Loyamba
, Meyi 25
1. KUDZINDIKILA KOLAKWIKA
a. Kodi ndi funso lanji limene ophunzira anamfusa Yesu pamene iwo anaona munthu amene anabadwa wakhungu? Yohane 9:1, 2.
b. Kodi ndilingaliro lanji lolakwika lokhuzana ndi zotsautsa limene limakhulupiliridwa ndi Ayuda komanso ophunzira, nanga ndimotani mmene Satana amapindulira nawo lingaliroli? Yohane 9:34 (Mbali yoyamba).
“Chimakhulupililidwa ponseponse pakati pa Ayuda kuti chimo chilango chake chimaperekedwa mmoyo womweuno. Bvuto lililonse limatengedwa kukhala chilango cha cholakwa chinachake, mwina kulakwa kwa odwalayo mwiniwake kapena kwa makolo ake. Ndizoona kuti kudwala konse ndizotsatila zakuphwanya kwa lamulo la Mulungu, Koma choona ichi chakhala chikupotozedwa. Satana, oyambitsa wa uchimo ndi zotsatila zake zonse, wakhala akutsogolera anthu kuti aziyang’ana pa matenda ndi imfa ngati zochokera kwa Mulungu zoperekedwa chifukwa cha chimo. Chotelo munthu amene matsautso akuulu kapena tsoka linalake lalikulu lagwera pa iye amakhalanso ndi cholemetsa choonjezera chomatengedwa ngati wochimwa wamkulu.
“Chotelo njira inakonzedwa yoti a Yuda akane Yesu. Iye amene `ananyamula zowawa zathu, ndikusenza zisoni zathu’ ayuda amayang’ana pa iye monyoza monga `okanthidwa ndi Mulungu ndi ovutidwa; Ndipo iwo anabitsa nkhope zawo kwa iye.” – The Desire of Ages, p. 471.
Lachiwiri
, Meyi 26
2. KUULEMERERO WA MULUNGU
a. Kodi ndi lankho lanji la Yesu limene linapereka kuunika zokhuzana ndi kubvutika ndi chimo? Yohane 9:3-5.
“Chikhulupiriro cha a Yuda chokhuzana ndi kugwirizana kwa chimo ndi matsautso limatengedwanso ndi ophunzira a Yesu. Pamene Yesu amakonza cholakwitsa chawo, iye sanafotokoze choyambitsa chamatsautso a Munthu, koma anawauza iwo chimene chingakhale chotsatira. Chifukwa cha ichi ntchito za Mulungu zionetsedwa. ‘Pakukhala ine padziko lapansi,’ Iye anati, ‘ine ndine kuunika kwa dziko lapansi.’ ”- The Desire of Ages, p. 471.
b. Kodi ndi chiyani chimene Yesu anachita patangodutsa nthawi pang’ono, nanga ndimotani mmene munthu wakhungu anagwirizilana ndi iye? Yohane 9:6, 7.
“Atatha kudzoza maso a munthu wakhungu, iye anamutumiza iye kuti akasambe muthamanda la Siloamu, ndipo maso amuthuyo anachilisidwa. Mukutele Yesu anayankha funso la ophunzira kudzera muchochitika, monga mmene iye nthawi zambiri amachitira mukuyankha mafunso operekedwa kwa iye mwamkwiyo. Ophunzira sanaitanidwe kuti azikakambirana funso lokhuzana ndi kuti ndi ndani amene anachimwa kapena sanachimwe, koma kuzazindikira mphanvu ndi chisomo cha Mulungu mukupereka kupenya kwa akhungu. Chinali choziwikilatu kuti munalibe mphanvu zamachilitso muthope, kapena muthamanda limene munthu wakhungu anatumizidwa kuti akasambe koma kuti mphanvu zinali mwa Khristu. “- Ibid.
c. Fotokozani mmene azinzake ndi omuzungulira anachitira –ndipo fotokozani kulankhulana kumene kunakhalapo pakati pa iye ndi anzake. Yohane 9:8-12.
“Anzake anyamata wachichepereyu-ndiiwo amene amamuziwa iye ali wakhungu mmbuyomu, anati, `Kodi siuyu uja wokhala ndikupemphapempha?.’ Iwo anayang’ana pa iye ndikukayika ;pakuti pamene maso ake anasegulidwa, nkhope yake inasinthika ndikuwalitsidwa, ndipo amaoneka ngati munthu wina. Pakati pa wina ndi mzake funso linafunsidwa. Ena amati, `ndiiyeyo’ Ena amati, ‘iye akufanana ndi iye.’ Koma iye amene analandira dalitso lalikulu kwambiri anathetsa funsoli kudzera mukuyankha kuti, `Ndiine amene.’” – Ibid., pp. 471, 472.
