Back to top

Sabbath Bible Lessons

Uthenga Wabwino Malinga ndi Yohane (GA WO LACHIWIRI)

 <<    >> 
PHUNZIRO 6 SABATA MEYI 10, 2025

YESU, KUUNIKA KWA DZIKO LAPANSI

VESI LOLOWEZA: “Pamenepo Yesu analankhulanso nao, nanena, Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata Ine sazayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo” (Yohane 8:12).

“Monga momwe mwedzi ndi nyenyezi zomwe zili mauniko athu zimawalira kudzera mu kuwala kochokera ku dzuwa, choteronso, ngati chiphunzitso chao chili choonadi, ndi momwe anthu anzeru zakuya a kudziko lapansi amawalitsira milezo ya Dzuwa la Chilungamo. Lingaliro lina lililonse, kutwanima kwa nzeru, ndi zochokera ku Kuunika kwa Dziko Lapansi.” – Education, p. 14.

Zowelenga Zoonjezera:   Testimonies for the Church, vol. 1, pp. 405–409

Loyamba , Meyi 4

1. KUBWEZERETSA CHILENGEDWE

a. Kodi ndi chiyani chimene Mulungu analenga pa tsiku loyamba la kulenga? Genesis 1:3-5.

“Pa liwu lakulenga pachiyambi, kuunika kunawalira kuchoka mundima.” – The Desire of Ages, p. 464.

b. Kodi ndi ndani amene analipo pakulengedwa kwa dziko lapansi- osati monga ongoonerera chabe, koma monga otenga nawo gawo mukulenga? Genesis 1:1, 2; Yohane 1:1, 2; Akolose 1:16.

“Pachiyambi, Mulungu amabvumbulutsidwa mu nchito zonse za kulenga. Ndi Khristu amene anayala thambo, ndi kuika madziko a dziko lapansi…Ndi Iyeyo amene anazaza dziko lapansi ndi zokongoletsa, ndi kuzaza mlenglenga ndi nyimbo. Ndipo pa zinthu zonse za padziko , ndi za mlengalenga, ndi za mu mpweya, Iye analembamo uthenga wa chikondi cha Atate.”- Ibid., p. 132.

“Dzanja limene limagwirizitsa maiko mlengalenga, dzanja limene limagwira zinthu zonse mwadongosolo ndi mosatopa kumayendetsa zochita zonse za muchilengedwe chonse cha Mulungu, ndi dzanja lomwelo limene linakhomeledwa pa mtanda chifukwa cha ife.” – Education, p. 132.


Lachiwiri , Meyi 5

2. KUUNIKA MU CHIPULULU

a. Kodi ana a Isalayeli amasongoloreredwa motani mu chipululu? Eksodo 13:21, 22.Fotokozani amene anaphimbika mu mtambo njo ndi mmotonjo? Eksodo 13:21 (mbali yoyamba); 1 Akorinto 10:1-4.

“Mukuonekera kwa Mulungu kwa anthu ake, kuwala kwakhala nthawi zonse kwakhala kuli chizindikiro cha kupezeka kwake. Pa mau akulenga pa chiyambi, kuunika kunawala kuchokera mundima. Kuunika kunaphimbidwa mu ntambonjo masana ndi mumoto njo usiku, kutsogolera khamu lalikulu la israyeli.” – The Desire of Ages, p. 464.

b. Kodi zinalembedwa zotani zokhuza kupedzeka kwa Khristu ndi ana a Israyeli muchipululu – nanga kodi ndi chitetezo chanji chimene Mulungu anachilonjeza kwa anthu ake? Masalimo 105:39; Yesaya 4:5, 6.

“Mu limodzi mwa malembo okongola ndi otonthoza kwambiri a uneneri wa Yesaya, akunena za mtambo njo ndi moyo njo kuimirira chisamaliro cha Mulungu kwa anthu ake mu kulimbana komaliza ndi mphamvu za zoipa.” – Patriarchs and Prophets, p. 283.

c. Kodi ndi motani mmene Khristu anazionetsera yekha pa Sinai – nanga kodi ndi motani mmene Mose ndi anthu anachitira? Eksodo 19:16-18; 20:18,19; Aheberi 12:21

“‘Ulemelero wa Mulungu unali ngati moto wonyeketsa pamwamba pa phiri’ pamatso pa khamu limene linasonkhana…Zionetsero za Yehova zinali zoopsa kwambiri kotelo kuti khamu la Israeli linanjenjemera ndi mantha, ndipo anagwetsa nkhope zawo pansi pamaso pa Ambuye”- Ibid., p. 304.

