chiyani? Luka 2:32.

“Simioni wokalamba, analankhula za Khristu monga ‘Kuunika kowalira amitundu, ndi ulemelero wa anthu anu Israeli,’ mukachisi mmene khristu tsopano amaphuzitsa. (Luka2:32). Mmawu amenewa Simeoni anali akukwanilitsa kwa Iye uneneri umene unali odziwika kwa Israyeli yense. Kudzera mwa mneneri Yesaya, Mzimu Woyera unalalikira kuti, ‘inde, ati, chili chinthu chopepuka ndithu kuti iwe ukhale mtumiki wanga wakuutsa mafuko a Yakobo, ndi kubwezera osungika a Israeli; ndizakupatsanso ukhale kuunika kwa amitundu, kuti ukhale chipulumutso changa mpaka ku malekezero adziko lapansi.’ Yesaya 49:6. Uneneri uwu umamvetsetsedwa bwino lomwe kuti umakamba za Mesiya, ndipo pamene Yesu amati, ‘Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi,’ anthu sakanalephela kudzindikira kuzinena kwake kukhala wolonjezedwayo.” – The Desire of Ages, p. 465.

“Oh, ndi phunziro lanji ili la nkhani yodabwitsa ya ku Betelehemu! Mmene imadzuzulira kutsakhulupilira kwathu, kunyada kwathu ndi kudzimva kukwanila kwathu kwa undekha. Ndi motani mmene imatichenjezera ife kukhala otsamala, kuti mwina kudzera mu mphwayi zathu za uchimo tikhonza nafenso kulephera kudzindikira zidzindikilo za nthawi, ndi kukhalanso otsaziwa tsiku la kuyendeledwa kwathu.”-The Great Controversy, p. 315.


Lachiwiri , Meyi 12

2. KUUNIKA KUKANIDWA

a. Kodi ndi motani mmene azitsogoleri achiyuda anachitila ndi utumiki wa Khristu? Yohane 1:11; 8:13.

“Moyo wake wonse wa Khristu komanso ndi kuphunzitsa kwake, zinali maphunziro opitilira akuzichepetsa, akuchita zinthu zabwino, akhalidwe lokoma, ndi odzikaniza wekha. Ichi chinali

chidzudzulo chopitilira kwa Ayuda amene amaonetsa mzimu odzilungamitsa, ndi waliuma opanda chifundo. Satana anawatsogolera iwo kufikizana anayamba kuoneka kuti amazunguzika wina akangonena za ntchito zodabwitsa za Khristu, zimene zimapangitsa kuti anthu achotse chidwi chawo kwa ayudawa ndi kupita kwa Khristu. Ndipo kwanthawi yaitali anazipanga mwa iwo okha kukhulupirira kuti anali wachinyengo womanamizira kuti ndi Mesiya, ndipo njira ina iliyonse imene angaigwiriste ntchito kuti amuchotse iye izakhala nchito yabwino kwa iwo.” – Spiritual Gifts, vol, 4a, p. 117.

b. Kodi ndi kufotokozera komveka bwino kotani kumene Yesu anakupereka kwa Afalisi osakhulupilirakomabe kodi ndi motani mmene iwo anayankhira? Yohane 8:14-18.

“(Afalisi) anali ndi umbuli okhudzana ndi khalidwe la umulungu la Khristu ndi utumiki wake chifukwa choti iwo samafufuza mauneneri okhudzana ndi Mesiya, monga mmene unalili mwayi wawo ndi udindo wawo kutelo. Ndipo iwo analibe kulumikizana kulikonse ndi Mulungu komanso kumwamba, ndipo ndichifukwa chake sanazindikile ntchito ya Mpulumutsi wa dziko lapansi, ndipo ngakhale analandira umboni otsimikizika oti Yesu ndiye Mpulumutsi, komano anakana kutsegula malingaliro awo kukumvetsetsa. Poyambilira pomwe anaika udani mmitima mwawo otsutsana ndi iye, ndi kukanitsitsa kukhulupilira umboni wa mphanvu kwambiri wa umulungu wake, ndipo zotsatira zake, mitima yawo inapitilira kuumitsitsa ndi kufikizana poti anazitsimikizira okha kuti sangamukhulupilire Iye kapena kumulandira Iye.”-The Spirit of Prophecy, vol. 2, pp. 334–355.

