Loyamba
, Meyi 18
1. ANA A ABRAHAMU
a. Kodi ndi chodziyeneleza chanji chimene Afalisi amachibwereza kuchilankhula? Yohane 8:33, 39 (mbali yoyamba). Komabe kodi chiyani chimene chimatsimikizira ubale umenewu? Yohane 8:39 (mbali yomaliza), 56; Aroma 9:6-8.
“Afalisi amazinena okha kuti iwo ndiye ana a Abrahamu. Yesu anawauza kuti kuzinena koteleku kungakhazikitsidwe pokhapokha kudzera mukuchita ntchito za Abrahamu. Ana owoona a Abrahamu, adzakhala monga iye amakhalira, moyo omvera nthawi zonse Mulungu. Ndipo iwo sazayesera kufuna kupha Iye amene akulankhula nawo choonadi chimene chinapelekedwa kwa Iye kuchokera kwa Mulungu. Pochita upo otsutsana ndi Khristu, arabi aja sanali kuchita ntchito za Abrahamu. Popanda kulumikizana kwa uzimu ndi iye, kumene kungazaonetsedwe mukukhala ndi Mzimu ofanana ndi iye, ndi kumachita ntchito zofanana ndi iye,amenewo sangakhale ana ake. “Mfundo iyi imanyamula kulemera komweko kofanana ndi funso limene lakhala likufunsidwa kwa nthawi yaiktali mu dziko la chikhristuli-Funso lokhudzana ndi olowa mmalo mwa atumwi. Kukhala mwana wa Abrahamu kumatsimikizilidwa, otsati ndi dzina kapena ubale wakuthupi, komano kufanana kwa khalidwe. Chotelonso kulowa mmalo mwa atumwi sikukudalira pakungotsamutsa ulamuliro wa mpingo, komano kukukhudzana ndi ubale wa uzimu. Moyo umene unaonetseledwa ndi Mzimu wa atumwi, chikhulupiliro ndi kuphunzitsa kwa choonadi chimene iwo amaphunzitsa, uwu ndiye umboni owona wa mlowa mmalo wa atumwi. Ichi ndi chimene chimawapanga anthu kukhala olowa mmalo aaphuzitsi oyambilira a uthenga wabwino.” – The Desire of Ages, pp. 466–467.
Lachiwiri
, Meyi 19
2. OTSATI ZIMENE AMAZINENA MWAMATAMA KUTI ALI
a. Ngakhale Ayuda anali mbumba yeniyeni ya Abrahamu, kodi iwowo anasanduka kukhala ana andani pamene anamukana Khristu? Yohane 8:41-44.
“Yesu anakana kuti Ayuda anali ana a Abrahamu. Iye anati, ‘Inu muchita ntchito za Atate wanu.’ Mwachipongwe iwo anamuyankha, ‘Ife sitinabadwe m’chigololo; tili naye Atate mmodzi, ndiye Mulungu.’ Mawu awa, polumikizana ndi zochitika za kubadwa kwake, anakonzedwa kuti akhale chida chomutsusira Khristu pamaso pa onse amene anayamba kumukhulupilira iye. Yesu sanalabadire mawu oneneza amwanowa, koma anati, ‘Ngati Mulungu akanakhala Atate wanu mukanandikonda ine; popeza Ine ndinatuluka ndi kuchokela kwa Mulungu.’ “Ntchito zawo zimachitila umboni za ubale wawo ndi iye amene anali wabodza ndi wakupha. ‘Inu atate wanu ndi mdielekezi,’ Yesu anatelo, ‘ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuzichita. Iye anali wakupha kuyambila pachiyambi, ndipo samaima mu choonadi chifukwa mwa iye mulibe choonadi… koma ine chifukwa ndinena choonadi, simunkhulupilira ine.’ Yohane 8:44,45. R.V. Choona choti Yesu amalankhula choonadi ndi kutsimikizika konse, ndi chifukwa chake sanalandilidwe ndi azitsogoleri achiyuda. Chinali choonadi chimene chinakhumudwitsa anthu ozilungamitsa okhawa. Choonadi chimaika poyela zolakwika zonse za chinyengo; ndipo chimatsutsa zophunzitsa zawo ndi machitidwe awo, ndipo chinakhala chotsalandilidwa. Ndipo iwo anachiona chinthu chabwino kuti atseke maso awo kuchoonadi koposera kuti angozichepetsa ndi kuvomeleza kuti ali muzolakwika. Iwo sanakonde choonadi. Ndipo iwo sanachikhumbe icho, ngakhale chinali choonadi.” – The Desire of Ages, p. 467.
