Loyamba
, Epulo 13
1. MOYO WA PAKHOMO WA YESU
a. Kodi Yesu anakumana ndi bvuto lanji lalikulu kunyumba kwake komwe? Yohane 7:5.
“Adakali wamng’ono kwambiri, Yesu anayamba kuchita zinthu mwa Iye yekha mukupanga khalidwe Lake, ndipo ingakhale ulemu ndi chikondi kwamakolo ake sizinamulepheretse kumvera mawu a Mulungu. 'Kwalembedwa' chinali chifukwa Chake cha mchitidwe uli wonse wosiyana ndi miyambo yam’banja mwawo. Koma chikoka cha arabi chinapangitsa moyo Wake kukhala wowawa. Ingakhale mu unyamata Wake anayenera kuphunzira phunziro lovuta la kukhala chete ndi kupirira moleza mtima.
“Abale ake, omwe amatchedwa ana a Yosefe, anali kumbali ya arabi. Iwo amakakamira kuti miyambo iyenera kumatsatiridwa, monga ngati inali zofuna za Mulungu. Iwo amaonanso kuti malamulo a anthu ndi apamwamba kuposa mawu a Mulungu, ndipo amakwiya kwambiri ndi kufotokoza momveka bwino kwa Yesu posiyanitsa pakati pa bodza ndi choonadi. Kumvera kwake mosamalitsa ku malamulo a Mulungu iwo amakutsutsa kuti ndi kuuma mtima. Iwo amadabwa ndi chidziwitso ndi nzeru zimene Iye amasonyeza poyankha arabi. Iwo ankadziwa kuti Iye sanalandire maphunziro kuchokera kwa anzeru, komabe iwo samalephera kuoona kuti Iye anali mphunzitsi kwa iwo. Iwo anazindikira kuti maphunziro Ake anali amtundu wa pamwamba kuposa awo. Koma iwo sanazindikire kuti Iye anali ndi mwayi wofika kumtengo wamoyo, gwero lachidziwitso chimene iwo anali mbuli.”— The Desire of Ages, p. 86.
Lachiwiri
, Epulo 14
2. ANA A YOSEFE
a. Kodi ndi ganizo lotani lomwe abale a Khristu adapereka kwa Iye poyembekezera Phwando la Misasa la pachaka? Yohane 7:3, 4.
“Abale [ake a Kristu] amaganiza kuti n’kulakwa kuti iye akhale ndi udani ndi anthu a akulu ndi ophunzira a dziko lawo. Iwo ankaona kuti amuna amenewa ayenera kukhala olondola, ndiponso kuti Yesu anali wolakwa podziika yekha m’chidani ndi iwo. Koma iwo anali ataona moyo wake wopanda chilema, ndipo ngakhale iwo sanali kudziika pa mdandanda wa ophunzira Ake, iwo anali atachita chidwi kwambiri ndi ntchito zake. Kutchuka kwake mu Galileya kunali kokhutiritsa ku chikhumbo chawo; iwo ankayembekezerabe kuti Iye adzapereka umboni wamphamvu zake zimene zikanatsogolera Afarisi kuona kuti Iye anali chimene Iye ankadzinenera kukhala. Bwanji ngati Iye akanakhala Mesiya, Kalonga wa Israeli! Iwo ankakondwelera ndi lingaliro limeneli ndi chikhutiro chodzikweza.
“Iwo amkakhumba ichi kwambiri mwa kuti anakakamiza Khristu kupita ku Yerusalemu. ‘Chokani kuno,” iwo anati, ‘ndipo mupite ku Yudeya, kuti ophunzira anunso akapenye ntchito zimene Inu mukuchita. Pakuti palibe munthu wa kuchita kanthu kalikonse mobisa, nafuna iye yekha kudziwika poyera. Ngati muchita izi, dziwonetseni nokha kudziko.’‘Ngati’adawonetsa kukayikira ndi kusakhulupirira. Iwo amamuika Iye kukhala wamantha ndi wofooka. Ngati Iye mwini amkadziwa kuti Iye anali Mesiya, nchifukwa ninji akudzisunga mwa chilendo kumeneku ndikusachitapo kanthu? Ngati Iye analidi ndi mphamvu yotere, bwanji osapita ku Yerusalemu molimba mtima, ndikukadziika molingana ndi kudzinenera kwake? Bwanji osachita mu Yerusalemu ntchito zodabwitsa zosimbidwa za Iye ku Galileya? Iwo adati, musabisale mmadera obisika, ndi kumachita ntchito zanu zamphamvu kukupindulirira anthu wamba ndi asodzi osaphunzira. Dziwonetsereni nokha kulikulu, pindulani ndi chithandizo cha ansembe ndi olamulira, ndikugwirizanitsa mtunduwu pakukhazikitsa ufumu watsopano.”— The Desire of Ages, p. 450.
b. Fotokozani vuto limene nthawi zonse anthu ofatsa akhala akukumana nalo. Masalmo 86:14.