c. Kodi ndi kusiyana kwakukulu kotani kumene Yesu anakufotokoza kumene kulipo pakati pa Iye ndi Afalitsi otsakhulupilira aja? Yohane 8:19-23.

d. .kodi ndi chiyani chimene chizakhala chotsatila choopsa kwambiri cha kukana Khristu kwa azitsogoleri achiyuda? Yohane 8:24; Mateyu 23:38.


Lachitatu , Meyi 13

3. MAGULU AWIRI OMVETSERA

a. Atatha kuchenjezedwa kuti iwo adzafa mmachimo awo, kodi ndi chiyani chimene Afalisi analamulira Yesu kuti awachitile, nanga chifukwa chiyani? Yohane 8:25 (mbali yoyamba).

“Pooneka ngati anyozera mawu ake ,iwo anamufunsa iye, ‘Kodi ndinu yani?’ Anachichita chinthuchi pofuna kumukakamiza iye kuti adzinene yekha kuti ndi Khristu. Maonekedwe ake ndi ntchito yake zinali zosiyana kwambiri ndi zimene anthu amayembekezera, ndipo izi zinapangitsa adani ake kukhulupirira kuti Kulankhula kwake poyankha funso lija mwachindunji kuti Iye ndi Mesiya zipangitsa kuti anthu amukane Iye ndi kumutenga ngati munthu wachinyengo.” – The Desire of Ages, p. 465.

b. Kodi ndi motani mmene Mpulumutsi anawayankhira iwo- pobvumbulutsa kulumikizana kwake kodabwitsa ndi Atate? Yohane 8:25 (Mbali yomalidza), 26-29.

“Khristu sanapatukepo ku kumvera ku mfundo za malamulo a Mulungu. Ndipo sanachitepo kanthu kalikonse kosemphana ndi chifuniro cha Atate wake. Pamaso pa angelo, anthu, ndi ziwanda Iye akhonza kulankhula mawu amene ngati angachokere pa kamwa pa munthu wina aliyense akhala kuchitira Mulungu mwano: ‘Ndichita Ine zimene zimkondweretsa Iye nthawi zonse.’ Yohane8:29. Tsiku ndi tsiku kwa dzaka zitatu adani ake anamutsatira iye, kuti ayesetse kupedza kadontho kenakake kolakwika mukhalidwe lake; Satana pamodzi ndi gulu lake lonse la zoipa, anayesesa kuti amugonjetse Iye; koma analephera kupedza kanthu ngakhale kamodzi mwa iye kuti apezerepo mwayi. Ngakhale ziwanda zinakakamizika kuti zichite umboni kuti: ‘khristu analidi woyera yekhayo wa Mulungu.’”-Testimonies for the Church, vol.8, p. 208.

c. Fotokozani mmene Khristu amayendela ndi Atate tsiku ndi tsiku- ndi mmene ife tingamaonetsere moyo womwewo? Yohane 15:10; Aefeso 2:4-6.

“Monga mmene Yesu analili mukhalidwe la umunthu, Chotelo Mulungu amafuna kuti omutsatira ake ayenera kukhala choncho. Tikuyenera ife kumakhala kudzera mumphanvu yake moyo wa chiyero ndi wangwiro umene mpulumutsi anakhala.’-Ibid., p. 289.

“Moyo wa mpulumutsi pa dziko lapansi ngakhale anaukhala pakati pa mkangano, unali moyo wa mtendere. Ngakhale adani ake okwiya amamulonda Iye kosalekedza, Iye anati `Iye amene anandituma ine ali ndi ine: Atate sanandisiye ine pandekha; popedza nthawi zonse ndimachita zinthu zimene zimamukondweretsa iye.’ Yohane 8:29. Panalibe namondwe wa anthu kapena mkwiyo wa Satana umene ukanatha kusokonedza bata la kulumikizana kwake kwa ngwiro ku ndi Mulungu.”-Thoughts from the Mount of Blessings, pp. 15, 14.