“Ulemerero unali waukulu kwambiri wakuonekera kwa Khristu kotelo kuti sizikanatheka kuti munthu wakuthupi athe kuyang’anapo. Mose, amene anali wokondeledwa kwambiri ndi Mulungu, anafuula kuti ‘ndili ndi mantha aakulu koposa’. Koma mulungu anamulimbikitsa iye kuti apilire ulemelero waukulu umenewo, ndikubweletsa kuchokela mphiri kunyezimilira kwaulemerero pa nkhope pake kotelo kuti anthu sanathe kuyang’anitsitsa pa iwo.”- Sons and Daughters of God, p. 225.


Lachitatu , Meyi 6

3. KUUNIKA PAMALO POKHALA MULUNGU

a. Kodi ndimotani mmene Khristu amaonetsera kupedzeka kwake Muchihema? Ekisodo 40:34, 35.

“Ndi chidwi chachikulu khamu lalikulu la Israeli linasonkhana kuzungulira kuti lione chomangidwa chopatulika. Pamene iwo anali kulingalira zachochitikachi ndi kukhutitsidwa kwakukulu, mtambo unatsika ndikuvindikila chihema.`Ndipo ulemerero wa Ambuye unadzadza muchihema.’Panali kubvumbulutsidwa kwa olemekezeka wa umulungu, ndipo kwakanthawi ngakhale Mose sanathe kulowamo. Ndi mantha aakulu anthu anayang’ana chizindikilo choti ntchito ya manja awo inalandilidwa. Panalibe mfuwu owonetsera chimwemwe. Bata lopatulika linakhala pa onse. Koma kusangalala kwa mmitima yawo kunaonekela mmisozi yachimwemwe ndipo iwo anang’ung’uza pansipansi, mawu otsimikizika achiyamiko oti Mulungu watsika kuti adzakhale pamodzi ndi iwo.”- Patriachs and Prophets, pp. 349,350.

“Pamwamba pa mpando wachisomo panali Shekina, kuonetseredwa kwa kupedzeka kwa umulungu; ndipo kuchokela pakati pa Akelubi, Mulungu amadzindikilitsa chifuniro chake. Mauthenga a Mulungu nthawi zina amapelekedwa kwa wamsembe wamkulu kudzera mmawu ochokela mumtambo. Nthawi zina kuwala kumagwa kuchokela kwa ngelo wakuzanja lamanja, kuonetsera kubvomeleza kapena kulandila, kapena mthuzi kapena mtambo umagwela paiye wakudzanja lamamzere kuonetsera kukana kapena kusabvomeleza ” – Ibid.

b. Kodi ndi chiyani chimene chinachitika patadutsa nthawi, munthawi imene kachitsi amapatulidwa? 2 Mbiri 7:1.

“Chihema cha ulemelero kwambiri chapangidwa, molingana ndichisanzo chimene chinaonetsedwa kwa Mose mphiri, ndipo kenako kuonetseredwa ndi Ambuye kwa Davide. Kachisi wapadziko lapansi anapangidwa mofanana ndi wakumwamba. Kuphatikiza akelubi omwe anali pamwamba palikasa, Solomoni anapanganso angelo ena awiri okulilanso, wina aliyense anaima pambali pa likasa, Kuimilira Angelo akumwamba amene nthawi zonse amateteza lamulo la Mulungu. Ndizosatheka kufotokoza kukongola ndiulemerero wa kachisi ameneyo. Mmenemu, monganso mkachisi, Likasa lopatulika linaikidwa pamalo polemekezeka kwambiri, pansi pamapiko aakelubi awili amene anaima mbali zonsezonse.

