Back to top

Sabbath Bible Lessons

Uthenga Wabwino Malinga ndi Yohane (GA WO LACHIWIRI)

 <<    >> 
  SABATA, JUNI 7, 2025

Zopereka Sabata Loyamba

Zamachalichi Awiri Mu Tamil Nadu, India

Maumboni azokumbakumba amaonetsera kuti ingakhale kuyambira muzaka za mma 2600 B.C,Chitukuko cha mmizinda cha gulu la Indus chinazakhala mudela limene lelo limachedwa kuti India. Chipembezo chachikulu chachikoka kumeneku chakhala chili chi Hindu(79.8%), Chosatila ndi chisilamu (14.2%),Chikhristu (2.3%),Sikchism(1.7%) ,ndi zina. Ngakhale pali mbili zina zakulumikizana ndi a SDA Reform Movement zilipo kuyambila mu 1920 ndi 1950, ndimu 1987 mmene kumpoto kwa India kunakhala ndi oimilirako oyambilira obvomelezeka pansonkhanu wakulu wa General Conference wa SDARM.

Mzinda wakummwera kwa India- Tamil Nadu- umatengedwa kukhala nkhokwe yamphanvu ya zokonzakonza komanso ulimi. Ntchito ya Ambuye inakhazikisidwa kumeneku kwa zaka zambiri, Koma kutumikira chiwelengelo chachikulu cha anthu choposa 72 milion mzinda umenewu, pakusoweka kukhala ndi mautumiki amphanvu.

Molingana ndi chiwelengelo cha anthu chaku india chamu 2001, mudzi wa Pattiveeranpatti uli ndi chiwelengelo chokwana 7,744. Chiwelengelo chaanthu ophunzira ndi 83%, chachikulu kwambiri kuposa chaanthu adziko lonse la India. Chinthu chachikulu chimene chimabweletsa ndalama mmanyumba ambiri ndi ulimi wa khofii, otsatilapo wanthochi, wamaolenji, wa cardamom, wasabola, ndi ma spice ena. Mudzi waukulu ndi pallapatti ndi okhala ndi chiwelengelo cha anthu okwana 13,701.

Kuyambira mu 1998, ntchito yosatopetsa yaolalikira uthenga wochokera ku Periyaklam yathandiza kukuza chiwelengelo cha ziwalo zampingo makamaka mmadela awiri amenewa. Zobechela zosiyanasiyana zapangitsa kukhala chovuta kwambiri kupiliza kukhala nyumba zobweleka, Chotelo panthawi ino, abale ammudzi mwa Pattiveeranpatti ndi Pallapatti akufunika malo awoawo opembezera.

Mzimu wachinenelo mwapadela umanena za India monga malo amene “Zikwizikwi za anthu sizinamvepo kwambiri za Mulungu ngakhale za chikondi chake chomwe chinabvumbulutsidwa mwa Khristu. Ndiufulu wawu kulandira chiziwitso chimenechi. Iwo ali ndichoyeneleza chofanana ndi chathu muchifundo cha mpulumutsi.” – Education p 263

Chotelo mwaulemu tikupempha abale ndi alongo athu kudziko lonse lapansi kuti mupeleke thandizo lanu lolowa mmanja kuti timange nyumba zakuunika za ambuye kuti ziziwala midzi imeneyi. “Ndi ntcchito yakuimilira malamulo aMulungu ndikumanga malo abwinja amene anapangidwa mulamulo lamulungu, tikuyenera ife kusakaniza chifundo kwa mtundu waanthu obvutika. Ife tikuyenera kuonetsera chikondi chachikulu kwa Mulungu; Tikuyenera kukweza chikumbutso chathu.”-Welfare Ministry,p 32. Tikukuthokozani inu, ndipo Ambuye athe kudalitsa mphatso ndi opereka!

Abale ndi alongo anu ochokela ku Pattiveeranpatti ndi Pallapatti.

 <<    >>