Lachinayi , Meyi 14

4. . KUUNIKA KUWARITSIDWA

a. Pamene khristu amalankhula choonadi chenicheni chakuthwa kwa Afalisi, kodi ndi motani mmene mawu Ake amakhudzira anthu oona mtima amene amamumvetsera- nanga ndi chifukwa chaiyani zinthu ngati izi zingatilimbikitse ife lero? Yohane 8:30.

“Khristu amaziwa mmene anagachitile modekha, ndi mwa mzeru, ndi kulepheretsa upo wa adani ake woti amubweretse iye kuciweruzo chomutsutsira iye. Mawu a Ambuye anali ngati mivi yokuthwa imene imayenda mwachindunji kupita kumene yalodza, ndipo amavuladza mitima ya iwo amene amamuneneza iye. Nthawi zonse pamene Khristu amalankhulana ndi anthu, kaya omvetserawo akhalapo ambiri kapena pang’ono, mawu ake amakhala ndi mphamvu zopulumutsa pa miyoyo ya anthu ena amene amamumvesera. Palibe uthenga umene unatuluka pa kamwa pa Khristu umene umayenera kungotaika chabe. Mawu alionse amene Iye walankhula amaika udindo watsopano paiwo amene awanva mawuwo. Azibusa amene akupereka uthenga otsiliza wa chifundo kudziko lapansi, amene akupereka choonadi moona mtima amene amadalira kotheratu pa Mulungu kuti awapatse mphanvu, sakuyenera kuopa konse kuti kulimbika kwawo ndi kopanda ntchito. Munthu wina asanene kuti muvi wa choonadi sungathe kupyoza pofikilapo, ndi kukalasa miyoyo ya iwo amene akumvetsera . Ngakhale diso la Munthu silingathe kuona kuyenda kwa muvi wa choonadi, ngakhale khutu la munthu silingathe kumva kulira kwa moyo ovulazidwa, komano choonadi chimakhala chapyoza mumtima mwake mwakachetechete. Mulungu amalankhula ndi moyo ulionse, ndipo pa tsiku lomaliza lotseka mbiri mtumiki wa Mulungu adzaima ndi mphoto za chisomo cha chiombolo kuti zipereke ulemu ndi kulemekedza kwa Khristu, amene akuyenera ulemu. Mulungu, amene amaona mtseri, azapereka mphoto moonekera kwa onse amene analalikira choonadi mu dzina lake.”-The signs of the Times, February 6, 1896.

b. Pambali pa azibusa, ndi ndani wina amene akudalitsika kudzera mukuunikila ena kuwala kochokela kumwamba? Masalmo 27:1; 147:15; Yesaya 55:10, 11.

“Anthu amene sanaitanidwe kuutumiki akuyenera kulimbikitsidwa kumugwirira ntchito Ambuye molingana ndi kuthekela kwawo kosiyanasiyana. Amuna ndi akazi mazana mazana amene angokhara opanda kuchitapo kanthu ku ntchito ya Ambuye, akhoza kuchitapo utumiki ovomelezeka pamaso pa Ambuye. Kudzera mukutengela choonadi mmakomo aabwenzi ndi anansi awo, akhonza kugwira ntchito yaikulu ya Ambuye. Mulungu alibe sankho. Ndipo iye adzagwiritsa ntchito anthu odzichepetsa, akhristu odzipereka, ngakhale iwo atakhala kuti sanalandile maphunziro okwanira monga amene ena analandilira. Aloleni anthu otelewo kuti alowe muutumiki mukutumikila iye kudzera mu ntchito yakhomo ndi khomo. Pokhala pambali pa moto, iwo akhonza- ngati ali ozichepesa, oganiza bwino, ndi akhalidwe la umulungu kuchita zambiri kukwanitsa kufikila zotsowa zenizeni za mabanja kupotsera mbusa odzozedwa.”- Testimonies for the Church, vol. 7, p. 21.


