Loyamba
, Juni 8
1. OKUBA NDI MBUSA
a. Kodi ndi motani mmene Yesu anasiyanisira pakati pa okuba ndi mbusa, Nanga ndi phunziro lanji lauzimu limene Iye amalionetsera? Yohane 10:1, 2.
“Khristu anagwiritsa ntchito mauneneri awa [onena zautumiki waubutsa wamesiya, monga mmene analembera mu Yesaya 40:9-11; Masalimo 23:1, Ezekieli 34:23,16,25,28] kwa iye yekha, ndipo iye anaonetsera kutsiyana kwa khalidwe lake laiye mwini ndila atsogoleri a Israeli. Afarisi anali atangothamangitsa kumene munthu mmodzi kuchokera mukhola, chifukwa choti iye anasimikiza mtima kuchitira umboni zamphanvu za Khristu. Iwo anadula moyo umene mbusa oona amaukokera kwa iye yekha muchimenechi iwo azionetsera okha kukhala osadziwa ntchito imene inaperekedwa kwa iwo, ndikukhala osayenera kuchidaliro chawo monga abusa agulu lankhosa. Yesu tsopano akuika pamaso pawo kusiyana pakati pa iwo ndi mbusa wabwino, ndipo iye akuzionesera iye mwini monga woweta weniweni wa gulu lankhosa.” – The Desire of Ages, p. 477.
“Khristu amatikonda ife chifukwa ndiife osowa thandizo ndi odalira.” – Selmons and Talks, Vol. 1, p. 248.
b. Kodi ndiubale wanji umene ulipo pakati pa nkhosa ndi mbusa wawo? Yohane 10:3, 4. Kodi ndi chiyani chimene nkhosa zimachita pamaso pa mlendo? Yohane 10:5.
Lachiwiri
, Juni 9
2. KHOMO LOLOWELA MUKHOLA
a. Kodi ndi motani mmene Yesu anabvumbulutsira kusiyana kwa iye mwini ndi Afarisi? Yohane 10:7-10.
“Khristu ndi khomo lolowela mukhola la Mulungu. Kupyolera pakhomo limeneli ana ake onse, kuyambira munthawi yoyambilira, akhala akupedza polowela. Mwa Yesu, monga zinaonetseredwa muzoimilira, monga zinaphimbilidwa muzizindikiro, monga zinaonetseredwa mumabvumbulutso aaneneri, monga zinaikidwa poyera mumaphunziriro amene anaperekedwa kwa ophunzira ake, ndi muzozizwitsa zimene zinachitidwa kwa ana aanthu, iwo anaona `mwanawankhosa wa Mulungu, amene achosa chimo lake ladziko lapansi’ (Yohane1:29), ndipo kudzera mwa iye iwo abweletsedwa mkati mwa khola lachisomo chake. Ambiri akhala akubwera kuzaphuzitsa ziphuzitso zina zachikhulupiriro cha dziko lapansi; miyambo ndimadongosolo akhala akukonzedwa amene kudzera mwa iwo anthu amayembekezera kulandira kulungamitsidwa ndi mtendere ndi Mulungu, ndipo mukutero kupedza khomo lolowela kukhola lake. Koma khomo lokha ndi Khristu, ndipo onse amene aika zinazake kuti zitenge malo a khristu, onse amene akhala akuyesera kulowa mukhola kudzera munjira ina, ndi okuba ndi ambanda.
“Afarisi sanalowe kudzera pakhomo. Iwo akwela kulowa mukhola kudzera munjira ina osati ya Khristu, ndipo iwo samakwanilisa ntchito ya mbusa oona. Ansembe ndi atsogoleri, Alembi ndi Afarisi, anaononga msipu wamoyo, ndikudetsa akatsupe amadzi amoyo. Mokhulupirika mawu aumboni akufotokoza za abusa aboza amenewa kuti ..`Zofooka simunazilimbitsa; yodwala simunaichilitsa, yothyoka simunailukira chika, yopitikisidwa simunaibweza…koma munazilamulira mwamphanvu ndi moopsa.’ Ezekieli 34:4.” – The Desire of Ages, pp. 477, 478.
b. Kodi ndimotani mmene mbusa woona amasiyanirana ndi olembedwa ntchito? Yohane 10:11-13.