b. Kodi ndi chiyani chimene chimatipanga ife kukhala ana a Abrahamu- nanga ndi motani mmene adzitsogoleri a chiyuda anaonetsera kuti sanali ana oona a Abrahamu? Agalatiya 3:6-9; Yohane 8:40.
“Popedza sitinalandila mzimu wa ukapolo kuti tiziopa; komano tinalandira mzimu wa umwana, ‘umene tifuula nawo Abba , Atate.’ Mzimu wa ukapolo umabwera kudzera mukufunafuna kukhala molingana ndi chipembezo cha mwambo, ndi kudzera mukuyestetsa kukwaniritsa lamulo mu mphanvu zathu. Pali chhiyembekezo chokhacho kwaife pokhapokha ngati tingabwere pansi papangano la Abrahamu, limene lili pangano la chisomo kudzera mwa chikhulupiliro mwa Khristu Yesu. Uthenga umene unalalikidwa kwa Abrahamu, umene unamupangitsa iye kukhala ndi chiyembekezo, ndi uthenga omwewo umene ukulalikidwa kwa ife lero lino, umene kudzera mwaiwo timakhala ndi chiyembekedzo. Abrahamu anayang’ana kwa Yesu, amene ali woyamba ndi wotsiliza wa chikhulupiliro chathu.” – The Youth’s Instructor, September 22, 1892.
Lachitatu
, Meyi 20
3. KHALIDWE LA KHRISTU
a. Kodi ndi funso lanji limene adani ake a Yesu analephera kuliyankha lokhudzana ndi khalidwe lake losadetsedwa? Yohane 8:46 (Mbali yoyamba).
“M’moyo wake wa pansi pano, Khristu anakudza khalidwe la ngwiro, ndipo iye anapereka kumvera kwa mbambande ku malamulo a Atate ake. Mukubwera ku dziko lapansi mukhalidwe la umunthu, mukukhala ogonjera kulamulo, mukubvumbulutsa kwa anthu kuti iye anasenza kudwala kwawo, nkhawa zawo, zolakwa zawo, Iyeyo sikuti anakhalano munthu wochimwa. Pamaso pa Afalisi iye amanena kuti, ‘Ndani wainu amene anditsutsa ine za chimo?’ Panalibe ngakhale kadontho ka tchimo kamene kanapezeka pa Iye. Iye anaima pamaso pa dziko monga nkhosa yopanda banga ya Mulungu.” – Sons and Daughters of God, p. 25.
“Yesu anakhala moyo osunga lamulo pamaso pa kumwamba, pamaso pa maiko amene sanagwepo, ndi pamaso pa anthu ochimwa. Ndipo iye amalankhula pamaso pa angelo, pamaso pa anthu ndi pamaso pa ziwanda mopanda omutsutsa, mawu amene akanakhala kuti akuchokera pa kamwa pa munthu wina akanakhala kuchitira Mulungu mwano: ‘Ndimachita zinthu zimene zimamutsangalatsa iye nthawi zonse.’” – The Desire of Ages, pp. 467–468.
b. Kupatula izo zimene Yesu anazilankhula monga mwana wa munthu,kodi ndi chiyani chimene malemba anafotokodza zokhudzana ndi khalidwe la Khristu? Ahebri 4:15; 1 Petro 1:18, 19.
