Back to top

Sabbath Bible Lessons

Uthenga Wabwino Malinga ndi Yohane (GA WO LACHIWIRI)

 <<    >> 
SABATA, JUNI 21, 2025 PHUNZIRO 12
YESU NDI LAZALO VESI LOLOWEZA: “Imfa ya okondedwa ake nja mtengo wake pamaso pa Yehova” (Masalmo 116:15). Zowelenga zoonjezera: The Ministry of Healing, pp. 219–228.
Zowelenga zoonjezera:   The ministry of healing, pp. 219–224 
“Mwa khristu muli moyo, weniweni, osabwerekedwa, osachokera kwina … Umulungu wa Khristu ndi chitsimikizo cha okhulupirira cha moyo wamuyaya.” – The Desire of Ages, p. 530.

1. BANJA LA KU BETANIYA Loyamba , Juni 15
a. Kodi ndi ophunzira anji amene Yesu anali nawo mu mzinda wa Betaniya? Yohane 11:5. “Mtima wa Khristu unamangililika ndi chingwe champhavu cha chikondi ndi banja la ku Betaniya ndipo kwa mmodzi wa iwo ntchito yake yodabwitsa kwa mbiri inachitidwa.“Ku nyumba kwa Lazalo, kawirikawiri Yesu amapezako mpumulo. Mpulumutsi analibe nyumba yakeyake Iye amadalira chisamaliro cha abwenzi ndi ophunzira ake, ndipo kawirikawiri akatopa, akakhala ndi ludzu chiyanjano cha umunthu, amakondwera kuthawira kunyumba ya bata imeneyi, kutali ndi kukayikira ndi nsanje ya Afarisi amkwiyo. Kumeneku Iye anapedza kulandilidwa koona, ubwenzi woyera ndi wangwiro. Kumeneku Iye amatha kuyankhula mwa ufulu, podziwa kuti mawu ake akhoza kumvetsetsedwa ndi kuyamikilidwa.” – The Desire of Ages, p. 524. b. Kodi ndi pa khomo pamtundu wanji pamene Mulungu amapezeka ndi madalitso ake apadera? Miyambo 3:33(mbali yomaliza). “Mpulumutsi wathu amayamikira banja labata ndi omvetsera achidwi. Iye amafuna chikondi, chisamaliro ndi chifundo cha umunthu. Iwo amene alandira langizo la kumwamba limeneiye amakhala nthawi zonse wokonzeka kupereka amakhala odalitsidwa kwakukulu.” – Ibid.