“Akufunika, osati anthu chabe oti angathe kulalikira, koma iwo amene ali ndi chiziwitso chamachitachita achinsinsi cha umulungu, amene angathe kuchitapo kanthu kuzosowa za pompopompo za anthu-iwo amene akumvetsetsa kufunikira kwa udindo wawo monga akapolo aKhristu, ndipo amene mokondwera azasenze mtanda umene iye anawaphuzitsa iwo kuti ausenze.
“Ndichofunikira kwambiri kuti mbusa azilumikizana kwambiri ndi anthu ake, ndipo mukutelo azikhala ozolowelana ndi magawo osiyanasiyana akhalidwe lachibadwa laumunthu. Iye azitha kumasinkhasinkha zimene zikuonekela pa mitima yaanthu, Kotelo kuti iye athe kukonza maphunziro ake kukugwirizana ndi mzeru za omumvetsera ake. Iye mukutelo azaphunzira chikondi chachikulu chimene alinacho iwo okha amene amaphunzira mwachidwi khalidwe lachibadwa ndi zosowa zaanthu.” – Gospel Workers, p. 191.
Lachitatu
, Juni 10
3. MBUSA WENIWENI WABWINO
a. Kodi ndi makhalidwe ena anji ambusa wabwino amene Yesu anawaonetsera? Yohane 10:14, 15.
“Monga mmene mbusa wakudziko lapansi amaziwila nkhosa zake, chotelonso ndimmene mbusa wa umulungu amadziwila gulu lake la nkhosa limene lamwazikana padziko lonse lapansi.`Ndipo inu nkhosa zapabusa panga, ndinu anthu, ndiine Mulungu wanu, ati Ambuye Yehova.’ Yesu akuti, Ndakuchula dzina lako, iwe uli wanga.’ndakulembera iwe pazikhato za manja anga.’ Ezekieli 34:31; Yesaya 43:1; 49:16.
“Yesu amatiziwa ife payekhapayekha, ndipo amakhuzika ndi zofooka zathu. Amatiziwa ife tonse ndi dzina lathu. Iye amadziwa nyumba imene ife timakhala, dzina la wina aliyense amene ali mnyumbamo. Iye nthawi zina anakhala akupeleka mapu kwa akapolo ake kuti apite kunjira yakutiyakuti mumzinda wakutiwakuti, kuti akapeze imodzi mwa nkhosa zake.
“Moyo winaulionse umaziwika modzaza kwa Khritsu monga ngati ndiokhawo umene mpulumutsi anaufera. Ziphinjo za wina aliyense zimakhuza mtima wake. Kulira kopempha thandizo kumafikira mmakutu ake. Iye anabwela kuzakokera anthu onse kwa iye yekha. Iye akuwapempha iwo kuti, `ndisatireni ine’ ndipo mzimu wake umayendayenda pamitima yawo kuti uwakoke iwo kuti abwere kwa iye. Ambiri amakana kuti akokedwe. Yesu amawaziwa otelewo. Iye amaziwanso iwo amene mwachimwemwe amanva kuitana kwake, Ndipo ndiokonzeka kudza pansi pa chisamaliro chaubusa wake. Iye akuti `Nkhosa zanga zimanva mawu anga, ndipo ine ndimaziziwa izo, ndipo zimandisatira ine.’ Iye amasamalira wina aliyense monga ngati kulibenso munthu wina kudziko lapansi.” – The Desire of Ages, pp. 479, 480.
b. Kodi ndi nkhosa zina zotani zimene mwapadera Yesu amaonetsera kukhuzika? Yohane 10:16.