“Oimba nyimbo zopatulika analumikiza mawu awo, ndi zida zoimbila za mitundu yonse, mukuyamika Mulungu. Ndipo pamene mawu ogwirizana ndi zida zoimbila nyimbo, amanveka modzadza kachisiyu, ndikumanveka muYelusalemu monse, mtambo waulemelero wa Mulungu unasikila ndikukhala mnyumbayi, monga mmene mbuyomuja unazazira muchihema. ‘ndipo chinachitika, kuti pamene ansembe anatuluka kuchoka mmalo opatulika, mtambo unadzadza mnyumba ya ambuye, kotelo kuti ansembe sanathenso kuima kuti atumikile chifukwa cha mtambo,pakuti ulemelero waambuye unadzadza mnyumba ya Yehova.’”-Spritual Gifts, vol 4a, pp. 113,114.


Lachinayi , Meyi 7

4. KUUNIKA KWA UTHENGA WABWINO

a. Kodi ndiuthenga wanji wa Khristu mu Yohane 8:12 umene ukubweletsa chiyembekezo chachikulu kwa ife?

“Siazibusa ophunzira kwambiri amene ali ndikumvetsetsa kwa choonadi chimenechi, ndikugwilitsidwa ntchito mukuchilalikira icho. Ngati awa akanakhala alonda okhulupilika kufufuza malembo mwapemphero ndi mwakhama, Iwo akanatha kuziwa nthawi yautsiku; mauneneri akanatha kusegulidwa kwa Iwo zochitikachitika zimene zinali pafupi kuti zichitike, koma iwo samagwira ntchito imeneyi, ndipo uthenga unapelekedwa kudzera mwa anthu ozichepetsa… Iwo amene atembenuka kuchoka kukuniika kumene Mulungu wakupeleka, kapena amene anyozera kufunafuna kuunikako pamene kuli pafupi ndiiwo, amasiidwa mumdima.” – The Great Controvesy, p. 312.

“Ambuye anapanga chikonzero chinachilichonse kotelo kuti ife tikathe kukhala ndichiziwitso chachimwemwe, chichikulu ndi chozaza.Yohane akulemba zokhuzana ndi Khristu, kuti, ‘mwa iye munali moyo; ndipo moyowo unali kuunika kwaanthu.’ Moyo ukulumikizana ndi kuunika, ndipo ife ngati tilibe kuunika kochokela ku Dzuwa la Chilungamo, sitingathe kukhala ndi moyo mwa iye. Koma kuunikaku kunapelekedwa kuti kukakhale kwa moyo wina ulionse, ndipo ndipokhapokha pamene ife tikupatuka kuchoka kukuniika kuti mdima umabwela kwa ife. Yesu anati, ‘Iye amene akundisatila ine sazayenda mumdima, koma azakhala nako kuunika kwamoyo.’ Motizungulira ife mudziko lapansi simungakhale moyo popanda kuunika. Ngati dzuwa lingachotse kuwala kwake, mbewu zonse, moyo wa nyama zonse uthera pomwepo. Ichi chikuonetsera choona choti ife tingathe kukhala nawo moyo wauzimu pokhapokha ife titaziika tokha pansi pamiledzo la Zuwa la Chilungamo. Ngati ife tingaike mtengo wamaluwa muchipinda cha mdima, iwo mwachangu unyala ndikufa; ndipo chotelo ife tingathe kukhala nawo kamoyo ka uzimu, komabe kuutaya kudzera mukukhala mmalo odzungulilidwa ndi kukaika ndi kukhumudwa.”- Sons and Daughters of God, p. 281.

b. Kodi ndi chitsimikizo chanji chimene chikubwela pamene ife tikutembenukira kwa Khristu? 2 Akolinto 3:18.

“Monga momwe duwa limatembenukila kudzuwa kotelo kuti miledzo yake yowala ikathe kuthandizira mukukongoletsa kukongola kwake ndimaonekedwe ake, Chotelo otsatila Akhristu akuyenera kutembenukira ku Dzuwa la Chilungamo, kotelo kuti kuunika kwa kumwamba kukathe kuwalira pa iwo kuyeretsa makhalidwe awo, ndikuwapatsa iwo chiziwitso cha kuya ndichokhazikika muzinthu za Mulungu. Ndichoposa mphanvu zathu kuzindikila madalitso amene abweletsedwa chifupi ndiife kudzera mw a Khristu, koma pokhapokha ngati ife tingalumikize kuyetsetsa kwathu kwa umunthu ndi chisomo cha umulungu.”-Ibid p. 26

“Wina aliyense amene ali ndi cholinga chimodzi chokha chakufunafuna kuchita chifunilo cha Mulungu, moona mtima kumasatila kuunika kumene kwapelekedwa, adzalandira kuunika kwakukulu; kumoyo umenewu nyenyezi inayake ya kuwala kwakumwamba izatumizidwa kuti izimutsogolera iye muchoonadi chonse.”-The Great Controversy, p. 312.