Lachitatu
, Meyi 27
3. FUNSO LIKULA
a. Ndi kwa ndani kumene atsogoleri aYuda anatengela munthu amene anabadwa osaona – nanga chifukwa chiyani? Ndipatsiku lanji pamene iye anachilitsidwa? Yohane 9:13, 14.
b. Fotokozani mmene anachitila Afarisi pa nkhaniyi? Yohane 9:15, 16.
“Afarisi anayembekezera kuti amuonetsere Yesu kukhala ochimwa, ndipo chotelo osati Mesiya. Iwo sanaziwe kuti ndiiyeyo amene anapanga Sabata ndikudziwa zofunikira zonse, pamene anachidza munthu wakhungu. Iwo amaoneka achangu modabwitsa za kutsunga kwa Sabata, komabe amakonza zakupha patsiku lomwelo.” – The Desire of Ages, p. 472.
c. Kodi ndindani amene Afarisi anawaitana kuzachita umboni zokhuzana ndi munthu amene anachilitsidwa? Yohane 9:18, 19.
“(Afarisi) anaitanitsa makolo ake, ndikuwafunsa iwo kuti,` kodi uyu ndi mwana wanu, amene inu mumati anabadwa osaona?.’
“Munthuyu anali pamenepa mwini wake, kumafotokoza kuti iye anali osaona, ndikuti kuona kwake kunabwezeretsedwa; koma Afarisi kunali kwabwino kwa iwo kukana umboni wapoyera koposa kubvomereza kuti iwo amalakwitsa. Ndi kwamphamvu kwambiri kuweluziratu, chilungamo cha chifarisi ndi chosokoneza kwambiri.” – Ibid.
d. Kodi ndimotani mmene ife timachenjezedwera zokhuzana ndi kuipa kwakukhala ndi lingaliro lokhazikitsiratu? Miyambo 18:13.
“Pali ambiri amene amapanga mawu a iwo okha kudzera pa zimene amva, kupanga lingaliro kuoneka losinthikiratu ndi limene oyankhula amayetsetsa kuti afotokoze. Ena, pakunva kudzera mumzeru zawo zoweluziratu, kapena zimene anakhazikitsiratu, amaimvetsetsa nkhaniyo monga mmene afunira kuti ikhalire monga mmene ingakwanilitsidwire bwino kuzolinga zawo.” – Testimonies to the Church, vol. 5, p. 695.
Lachinayi
, Meyi 28
4. KUKUMANA NDI CHIOPSEZO
a. Kodi ndimotani mmene Afarisi anayetserera kuopseza makolo amunthu amene anabadwa wakhunguNanga ndimotani mmene iwo anayankhira? Yohane 9:20, 21. Chifukwa chiyani iwo anapeleka yankho lolambalala? Yohane 9:22, 23.
“Afarisi anatsala ndi chiyembekezo chimodzi chokha, ndipo chinali choti aopseze makolo amunthuyo, ndimaonekedwe ooneka achidwi choona iwo anafunsa `ndipo apenya bwanji tsopano’? Makolowa pochita mantha kuti aziika okha pachiopsezo; popedza chinalengezetsedwa kuti wina aliyense amene angabvomeleze Yesu kuti ndi Khristu akuyenera `kuletsedwa mu Sunagoge’ kuti , akuyenera kuchotsedwa kuchoka musunagoge.munthawi imeneyi palibe mwana amene angadulidwe kapena wakufa kulilidwa kubanja lolakwali. Chigamulochi chimatengedwa kukhala tsoka lalikulu; ndipo ngati chingalephere kubweletsa kulapa, chilango chokulirapo chimatsatila. Ntchito yaikulu imene inachitidwa kwa mwana wawo inabweretsa kukhuzika kwakukulu kwa makolowa, komabe iwo anayankha kuti, ‘tidziwa kuti uyu ndi mwana wathu, ndikuti anabadwa osaona; koma sitiziwa umo apenya tsopano; kapena sitimziwa amene anamutsegulira maso ake;mufunse iye.’ Mukutelo iwo anatsamutsa udindo wonse kuchokera pa iwo okha kupita kwa mwana wawo; pakuti iwo sanayelekedze kuti abvomereze kuti achitire umboni Khristu.”- The Desire of Ages, 471, 473.
b. Pamene tadzungulilidwa ndi chiopsezo, kodi ndi chiyani chomwe tikuyenera kuchisunga mmalingaliro? Masalmo 118:6.
“Imani nji ndipo musayelekeze kuchita chinachilichonse choipa nkwabwino kuchulidwa opusa. Musalore kuti kunyoza, kuopseza, kapena mawu opeputsa, kuti akupangitseni inu kuvuladza chikumbumtima chanu ingakhale pang’ono.” – Fundumentals of Christian Education, p. 93.