“Abale a Yesu amenewa analingalira mwazolinga zadyera zopezeka kawirikawiri m’mitima ya anthu ofunitsitsa kudzionetsera. Mzimu umenewu unali mzimu womwe umalamulira dziko lapansi. Iwo anakhumudwitsidwa chifukwa, m’malo mofunafuna mpando wachifumu wosakhalitsa, Kristu anadzitcha yekha kukhala mkate wamoyo. Iwo anakhumudwa kwambiri pamene ophunzira ake ambiri anamusiya. Iwo eni adachoka kwa Iye kuthawa mtanda wakuvomereza zomwe ntchito Zake zidawululira—kuti Iye anali Wotumidwa wa Mulungu.”—Ibid., p. 451.
Lachitatu
, Epulo 15
3. KUKANGANA ZA YESU
a. Kodi ndi malingaliro otsutsana otani amene anadzutsidwa okhuzana ndi za Yesu? Yohane 7:11, 12.
“Kuchokera ku Yerusalemu mbiri yazozizwitsa za Kristu inafalikira kuli konse kumene Ayuda anamwazikana; ndipo ngakhale miyezi ingapo sanakhale nawo m’maphwando, chidwi cha Iye sichinazilale. Anthu ambiri ochokera kumadera onse a dziko lapansi anabwera ku Phwando la Misasa ndi chiyembekezo choti adzamuone. Kumayambiriro kwa phwando anthu ambiri anamfunsa za Iye. Afarisi ndi olamulira anali kuyembekezera kuti Iye abwera, ndi kuyembekezera mwayi woti amutsutse Iye. Iwo adafunsa mwankhawa kuti, ‘Ali kuti Iyeyo?’ koma palibe amene amkadziwa. Lingaliro la Iye linali la pamwamba kwambiri mu malingaliro a onse. Chifukwa cha mantha kuwopa ansembe ndi olamulira, palibe amene adalimba mtima kumuvomereza kuti Iye ndi Mesiya, koma paliponse panali kukambirana mwakachetechete koma mozama za Iye. Ambiri ankamumuikira kumbuyo kuti ndi munthu wotumidwa kuchokera kwa Mulungu, pamene ena ankamunyoza Iye kuti ndi wonyenga wa anthu.”— The Desire of Ages, pp.451, 452.
b. Kodi motani mmene Yesu anakhazikitsira chete maganizo otsutsana okhudza Iye mwini? Yohane 7:14-18; Luka 4:32.
“Pakati pa phwando, pamene chiyembekezo chokhuzana ndi Iye chinali pa chimake, Iye analowa m’bwalo la Kachisi pamaso pa khamu la anthu. Chifukwa cha kusakhalapo kwake pa phwandolo, anthu amafotokoza kuti akuopa kudziika yekha mu mphamvu ya ansembe ndi olamulira. Onse anadabwa ndi kupezeka kwake. Mawu onse anatonthola. Onse anadabwa ndi kulemekezeka ndi kulimba mtima kwakupirira Kwake pakati pa adani amphamvu amene anali ndi ludzu lofuna moyo Wake.
“Ataimirira motere, phata la chikoka chakhamu lalikululo, Yesu analankhula kwa iwo mwakuti palibe munthu wina ali yense analankhulapo motere. Mawu ake anasonyeza chidziwitso cha malamulo ndi zikhazikitso za Israyeli, za utumiki wa nsembe ndi ziphunzitso za aneneri, choposatu chija cha ansembe ndi arabi. Iye anagamula nadutsa zochinga za myambo ndizikhazikitso zawo. Zochitika za moyo wa mtsogolo zinkawoneka ngati zatambasulika pamaso Pake. Monga munthu wopenya Wosaoneka, Iye analankhula za pa dziko lapansi ndi zakumwamba, munthu ndi Mulungu, ndi ulamuliro wotsimikizika. Mawu ake anali omveka bwino ndi okhuza kwambiri; ndipo kawirinso, monga ku Kapernawo, anthu anazizwa ndi chiphunzitso cace; 'pakuti mawu ake anali ndi mphamvu.' Luka 4:32. Onse anazizwa ndi chidziwitso chake cha malamulo ndi mauneneri.”—Ibid., pp. 452, 453.
Lachinayi
, Epulo 16
4. CHIDANI CHOLIMBANA NDI WOYERAYO
a. Kodi Yesu anazindikira chiyani mwa arabi ndipo Iye anawafunsa iwo funso lotani? Yohane 7:19.
“Yesu anapatsa arabi umboni wa umulungu Wake kudzera mukuwaonetsera kuti amawerenga mitima yawo. Kuyambira pa machiritso a ku Betesda iwo anali akumkonzekera Iye imfa. Motero iwo eniwo analikuswa lamulo limene ankati anali kuliteteza. ‘Kodi Mose sanakupatseni inu chilamulo,’ Iye anatero, ‘ndipo palibe mmodzi wainu amene amasunga chilamulo? M’chifukwa chiyani mufuna kundipha Ine?”— The Desire of Ages, p. 456.
b. Mu kuyankha kwawo kwa Khristu, kodi ndi za chiyani zimene arabi anamuneneza Iye—ndipo ndimotani momwe Iye anayankhira? Yohane 7:20-23.
