Back to top

Sabbath Bible Lessons

Uthenga Wabwino Malinga ndi Yohane (GA WO LACHIWIRI)

 <<    >> 
PHUNZIRO 4 SABATA, EPULO 26, 2025

PALIBE AMENE ANAYANKHULA MONGA MUNTHU UYU

VESI LOLOWEZA: “Anyamatawo anayankha, Nthawi yonse palibe munthu analankhula cotero.” (Yohane 7:46).

“Kuzindikira ndi kuyamikira kwa chowonadi, Iye anati, kumadalira pang'ono pamalingaliro koposa pamtima. Choonadi chiyenera kulandiridwa mu moyo; icho chimaitanitsa chigonjero cha chifuniro.”— The Desire of Ages, p. 455.

Zowelenga Zoonjezera:   Testimonies to Ministers, pp. 506–512

Loyamba , Epulo 20

1. ZOKHUMBA ZA ANTHU MWA YESU

a. Pakumva ndi kuona Yesu akulalikira poyera, Kodi ndi chiyani chomwe a Yuda ena anafunsa? Yohane 7:25, 26.

“Ambiri mwa omvetsera Kristu anali anthu amene analikukhala kuYerusalemu, amene anali asakudziwa za ziwembu za olamulira pa Iye, anadzimva kukhala okokeredwa kwa Iye ndi mphamvu yosakanizika. Kukhudzika kunasindikiza pa iwo kuti Iye anali Mwana wa Mulungu.”— The Desire of Ages, p. 457.

b. Kodi Satana anachita chiyani pa olamulirawo kuti alimbikitse kukayikira? Yohane 7:27.

“Satana anali wokonzeka kubweretsa kukayikira; ndipo chifukwa cha ichi njira inakonzedwa kudzera malingaliro awo olakwika okhudza Mesiya ndi kudza kwake. Anthu ambiri amakhulupirira kuti Khristu adzabadwira ku Betelehemu, koma kuti pakapita nthawi adzasowa, ndipo pakuwonekera Kwake kachiwiri palibe amene adzadziwe kumene achokera. Si ochepa okha amene ankakhulupirira kuti Mesiya sadzakhala ndi unansi wachibadwa ndi anthu. Ndipo chifukwa chakuti lingaliro lotchuka la ulemerero wa Mesiya silinakwaniritsidwe ndi Yesu wa ku Nazarete, ambiri analimbikira kulingaliro lakuti, ‘Koma ife tikudziwa Munthu uyu kumene Iye achokera: koma pamene Khristu akadzadza, palibe mmodzi adzadziwa uko achokera. ”—Ibid.


Lachiwiri , Epulo 21

2. DONGOSOLO LA UPANDU LITSEKELEZEDWA

a. Powerenga maganizo a anthu omumvetsera omwe anali kukaika, kodi Yesu anawauza chiyani iwo? Yohane 7:28.

“Pamene iwo anali kugwederagwedera pakati pa chikaiko ndi chikhulupiriro, Yesu anatenga malingaliro awo, nati kwa iwo: ‘Mundidziwa Ine, ndiponso mudziwa kumene ndi chokera; ndipo sindinaza Ine ndekha, koma Iye wondituma Ine amene inu simumudziwa, ali woona.’ Iwo amazinena kuti amadziwa mmene chiyambi cha Khristu chidzakhalire, koma iwo anali osadziwa kotheratu.Ngati akanakhala moyo wogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu, akanadziwa Mwana wake pamene anaonekera kwa iwo.”— The Desire of Ages, p. 457.

b. Posowa zifukwa zomutsutsa Yesu, kodi ndi kudzera mu njira yanji imene atsogoleri achiyuda anafuna kumukhalitsa chete Iye? Yohane 7:30 (gawo loyamba). M’chenicheni, n’chifukwa chiyani sanathe kum’manga Iye? Yohane 7:30 (gawo lomaliza).

