Loyamba
, Juni 22
1. YESU MU BETANIYA
a. Atamva kuti Yesu akubwera ku Betaniya, kodi ndi chiyani chimene Malita anachita nanga ndikukhuzika kwanji kumene iye anakufotokoza? Yohane 11:20-22.
“Pakati pa abwenzi amene amalira panalinso achibale abanjali, ena mwa iwo anali ndi maudindo apamwamba kwambiri mu Yerusalemu. Pakati pa amenewa panali ena mwa adani kwambiri a Khristu. Khristu anaziwa zolinga zawo, ndipo chotelo iye sanazionetsere yekha mwachangu. Uthenga unaperekedwa kwa Malita mwakachetechete kotelo kuti ena muchipindamu sanamve…
“Malita anafulumira kuti akakumane ndi Khristu, mtima uli wosausika ndi malingaliro otsutsanatsusana. Pa maonekedwe apankhope pake iye anawelenga chifundo ndi chikondi chimene nthawi zonse chakhala chili pamenepo. Chidaliro chake mwa Iye sichinaonongeke, koma iye amalingalira za mchimwene wake wokondedwa kwambiri, amene Yesuso amamukonda. Ndinkhawa imene imakula mumtima mwake chifukwa Khristu sanabwele mmbuyomu, komabe ndi chiyembekezo choti ingakhale tsopano iye angathe kuchita chinachake choti awatonthoze iwo, iye anati ‘Ambuye, mukadakhala kuno mlongo wanga sakadafa. Kawiri ndi kawiri, pakati pa phokoso limene limapangidwa ndi olira, alongowa anakhala akubweleza mawu amenewa.
“Ndi chisoni chaumunthu ndi umulungu Yesu anayang’ana pankhope pake pachisoni ndi podzazidwa ndi nkhawa. Malita analibe khumbo lakulankhula zambuyo; zonse zimafotokozedwa kudzera mmawu okhuza kwambiri oti, ‘Ambuye, mukadakhala kuno mlongo wanga sakadafa.’ Koma poyang’ana pankhope paja yachikondi, iye anaonjezera kunena kuti, ‘ndiziwa kuti ngakhale tsopano, zinthu zilizonse mukapempha Mulungu, azakupatsani inu.’ ” – The Desire of Ages, pp. 529, 530.
Lachiwiri
, Juni 23
2. LONJEZO LAPOMPOMPO LACHIYEMBEKEZO
a. Ndizachiyani zimene Yesu anamusimikizira Malita? Yohane 11:23. Kodi ndi chiyani chimene iye anachizindikira kudzera muchimenechi? Yohane 11:24.
“Yesu analimbikitsa chikhulupiriro chake, ponena kuti, ‘Mlongo wako azauka.’ Yankho lake silinaperekedwe ndi cholinga choti libweletse chiyembekezo chakusintha mwachangu. Iye anatengela malingaliro a Malita kupyola kubwezeletsedwa kwapanopo kwa mlongo wake, ndikuwakhazikitsa iwo pa mzukiro pa kuuka kwa anthu olungama. Ichi anachita Iye kotelo kuti iye akathe kuona kukuukitsidwa kwa Lazalo lonjezo lakuuka kwa olungama onse amene anafa, ndi chitsimikizo choti kuzakwanilitsidwa kudzera mumphanvu za Mpulumutsi. Malita anayankha kuti, ‘ndikuziwa kuti adzauka mkuuka tsiku lomalidza.’“ – The Desire of Ages, p. 530.
b. Ndipamawu anji amene Yesu anabvomeledza chikhulupiliro cha Malita? Yohane 11:25; 1 Yohane 5:12.
“Pofunitsitsabe kuti apeleke chitsogozo choona kuchikhulupiriro chake, Yesu ananena kuti, ‘ine ndine kuuka ndi moyo.’ Mwa Khristu muli moyo, weniweni, osabwelekedwa, osachokera kwina. ‘Iye amene ali ndi mwana ali nawo moyo.’ 1Yohane 5:12. Umulungu wa Khristu ndichitsimikizo chaokhulupirira cha moyo wosatha.” – Ibid.
c. Kodi ndi lonjezo lanji limene lili madziko achiyembekezo chathu kupyola manda, Nanga kodi ndimotani mmene chikhulupiliro cha Malita chikugwirizana ndi chozizwa cha Khristu? Yohane 5:26; 11:26, 27.
“Apa Khristu akuyang’ana chitsogolo kunthawi yakubwera kwake kwachiwiri. Pamenepo wolungama wokufa azaukitsidwa osavunda, ndipo olungama amoyo azasinthidwa kupita kumwamba popanda kuona imfa. Chozizwa chimene Khristu anali pafupi kuti achichite, mukuzutsa Lazalo kuchokera kwaakufa, kuzaimilira kuukitsidwa kwa olungama onse okufa. Kudzera mmawu ake ndi munchito zake iye anazilengezetsa iye yekha kuti ndi mwini wake wakuuka kwa kufa. Iye amene mwini wake posachedwa anali kuti afa pamtanda anayima ndi makiyi aimfa ogonjetsa wamanda, ndikusimikizira za kuyenera ndi mphanvu zake zakupereka moyo wosatha.” – Ibid.
