Back to top

Sabbath Bible Lessons

Uthenga Wabwino Malinga ndi Yohane (GA WO LACHIWIRI)

 <<    >> 
PHUNZIRO 10 SABATA, JUNI 7, 2025

KUKUMANA NDI KHUNGU LAUZIMU

VESI LOLOWEZA: “Chifukwa chake ndinena kwa inu, Machimo onse, ndi zonena zonse zamwano, zidzakhululukidwa kwa anthu; koma chamwano chapamzimu woyera sichizakhululukidwa. Ndipo amene ali yense anganenere mwana wa munthu zoipa, adzakhululukidwa; koma amene aliyense anganenere Mzimu woyera zoipa sadzakhululukidwa nthawi ino kapena irinkudzayo.” (Mateyu 12:31, 32).

“Si Mulungu amene amapangitsa khungu maso a anthu kapena kuumitsa mitima yawo. Iye amawatumizira iwo kuunika kuti akonze zolakwa zawo, ndikuwatsogolera iwo kunjira yotetezeka; ndikudzera mukukana kuunika kumeneku kuti maso amachititsidwa khungu ndi mitima imaumitsidwa.”- The Desire of Ages, p. 322.

Zowelenga zoonjezera:   Testimonies for the Church, vol. 2, pp. 489–497

Loyamba , Juni 1

1. KUFUNSANA KOYAMBIRANSO

a. Atamuitanisa kwanthawi yachiwiri mnyamata wachichepele amene kuona kwake kunabwezeretsedwa ndi Khristu, kodi ndi chiyani chimene Afarisi anayesera kumukakamiza iye kuti achite? Yohane 9:24.

“Afarisi anaona kuti iwo akufalitsa ntchito imene yachitidwa ndi Yesu. Iwo sangathe kukana chozizwacho. Munthu wakhungu anazazidwa ndi chimwemwe ndi chiyamiko iye anaona zinthu zodabwitsa zamchilengedwe, ndipo anazazidwa ndichisangalalo pakuona kukongola kwa dziko ndi thambo. Iye mwaufulu amafotokoza zomwe zinachitika kwa iye, ndipo kawirinso anayetsetsa kuti amukhazike iye chete, Poonena kuti `lemekedza Mulungu tidziwa kuti munthuyu ali wochimwa.’ Kutanthauza kuti, usamanenenso izi kawiri kuti munthu uyu anakupatsa iwe kuona; ndi Mulungu amene anachichita ichi.” – The Desire of Ages, p. 473.

b. Kodi ndi chozikanira chanji chokhazikika chimene mnyamata wachichepere anachiyankhula? Yohane 9:25.


Lachiwiri , Juni 2

2. KUFUSANANSO KOYAMBIRANSO (kupitiliza)

a. Kodi ndi chiyani chimene Afarisi kawirinso anafunsa mnyamata wachichepere amene kuona kwake kunabwezeretsedwa-nanga ndi cholinga chanji chimene iwo anali nacho? Yohane 9:26.

“(Afarisi) anafunsanso kawiri, `anakuchitira iwe chiyani? Anakusegulira iwe maso bwanji?’ Ndimawu ambiri iwo anayesetsa kuti amutsokonedze iye, kotelo kuti iye azizilingalira yekha kuti wasokonezeka mmutu. Satana ndi Angelo ake oipa anali kumbali ya Afarisi, ndipo polumikizitsa mphanvu zawo ndi ukachenjele wawo ndimalingaliro amunthu ndi cholinga choti apotodze ndikufufuta chikoka cha khristu. Iwo anasokoneza kukhuzika kumene kumakula mmitima ya Ambiri.” – The Desire of Ages, p. 473.

b. Kodi ndimotani mmene mnyamata wachichepereyu anawayankhira iwo- nanga kodi ndindani amene anaima kumbali yake kuti azimulimbikitsa iye? Yohane 9:27.

“Angelo a Mulungu analinso pamalopa kuti azimulimbikitsa munthu amene kuona kwake kunabwezeretsedwa. “Afarisi sanazindikile kuti iwo akuchita ndi wina woposa munthu wosaphunzira amene anabadwa wakhungu; Iwo samamuziwa iye amene anali naye mukulimbana. Kuunika kwa umulungu kunawalira mumtima wamunthu wakhungu. Pamene achinyengo amenewa amayetsera kumupanga iye kuti asakhulupirire, Mulungu anamuthandiza iye kuti aonetsere, kudzera mumayankho ake amphanvu komanso achindunji, kuti iye sangathe kupotozedwa.” – Ibid ., pp. 473,474.

c. Kodi ndi motani mmene ife tikusimikiziridwa za thandizo longa lomweli lero? Luka 12:11, 12.