“Kubodza la [kuti ntchito Zake zodabwitsa zinali kusonkhezeredwa ndi mzimu woipa] Kristu sanalabadire. Iye anapitiriza kuwasonyeza kuti ntchito Yake yochiritsa pa Betsaida kuti inali yogwirizana ndi lamulo la Sabata, ndipo inalungamitsidwa ndi kumasulira kumene Ayudawo anaika pa chilamulo. Iye anati, ‘Mose anakupatsani inu mdulidwe; . . . ndipo mudula munthu tsiku la Sabata.’ Malinga ndi lamulo, mwana aliyense ayenera kudulidwa patsiku la chisanu ndi chitatu. Ngati nthawi yoikidwiratu ifika pa Sabata, mwambowo uyenera kuchitidwa. Koposa kotani nanga kukuyenera kukhala kogwirizana ndi mzimu walamulo kumupanga munthu kukhala ‘wangiro kwanthunthu pa Sabata.’ ”— Ibid., pp. 456, 457.
c. Fotokozani tanthauzo lalikulu la chenjezo lotsatira la Kristu. Yohane 7:24.
“Olamulira anakhala chete; ndipo ambiri a anthuwo adati, “Si uyu kodi afuna kumupha uja? Koma tawonani, Iye alankhula molimbika mtima, ndipo iwo sakunena kanthu kwa Iye. Kodi olamulira akudziwa mwandithu kuti ameneyi ndiye Kristu? ”—Ibid., p. 457.
“[Khristu] sayang’ana maonekedwe akunja; Saweruza monga momwe munthu amaweluzira. Iye salemekeza munthu kutengera udindo, luso, maphunziro, kapena ntchito yomwe munthu amagwira. ‘Ndidzayang’ana kwa munthuuyu,’ akutero, ‘ingakhale kwa munthu wosauka, ndi wa mzimu wosweka, nanthunthumira ndi mawu anga. ”— The Signs of the Times, October 21, 1897.
Lachisanu
, Epulo 17
5. CHIWELUZO CHA MUNTHU KUSIYANITSA NDI CHA MULUNGU
a. Kodi ndi motani mmene Malemba amaonetsera m’khalidwe wa maganizo a anthu m’dziko lino— kawirikawiri monga momwe zimaonekera m’nthawi zakale, koma makamaka lero lino? Yesaya 59:14, 15.
“Mabungwe a zoyipa akuphatikizana mphamvu zawo ndi kugwirizana. Iwo akudzilimbitsa kukonzekera mkangano waukulu wotsiriza. Kusintha kwakukulu kudzachitika posachedwapa pa dziko lapansi, ndipo migwirizano womaliza udzakhala ofulumira kwambiri. . . ..
“Mdani wapambana popotoza chilungamo, ndikudzaza mitima ya anthu ndi chikhumbo cha phundu lakudzikonda. . . .. Kulira kwa anthu ovutika ndi anjala kukubwera pamaso pa Mulungu, pamene kudzera mumtundu uli wonse wakuponderezana ndi kulanda anthu uunjika chuma chambiri.”— Testimonies for the Church, vol. 9, pp. 11, 12.
b. M’kati mwa chipwirikiti, n’chifukwa chiyani tingadalire njira za Mulungu? Yesaya 55:8, 9.
“Ngakhale malingaliro okhala ndi malire a anthu ali osakwanira kulowa mu uphungu wa Wopanda malire, kapena kumvetsetsa bwino momwe zifuno Zake zimagwirira ntchito, komabe nthawi zambiri ndi chifukwa cha zolakwika zina kapena kunyalanyaza kwawo komwe kumawapatsa kusamvetsetsa mauthenga a Kumwamba. Kawirikawiri malingaliro aanthu, ngakhalenso a atumiki a Mulungu, amachititsidwa khungu ndi malingaliro a anthu, miyambo ndi ziphunzitso zonyenga za anthu, kotero kuti amatha kuzindikira pang’ono zinthu zazikulu zimene Iye wavumbulutsa m’mawu Ake.”— The Great Controversy, p. 344, 345.
“Cholinga cha Mulungu kwa ana ake ndi chapamwamba kuposa momwe malingaliro amunthu angafikire. Iye wapereka m’chilamulo Chake chopatulika kukhala chithunzithunzi cha khalidwe Lake.”— Testimonies for the Church, vol. 8, p. 63.
Lachisanu ndi chimodzi
, Epulo 18
6. MAFUNSO OBWEREZA PAWEKHA
1. Fotokozani khalidwe la pakhomo pamene Yesu analeledwa.
2. Kodi ndi motani momwe chidwi cha abale ake a Khristu chimabwerezedwera masiku ano?
3. Kodi ndi malingaliro otsutsana otani amene anafalitsidwa ponena za Yesu?
4. Fotokozani mzimu umene arabi anaonetsa kwa Yesu.
5. Fotokozani kusiyana kwakukulu pakati pa njira za anthu ndi za Mulungu.