“Chikhulupiliro cha anthu mwa khristu monga Mesiya sichikuyenera kukhazikika pa maumboni owoneka ndi maso, kapena kumukhulupilira iye chifukwa cha maonekedwe ake okopa, komano chifukwa cha khalidwe lake la ngwiro limene linapezeka mwa Iye, limene silinayambepo litapedzeka kapena kupedzeka mwa wina aliyense.” – The SDA Bible Commentary (E.G.White Comments), vol.7. p. 904.
c. Kodi ndi motani mmene tingakhuzikile ndi moyo wa Yesu? Afilipi 2:6-8.
“Kodi Chitsanzo chathu sichinayende munjira yolimba, yodzikaniza wekha, ndi yodzipereka nsembe, yodzichepetsa mmalo mwathu ndi cholinga chofuna kutipulumutsa ife? Iye anakumana ndi zokhoma, ndi kukumana ndi zokhumudwitsa, ndi kudzunzika ndi chitonzo komanso mazunzo muntchito yake yopulumutsa ife. Nanga kodi tidzakana kusatira kumene mfumu ya ulemerero akutitsogolera ife munjira? Kodi tidzadandaula za mabvuto ndi mayeselo mu ntchito yoti ifeyo tiyenera kugonjetsa mwakuthekela kumene kunapatsidwa kwaife, Pamene tikukumbukila mazunzo a Mombolo wathu? – Testimonies for the Church, vol.3, p. 371.
Lachinayi
, Meyi 21
4. KHALIDWE LA OTSATIRA A KHRISTU
a. Kodi cholinga chenicheni cha anthu otsatira Khristu ndi chiyani? 1 Petro 1:13-16.
“Ntchito yathu ndiyo kulimbikila kupedza ungwiro mmachitachita athu umene khristu anauonetsera mmoyo wake pa dziko lapansi mmakhalidwe ake onse amachitachita.” – That I May Know Him, p. 130.
b. Kodi ndi motani mmene tingafikile cholinga chimenechi? Ahebri 12:1-4; Agalatiya 5:6 (Mbali yomaliza); Afilipi 3:12-15; 4:13.
“Ndimotani mmene tingafikile ungwiro umene umaonetseredwa ndi ambuye komanso Mpulumutsi wathu Yesu Khristu- Mphuzitsi wathu wamkulu?Kodi tingakwanitse zofuna zake ndi kukwanitsa kufikila muyeso wapamwamba ngati otele? Tikhonza kukwanitsa, apo ayi Khristu sakanatilamulira ife kuti tiyenera kutelo. Iyeyo ndiye chilungamo chathu. Muumunthu wake iye anatitsogolera ife ndi kutionetsera ife ungwiro wa khalidwe labwino. Tikuyenera kukhala ndi chikhulupiliro mwa Iye chimene chimachititsa mwa chikondi ndi kuyeretsa moyo. Ungwiro wa khalidwe umakhazikika pa chimene Khristu ali kwa ife. Ngati tingamakhale ndi kudalira kwa nthawi zonse pa kuyenera kwa Mpulumutsi wathu, ndi kumayenda mmapadzi ake, tizakhala ngati iye, oyera ndi osadetsedwa.”-Ibid..
c. Ndi motani mu zenizeni zake tingakhalire oyera ndi opanda banga pamaso pa Mulungu? Aroma 5:18- 20; Ahebri 10:14.
“Khristu samakhululukira aliyense koma olapadi yekha, komano kwa munthu amene iye wamukhulukira koyambilira komwe amamupangitsa kusweka mtima.” – Selected messages, bk.1.pp.393,394.
“Munthu wochimwa akuyenela nthawi zonse kumayang’ana pa kavali; ndipo ndi chikhulupiliro chophweka ngati cha mwana wa ng’ono, akuyenera kumadalira mukuyenera kwa Khristu, ndi kuvomereza chilungamo chake ndi kumakhulupilira mu chifundo chake…
“Ndi chikondi chotani chotele- ndi chikondi chodabwitsa ndi chotsamvetsetseka motani- chimene chinatsogolera khristu kuti atifere ife tikadali chichimwile chomwecho! Ndi kuluza kotani ku moyo umene wanvetsetsa zofunikila za lamulo za mphanvu, komano amalephela kumvetsetsa chisomo cha Khristu chimene chinaikidwa kochuluka kwaife!” – Ibid., p. 384
Lachisanu
, Meyi 22
5. KHALIDWE LATHU KUKHALANGATI LA IYE
a. Ndi motani mmene tingapangile maitanidwe athu ndi kusankhidwa kwathu kukhala kotsimikizika? 2 Petro 1:4-11; Chibvumbulutso 19:8.