Lachisanu , Meyi 15

5. UKAPOLO KUSIYANITSA NDI UFULU

a. Kodi ndi chiyani chimene Yesu analankhula kwa a Yuda amene anamulandira iye? Yohane 8:31, 32. Mosiyana, kodi ndi motani mmene anthu osakhulupilira amalephera kuona chinthu chofunikila chokhacho chimene chingatipangitse ife kumatsulidwa kuuchimo ndi kukhala mfulu? Yohane 8:33-36.

“(Afalisi) anali muukapolo oyipitsitsa ndi omvetsa chisoni- omalamuliridwa ndi mzimu oyipa.

“Moyo ulionse umene umakana kuzipereka okha kwa Mulungu umakhala pansi pa ulamuliro wa mphanvu zina. Ndipo munthuyo samakhala wa iye yekha. Akhonza kumalankhula za ufulu komano iye mwini ali muukapolo wa zaoneni. Ndipo iye samaloredwa kuti awone kukongola kwa choonadi, popeza malingaliro ake ali pansi polamulilidwa ndi satana. Pamene iye angamapange matama kuti iye akutsatira chigamulo cha malingaliro ake, iye amakhala akumvera chifuniro cha karonga wa mdima. Khristu anabwera kuti adzaphwanye maunyolo amsinga za ukapolo wa uchimo kuchoka mmoyo….

“Mu ntchito ya chiombolo mulibemo kukakamizana. Palibe kukakamiza kochokela kunja kumene kumagwiritsidwa ntchito. Pansi pa chikoka cha mzimu wa Mulungu, munthu amasiidwa ndi ufulu kuti asankhe iye amene angamutumikile. Mukusintha kumene kumachitika pamene moyo wozipereka kwa Khristu, umamva ufulu weniweni mumtima. Kuthamangitsidwa kwa tchimo mumtima ndi chochitika cha moyo pachokha. Ndizoonadi, tilibe mphanvu zoti tingazimasule tokha kuulamuliro wa Satana; komano pamene ife tikukhumba kuti timasulidwe kuuchimo, ndipo mukusowa kwathu kwakukulu tikulilira thandizo la mphanvu zochokela kunja kwanthu komanso zoposa zathu, mphanvu za moyo zimapatsidwa mphanvu za umulungu za mzimu woyera, ndipo zimanvera zolamula za chifuniro mukukwaniritsa chifuniro cha Mulungu.

“Choyenereza chokhacho chimene munthu angathe kupezadi ufulu, ndiko kukhala mmodzi ndi Khristu. `Choonadi chidzakumasulani;’ndipo Khristu ndiye choonadi. Chimo likhonza kupambana pokhapokha ngati lagonjetsa ndi kufooketsa malingaliro, ndi kuononganso ufulu wa moyo. Kudzipereka mogonja kwa Mulungu ndi kudzibwezeletsa wekha ku ulemelero weniweni ndi ulemu wa munthu. Lamulo lopatulika, limene ife tonse timabweletsedwa kuti tiligonjere, ‘ndi lamulo la ufulu.’ Yakobo 2:12.” – The Desire Of Ages, p. 466,


Lachisanu ndi chimodzi , Meyi 16

6. MAFUNSO OBWEREZA PAWEKHA

1. Fotokozani kufunikila kwa mawu a Simioni okhudzana ndi Yesu.

2. Fotokozani zimene Alembi ndi Afalisi amamuchitila Khristu.

3. Kodi ndi chiyani chimene chimayenera kuzachitika ndi dziko lawo chifukwa chakukana Yesu?

4. .Kodi ndi motani mmene miyoyo yoona mtima imachitila ndi uthenga wa Khristu mu nthawi yake komanso pano?

5. Fotokozani tanthauzo la mau oti “Ufulu” mukuunika kwa uthenga wabwino wa choonadi.

 <<    >>