“Tsopano, ndimabaibulo anu mukufunika kupita pamaso pa Mulungu, atseguleni iwo pamaso pa Mulungu ndikupemphera kwa Mulungu. Mukufunika inu kuti kuzindikila kwanu kutsistimutsidwe; mukufunika inu kudziwa kuti mukuziwa mfundo zenizeni za choonadi, ndipo kenako pamene mwakumana ndi okutsutsani inu simuzakumana nawo mumphanvu za inu nokha angelo a Mulungu azaima pambali panu kuti akuthandizeni inu kukuyankha funso lililonse limene lizafunsidwe kwa inu. Komanso pa nthawi yomweyomweyo Satana azaima pambali pa okutsutsani inu kuti awalimbikitse iwo kuti alankhule zinthu zovuta kwa inu kuzipilira, ndicholinga choti akukwiitseni inu kuti mulankhule mosayenera; koma lolani inu kuti kulankhula kwanu kukhale koti Satana sangathe kutengelapo mwayi pa mawu anu.” – The Review and Herald, May 3, 1887.


Lachitatu , Juni 3

3. KULIMBA MTIMA PAMASO PA KHUNGU LADALA

a. Atalephera kunamidza mnyamata wachichepele amene anachiritsidwa, kodi ndi motani mmene Afarisi anamupeputsira iye-nanga ndimotani mmene umbuli wotele wakhala ukuonetseredwa mumbiri? Yohane 9:28, 29; 1 Akolinto 1:18, 19, 26-28.

“Ku mpingo wake kumibadwo ulionse Mulungu amakhala ndi choonadi chapadera ndi ntchito yapadera. Choonadi chimene chimabitsika kwa amzeru ndi ozindikira adziko lapansi chimabvumbulutsidwa kwa ozichepetsa ndi okhala ngati ana. Chimaitanitsa kudzipereka nsembe wekha. Chili ndi nkhondo zoti zimenyedwe ndi zipambano zoti zipambanidwe. Poonekera chili ndi ochiimirira ochepa mwa anthu aakulu akulu adziko lapansi ndimupingo oyendera limodzi ndi dziko lapansi, iwo amatsutsidwa ndi kupeputsidwa …

“Atsogoleri akulu azipembezo amaganiza mum’badwo uno zoyamikira ndi kumanga zikumbutso za iwo amene anadzala mbewu ya choonadi mmibadwo yapita. Kodi ambiri samatembenuka kuchokera kuntchito imeneyi kuti azipondereza pansi mphukira zophuka kuchokera kumbewu yomweyi lero? Kufuula kwa kalekale kumabwerezedwa, `Tiziwa ife kuti Mulungu analankhul ndi Mose; koma s kumene za munthu uyu (Khristu mwa mtumiki amene iye wamutuma) sitiziwa kumene achokera.’ Yohane 9:29. Monga mmibadwo yoyambilira, choonadi chapadera chanthawi ino chimapedzeka, osati ndi akuluakulu achipembezo, koma ndi amayi ndi abambo amene sali ophunzira kwambiri ndi amzeru kwambiri kuti akhulupilire mawu a Mulungu.”- Christ’s Objects Lesson, pp. 78, 79.

b. Kodi ndichisanzo chanji chimene ife tingachiphunzire kuchokera kuumboni owona mtima wamnyamata wachichepere, pamodzi ndi okhulupirira oona ena akhristu? Yohane 9:30-33; Machitidwe 4:19, 20.

“Mwaulemu wonse, muuzimu wachisomo, ndimuchikondi cha Mulungu tikuyenera kuwalodzera anthu kuchoona choti Ambuye Mulungu ndi mulengi wakumwamba ndi dziko lapansi ndikuti tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata la Ambuye.

“Mudzina la Ambuye tikuyenera ife kupita chitsogolo, kutambasula mbendera yake, kuimilira mawu ake. Pamene olamulira atilamula ife kuti tisachite ntchito imeneyi, pamene iwo atiletsa ife kuti tilalikire malamulo a Mulungu ndichikhulupiliro cha Yesu, pamenepo chidzakhala chofunikira kwa ife kuti tilankhule monga anachitira ophunzira…`weludzani ngati mkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu kapena Mulungu. Pakuti sitingathe ife kuleka kulankhula zimene tinaziona ndi kuzimva.’ Machitidwe 4:19, 20.” – Testimonies for the Church, Vol. 6, p. 395.


Lachinayi , Juni 4

4. MALINGALIRO AMDIMA, MACHITIDWE AMDIMA

a. Popedza Afarisi okwiya samafuna kubvomereza umboni, kodi ndi chiyani chimene iwo anachita ndi mnyamata wachichepere amene amachitira umboni za kuchilitsidwa kwake? Yohane 9:34.

“Munthuyu anakumana ndi omufunsa mafunso pamalo awo. Mfundo zimene iye amayankhula zinali zosayankhika. Afalisi anadabwitsika, ndipo anakhala duu- opanda mawu pamaso pa mawu ake osimikizika komanso achindunji. Kwamphindi zochepa panali bata. Kenako Ansembe ndi Arabi amkwiyo anakonza mikanjo yawo moisonkhanisa ngati mwina akuopa kudetsedwa kochokera kukukhuzana ndi iye; anasasa fumbi lakumapadzi awo, ndikuyankhula zonyoza zambirimbiri kwa iye `Wabadwa iwe konse mzoipa, ndipo iwe utiphuzitse ife kodi?’Ndipo iwo anamchosa mkachisi.” – The Desire of Ages, p. 474.

b. Mosiyana, kodi ndimotani mmene Yesu anachitira ndi mnyamata wachichepele? Yohane 9:35-38.