“Mulungu chimene amafuna lero ndi chimene iye amachifuna kwa Adamu, kumvera kwa mbambande, chilungamo chopanda chinyengo, chotsapepuka pamaso pa Mulungu. Mulungu atithandize ife kuti tikakwanirite kwa iye chimene lamulo limafuna kwa ife. Sitingakwanitse kuchita zimenezi popanda chikhulupiliro chimene chimabweletsa chilungamo cha Khristu mmachitachita athu a tsiku ndi tsiku.” – Selected Messages, bk. 2, p. 381.
“Ngati Satana akulamulilabe, tizakhala ndi ntchito yogonjetsa uchimo otibwezeletsa mmbuyo; ndipo nthawi zonse pamene tingakhalire ndi miyoyo, sipazakhala malo oti tipume, kapena kufika muyeso umene tinganene kuti, ndatha kufikapo modzadza ndagonjetsa. Kuyeretsedwa ndi zotsatira za kumvera kwa moyo kwa nthawi yaitali.” – The Acts of the Apostles, pp. 560–561.
“Tikuyenela kudzindikila kuti kudzera mwa chikhulupiliro mwa iye ndi mwayi wathu kuti tikakhale nawo mwayi otenga nawo mbali mu khalidwe la Umulungu ndi kuti chotelo tikathawe chibvundi chimene chili mdziko kudzera mu chilakolako. Pamenepo timayeletsedwa kuchoka ku machimo onse, ndi zolakwika zonse za khalidwe. Ndipo sitikuyenelanso kubwezeletsanso ngakhale mchitidwe umodzi wa chimo…
“Pamene tikutenga nawo mbali mukhalidwe la umulungu, zizolowedzi zonse zolakwika za chibadwa kapena zotengela kwa ena, zimadulidwa mu khalidwe lathu, ndipo timapangidwa kukhala ndi mphanvu zochitila zabwino. Kumphunzira kwa nthawi zonse zaMphunzitsi wa umulungu, ndi tsiku ndi tsiku kumakhala tikutenga nawo mbali mukhalidwe lake, timakhala tikulumikizana ndi Mulungu mukugonjetsa mayesero a Satana. Mulungu amagwira ntchito, ndipo munthu amagwiranso ntchito, ndi kuti munthu akhale limodzi ndi Khristu monga khristu ali amodzi ndi Mulungu..
“Ndi Mulungu amene amatipatsa phanvu zogonjetsera. Iwo amene amanvera mawu ake ndikumbvera malamulo ake amayenelezedwa kupanga makhalidwe achilungamo.” – The SDA Bible Commentary(E.G White comments) Vol 7.p, 943.
Lachisanu ndi chimodzi
, Meyi 23
6. MAFUNSO OBWEREZA PAWEKHA
1. Kodi ndi chifukwa chiyani Afalisi sangathe kupeza moyo osatha pakungotengela pa ndanda wa chibadwa chawo chakumene anabadwira kapena wina aliyense wa ife lero kumadalira makolo kapena D.N.A monga chinthu chopezera chipulumutso?
2. Fotokozani makhalidwe enieni owona aana a Abrahamu?
3. Motengela ndi khalidwe lake, kodi ndi chiyani chimene Yesu amakwanitsa kuchifotokoza?
4. .kodi ndi cholinga chanji chimene chinayikidwa pa maso pa Mkhristu aliyense kuti achifikile?
5. Ndimotani mmene tingapezedwere kukhala angwiro ndi opanda banga pa maso pa Mulungu?