Lachitatu
, Juni 24
3. YESU ALIRA
a. Fotokozani machitachita ndi mawu a Mariya ogwidwa ndi chisoni. Yohane 11:28-32.
b. Pamene Yesu anaona Mariya ndi Ayuda ena akulira, kodi ndi chiyani chimene Yesu anachita-ndipo chifukwa chiyani? Yohane 11:33-35.
“‘Pamenepo Yesu pakumuona iye akulira, ndi Ayuda akumperekeza iye akulira, anazuma muuzimu, nabvutika mwini.’ Iye anawelenga mitima ya anthu onse amene anasonkhana. Iye anaona kuti kwa ambiri, chimene chimaonetseredwa ngati chisoni chinali kunamizira chabe. Iye anaziwa kuti anthu ena pagulupa, amene tsopano akuonetsera chisoni cha chinyengo, posachedwapa akhala akukonza madongosolo akupha, osati ochita chozizwa chachikulu yekha basi, komanso aiye amene atadzusidwe kuchokera kuimfa. Khristu akanatha kubvula kuchokera kwa iwo mikanjo yawo yachisoni chabodza. Koma iye anabweza mkwiyo wake wachilungamo. Mawu amene mwachilungamo chonse akanatha kuwanena, iye sanawanene, chifukwa cha okondedwa amene anagwada pamapadzi ake mwachisoni, amene moonadi anakhulupilira mwa Iye.
“`Mwamuika iye kuti?’ Iye anafunsa, ‘ananena ndi iye, Ambuye tiyeni mukaone.’ Limodzi iwo anayenda kupita kumanda. Chinali chochitika cholilitsa. Lazalo anali okondedwa kwambiri, ndipo adzilongo ake anamulirira iye ndimitima yotsweka, Pamenenso iwo amene anali abwenzi ake anasakanidza misodzi yawo ndi ya alongo ake achisoni. Poona kutsautsika uku kwa umunthu, ndichoona choti abwenzi otsautsikawa akhoza kulirira wokufa wawo pamene mpulumutsi wadziko lapansi akuima pomwepo- `Yesu analira.’ Ngakhale iye anali mwana wa Mulungu, komabe iye anatenga khalidwe la umunthu pa
Iye, ndipo iye anakhuzika ndi chisoni cha umunthu. Mtima wake wachifundo, wachisoni nthawi zonse umazutsidwa ku chisoni kudzera mu kuvutika. Iye amalira limodzi ndiiwo amene akulira, ndikukondwa ndiiwo amene akukondwa.” – The Desire of Ages, p. 533.
c. Kodi ndi motani mmene nthawi imeneyi mumoyo wa Khristu ingakhalire chisanzo kwa ife? Aroma 12:15.
“Chisanzo chodabwitsa cha Khristu, chifundo chosafanizilika chimene pamodzi nacho iye amalowela muzokunva mumtima za ena, kulira ndiiwo amene akulira, kukondwa ndiiwo amene akukondwa zikuyenera kukhala ndi chikoka chakuya pakhalidwe la onse amene amamutsatila iye moonadi. Kudzera mumawu ndi ntchito zachifundo iye azayetsetsa kupanga njira yophweka yamapadzi otopa.” – The Ministry of Healing, pp. 157–158.
Lachinayi
, Juni 25
4. MGWIRIZANO PAKATIKA MULUNGU NDI UMUNTHU
a. Kodi ndikulamula kwanji kumene Yesu anakupereka kwa iwo amene anamuzungulira iye? Yohane 11:39(mbali yoyamba).Kodi ndi motani mmene Malita anayankhira ndipo ndi chiyani chimene Yesu anayankhula kwa iye? Yohane 11:39 (mbali yomaliza).
“Pamene Ambuye alipafupi kuti achite ntchito inayake, Satana amayenda pa wina wake kuti atsutse. ‘chotsani mwala,’ Khristu anatelo. Monga mmene mungathele, konzani njira ya ntchito yanga. Koma khalidwe la chibadwa lamatama ndi lozionetsera la Malita linazikweza lokha. Iye sanafune kuti thupi lobvundalo libweletsedwe kuti lionedwe. Mtima waumunthu ndi ochedwa kuzindikira mawu aKhristu, ndipo chikhulupiliro cha Malita sichinamvetsetse tanthauzo lenileni la lonjezo lake.
“Khristu anamudzuzula Malita, koma mawu ake anayankhulidwa modekha kwambiri. ‘Sindidati kwa iwe, ngati ukhulupirira uzaona ufumu wa Mulungu?’ Kodi ndi chifukwa chiyani ukuyenera kukaikira zokhuzana ndi mphanvu zanga? Kodi chifukwa chiyani ukulingalira motsutsana ndi zofuna zanga? Ndanena mawu anga. Ngati iwe uzakhulupirira, udzaona ulemerero wa Mulungu. Zosatheka mwa chilengedwe sizingathe kuletsa ntchito ya opanda malire. Kukaikira ndi kusakhulupirira sikuzichepetsa. Kukhulupirira mwa ndendende mumawu a Khristu ndiko kudzichepetsa koona, kuzipereka wekha koona.
