Back to top

Sabbath Bible Lessons

Uthenga Wabwino Malinga ndi Yohane (GA WO LACHIWIRI)

 <<    >> 
PHUNZIRO 1 SABATA, EPULO 5, 2025

YESU, MKATE WA MOYO

VESI LOLOWEZA: “Yesu anati kwa iwo, Ine ndine mkate wa moyo; iye amene adza kwa Ine sadzamva njala, ndi iye amene akhulupilira Ine sadzamva ludzu nthawi zonse” (Yohane 6:35).

“Timadya thupi la Khristu . . . pamene tigwira zolimba pa Iye mwa chikhulupiliro monga mpulumutsi wathu.”—The SDA Bible Commentary [E. G. White Comments], vol. 5, p. 1135.

Zowelenga zoonjezera:   Thoughts From the Mount of Blessing, pp. 18–21

Loyamba , Marichi 30

1. CANGU CHOFUNA KUTCHUKA

a. Chitatha kuchitika chozizwitsa cha mikate, kodi anthu ambiri anakhala ndichikhulupiliro chotani? Yohane 6:14. Kodi amkafunitsitsa kuchita chiyani? Yohane 6:15 (gawo loyamba).

“Tsiku lonse chikhulupiliro chinalimbikitsika. Mchitidwe womalizira umenewo unali chitsimikizo choti Mpulumutsi woyemebekezeredwa kwa nthawi yayitali ali pakati pawo. Ziyembekezo zonse za anthu zinakwera pamwamba kwambiri. Uyu ndiye amene azamupanga Yudeya kukhala paradizo wapadziko lapansi, dziko loyenda mkaka ndi uchi. Iye akhonza kukukhutiritsa khumbo lilironse. Iye angathe kthyola mphamvu za Aroma odanidwa. Iye angathe kupulumutsa Yuda ndi Yerusalemu. Iye angathe kuchiritsa Asilikali ovulazidwa mu nkhondo. Iye akhonza kupereka chakudya kwa khamu lonse la nkhondo. Iye akhonza kugonjetsa amitundu, ndi kupereka kwa Irayeli ulamuliro omwe wakhala ukufunidwa kwa nthawi yayitali.

“Mwa changu chawo, anthu anali okonzeka nthawi yomweyo kumuveka Iye ufumu. Iwo anawona kuti Iye sachita kuyesetsa kulikonse kuti akope chidwi kapena ulemu wa kwa Iye mwini. Mwa ichi Iye anali wosiyana kwambiri ndi Ansembe ndi Olamulira, ndipo amaopa kuti Iye sadzaumiliza konse ndi kunena kuti atenge mpando wachifumu wa Davide. Atatha kufunsana pamodzi, adagwirizana kuti amugwire Iye mwa mphamvu, ndi kumutchula Iye kuti ndi Mfumu ya Israeli. Ophunzira adagwirizana ndi khamu la anthu ponena za mbuye wao kukhala wolowa woyenera kukhalapo pa mpando wa chifumu wa Davide. Iwo amati, chifukwa cha kudzichepetsa kwa Khristu, kudamupangitsa Iye kukana ulemu oterewo. Bola anthu akweze mpulumutsi wawo. Kuti Ansembe odzikuza ndi Olamilira akakamizidwe kumulemekeza Iye amene wabwera atabvekedwa ndi ulamuliro wa Mulungu.”—The Desire of Ages, pp. 377, 378.


Lachiwiri , Marichi 31

2. KUZIZILITSA CHANGU CHOLAKWIKA

a. Kodi Yesu anachita chiyani kuti alepheretse anthuwa ndi ophunzira kuti akwaniritse zolinga zawo kuti amuike Iye pampando wachifumu wapadziko lapansi? Yohane 6:15.

“[Ophunzirawo ndi khamulo] mwakhama anakonza zakuti akwaniritse cholinga chawo; koma Yesu akuwona zomwe zikuyendayenda. Ngakhale tsopano ansembe ndi olamulira akusaka moyo wake.Iwo akumuneneza Iye za kuchotsa anthu kwa iwo.Chipolowe ndi kuukira kutha kuchitika potsatira lingaliro la kumuika Iye pa mpando wa chifumu, ndipo nchito ya ufumu wauzimu isokonezedwa. Popanda kuchedwachedwa lingaliroli likuyenera kuimitsidwa. Anaitana ophunzira Ake, nawalamulira kuti atenge bwato ndikubwerera nthawi yomweyo kupita ku Kapernao, ndikumusiya kuti abalalitse anthu.

