a. Kodi ndifunso lanji limene Yesu anamufunsa Mzimayi atatha kuchoka omuneneza ake-nanga ndimotani mmene njira yake ya kuchitila ndi nkhaniyi ingakakhuzire moyo wake wa mzimayiyu? Yohane 8:10, 11.“Mzimayi anaima pamaso pa Yesu, odzazidwa ndimantha. Mawu ake oti, ‘iye amene mwainu ali opanda chimo, ayambe kumponya mwala,’ Anabwela kwa iye ngati chigamulo cha imfa. Iye sanayelekeze kutukula maso ake kuyang’ana nkhope ya Mpulumutsi, Koma mwakachetechete anayembekezera imfa yake. Modabwa iye anaona omuneneza ake akuchoka opanda mawu ndi okhazikitsidwa chete; kenako mau achiyembekezo anafika mmakutu ake,`inenso sindikutsutsa iwe; pita; kuyambila tsopano usachimwenso.’ Mtima wake unasukunulidwa, ndipo, ndi pozigwetsa yekha pamapazi a Yesu, iye analira ndichikondi chake chachiyamiko ndimisozi yowawidwa mtima anavomeleza machimo ake.“Ichi kwa iye chinali chiyambi cha moyo watsopano, moyo wachiyelo ndi mtendele, wozipereka kwa Mulungu. Mukukweza kwa moyo wakugwa umenewu, Yesu anachita chozizwa chachikulu kwambiri kupotsera kuchilitsa nthenda yaikulu kwambiri yakuthupi; iye anachilitsa nthenda yauzimu imene ili yofikila kuimfa yamuyaya. Mzimayi wolapayu anakhala mmodzi waotsatira ake ozipereka kwambiri. Ndi chikondi chozipereka yekha nsembe iye anaonetsera chiyamiko chake pachifundo chake chakukhululukira. Kwa mzimayi olakwitsayu dziko linali ndi chiweluzo ndi kunyoza basi, koma Osalakwayo anamvera chisoni kufooka kwake ndipo anamuyandikira iye ndikumutambasulira dzanja la chithangato. Amene Afalisi achinyengo anatsutsa, Yesu anamulamulira iye kuti, `pita, kuyambira tsopano usakachimwenso.’”- The Ministry of Healing, p. 89.“Mumchitidwe wake wakukhululukira mzimayiyu ndikumulimbikitsa iye kuti akhale moyo wabwino, khalidwe la Yesu linawala ponseponse mukukongola kwa chilungamo chodzadza. Pamene Iye sabvomeleza chimo, kapena kuchepetsa kuipa kwachimo, iye amafunitsitsa osati kususa, koma kupulumutsa. Kwa mzimayi wolakwayu dziko linali ndi kusutsa ndi kunyodza basi; koma Yesu akuyankhula mawu achitonthozo ndi chiyembekezo.”- The Desire of Ages, p. 462b. Fotokozani zotsatira zachisomo chopulumutsa cha Khristu. Luka 7:37-40, 47, 48.“Yesu amadziwa zochitikachitika zamoyo winaulionse. Monga Kukula kwa kuipisisa kwa ochimwa momwemonso ndi momwe amafunira mpulumutsi. Mtima wake wachikondi ndi chisoni cha Umulungu ukukoka koposa wina aliyense iye amene ndiosowelatu thandizo ogwidwa mmisampha ya mdani. Ndimwazi wa iye yekha iye anasindikiza chizindikiro pamapepala akumasula mtundu waanthu.”-The Ministry of Healing, pp. 89–90.