“Omvera sakanatha kumvetsa mawu a Kristu. Mwa chionekere iwo anali kubwereza zonena zimene Iye ananena pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayuda miyezi yambiri m’mbuyomo, pamene anadzilengeza yekha kuti ndi Mwana wa Mulungu. Monga olamulira pamenepo anayesera kuzinga Iye kuti amuphe, koterotso pano anafuna kumgwira Iye; koma anatsekeredwa ndi mphamvu yosaoneka, imene inaika malire kuukali wawo, ndikunena kwa iwo, mlingo uwu ndi umene mungathe kufikira, ndipo simupitirira apa.” — Ibid.

c. Kodi ambiri anasonyeza bwanji chikhulupiriro chawo mwa Yesu—ndipo kodi olamulirawo analinganiza kuchita chiyani atazindikira kuti anthu anali kumumvera chisoni? Yohane 7:31, 32.

“Atsogoleri a Afarisi, amene anali kuyang’ana mwa chidwi zochitikazo, anaona nkhope zoonetsa kumumvera chisoni pakati pa khamulo. Ndipo anafulumira kunka kwa ansembe a akulu, nakonza dongosolo loti amgwire Iye. Koma adapangana kuti amgwire Iye ali yekha; pakuti sanalimbika mtima kumgwira Iye pamaso pa anthu.”—Ibid., pp. 457, 458.


Lachitatu , Epulo 22

3. KUITANIRA

a. Pa tsiku lomaliza la phwandolo, kodi ndi fanizo lochititsa chidwi lotani limene Yesu anagwiritsa ntchito popereka chitonthozo kwa miyoyo yotopa ndi uchimo? Yohane 7:37, 38.

“Mtima umene umalandira mawu a Mulungu sulingati thamanda lomwe madzi ake amangouma, sulingati chitsime chong’ambika chimene chitaya chuma chake. Uli ngati mtsinje wam’phiri, wodyetsedwa ndi akasupe osatha, amene madzi ake ozizira, othwanima amatumpha kuchokera kuthanthwe kupita kuthanthwe, kutsitsimula otopa, aludzu, olemedwa. Uli ngati mtsinje woyenda mosalekeza, ndipo pamene ukuyenda, umaya kwambiri ndi kukulirakulirabe, kufikira madzi ake opatsa moyo atafalikira padziko lonse lapansi. Mtsinje umene umayimba munjira yake pamene ukuyenda umasiya m'mbuyo mphatso yake yamaluwa ndi zipatso. Udzu womwe uli m'mphepete mwake ndi wobiriwira bwino, mitengo imakhala yobiriwira, maluwa ake amakhala ochuluka kwambiri. Pamene dziko likakhala lopanda kanthu ndi lofiirira chifukwa cha kutentha kwa m'chilimwe, mzere wamaluwa umalemba m'njira ya mtsinjewu.

“Zimakhalaso chomcho ndi mwana weniweni wa Mulungu. Chipembedzo cha Khristu chimadziwonetsera chokha ngati mfundo yofunikira kwambiri ndiyofalikira, mphamvu ya uzimu ya moyo, yogwira ntchito. Pamene mtima utsegukira kuchikoka cha kumwamba cha choonadi ndi chikondi, mfundo zimenezi zidzasefukiranso ngati mitsinje ya m’chipululu, kuchititsa kuti zipatso ziwonekere kumene tsopano kuli chilala ndi ng’amba.”—Prophets and Kings, p. 233, 234 .

“‘Ngati wina akumva ludzu’ la chiyembekezo chopumulitsa, cha kumasulidwa ku zilakolako za uchimo, Khristu akuti, ‘abwere kwa Ine, namwe.’ Yohane 7:37.”— The Ministry of Healing, p. 179.

b. Kodi ndi motani mmene kuitanira kumeneku kuyenera kumvetsetsedwanso? Yohane 7:39.