“Khalidwe loona lachikhristu likuyenera kuonetseredwa kudzera mukukhala oima njii mucholinga, kutsimikizika kosasinthika, limene silingaumbidwe kapena kugonjesedwa ndi dziko lapansi kapena jehena. Iye amene Sali wakhungu kuzokopa za ulemu wa dziko lapansi, osunthika ndi ziopsezo, komanso ogwedezeka ndi zokopa azakhala, mosayembekezera kwa iye mwini, ogonjesedwa ndi misampha ya satana.” -Testimonies for the Church, vol. 4, pp. 543, 544.
“Ife tizalandira kutsutsa kwakukulu kwambiri kuchokera kwa ma Adventist amene amatsutsa lamulo la Mulungu. Koma monga omanga linga la yelusalemu, Ife sitikuyenera kupatutsidwa kapena kuchingilidwa kuchoka kuntchito yathu kudzera muzoneneza, kudzera mwa amithenga ofuna kukambirana kapena kulimbana, kapena kudzera mu mawu aziopsezo, zolembera za bodza, ingakhale zida zilizonse zimene satana angazigwiritse ntchito.”-Ibid., vol. 3, p. 574.
Lachisanu
, Meyi 29
5. MBIRI IBWELEZEDWA
a. Fotokozani chochitika chimene akumane nacho anthu a Mulungu osunga malamulo - Nanga kodi ndi motani mmene ife tikuyenera kuyankhira kuchochitikachi? Chibvumbulutso12:17; Machitidwe 4:18-20.
“Pamene mkangano ukufalikira kupita mmadera atsopano ndipamenenso malingaliro aanthu aitanitsidwe kulamulo lamulungu lopondelezedwa, Satana walutsa. Mphanvu zimene zikuyendera limodzi ndi uthenga zizangowakwiyitsa kwambiri basi iwo amene akuutsutsa uthengawu. M’busa azaika mphanvu zonse zopotsa za umunthu kuti achingire kuunika kuopa kuti kungathe kuwalira pa gulu lake lankhosa. Mwanjira iliyonse imene ili pamaso pawo iwo azayesesa kupondereza kukambirana kwina kuli konse kwa mafunso ofunikira amenewa. Mpingo uzapempha thandizo ku zanja lamphanvu laboma, ndipo ntchito imeneyi, ansembe ndi otsutsa azagwirizana pamodzi. Pamene mgwirizano wolimbikitsa kukhazikitsidwa kwa Sunday ungazakhale wamphanvu ndi wokhazikika, lamulo lizaikidwa lolimbana ndi osunga malamulo. Iwo azaopsezedwa ndi zindaputsa komanso kusekeledwa mundende, ndipo ena azapatsidwa maudindo olemekezeka, ndimphoto ndi maulemu osiyanasiyana, monga zokopa kuti iwo asiye chikhulupiriro chawo, koma yankho lawo lokhazikika ndiloti…` Tionetseni ife kuchokera mmalembo a Mulungu cholakwa chathu’- Pempho lomwelo limene analipempha Martin Luther atakumana ndi zochitika zofanana. Iwo amene azaitanitsidwe kukaima mmabwalo amilandu azachitila umboni mwamphanvu choonadi, ndipo ena amene azawanve iwo azatsogoleredwa kutenga mbali yawo kuti azisunga malamulo onse a Mulungu. Motero kuunika kuzabweretsedwa pamaso pazikwizikwi amene mwanjira ina sakanaziwa kenakalikonse kokhuza choonadi chimenechi.” – The Desire of Ages, p. 607.
b. Pokumana ndi kutsutsidwa, kodi ndi chiyani chimene ife nthawi zonse tikuyenera kuchiika mmalingaliro? Yohane 9:39; Machitidwe 4:33; Masalmo 10:28.
“(Ophunzira) sanathe kukakamizidwa kapena kuopsezedwa ndi ziopsezo” – The Acts of Apostles, p. 48.
Lachisanu ndi chimodzi
, Meyi 30
6. MAFUNSO OBWEREZA PAWEKHA
1. Kodi ndi motani mmene atsogoleri achiyuda amaweluzira odwala ndi otsautsika?
2. Kodi ndi chiyani chimene moonadi chinachilitsa munthu wakhungu?
3. Kodi ndi chifukwa chiyani azinzake amunthu wakhungu anasokonezeka?
4. Kodi ndi chochitika chanji chimene mnyamata wachichepere anakumana nacho atatha kuchilitsidwa?
5. Kodi ndi motani mmene ine ndingapewere kugwera mumsampha omwewo umene anagwera makolo ake?