“Mbuyo monsemu sanakhalepo ndi lamulo lochokera kwa Khristu lomwe limawoneka losatheka kulikwaniritsa. Ophunzirawo anali atayembekezera kwa nthawi yaitali mgwirizano wamphamvu wotere kuti ayike Yesu pampando wachifumu; Iwo sanathe kupirira lingaliro loti khumbo lonseli lithetsedwa. Ambiri omwe anali kusonkhana kuti asunge paska anali ndi nkhawa kuti awone mneneri watsopanoyo. Kwa otsatira ake izi zidawoneka ngati mwayi waukulu wakukhazikitsa Mbuye wawo wokondedwa pa mpando wachifumu wa Israeli. Mukukula kwa khumbo latsopanoli chinali chovuta kuti achoke paokha, ndikusiya Yesu yekha pagombe lopanda malo okhala lija. Iwo adatsutsana ndi chikonzerochi; Koma tsopano Yesu analankhula ndi ulamuliro womwe mbuyo monse sanayambe waugwiritsa nchito kwa iwo. Iwo anadziwa kuti kutsutsa kopitirira mbali yawo kukhala kopanda phindu, ndipo mwa kachetechete iwo anatembenuka ndikumapita kunyanja.” —The Desire of Ages, p. 378

b. Tsiku lotsatira chitatha kuchitika chozizwitsa, kodi ndi chiyani chimene anthu anachita? Yohane 6: 22-25.

“Chozizwa cha mikate chinafalitsidwa pafupi ndi patali, ndipo mmamawa kwambiri wa tsiku lotsatira anthu ambiri anabwera ku Betsaida kuti azawone Yesu. Iwo adabwera mwa unyinji, kudzera pa ntunda ndi pa nyanja. Iwo amene anali atamusiya usiku wapitawo, akuyembekezera kuti akamupezabe ali pomwepo; popeza padalibe bwato lomwe angagwiritse nchito kuti apite tsidya linalo. Koma kufunafuna kwawo kunali kopanda phindu, ndipo ambiri anabwerera ku Kapernao, napitiriza kumufunafuna Iye.

“Munthawi imeneyi Iye anali atafika ku Genessarete, pambuyo pa tsiku limodzi chabe. Mwachangu pamene zinangodziwika kuti wafika, anthuwa 'adathamangira dera lonselo nayamba kunyamula anthu odwala pa akama ao, kufika nao kumene anamva kuti analiko Iye.' Maliko 6:55.”—Ibid., pp.383, 384


Lachitatu , Epulo 1

3. ZOLINGA ZABWINO, THANDIZO LAUMULUNGU

a. Kodi ndi uthenga wachindunji komabe ozusa malingaliro otani umene Yesu anaupereka ku khamu la anthu? Yohane 6:26, 27.

“Yesu sanakhutitse khumbo lawo. Iye mokhumudwa anati, ‘Mundifuna Ine, si chifukwa munaona zizindikiro, koma chifukwa munadya mkate, nimunakhuta.’

Iwo samamufunafuna iye ndi zolinga zoyenera; koma chifukwa choti anadyetsedwa, iwo amayembekezerabe kulandira zinthu zakanthawi kudzera mukulumikizana ndi Iye. Mpulumutsi anawapempha iwo kuti, ‘Gwirani nchito si chifukwa chacakudya chimene chitayika koma cha chakudya chimene chitsalira ku moyo wosatha.’ Musamangofunafuna kungokhala ndi mwayi woti mupindule zinthu zakuthupi. Chisakhale cholinga chanu chachikulu kupedza zinthu za moyo uno womwe tikukhalawu basi, koma funafunani chakudya cha uzimu, inde nzeru zimene zingapirire kufikira ku moyo wosatha.”—The Desire of Ages, p. 384

b. Kodi ndi funso lanji limene Ayuda anamufunsa Yesu lokhudzana ndi ntchito za Mulungu? Yohane 6:28. Fotokozani yankho limene Ambuye adapereka. Yohane 6:29.