“Munthuyu anazigwetsa yekha pamapadzi ampulumutsi kumupembeza. Osati kuona kwake kwachibadwa kokha kunabwezeretsedwa, koma maso akuzindikira kwake anasegulidwa Khristu anaonetsedwa kumoyo wake, ndipo iye anamulandira iye ngati wotumidwa ndi Mulungu.” – The Desire of Ages, p. 475.

c. Fotokozani kusiyana kwakukulu pakati pa kuchosa maina anthu opanduka ouma mtima kusiyanitsa ndi akhungu ouma mtima okana Khristu kuchotsa kwawo miyoyo imene imakonda kumvera Mulungu? 1mafumu 9:6-9; Mateyu 12: 31, 32; Masalmo 11:3.

“(Wycliffe anaona,) palibe munthu amene moonadi angachotsedwe dzina mumpingo pokhapokha iye atayamba kaye kuzibweletsera pa iye yekha kutsutsa kwa Mulungu.” – Great Controversy, p. 84.

“Kutsusidwa ndi gawo la onse amene Mulungu amawagwiritsa ntchito yolalikira choonadi makamaka chokhuzana ndi nthawi yawo. Kunali choonadi chalero mmasiku a Luther- choonadi chofunikira mwapadera munthawi imeneyo; pali choonadi chalero kumpingo lero… iwo amene akulalikira choonadi chanthawi ino sakuyenera kumayembekezera kulandilidwa ndikukondera kwakukulu kupotsera okonzanso oyambilira. Kulimbana kwakukulu pakati pa choonadi ndi boza, pakati pa Khristu ndi Satana, kuzikulirakulira mwamphanvu mpakana kumapeto a mbiri adziko lino lapansi.”- Ibid., pp. 143, 144.


Lachisanu , Juni 5

5. KUDALITSIKA KUSIYANITSA NDI KUWELUDZIDWA NDI KUUNIKA

a. Kodi ndi chiyani chimene Yesu ananena zokhuzana ndi zotsatira za ntchito yake? Yohane 9:39.

“Gulu la Afarisi linasonkhana pafupi, ndipo kuonekera kwawo kunabweletsa kumalingaliro a Yesu kusiyana koonekera kwa nthawi zonse kuzotsatira za mawu ndi ntchito yake… Khristu anabwera kuzatsegula maso aakhungu, kuzapereka kuunika kwa iwo amene ali mumdima, iye anazilengezetsa yekha kuti ndikuunika kwa dziko lapansi, ndipo chodzizwa chimene changochitidwa kumene chinali umboni waukulu wa utumiki wake. Anthu amene anamuona mpulumutsi pakudza kwake koyamba anakondeledwa ndikuonekera kodzadza kwakupedzeka kwa Umulungu kupotsera kumene dziko linakhala nako mmbuyo mmosemu. Chiziwitso cha Mulungu chinabvumbulutsidwa mwabwino kwambiri. Koma mukubvumbulutsa kotele komweku, chiweludzo chinapita pa anthu. Khalidwe lawo linayesedwa, chimalidzilo chawo chinatsimikizidwa.” – The Desire of Ages, p. 475.

b. Kodi ndimotani mmene Afarisi anayankhira kumawu a Yesu? Yohane 9:40. Pamene iye amayankhula kwa iwo, kodi ndimotani mmene Yesu anaonetsera kulakwa kwawo za khungu la iwo eni? Yohane 9:41.

“Kuoneseledwa kwa mphanvu za Umulungu kumene kunapeleka kwa Munthu wakhungu kuona kwachibadwa komanso kwa uzimu kunawasiya Afarisi mumdima waukulube….Ngati Mulungu sakanachipanga icho kukhala chotheka kwa inu kuti muone choonadi, kusazindikira kwanu sikukanakhala nawo chimo. `koma sopano munena, tipenya.’inu mumazikhulupirira mwanokha kukhala oona, ndikumakana njira yokhayo imene inu mungathe kulandira kuona. Kwa onse amene adzindikira chosowa chawo, Khristu amabwera ndi thandizo lenileni. koma Afarisi samavomeleza chosowa chilichonse; iwo

anakana kuti abwere kwa Khristu, ndipo chotelo iwo anasiidwa mukhungu – limene ndi iwo okha anali olakwa. Yesu anati, `Chimo lanu likhala.”- Ibid.


Lachisanu ndi chimodzi , Juni 6

6. MAFUNSO OBWEREZA PAWEKHA

1. Ndi za chiyani zimene Afarisi anayesesa kuti amupange munthu amene anali wakhungu kale kuti akhulupilire?

2. Kodi ndindani amene amawagwiritsa ntchito Afarisi osakhulupilira?

3. Kodi ndi ndani amene anathandiza mnyamata wachichepele kupeleka mayankho achindunji komanso okhuza?

4. Kodi ndichiyani chimene chinachitika pamene iye molimba mtima, mwapoyera anachitila umboni Khristu?

5. Fotokozani mtundu woopsetsetsa wakhungu, nanga chifukwa chiyani?

 <<    >>