Back to top

Sabbath Bible Lessons

Uthenga Wabwino Malinga ndi Yohane (GA WO LACHIWIRI)

 <<    >> 
  SABATA, EPULO 5, 2025

Zopereka Sabata Loyamba

Zomangira Tcharichi ku Prokhorovka, Russia

Russia, potengela malo, ndi dziko lalikulu kwambili padziko lonse lapansi, liri ndi malo okwanila 6,612,073.2 sikweya mailosi (17,125,191km) lili ndi chiwelengelo cha anthu okwana 147,000,000. Anthu ochokela mumaiko oposa 180 amakhala mudziko lalikulu limeneli. Chifukwa cha ichi, Iwo amasatila zikhulupiliro za zipembezo zosiyanasiyana. Chimene chilli ndi anthu kwambili ndi chipembezo chochedwa Russsian Orthodox (41.1%), kutsatidwa ndi zikhulupiliro zina zachikhristu (6.3%),Chisilamu(6.5%), Neopagans ndi Tengrist (1.2%), Buddhism(1.22%),Osakhulupilira(25.2%),Anthu osakhulupilira kuti kuli Mulungu(13%),ndi ena osala oti Sali pa mpingo wina ulionse.

Chiyambileni SDARM, uthenga wabwino wosatha wakhala ukukula kuno pansi pa zochitikachitika zovuta kwambili. Ambili mwa okhulupilira akhala akusautsika ndi zitsautso zazikulu kwambiri-ndipo ena alalikila za mombolo opachikidwa ndikuukitsidwa ndikutaya miyoyo yawo.

Kumamaliziro kwa 1990 mlaliki wauthenga wabwino ndi mkadzi wake anasamukila mudela lapakati ladziko la Russia ndicholinga chopititsa patsogolo ntchito ya Uthenga wabwino. Monga chotsatila cha kuyetsetsa kwawo ndi mapemphero awo, gulu la okhulupilira linakonzedwa. Koma iwo analibe malo okomanilana ndi kupemphera. Mapeto ake, muchaka cha 2006 iwo anapeza nyumba yaing’ono pamalo ena mudela la Prokhorovka, dela lapatikati lotukuka lantchito za utsogoleri laboma la Prokhorovsky mu Belgorod Oblast-dela la zaulimi limene limalima zambewu, mizimbe, mpendazuwa, ndizipatso mmbali mwa msinje wochedwa PSYOL kummawa kwa mzinda wa Kursk, mmene uli ndi migodi yaikulu kwambili ya Iron.

Ife tikuona mwachindunji zanja la Mulungu likugwira ntchito pamene Iye mozizwizwitsa anachotsa zochinga zambiri ndikudalitsa kugula kwa nyumba imeneyi.Ntchito mudela limeneli yakhala ikupitilira kukula, Ndipo sipanatenge nthawi kuti nyumba ikhale yochepa kwambiri kuti ikwanire kukhalamo anthu onse opembeza Mulungu. Zaka zochepa zapitazo, tinalandila chilolezo chochokela kwa atsogoleri aboma ndikuyamba kumanga nyumba yopempherera. Abale anapeleka thandizo ndikugwira ntchito mwakhama, Koma kuti timalidze ntchitoyi tikusowa thandizo loolowa manja laanthu kudziko lonse lapansi amene amamukonda Ambuye. Kumalidza kwa ntchito imeneyi kudzapeleka mwayi wakupititsa patsogolo ntchito ya uthenga wabwino mmadela odzungulira, monga chidzindikilo chakuunika mukufalitsa uthenga womalidza wachipulumutso. Tilole Ambuye kuti adalitse wina aliyense amene mtima wake ndiokonzeka kuthandiza kupita patsogolo kwa choonadi chalero!

Abale ndi Alongo anu kuchokela kumpingo wa Prokhorovka ndi Unioni ya Russia

 <<    >>