“Kwa kamphindi chidwi cha omvetsera chinazutsidwa. Iwo anati, 'Tichite chiyani, kuti tichite ntchito za Mulungu?’ Iwo anali akugwira ntchito zambiri komanso zolemetsa kuti azidziyamikira iwo okha kwa Mulungu; Ndipo anali okonzeka kumva mwambo watsopano womwe kudzera mu iwo iwo atha kupedza kuyenera kwakukulu. Funso lawo limatanthauza kuti, kodi ife tidzatani kuti tikhale oyenera kumwamba? Kodi ndi mtengo wanji womwe ife tikufunikira kulipira ndi cholinga choti tidzapeze moyo umene ukubwerawo?

“‘Yesu adayankha nati kwa iwo, ntchito ya Mulungu ndi iyi, kuti mukhulupirire Iyeyo amene Iye adamutuma.’ Mtengo wa kumwamba ndi Yesu. Njira yopita kumwamba ndiyo kudzera mwa chikhulupiriro mwa 'Mwanawankhosa wa Mulungu, amene achotsa tchimo la dziko lapansi.' Yohane 1:29." — Ibid., p. 385

“Kulapa ndiko kutembenuka kuchoka ku undekha kupita kwa Khristu; Ndipo pamene Ife tamulandira Khristu kuti kudzera mu chikhulupiriro Iye akhoza kukhala moyo wake mwa ife, ntchito zabwino zidzawonekera.” —Thoughts From the Mount of Blessings, p. 87.

“Ambuye athandize anthu ake kuti azindikire kuti pali ntchito yofunika kuti ichitidwe. . .. Mnyumba, mu mpingo, komanso mdziko lapansi iwo akuyenera kugwira ntchito ntchito za Khristu. Iwo sanasiyidwe kuti agwire ntchitozi okha. Angelo ndi owathandiza awo. Ndipo Kristu ndiye mthandizi wawo."— Testimonies for the Church, vol. 8, p. 18.


Lachinayi , Epulo 2

4. MKATE WAKUMWAMBA

a. Kodi ndi chizindikiro chanji chimene Ayuda amafuna nanga kodi ndi choona chanji cha mumbiri chimene iwo anachinena? Yohane 6:30, 31. Kodi Yesu anati chiyani za mkate wochokera kumwamba? Yohane. 6:32, 33.

“Ayudawo amalemekeza Mose monga wopereka manna, Kupereka matamando ku chida, osamamuwona Iye amene kudzera mwa Iye ntchitoyi idakwaniritsidwa. Makolo awo anali atang'ung'udza motsutsa Mose, ndipo anali kukaikira ndi kumakana utumiki wake wa Umulungu. Tsopano mu Mzimu womwewo anaawo akana Yemwe akufotokoza uthenga wa Mulungu kwa iwo eni. ‘Chifukwa chake Yesu adati kwa iwo, indetu, indetu, ndinena kwa inu, si Mose amene anakupatseni inu mkate wa kumwamba.’ Wopatsa manna anali atayimirira pakati pawo. Anali Khristu Mwini Yemwe adatsogolera Ahebri kudutsa m'chipululu, ndipo tsiku lililonse anali kuwadyetsa iwo ndi mkate wochokera kumwamba. Chakudya chimene chija chinali choyimirira cha mkate weniweni wochokera kumwamba. Mzimu wopatsa moyo, woyenda kuchokera ku chizalo cha umulungu, ndiye Manna weniweni." —The Desire of Ages, pp. 385, 386.

b. Pokhala ndi malingaliro awo ogokhazikika pa mkate wachilengedwe, wakuthupi, kodi ndi pempho lanji limene iwo adalipereka- nanga kodi ndi chiyani chimene Ambuye anafotokoza? Yohane 6: 34-36.