2. LAZARO ADWALA Lachiwiri , Juni 16
a. Kodi ndi chiyani chimene alongo ake a Lazalo anachita pamene mlongo wawo anadwalika kwambirinanga ndi yankho lanji limene iwo analilandira? Yohane 11:1-4. “Lazaro anadwala mwazizizi, ndipo alongo ake anatumiza uthenga kwa mpulumutsi, nanena, ambuye onani amene mumkonda adwala.’ Iwo anaona kuipitsitsa kwa nthenda imene inagwira mlongo wawo, koma amadziwa kuti Khristu anazionetsera yekha kutha kuchilitsa nthenda iliyonse. Iwo amakhulupirira kuti iye awamvera iwo chisoni mukusausika kwawo. Chotelo iwo sanapemphe kupezeka kwake kwa pompopompo, koma anangomutumizira uthenga wachidaliro woti, ‘Iye amene inu mumkonda adwala.’ Iwo anaganiza kuti iye akhoza kuyankha mwachangu kuuthenga wawo, ndi kubwela kudzakhala nawo mwamsanga pompopompo akangofika ku Betaniya.“Mwa chidwi iwo anadikirira mawu ochokera kwa Yesu. Nthawi zonse pamene moyo unalipo mwa mlongo wawo, Iwo amapemphera ndi kuyang’anira koma mnthenga anabwerera opanda Iye. Koma anangobweretsa uthenga oti `kudwala kumene sikuli kwa imfa,’ ndipo iwo anakakamira kuchiyembekezo choti Lazalo akhala ndi moyo. Mwachikondi iwo amayesera kuyankhula mawu a chiyembekezo ndi chilimbikitso kwa odwala wodwalikayu.” – The Desire of Ages, pp. 525–526. b. Fotokozani mawu ndi machitidwe a khristu patangopita masiku ochepa. Yohane 11:5-8. “kwa masiku awiri Khristu amaoneka ngati wachotsa uthenga uja mu malingaliro ake; popedza iye sanayankhule za Lazalo. Ophunzira analingalira za Yohane m’batizi, wokonza njira ya Yesu. Iwo amadabwitsika kuti ndi chifukwa chiyani Yesu, ndi mphanvu za kuchita zozizwa yodabwitsa analolera kuti Yohane abvutike mundende, ndi kufa imfa yankhaza. Pokhala nazo mphanvu zotere, kodi ndi chifukwa chiyani Khristu sanapulumutse moyo wa Yohane? Funso limeneli kawirikawiri limafunsidwa ndi Afarisi amene amalipereka ilo ngati msunso wosayankhika wosusa kuzinena kwa Khristu koti ndi mwana wa Mulungu. Mpulumutsi anachenjeza ophunzira ake za mayesero, kuluza zinthu, ndi zisautso.Kodi iye azawasiya iwo mmayesero? Ena amakhala ndi mafunso ngatidi iwo alakwitsa utumiki wake. Onse anasausika mumtima kwakukulu…“Ophunzira anafunsa chifukwa chiyani ngati Yesu amapita ku Yudeya, iye wadikira matsiku awiri. Koma nkhawa za kwa khristu ndi za kwa iwo eni zinali zambiri mmitima yawo. Iwo samaonanso china chilichonse koma choopsa muulendo umene iye amafuna kuuyenda.” – Ibid., pp. 526, 527.

3. CHOKHUMUDWITSA CHISANDULIKA CHIYEMBEKEZO Lachitatu , Juni 17
a. Kodi ndi uthenga wanji wopanda nthawi umene ife tingaugwiritsise kuchokera ku mmene Khristu anachitira ndi zotsatira zosokonezeka za zinthu zimene zinazungulira kudwala kwa Lazalo? Yohane 11:9, 10. “Iwo amene anakhalapo ogwira ntchito limodzi ndi Khristu, koma amakana amithenga ndi uthenga wawo, azagwa ndi kutaya kulimbika kwawo. Iwo azayenda mumdima osadziwa pamene agwera, oterewa ndi okonzeka kunyengedwa ndi zinyengo za mmasiku otsiriza. Malingaliro awo azazidwa ndi zinthu zazing’onozing’ono, ndipo iwo amaluza mwayi wodalitsika wa kuvala goli ndi Khristu, ndi kukhala ogwira ntchito limodzi ndi Mulungu.”- Fundamentals of Christian Education, p. 471. b. Kodi ndi bvumbulutso lanji lodabwitsa limene Yesu analipereka kwa ophunzira ake komabe kodi ndi motani mmene iwo anatanthauzira mawu ake? Yohane 11:11, 12. “‘Izi anati, ndipo zitatha izi ananena nawo, Lazalo bwenzi lathu ali m’tulo, koma ndimuka kukamuukitsa Iye ku tulo take.’ ‘Bwenzi lathu ali mtulo,’ kodi ndi mawu okhuza bwanji! Ozaza bwanji ndi chisoni! Ndi lingaliro la chiopsyezo chomwe Mbuye wawo amati akakumane nacho akapita ku Yerusalemu, ophunzira anaiwalira za banja losausika la ku Betaniya. Koma sizinali choncho kwa Khristu. Ophunzira anamva kuzuzulika. Iwo anakhumudwitsika chifukwa Khristu sanayankhe mwachangu ku uthenga. Iwo anayesedwa kuti azilingalira kuti Iye analibe chikondi chachikulu kwa Lazaro ndi alongo ake chimene iwi amaganiza kuti ali nacho,apo ayi Iye akanatha kubwerera mwachangu ndi mthenga. Koma mawu oti, ‘bwenzi lathu Lazaro ali mtulo,’ Unazusa malingaliro oyenera mu mitima yawo. I anakhulupirira kuti Khristu sanaiwalire abwenzi ake osausika.” – The Desire of Ages, p. 527. c. Fotokozani chimene mawu a Khristu amatanthauza kwenikweni? Yohane 11:13, 14. “Khristu amaonetsera imfa ngati kugona tulo kwa ana ake okhulupirira. Moyo wawo wabisidwa mwa Khristu kwa Mulungu, ndipo kufikira lipenga lomaliza lizalire iwo amene anafa azagona mwa iye.” – Ibid.