Lachisanu , Meyi 8

5. KUWALILA MITIMA YATHU

a. Kodi ndimotani mmene ife tingakwezedwe pamwamba kuzera kukufotokoza kolimbikitsa kwa Paulo kokhuza kuunika kwadziko lapansi? 2 Akolinto 4:6.

“Lolani kuti malingaliro a ulemerero a Mulungu adzaze mu mtima wanu. Lolani kuti moyo umangililidwe pamodzi ndi zingwe zobisika kumoyo wa Yesu. Iye amene analamulila kuti kuwala kuwalire kuchoka mumdima ndiofunitsitsa kuti awalire mmitima yanu, kuti apeleke kuunika kwa chiziwitso chaulemelero wa Mulungu pankhope pa Yesu Khristu. Mzimu woyela uzatenga zinthu za Mulungu ndikuzionetsa izo kwa inu, kuzisamutsila izo monga mphanvu za moyo kupita nazo mumtima womvela. Khristu azasogolera inu kupita nanu kumsipu wamuyaya, muzaona ulemelero kupyola chophimba, ndikumbvumbulutsa kwa anthu kukwanila kwa Iye amene ali ndi moyo chikhalire kutipembezera ife.” – Christ’s Object Lesson, p. 149.

“Kubvumbulusidwa kwa ulemelelo wake muthupi la umunthu zizabweletsa kumwamba pafupi kwambiri ndi anthu kotelo kuti kukongola konyezimila kwa mkati mwa kachisi kuzaonekela mmoyo wina ulionse umene Khristu Mpulumutsi akukhalamo. Anthu azakopeka ndiulemelero waKhristu wokhala mkati. Ndipo mumiledzo yachiyamiko ndi kuthokoza kuchokela mumiyoyo yambili imene yapindulidwa mwa Mulungu motelemu, ulemelero uzasefukila ndikupita kwa opeleka wamkulu.

‘Nyamuka, wala pakuti kuunika kwako kwafika, ndi ulemelero wa Yehova wakutulukira.’ Yesaya 60:1. Kwa iwo amene akupita kukakumana ndi mkwati uthenga uwu unapelekedwa. Khristu akubwela ndi mphanvu ndiulemelero waukulu. Iye akubwela ndiulemelero wa Iye mwini komanso ndiulemelero wa atate. Iye akubwela ndi angelo onse oyela pamodzi ndi Iye. Pamene dziko lonse lapansi lazazidwa ndi mdima, padzakhala kuunika konsekonse pamene akukhala olungama. Iwo adzaona kuunika koyambilira kwakubwela kwake kwachiwili. Kuunika kosadetsedwa kuzawalira kuchokela mmaonekedwe ake aulemelero, ndipo Khristu mombolo azasililidwa ndi onse amene anamutumikila iye. Pamene oyipa azathawa kuchoka pamaso pake, otsatila a Khristu azakondwera.”- Ibid., pp. 420, 421.


Lachisanu ndi chimodzi , Meyi 9

6. MAFUNSO OBWEREZA PAWEKHA

1. Kodi ndi motani mmene Baibulo limaphuzitsira zokhuzana ndi umulungu muntchito ya kulenga?

2. Fotokozani mmene Yesu anazionetsera mwini yekha kwa anthu ake Muchipululu.

3. Kodi ndi motani mmene kuunika kwa Yesu kunawalira muchihema ndi mukachisi?

4. Fotokozani mmene Yesu anazionetsera mwini Yekha mukupatulidwa kwa kachisi.

5. Kodi ndi motani mmene Khristu amazibvumbulutsila mwini yekha kwa ife ndikudzera mwa ife?

 <<    >>