“Yesu amalingalira za miyoyo yonse imene ili padziko lapansi imene yasocheletsedwa ndi abusa abodza. Iwo amene iye amafunitsitsa kuti awasonkhanitse monga nkhosa zapabusa pake abalalikana pakati pa mimbulu, ndipo iye akuti `Nkhosa zina ndili nazo, zimene siziri za khola ili; izinso ndiyenera kuzitenga, ndipo zizanva mawu anga; ndipo zidzakhala gulu limodzi, mbusa mmodzi.’ Yohane 10:16.” – Ibid., p. 483.
“Mulungu ali ndi ngale mumipingo yonse, ndipo sichili kwa ife kumapanga mawu onyoza zamipingo imene ili kudziko lapansi, koma mozichepetsa ndi mwa chikondi, phuzitsani kwa onse choonadi monga chilili mwa Yesu. Lolani anthu kuti aone chifundo ndikuzipereka, lolani iwo aone khalidwe lofanana ndi la Khristu, ndipo iwo azakokeredwa kuchoonadi.” – The SDA Bible Commentary [E.G. White comments], vol. 4, p. 1184.
Lachinayi
, Juni 11
4. MPHANVU ZA UMULUNGU
a. Kodi ndimphanvu yanji yaumulungu imene Khristu analengeza kuti alinayo? Yohane 10:17, 18.
“‘Chifukwa cha ichi Atate andikonda chifukwa nditaya moyo wanga kuti ndikautengeso.’ Ndiko kuti, Atate wanga anakukondani kwambiri inu, kuti iye amandikondanso ine kwambiri chifukwa choti ndinapereka moyo wanga kuti ndikupulumutseni inu. Pakukhala mlowammalo ndi chikole chanu, kudzera mukupereka moyo wanga ndikutenga zothodwetsa zanu, zolakwa zanu, ine ndimakondedwa kwambiri ndi Atate wanga.
“‘Ndili nayo mphanvu yakuutaya, ndi mphanvu ndiri nayo yakuutenganso; lamulo ili ndinalandila kwa Atate wanga.’ Pamene anali monga chiwalo cha banja lamunthu iye anali woti akhoza kufa, monga Mulungu iye anali kasupe wamoyo wadziko lapansi. Iye akanatha kugonjetsa mphanvu za imfa, ndikukana kudza pansi paulamuliro wake; koma mwakufuna mwini iye anasiya pansi moyo wake, kotelo kuti iye akathe kubweletsa moyo ndiumuyaya poonekela. Iye anasenza nchimo ladziko lapansi, kupilira themberero lake, kupereka moyo wake monga nsembe, kuti anthu asazathe kufa kwamuyaya.`Zoonadi iye ananyamula zowawa zathu, ndikusenza zisoni zathu; ….Iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, natunduzidwa chifukwa cha mphulupulu zathu; chilango chotitengela ife mtendere chinamgwera iye; ndipo ndi mikwingwirima yake ife tachilisidwa.Tonse tasochela ngati nkhosa; tonse tayenda yense mnjira ya mwini yekha; ndipo Yehova anaika pa iye mphulupulu ya ife tonse.’Yesaya 53:4-6.” – The Desire of Ages, pp. 483–484.
b. Kodi ndi chiyani chimene chimasogolera anthu kuti atsatire Khristu? Yohane 10:27; 1 Yohane 4:10, 19.
“Simantha oopa chilango, kapena chiyembekezo cha mphoto ya muyaya, zimene zimatsogolera ophunzira a Khristu kuti azimutsatira Iye. Iwo amaona chikondi choposa champulumutsi, chimene chinaonetsedwa mkuyendayenda kwake konse kwa mudziko lapansi, Kuchokera muchodyera cha ng’ombe mu Betelehemu mpaka pa mtanda wakavale, ndipo maonekedwe ake amakopa, ndipo amafewetsa ndikugonjetsa moyo. Chikondi chimadzuka mmutima wa oyang’ana zotelezi. Iwo amanva mawu ake, ndipo iwo amamutsatira Iye.” – Ibid., p. 480.