4. KUDIKILA, KUDIKILA, KUDIKILA Lachinayi , Juni 18
a. Kodi ndichifukwa chiyani Yesu sanapite kuBetaniya ngakhale ataziwa kuti Lazalo wamwalira? Yohane 11:15. “Ophunzira anadabwa pamawu a Khristu pamene iye anati, ‘Lazalo wamwalira. Ndipo ndikondwera ….Kuti kunalibe ine komweko.’ Kodi mpulumutsi kudzera muchisankho cha Iye mwini anapewa khomo la abwenzi ake osausika? Moonekera Mariya ndi Malita ndi Lazalo amene anali pafupi kufa anasiidwa okha. Koma iwo sanali okha. Khristu amaona zochitika zonse, Ndipo atamwalira Lazalo, azilongo okhuzikawo analimbikitsidwa kudzera muchifundo chake. Yesu anachitila umboni nkhawa ya mitima yawo yosweka, pamene mlongo wawo amalimbana ndi mdani wake wamkulu, imfa. Iye amanva muntima kusautsika kwinakulikonse, pamene iye anati kwa ophunzira ake, ‘Lazalo wamwalira.’ koma Khristu sanali ndiokondedwa okhawa ku Betaniya kuti azilingalira za iwo okha; Iye ali ndi lingaliro lakuphunzitsa ophunzira ake. Iwo akuyenera kudzakhala omuimilirako iye kudziko lapansi, kotelo kuti mdalitso wa Atate ukathe kuwafikira onse. Chifukwa cha iwo iye analorera Lazalo kuti afe. Ngati iye anakamuchilitsa iye kuchokera kunthenda yake kuti akhale wathanzi, chozizwitsa chimene ndiumboni wamphanvu kwambiri wakhalidwe lake la umulungu, sichikanachitidwa.” – The Desire of Ages, p. 528. b. Kodi ndi chiyani chimene ife tikuyenera kuzindikira kudzera mu njira imene mchilitsi wamkulu analorela Lazalo bwenzi lake, kuti adwale kwambili ndikufadi? 1 Akolinto 15:17-19; Masalimo 18:28. “Ntchito ya Khristu siinaimile poonetsera mphanvu zake pamatenda. Iye anapanga ntchito iliyonse yakuchilitsa kukhala chochitika chakudzalira mumtima mfundo za Umulungu zachikondi ndi kuzipeleka kwake.” – Counsels on Health, p. 249.“Ngati Khristu anakakhala mchipinda chimene Lazalo amadwalira, Lazalo sakanafa; pakuti Satana sakanakhala ndi mphanvu pa iye. Imfa sikanaika mivi yake pa Lazalo pamaso pa opereka moyo. Chotelo Khristu sanapiteko kumeneko iye analorera kuti mdani achite mphanvu zake, kotelo kuti iye akathe kumuthamangitsa iye, mdani ogonjetsedwa. Iye analorela Lazalo adutse kupyola mumphanvu zaimfa; ndipo alongo osautsika anaona mlongo wawo akuikidwa mmanda. Khritsu anadziwa kuti pamene iwo akuyang’ana pankhope yokufa yamlongo wawo chikhulupiliro chawo mwa mombolo wawo chiyesedwa kwakukulu. Koma iye anaziwa kuti chifukwa cha mikwingwirima imene iwo tsopano akudutsamo tsopano chikhulupiliro chawo chizawala ndi mphanvu zazikulu. Iye analolera nkhawa yamtundu wina ulionse imene iwo anadutsamo. Iye amawakonda iwo osati mochepelako chifukwa chake iye anachedwa; koma iye amadziwa kuti chifukwa cha iwo, chifukwa cha Lazalo, chifukwa cha iye mwini, ndi chifukwa cha ophunzira ake, chipambano chizapezedwa.” – The Desire of Ages, p. 528.

