Zopereka Sabata Loyamba
Za Mauthumiki a pa dziko Lonse
Lero, uthenga wa panthawi yake ukumvekanso:
“Mzimu wa umishonale uyenera kudzutsidwanso m’mipingo yathu. Membala aliyense wa mpingo ayenera kuphunzira momwe angathandizire kupititsa patsogolo ntchito ya Mulungu, mu ma mission a kunyumba ndi am’maiko akunja. Pafupifupi gawo limodzi mwamagawo 1,000 la ntchito imenei ikuyenera kuchitidwa m’magawo a amishonale ikuchitika mochepa kwambiri. Mulungu akuitana antchito Ake kuti amuwonjezere malo atsopano. Pali minda ya chonde kwambiri yomwe ikuyembekezera wantchito wokhulupirika. Ndipo angelo otumikira adzagwirizana ndi membala aliyense wamumpingo amene adzagwira ntchito mopanda undekha chifukwa cha Ambuye.
“Mpingo waKhristu pa dziko lapansi unakhazikitsidwa ndi cholinga cha utumiki, ndipo Ambuye akufuna kuona mpingo wonse ukukonza njira zomwe anthu apamwamba ndi otsika, olemera ndi osauka, angamvere uthenga wa choonadi. Si onse amene amaitanidwa kukagwira ntchito eni okha m’maiko akunja, koma onse angachite china chake mwamapemphero awo ndimphatso zawo kuthandiza ntchito ya umishonale.
“Wamalonda wina wa ku Amereka amene anali Mkristu wolimbikira, pocheza ndi wantchito mnzake ananena kuti iye mwiniyo amagwirira ntchito Khristu maola makumi awiri ndi anayi a tsiku. ‘Muzamalonda zanga zonse,’ iye anatero, ‘ndimayesetsa kuimira Mbuye wanga. Pamene ndili ndi mwayi, ndimayesetsa kukopa ena kwa Iye. Tsiku lonse ndi kugwirira ntchito Khristu. Ndipo usiku, pamene ndilikugona, ndili ndi munthu womugwirira ntchito Khristu ku China.’
“Pofotokoza iye anawonjezera kuti: ‘Mu ubwana wanga ndinatsimikiza mtima kupita monga mmishonale kwa anthu akunja. Koma bamboo anga atamwalira ndinatenga bizinezi yawo kuti ndizipeza zofunikira za pabanja langa. Tsopano, m’malo moti ndizipita ndekha, ndimathandiza mumishonale. M'tauni yotere yachigawo chotere cha China, wantchito wanga amaima. Ndipo kotero, pokhala ine m’tulo, ndikhala ndikumugwirira ntchito Kristu kudzera mwa wondiimira. ”— Testimonies for the Church, vol. 6, pp. 29, 30 .
Tsopano kuposa kale ndi nthawi yoti muyike ndalama mu banki ya Kumwamba kudzera mu mamishoni a padziko lonse lapansi. Sizidzakhala zosavuta, ndipo m’tsogolo mutha kukhala mochedwa kwambiri. Miyoyo ikuwonongeka wopanda Khristu ndi choonadi chamunthawi ino, ndipo Ambuye watipatsa kuwala kwa mtengo wapatali kuti tifalitse dziko lonse lapansi.
Chonde perekani mowolowa manja, ndipo Ambuye akudalitseni kwambiri ndi mphatso yanu. Zikomo!
A Dipatimenti ya Sabata sukulu ya General Conference