“Ife tikulingalira zamoyo wake padziko lapansi, nsembe yake kwa ife, ntchito yake kumwamba monga otiimilira wathu, ndi nyumba za chifumu zimene iye akukonzera onse amene amamukonda iye, ndipo ife tingathe kufuula basi kuti,Oo kutalika ndi kuya kwa chikondi cha Khristu!” – The Acts of Apotsles, p. 334.
Lachisanu
, Juni 12
5. CHITSIMIKIZO CHA CHIPULUMUTSO
a. Kodi ndi chitsimikizo chanji chimene Yesu akupereka kunkhosa zake? Yohane 10:28, 29.
“Ngakhale tsopano Iye anakwela kumwamba kupita pamaso pa Mulungu, ndikumagawana nawo mpando wachifumu wachilengedwe chonse, Yesu sanataye khalidwe lake lachikondi. Lero mtima womwewo wachifundo, wonvera chisoni ndiosegukira kumabvuto onse a anthu. Lero dzanja limene linakhomedwa latambasulidwa kuti lidalitse modzadza anthu ake amene ali mudziko lapansi ‘ndipo sitizaonongeka kunthawi yonse ndipo palibe munthu azazikwatula mzanja langa.’ Moyo umene wazipereka okha kwa Khristu ndiwamtengo wapatali kwambiri pamaso pake kupotsera dziko lonse lapansi. Mpulumutsi akanatha kudutsa mumasautso onse akavale kuti moyo umodzi umenewu ukathe kupulumutsidwa muufumu wake. Iye sazataya ingakhale mmodzi waiwo amene iye anawafela. Pokhapokha omutsatila ake asankha kuti amusiye iye, apo ayi Iye azawagwira iwo zolimba. “-The Desire of Ages, pp. 480–483.
b. Kodi ndi pachiyani pamene chitetezo chathu chauzimu ndichitsimikizo chathu chachipulumutso chagonela? Aroma 8:31-39.
“Mmabwalo akumwamba, Khristu akuchondelera za Mpingo wake- kuchonderera za iwo amene iye anapereka mtengo wachiombolo wa mwadzi wake. Zakazaka, mibadwomibadwo, sizingachepetse konse kuthekera kwa nsembe yake yotetezera ngakhale imfa kapena moyo, kutalika kapena kuya, sizingathe kutisiyanitsa ife kuchoka kuchikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu; osati chifukwa choti ife tinamamugwira iye zolimba, koma chifukwa choti iye amatigwira ife zolimba kwambiri. Ngati chipulumutso chathu chimadalira mukuyetsetsa kwa ife eni, sitikanatha ife kupulumutsidwa; Koma icho chikudalira mwa iye amene ali kuseli kwa malonjezo onse. Kumugwira kwathu iye kukhoza kuoneka kofooka, koma chikondi chake ndi chonga cha m’bale wamkulu; pokha pamene ifeyo tikupitiliza mgwirizano wathu ndiiye, palibe wina aliyense amene angatikwatule ife kuchoka mmanja mwake.” – The Acts of Apostles, pp. 552,553.
Lachisanu ndi chimodzi
, Juni 13
6. MAFUNSO OBWEREZA PAWEKHA
1. Fotokozani kusiyana kwa machitidwe pakati pa mbusa ndi wokuba?
2. Ndikudzera muchizindikiro china chanji chimene Yesu akuzifotokoza yekha?
3. Kodi ndi motani mmene amachitila abusa oona ndi nkhosa zawo?
4. Kodi ndi chifukwa chiyani nkhosa zimasatira mbusa osati mlendo?
5. Fotokozani mmene ife tingakhalire otsimikizika zachipulumutso?