“Chisanzo chomwe Khristu adagwiritsa ntchito chinali chodziwika kwa Ayuda. Mose, kuzera mukuuzira kwa Mzimu Woyera, ananena kuti, ‘munthu sakhala wamoyo ndi mkate wokha, koma munthu akhala wa moyo ndi zonse zakutuluka m’kamwa mwa Yehova.’ Ndipo mneneri Yeremiya analemba kuti, 'Mau anu anapezeka, ndipo ndinawadya; mau anu anakhala mwa ine chikondwerero ndi chisangalaro ca mtima wanga.’ Deuteronomo 8:3; Yeremiya 15:16. Arabi iwo eni anali ndi muyambi woti, kudya kwa Mkate, mu tanthauzo lake la uzimu, kunali kuwerenga kwa malamulo; ndi kuchita nchito zabwino; ndipo kawirikawiri zimanenedwa kuti pa kubwera kwa Mesiya a Israyeli onse azadyesedwa. Ziphunzitso za aneneri zimamvekesa bwino phunziro lokuya la uzimu la chozizwitsa cha mikate. Phunziro limeneli Khristu amafunisisa kuti atsegule kwa omvetsera ake mu sunagoge. Ngati iwo akanamvesesa malemba, Iwo akanatha kuzindikira mawu ake pamene Iye anati, ‘Ine ndine mkate wa moyo.’ Tsiku limodzi lapitalo, unyinji waukulu, utafooka ndi kutopa, udadyetsedwa mkate womwe Iye adapereka. Monga momwe kuchokera ku mkate uja iwo adalandira mphamvu zakuthupi ndi kusisimutsidwa, choteronso kuchokera kwa Khristu iwo akhoza kulandira mphamvu zauzimu kufikira ku Moyo Wamuyaya."—Ibid., p. 386


Lachisanu , Epulo 3

5. KUUKITSIDWA NDI MOYO WAMUYAYA

a. Kodi ndi malonjezo awiri anji ogwirizana amene akuperekedwa kwa iwo amene azilumikiza okha ndi Khristu – nanga ndi motani mmene izi zimabweretsera chiyembekezo kwa wochimwa aliyense? Yohane 6: 37-40.

“Onse amene adamlandira Iye mwa chikhulupiriro, [Yesu] adati, azakhala ndi moyo wamuyaya. Palibe ndi mmodzi yense amene azatayika."—The Desire of Ages, p. 387

“Musamvere lingaliro la mdani kuti mukhale kutali ndi Khristu mpaka mutadzipanga nokha kukhala wabwino; kufikira mutakhala wabwino mokwanira kubwera kwa Mulungu. Ngati inu mungayembekezere kufikira nthawi imeneyo, simuzabwera konse. Pamene Satana aloza kuzobvala zanu zokuda, bwerezani lonjezo la Yesu loti, ‘Ndipo iye wakudza kwa ine sindizamutaya iye kunja.’ Yohane 6:37. Muuzeni mdani kuti mwazi wa Yesu Khristu umayeretsa kuchoka ku uchimo wonse. Pangani pemphero la Davide kukhala lanu, ‘Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndizayera; Munditsuke ndipo ndizakhala wa mbu woposa matalala.’ Masalimo 51: 7.

“Nyamukani nimupite kwa abambo anu. Adzakumana nanu mudakali patali. Ngati inu mungatenge khwerero ngakhale limodzi chabe kupita kwa Iye molapa. Iye azathamanga kuzakukhumbatirani inu mumanja a chikondi chopanda malire. Khutu Lake ndi loseguka ku kulira kwa mtima wolapa. Kupempha koyambirira komweko kwa mumtima kwa Mulungu kumaziwika kwa Iye. Palibe pemphero limene linapempheredwapo, ngakhale monon’gona motani, palibe msozi umene unagwetsedwa, ngakhale mtseri motani, palibe khumbo loona mtima lofuna Mulungu limene limakhalapo, ngakhale mofooka, muzonse Mzimu wa Mulungu umapita kukakumana ndi zonsezi. Ngakhale lisanaperekedwa pemphero kapena

kukhumba kwa mtima kusanaziwike, chisomo cha Khristu chimapita kuti chikakumane ndi chisomo chimene chikugwira nchito pa mzimu wa munthu.” – Christ’s Object Lessons, pp. 205, 206.

b. Kodi Ayuda osakhulupirira anang'ung'udza chiyani nanga kodi Yesu analonjeza chiyani kwa amene akhulupirira mwa Iye? Yohane 6: 41-51.


Lachisanu ndi chimodzi , Epulo 4

6. MAFUNSO OBWEREZA PAWEKHA

1. Patsogolo pa chozizwitsa cha mikate, kodi otsatira a Khristu adafuna kuchita chiyani?

2. Fotokozani cholinga chachikulu cha khamu lomwe limamutsatira Yesu.

3. Fotokozani mawu a Yesu mu Yohane 6:29.

4. Kodi ndi chisanzo chanji chomwe Khristu anagwiritsa ntchito kuwonetsera gwero la moyo wa uzimu?

5. Kodi atsogoleri achiyuda anaonetsa bwanji kuweruziraru koipa kolimbana ndi Khristu?

 <<    >>