“Khristu anapereka mfundo za choonadi mu uthenga wabwino. Muchiphunzitso Chake tikhoza kumwa mitsinje yoyera yomwe ikuyenda kuchokera kumpando wachifumu wa Mulungu.”— Testimonies for the Church, vol. 8, p. 309.

“Chomwe timafunikira ndi chipembedzo chamoyo. Munthu mmodzi amene ali ndimalingaliro owonjezereka a udindo, amene moyo wake uli m’chiyanjano ndi Mulungu ndiponso amene ali wokangalika kaamba ka Kristu, adzakhala ndi chikoka cha mphamvu cha kuchita za bwino. Iye samamwa pa mtsinje wochepa, wakuda, woipitsidwa, koma wamadzi oyera, ochokera pa akasakupe a m’mwamba; ndipo iye akhoza kofotokozera mphamvu ndi mzimu watsopano ku mpingo. Pamene chitsenderezo chochokera kunja chikuchulukirachulukira, Mulungu akufuna kuti mpingo wake ukhale wopatsidwa moyo ndi choonadi chopatulika chimene iwo amakhulupirira. MzimuWoyera wochokera Kumwamba, wogwira ntchito limodzi ndi ana a amuna ndi a akazi a Mulungu, adzagonjetsa zopinga ndikukhala ndi chipambano mukulimbana ndi mdaniyo. Mulungu ali ndi zigonjetso zazikulu zosungira anthu Ake okonda chowonadi, osunga malamulo.”—Ibid., vol. 5, p. 581.


Lachinayi , Epulo 23

4. MAWU OSAFANANA KONSE NDI ENA

a. Monga chotsatira cha mawu a Khristu okamba za madzi a moyo, kodi ambiri ananena chiyani— ndipo chifukwa chiyani? Yohane 7:40 (fananisani ndi Deuteronomo 18:15).

b. Pamene ena analimbikitsidwa ndi chiyembekezo kudzera mu chochitika chimenechi, kodi ena anatani? Yohane 7:41-44.

c. Kodi ndi ulamuliro otani omwe anyamata analandira kuchokera kwa olamulira awo? Yohane 7:45. N’cifukwa chiyani sanathe kugwilaYesu? Yohane 7:46.

“Pa tsiku lomaliza la phwando, anyamata amene anatumidwa ndi ansembe ndi olamulira kuti akamugwire Yesu, anabwerera opanda Iye. Iwo adafunsidwa mokwiya, Chifukwa chiyani simunabwere naye? Ndi nkhope zaulemu iwo anayankha, ‘Palibe munthu analankhula monga Munthu uyu analankhulira.’

“Owumitsidwa monga momwe inaliri mitima yawo, iwo anasungunulidwa ndi mawu Ake. Pamene Iye anali kulankhula m’bwalo la kachisi, iwo anayandikira pafupi kuti apeze china chake chimene chingam’tembenukire Iye. Koma pamene iwo amamvetsera, cholinga chimene iwo anatumizidwira chinaiwalika. Iwo anaima ngati anthu opepetulidwa. Khristu adadzibvumbulutsa yekha ku miyoyo yawo. Iwo anaona izo zimene ansembe ndi olamulira samatha kuziona— umunthu osefukiridwa ndi ulemerero wa umulungu.”— The Desire of Ages, p. 459.