“‘Chotsani mwala.’ Khristu akanatha kulamulira mwala kuti uchoke, ndipo iwo ukanatha kumvera mawu ake. Iye akanatha kulamulira angelo amene anali pafupi pambali pake kuti achite chimenechi. Pakulamula kwake, manja osaoneka akanatha kuchotsa mwala. Koma iwo umayenera kuchotsedwa ndi manja aumunthu. Mukutelo Khristu amaonetsera kuti umunthu ukuyenera kugwirizana ndi umulungu. Chimene mphanvu za umunthu zingathe kuchita mphanvu za umulungu sizimaitanitsidwa kuchichita.Mulungu samanyozera thandizo la Munthu. Iye amamulimbikitsa iye, kugwira ntchito limodzi ndi iye, pamene iye akugwiritsa ntchito mphanvu ndi kuthekera zimene iye anapatsidwa.” –The Desire of Ages, p. 535.
b. Kodi ndimawu anji a Khristu amene modekha akudzudzula kusakhulupirira kwathu lero? Yohane 11:40.
“Ambiri alibe chikhulupiriro cha moyo. Ichi ndi chifukwa chake iwo samaona zambiri zamphanvu ya Mulungu. Kufooka kwawo ndichotsatira cha kusakhulupirira kwawo…Iwo amakonza madongosolo ndikuwachita, koma amapemphera pang’ono, ndipo ali ndi chidaliro chochepa chenicheni mwa Mulungu. Iwo amaganiza kuti ali ndi chikhulupiriro,koma ndikuzizimuka chabe kwa kanthawi. Polephera kuzindikira chosowa chawo, kapena khumbo la Mulungu lakupereka, iwo samapilira mukuika zopempha zawo pamaso pa Mulungu.” – Christ’s Object Lessons, pp. 145–146.
Lachisanu
, Juni 26
5. YESU AUKITSA LAZALO
a. Kodi ndi pemphero lanji limene Yesu analipereka pambali pa manda? Yohane 11:41, 42.
“Kulamula kunamveredwa. Mwala wachosedwa. Chinachilichonse chikuchitidwa pambalambanda komanso ndi cholinga. Onse apatsidwa mwayi kuti awone kuti palibe chinyengo chilichonse chimene chikuchitidwa. Thupi la Lazalo ilo lagona potelopo mmanda amwala, lozizila ndi lachete muimfa. Kufuula kwa olira kwalekeka. Odabwisika ndi oyembekezera, gulu lonse linaima mozungulira manda, kuyembekezera kuti aone chimene chingasatire…
“Apa khristu akunena Mulungu monga Atate wake, ndipo ndichidaliro chozaza akunena kuti iye ndi mwana wa Mulungu.” – The Desire of Ages, p. 535, 536.
b. Ndimawu anji amene Yesu anazutsira Lazalo? Yohane 11:43.Kodi ndichiyani chimene chinachitika pompopompo? Yohane 11:44
“Mawu akhristu,omveka bwino ndi opyoza, analowa mukhutu laokufa. Pamene iye amalankhula, Umulungu unawala kudzera mumunthu. Pankhope pake, pamene panawalisidwa ndi ulemerero wa Mulungu, anthu anaona chisimikizo cha mphanvu zake. Diso linalililonse linayang’anitsitsa pakhomo lamphanga lamanda. Khutu linalililonse linachela kuti linvesele liwu lina lililonse. Ndichidwi chachikulu komanso chopweteka onse anadikilira yetsero la umulungu la Khristu, umboni umene ungasimikizire kuzinena kwake koti ndi mwana wa Mulungu, kapena woti ufufute chiyembekezo kwa muyaya.
“Panamveka ngati kukuyenda munthu mumanda achete, ndipo iye amene anali wakufa anaima pakhomo lamanda… Umunthu ukuyenela kugwilila ntchito umunthu. Lazalo wamasulidwa zomangila, ndipo waima pamaso pa gulu limene linasonkhanalo, osati ngati munthu ochilitsidwa kumatenda, okhala ndi thupi lofooka, oonekela nthiti, koma monga munthu wathanzi lachikhalire, munthu wamphanvu zake olemekezeka. Maso ake anawala ndi nzeru ndi chikondi kwa mpulumutsi wake. Iye anazigwetsa mwini yekha mukupembeza pamapazi a Yesu.” – Ibid., p. 536.
Lachisanu ndi chimodzi
, Juni 26
6. MAFUNSO OBWEREZA PAWEKHA
1. Fotokozani chidaliro chimene azilongo ake a Lazalo anali nacho mwa Yesu?
2. Kodi ndi chiyani chimene Yesu anachilonjeza kwa Malita, kwa Mariya ndi kwa okhulupirira wina aliyense?
3. Kodi ndi chifukwa chiyani Yesu analira?
4. Kodi ndi motani mmene umunthu unagwirira ntchito limodzi ndi umulungu muchozizwa chimenechi?
5. Fotokozani machitidwe a Lazalo Yesu ataitana?