5. SITI NTHAWI ZONSE MONGA IFE TIKUYEMBEKEZERA Lachisanu , Juni 19
a. Kodi ndi chiyani chimene nthawi zonse tikuyenera kumachilingalira zokhuzana ndi imfa ya akapolo okhulupirika a Mulungu, posatengela mmene yachitikira? Masalmo 116:15. Pelekani chisanzo. “Sichinapelekedwe kwa Elisa kuti asatile Mbuye wake mugaleta wamoto. Pa iye Ambuye analorera kuti pabwele nthenda yokhalitsa. Munthawi yaitali yakufooka ndi kusautsika kwa umunthu chikhulupiriro chake chinagwira zolimba pamalonjezo a Mulungu. Ndipo iye nthawi zonse amaona pozungulira pake amithenga akumwamba achitonthozo ndi mtendere…. Chikhulupiriro chinakwhima kufikira muchidaliro chokhazikika mwa Mulungu wathu, ndipo pamene imfa inamuitana iye anali wokonzeka kupumula kuchoka kuntchito yake.” – Prophets and Kings, pp. 263, 264. a. Kodi ndizochitika zanji zimene zinachitika kuBetaniya asanafike Yesu-Nanga ndi ndani ena amene analikonso pamene iye anabwera? Yohane11:17-19. “Mukuchedwa kupita kwa Lazalo, Khristu anali ndi cholinga chachifundo pa iwo amene sanamlandile iye. Iye anachedwa, kuti kudzera mukuukitsa Lazalo kuchokela kuimfa iye akathe kupeleka kwa anthu ake ouma mtima, osakhulupilira umboni wina kuti iye moonadi ‘ndikuuka, ndimoyo.’ Iye samafuna kutaya chiyembekezo chonse pa anthu, osauka, nkhosa zosochera zanyumba ya Israeli. Mtima wake umasweka chifukwa cha kusakhulupirira kwawo. Muzifundo zake iye analingalira zakuwapatsa iwo umboni waukulu woti iye ndiobwezera moyo, iye amene ndiyekha amene angathe kubweletsa moyo poonekera. Uwu ukhala umboni woti ansembe sangathe kuutanthauzira mwa bodza. Ichi ndi chifukwa cha kuchedwa kwake kupita ku Betaniya. Chozizwa ichi choposa zozwizwitsa zonse, kuukitsa kwa Lazalo, kunaika chizindikiro cha Mulungu kuntchito yake chakuzinena kwake kokhala ndi umulungu.”- The Desire of Ages, p. 529.

6. MAFUNSO OBWEREZA PAWEKHA Lachisanu ndi chimodzi , Juni 20
1. Kodi ndi ndani amene anali abanja la Lazalo? 2. Kodi ndichifukwa chiyani Yesu pompo sanayankhe pempho la abwenzi ake? 3. Kodi ophuzira analingalira chiyani kukhalidwe la Khristu? 4. Kodi ndimotani mmene imfa ikuyenera kutengeledwa ndi okhulupirira mwa Khristu? 5. Ndichifukwa cha cholinga chanji kuti Khristu analorela Lazalo kuti afe?
 <<    >>