“[Khristu] amagwiritsa ntchito zinthu za m’chilengedwe zimene iwo ankazidziwa bwino pofotokoza choonadi cha Mulungu. Motero nthaka ya mu mtima imakonzetseredwa kuti ilandire mbewu ya bwino. Iye anapangitsa omvera Ake kumva kuti zokhumba Zake zimagwirizana ndi zawo, kuti mtima Wake umagunda molingana ndi chimwemwe ndi chisoni chawo. Pa nthawi yomweyo iwo amawona mwa Iye mawonetseredwe a mphamvu ndi ubwino waukulu kwambiri kuposa zomwe analinazo arabi olemekezeka kwambiri. Ziphunzitso za Kristu zinali zodziwika ndi zophweka, ulemu, ndi mphamvu zimene sizinali zodziwika m’kale kwa iwo, ndipo mfuwu yawo yokakamizika inali ya kuti: 'Nthawi zonse palibe munthu analankhula monga Munthu uyu analankhulira.' Anthu anamvera Iye mokondwera; koma ansembe ndi olamulira—iwo eni onyenga ku udindo omwe anadalilidwa nawo monga alonda a chowonadi—anadana ndi Khristu chifukwa cha chisomo chomwe chinavumbulutsidwa, chimene chinakokera makamu kutali ndi iwo kuti atsatire kuunika kwa moyo. Kupyolera mu chikoka chawo mtundu wa Chiyuda, polephera kuzindikira Umulungu wa Khalidwe lake, unamukana mombolo.”— Testimonies for the Church, vol. 5, p. 747.


Lachisanu , Epulo 24

5. WOFUNAFUNA WOONA AKULIRATU

a. Kodi ndi motani momwe ansembe a akulu ndi Afarisi anadzudzulira anyamatawo? Yohane 7:47-49.

b. Fotokozani zokambirana zomwe zinatsatirapo ndi Nikodemo—kuwulula kukula kwake kuyambira pa zokambirana zake ndi Khristu usiku mu Yohane chaptala 3. Yohane 7:50–52.

“[Nikodemo] anabisa chowonadi mu mtima mwake, ndipo kwazaka zitatu panalibe zipatso zowonekera. Koma ngakhale Nikodemo anali asanavomereze Khristu poyera, mu Khonsolo Lalikulu la Asaduki mobwerezabwereza amalepheretsa machenjerero a ansembe oti amuwononge Khristu.”— The Acts of the Apostles, p. 104.

“Phunziro limene Kristu anapereka kwa Nikodemo [pa ulendo wake wausiku mu Yohane chaputala 3] silinapite pa chabe. Kutsimikiza kudakhazikika pamalingaliro ake, ndipo mu mtima mwake adalandira Yesu. Kuchokera pakuyankhulana kwake ndi Mpulumutsi, iye adasanthula mowona mtima Malemba a Chipangano Chakale, ndipo adawona chowonadi chikuyikidwa m'malo enieni a uthenga wa bwino.

“Funso limene iye anafunsa linali la nzeru, ndipo likanadziyamikiritsa lokha kwa amene anali kutsogorera pa khonsoloyo akanapanda kunyengedwa ndi mdani. Koma iwo anali odzala ndi tsankho moti palibe umboni uli wonse wokomera Yesu wa ku Nazarete, ngakhale unali wokhutiritsa bwanji, umene unali ndi kukhuza kwa iwo. Yankho limene Nikodemo analandira, linali lakuti, ‘Kodi iwenso uli woturuka m’ Galileya? santhula, nuwone kuti palibe mneneri anachokera ku Galileya.’

Ansembe ndi olamulira ananyengedwa, monga momwe Satana anafunira, kuti akhulupirire kuti Kristu anachokera ku Galileya. Ena amene anadziwa kuti iye anabadwira ku Betelehemu, anangokhala chete, kuti mabodza woasala ndidwe mphamvu zake.”— The SDA Bible Commentary [EG White Comments], vol. 5, p. 1136.


Lachisanu ndi chimodzi , Epulo 25

6. MAFUNSO OBWEREZA PAWEKHA

1. Kodi ndi chifukwa chiyani Yesu anakopa chidwi ndi ulemu wa anthu?

2. Kodi ndi motani mmene olamulira achiyuda analimbikirira mukuyesesa kumuimitsa Yesu?

3. Kodi ndi pempho lanji la poyera limene Yesu analipanga pa tsiku lomaliza la phwando?

4. Fotokozani mkangano waukulu umene unatsatirapo.

5. Poganiza za anthu amene ndimawadziwa, kodi ndiyenera kukumbukira chiyani za Nikodemo?

 <<    >>